-
“Mulungu Ndi Amene Anayamba Kutikonda”Yandikirani Yehova
-
-
MUTU 23
“Mulungu Ndi Amene Anayamba Kutikonda”
1-3. Kodi ndi zinthu ziti zomwe zinachititsa kuti imfa ya Yesu ikhale yosiyana ndi imfa ya munthu aliyense?
TSIKU lina zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, munthu wina wosalakwa anaimbidwa mlandu, anamupeza wolakwa pa milandu imene sanapalamule ndipo kenako anamuzunza mpaka kumupha. Sanali munthu woyamba kuphedwa mwankhanza ndiponso mopanda chilungamo, koma n’zomvetsa chisoni kuti sanalinso womaliza. Komabe imfa yake inali yosiyana kwambiri ndi imfa ya munthu aliyense.
2 Pamene munthuyo ankavutika kwambiri, kutatsala maola ochepa kuti afe, kumwamba kunachitika zinthu zodabwitsa zomwe zinasonyeza kuti imfa yake inali yapadera. Ngakhale kuti anali masana, mwadzidzidzi kunagwa mdima. Wolemba mbiri wina anati pa tsikulo “dzuwa linachita mdima.” (Luka 23:44, 45) Munthuyo atangotsala pang’ono kufa ananena mawu osaiwalika akuti: “Ndakwaniritsa chifuniro chanu!” Zoonadi, imfa yake inakwaniritsa chinthu chofunika kwambiri. Nsembe imene iye anapereka inali njira yaikulu kwambiri yosonyezera chikondi yoti palibe munthu aliyense anachitapo.—Yohane 15:13; 19:30.
3 Munthuyu ndi Yesu Khristu. Anthu ambiri amadziwa bwino mmene anavutikira ndiponso mmene anafera pa Nisani 14, mu 33 C.E., pa tsiku lamdimali. Komabe, nthawi zambiri anthuwa amanyalanyaza mfundo yofunika kwambiri. Ngakhale kuti Yesu anavutika kwambiri, Yehova ndi amene anavutika kuposa pamenepa. Pa tsikuli, iye analolera kudzimana kwambiri ndipo anasonyeza chikondi chachikulu kuposa chimene munthu aliyense anasonyezapo. Kodi anachita chiyani? Yankho la funsoli litiphunzitsa zambiri zokhudza khalidwe lofunika la Yehovayo, lomwe ndi chikondi.
Njira Yaikulu Kwambiri Imene Yehova anasonyezera Chikondi
4. Kodi msilikali wa Chiroma anadziwa bwanji kuti Yesu sanali munthu wamba, nanga ananena kuti chiyani?
4 Mtsogoleri wa asilikali a Roma yemwe ankayang’anira kuphedwa kwa Yesu anadabwa kwambiri ndi mdima umene unagwa Yesu asanafe ndiponso chivomerezi champhamvu chimene chinachitika Yesuyo atangofa. Iye ananena kuti: “Ndithu, uyu analidi Mwana wa Mulungu.” (Mateyu 27:54) N’zodziwikiratu kuti Yesu sanali munthu wamba. Msilikaliyo anathandiza pakuphedwa kwa Mwana wobadwa yekha wa Mulungu Wam’mwambamwamba. Koma kodi Mwana ameneyu anali wofunika bwanji kwa Atate ake?
5. Kodi Yehova ndi Mwana wake anakhala limodzi kumwamba kwa nthawi yaitali bwanji?
5 Baibulo limati Yesu ndi “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse.” (Akolose 1:15) Tangoganizani, Mwana wa Mulunguyu anali ndi moyo zinthu zonse zimene timaona m’chilengedwechi zisanakhalepo. Ndiye kodi Yehova ndi Yesu anakhala limodzi kwa nthawi yaitali bwanji? Asayansi ena amakhulupirira kuti chilengedwechi chakhala chilipo kwa zaka 13 biliyoni. Kwa anthufe, n’zovuta kumvetsa kuti nthawi imeneyi ndi yaitali bwanji. Komabe ngati zimene asayansi amanenazi ndi zoona, ndiye kuti Mwana wa Mulungu wakhala alipo kwa zaka zoposa 13 biliyoni. Ndiye kodi ankachita chiyani pa nthawi yonseyi?
6. (a) Kodi Mwana wa Yehova ankatani asanabwere padzikoli? (b) N’chiyani chikusonyeza kuti Yehova ndi Mwana wake amakondana kwambiri?
6 Mwana ameneyu ankagwira ntchito mosangalala ngati “mmisiri waluso” wa Atate ake. (Miyambo 8:30) Baibulo limati: “Palibe chinthu ngakhale chimodzi chimene chinakhalapo popanda [Mwanayo].” (Yohane 1:3) Choncho Yehova ndi Mwana wake anagwira ntchito limodzi popanga zinthu zina zonse. Imeneyitu inali nthawi yosangalatsa kwambiri. Tonsefe timadziwa kuti kholo limakondana kwambiri ndi mwana. Ndipo chikondi “chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.” (Akolose 3:14) Choncho popeza Yehova ndi Yesu anakhala limodzi kwa nthawi yaitali, ankakondana kwambiri kuposa mmene tingaganizire. Apa n’zodziwikiratu kuti chikondi chinagwirizanitsa kwambiri Yehova Mulungu ndi Mwana wake kuposa mmene zilili ndi anthu alionse omwe anagwirizanapo.
7. Yesu atabatizidwa, kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti anasangalala ndi zimene Mwanayu anachita?
7 Ngakhale zinali choncho, Atate anatumiza Mwana wake padzikoli kuti adzabadwe ngati mwana wakhanda. Zimenezi zikusonyeza kuti kwa zaka zambiri Yehova analolera kuti asakhale ndi Mwana wakeyu kumwamba. Ali kumwambako, ankaona pamene Yesu ankakula n’kukhala munthu wangwiro ndipo ankachita chidwi ndi zimene zinkachitika pa moyo wake. Ali ndi zaka pafupifupi 30, Yesu anabatizidwa. Kodi Yehova anamva bwanji Mwana wakeyu atachita zimenezi? Iye analankhula kuchokera kumwamba kuti: “Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa ndipo amandisangalatsa kwambiri.” (Mateyu 3:17) Yehova anasangalala kwambiri ataona kuti Yesu wachita mokhulupirika zonse zimene zinanenedweratu ndiponso zonse zimene anamuuza kuti adzachite.—Yohane 5:36; 17:4.
8, 9. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene zinachitikira Yesu pa Nisani 14, 33 C.E., nanga Atate ake akumwamba zinawakhudza bwanji? (b) N’chifukwa chiyani Yehova analola Mwana wake kuti avutike ndiponso kufa?
8 Koma kodi Yehova anamva bwanji pa Nisani 14, mu 33 C.E.? Mwachitsanzo, kodi anamva bwanji pamene Yesu anaperekedwa komanso pamene gulu la anthu linabwera n’kudzamugwira usiku? Nanga anamva bwanji pomwe anzake anamuthawa kenako n’kuyamba kuzengedwa mlandu mosemphana ndi malamulo? Kodi anamva pamene ankamunyoza, kumulavulira, kumumenya ndiponso kumukwapula mpaka kumsana kwake kumatuluka magazi? Nanga anamva bwanji pamene ankakhomerera manja ndi miyendo yake pamtengo, n’kumusiya pompo anthu akumunyoza? Kodi Yehova anamva bwanji pamene Mwana wake wokondedwa anamulirira pamene ankamva ululu woopsa? Nanga anamva bwanji pamene Yesu anamalizika? Ndipo kodi anamva bwanji pamene kwa nthawi yoyamba kuchokera pamene zinthu zonse zinalengedwa, Mwana wake wokondedwayu kunalibeko?—Mateyu 26:14-16, 46, 47, 56, 59, 67; 27:38-44, 46; Yohane 19:1.
9 Timasowa chonena ndipo sitingathe kufotokoza ululu umene Yehova anamva pamene ankaona mwana wake akuzunzidwa komanso kufa. Zimene tingathe kufotokoza ndi chifukwa chake Yehova analola kuti zimenezi zichitike. N’chifukwa chiyani Yehova analolera kuti amve kupweteka chonchi? Iye akutiuza chifukwa chake pa Yohane 3:16, vesi lofunika kwambiri limene ena amati ndi chidule cha uthenga wonse wabwino wonena za Yesu. Vesili limati: “Mulungu anakonda kwambiri dziko moti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense womukhulupirira asawonongedwe koma akhale ndi moyo wosatha.” Choncho Yehova anachita zonsezi chifukwa cha chikondi. Anasonyeza chikondi chachikulu kuposa wina aliyense pamene anatipatsa mphatso yapadera. Iye anatumiza Mwana wake kuti adzavutike n’kutifera.
“Mulungu . . . anapereka Mwana wake wobadwa yekha”
Tanthauzo la Chikondi
10. Kodi anthu amafunika chiyani, nanga n’chifukwa chiyani n’zovuta kudziwa tanthauzo lenileni la mawu akuti “chikondi”?
10 Kodi mawu akuti “chikondi” amatanthauza chiyani? Ambiri amanena kuti anthu amafunikira kwambiri chikondi kuposa chilichonse. Kuchokera pamene abadwa mpaka pa nthawi yomwalira, anthu amafunitsitsa kukondedwa, amasangalala akamakondedwa komanso amawonda mwinanso kufa kumene chifukwa chosowa chikondi. Ngakhale zili choncho, n’zovuta kwambiri kufotokoza kuti chikondi n’chiyani. Anthu amalankhula zambiri zokhudza chikondi. Pali mabuku, ndakatulo ndiponso nyimbo zambirimbiri za chikondi. Koma si nthawi zonse pamene zimenezi zimathandiza anthu kudziwa tanthauzo la chikondi. Kungoti mawuwa amagwiritsidwa ntchito kwambiri moti tanthauzo lake lenileni limaoneka kuti silingadziwike.
11, 12. (a) Kodi Baibulo limatithandiza bwanji kumvetsa tanthauzo la chikondi? (b) Kodi ndi mitundu iti ya chikondi yomwe inkatchulidwa m’Chigiriki chakale, nanga ndi mawu ati otanthauza “chikondi” amene anagwiritsidwa ntchito kwambiri m’Malemba a Chigiriki a Chikhristu? (Onaninso mawu am’munsi.) (c) Kodi mawu akuti a·gaʹpe amatanthauza chiyani?
11 Komabe, Baibulo limatithandiza kumvetsa bwino kuti chikondi n’chiyani. Dikishonale ina yomasulira mawu a m’Baibulo inati: “Chikondi chimadziwika ndi ntchito zake.” (Vine’s Expository Dictionary of New Testament Words) Baibulo limatiuza zambiri zokhudza zimene Yehova anachita posonyeza anthu chikondi ndiponso kukoma mtima. Mwachitsanzo, n’chiyaninso chingatithandize kumvetsa khalidweli kuposa chinthu chamtengo wapatali chimene Yehova anachita chomwe takambirana chija? M’mitu ikubwerayi, tiona zitsanzo zinanso zofotokoza mmene Yehova anasonyezera chikondi. Tingaphunzirenso zambiri kuchokera pa mawu a chilankhulo choyambirira omwe m’Baibulo anawamasulira kuti “chikondi.” M’Chigiriki chakale munali mawu 4 otanthauza “chikondi.”a Pa mawu amenewa, mawu amene anawagwiritsa ntchito kwambiri m’Malemba a Chigiriki a Chikhristu ndi akuti a·gaʹpe. Dikishonale ina yomasulira mawu a m’Baibulo imati amenewa ndi “mawu amphamvu kwambiri onena za chikondi omwe munthu angawaganizire.” Chifukwa chiyani tikutero?
12 Mawu akuti a·gaʹpe amanena za chikondi chimene munthu amasonyeza chifukwa chotsatira mfundo zinazake. Choncho sikuti munthu amasonyeza chikondichi chifukwa chongotengeka. Timachita kusankha kuti tisonyeze chikondi chimenechi chifukwa timadziwa kuti kuchita zimenezi n’koyenera. Munthu amene ali ndi chikondi cha a·gaʹpe amaganizira kwambiri zofuna za ena kuposa zake. Mwachitsanzo, taonaninso lemba la Yohane 3:16. Kodi “dziko” limene Mulungu analikonda kwambiri moti mpaka anapereka Mwana wake wobadwa yekha ndi chiyani? Amenewa ndi anthu amene akhoza kuwomboledwa. Ena mwa anthu amenewa amachita zinthu zosasangalatsa Mulungu. Kodi Yehova amakonda aliyense wa anthuwa ngati mnzake wapamtima, mofanana ndi mmene ankakondera Abulahamu? (Yakobo 2:23) Ayi, koma mwachikondi Yehova amachitira zabwino aliyense, ngakhale pamene zingachititse kuti aluze zambiri. Amafuna kuti anthu onse alape n’kusiya kuchita zoipa. (2 Petulo 3:9) Ambiri amachitadi zimenezi ndipo iye amasangalala n’kuyamba kuwaona kuti ndi anzake.
13, 14. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti nthawi zambiri chikondi cha a·gaʹpe chimakhudza mmene munthu akumvera komanso chimakhala chochokera mumtima?
13 Komabe anthu ena ali ndi maganizo olakwika okhudza chikondi cha a·gaʹpe. Amaganiza kuti ndi chikondi chimene anthu amangochisonyeza potengera zimene akudziwa osati chifukwa cha mmene akumvera mumtima mwawo. Komatu zoona n’zakuti nthawi zambiri chikondi cha a·gaʹpe chimakhudza mmene munthu akumvera. Mwachitsanzo, pamene Yohane analemba kuti, “Atate amakonda Mwana,” anagwiritsa ntchito mawu ochokera ku mawu akuti a·gaʹpe. (Yohane 3:35) Kodi chikondi chimenechi ndi chongosonyezedwa potengera zomwe ukudziwa osati kuchokera mumtima? Ayi. Pa Yohane 5:20, pamene Yohane analemba mawu a Yesu akuti “Atatewo amakonda Mwana,” anagwiritsa ntchito mawu ochokera ku mawu akuti phi·leʹo. Choncho chikondi chimene Yehova amasonyeza, nthawi zambiri chimakhudza mmene akumvera komanso chimakhala chochokera mumtima. Komabe sikuti amachisonyeza chifukwa chongotengeka maganizo. Nthawi zonse amachisonyeza chifukwa chotsatira mfundo zake zanzeru zomwenso ndi zolungama.
14 Monga taonera, makhalidwe onse a Yehova ndi apamwamba komanso osangalatsa. Koma khalidwe lake losangalatsa kwambiri ndi chikondi. Palibe chimene chimatichititsa kuti tizifuna kukhala anzake a Yehova kuposa chikondi. N’zosangalatsanso kuti chikondi ndi khalidwe lake lalikulu kwambiri. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi?
“Mulungu Ndi Chikondi”
15. Kodi Baibulo limanena chiyani zokhudza chikondi cha Yehova zomwe silinena likamafotokoza za makhalidwe ake ena akuluakulu? (Onaninso mawu am’munsi.)
15 Baibulo limatiuza mfundo ina yokhudza chikondi, koma silitchula mfundoyi ponena za makhalidwe ena akuluakulu a Yehova. Malemba sanena kuti Mulungu ndi mphamvu, Mulungu ndi chilungamo kapenanso kuti Mulungu ndi nzeru. Iye ali ndi makhalidwe amenewo, makhalidwewa amachokera kwa iye ndipo palibe amene amasonyeza kwambiri makhalidwe atatuwa kuposa iyeyo. Koma Baibulo limanena chinthu china chokhudza chikondi, lomwe ndi khalidwe lake la nambala 4. Limati: “Mulungu ndi chikondi.”b (1 Yohane 4:8) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?
16-18. (a) N’chifukwa chiyani Baibulo limanena kuti “Mulungu ndi chikondi”? (b) Pa zolengedwa zonse zapadzikoli, n’chifukwa chiyani m’pake kuti munthu ndi amene amaimira chikondi cha Yehova?
16 Kunena kuti “Mulungu ndi chikondi” n’kosiyana ndi kungonena kuti chinthu ichi n’chofanana ndi ichi. Mwachitsanzo, sitinganene kuti “Mulungu ndi wofanana ndi chikondi.” Komanso kungakhale kulakwitsa kutembenuza mawuwa n’kunena kuti “chikondi ndi Mulungu.” Yehova ndi weniweni osati khalidwe basi. Iye ndi Mulungu amene amaganiza, amasangalala kapena kukhumudwa komanso ali ndi makhalidwe ena kuwonjezera pa chikondi. Komabe khalidwe lake lalikulu ndi chikondi. Choncho buku lina ponena za vesili limati: “Mulungu ndi wachikondi pa chilichonse.” Kuti timvetse bwino zimenezi, taganizirani izi: Mphamvu za Yehova zimamuthandiza kuti akwanitse kuchita zinthu. Chilungamo ndi nzeru zake zimamuthandiza kudziwa njira imene angachitire zinthuzo. Koma chikondi ndi chimene chimamupangitsa kuti achite zinthuzo. Ndipo nthawi zonse akamasonyeza makhalidwe enawo, amasonyezanso chikondi.
17 Nthawi zambiri timanena kuti Yehova ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yosonyeza chikondi. Choncho ngati tikufuna kuphunzira chikondi chimene munthu amasonyeza chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo, tiyenera kuphunzira za Yehova. Koma anthu nawonso amatha kusonyeza khalidwe labwinoli. N’chifukwa chiyani zili choncho? Pa nthawi imene ankalenga zinthu, Yehova analankhula mawu awa ndipo ayenera kuti ankauza Mwana wake: “Tiyeni tipange munthu m’chifaniziro chathu, kuti akhale wofanana nafe.” (Genesis 1:26) Pa zolengedwa zonse zapadzikoli, ndi anthu okha amene angasankhe kuti azikonda ena ndipo akamachita zimenezi amakhala kuti akutsanzira Atate awo akumwamba. Kumbukirani kuti Yehova anasankha zolengedwa zosiyanasiyana kuti ziziimira makhalidwe ake akuluakulu. Koma iye anasankha munthu, yemwe ndi wapamwamba pa zolengedwa zonse zapadzikoli, kuti aziimira chikondi, lomwe ndi khalidwe lake lalikulu.—Ezekieli 1:10.
18 Tikamasonyeza chikondi chopanda dyera komanso tikamachisonyeza chifukwa choti tikutsatira mfundo za m’Baibulo, timasonyeza khalidwe lalikulu la Yehova. Zimenezi n’zogwirizana ndi zimene mtumwi Yohane analemba kuti: “Timasonyeza chikondi, chifukwa Mulungu ndi amene anayamba kutikonda.” (1 Yohane 4:19) Koma kodi Yehova anayamba ndi iyeyo kutikonda m’njira ziti?
Yehova Ndi Amene Anayamba Kusonyeza Chikondi
19. N’chiyani chinalimbikitsa Yehova kuti ayambe kulenga zinthu zamoyo?
19 Chikondi sichinayambe lero. N’chifukwa chiyani tikutero? Taganizirani funso ili: N’chiyani chinachititsa Yehova kuti ayambe kulenga zinthu zamoyo? Sikuti ankasowa wocheza naye. Yehova ndi wokwanira payekha ndipo ali ndi zonse, moti safunikira kuti winawake amupatse chinachake. Koma chikondi, chomwe ndi khalidwe limene limalimbikitsa munthu kuchitira ena zabwino, chinamulimbikitsa kuti apatse moyo anthu ndi angelo kuti nawonso azisangalala. Choyamba, iye analenga Mwana wake wobadwa yekha, yemwe ndi “woyamba wa chilengedwe cha Mulungu.” (Chivumbulutso 3:14) Kenako Yehova anagwiritsa ntchito Mmisiri Walusoyu polenga zinthu zina zonse, kuyambira angelo. (Yobu 38:4, 7; Akolose 1:16) Yehova anapatsa angelo amphamvuwa ufulu ndi nzeru komanso anawalenga m’njira yoti azitha kukhumudwa kapena kusangalala ndi zinthu. Zimenezi zimawachititsa kuti azitha kusonyeza chikondi ndiponso kugwirizana, koma chofunika kwambiri n’chakuti amathanso kukhala anzake a Yehova Mulungu. (2 Akorinto 3:17) Choncho iwo amakonda ena chifukwa choti Yehova ndi amene anayamba kuwakonda.
20, 21. N’chiyani chikanathandiza Adamu ndi Hava kudziwa kuti Yehova amawakonda, koma kodi iwo anachita zotani?
20 Ndi mmenenso zinalili ndi anthu. Yehova atangolenga Adamu ndi Hava, anawasonyeza kuti ankawakonda m’njira zambiri. Chilichonse chomwe ankaona m’Paradaiso m’munda wa Edeni chinkasonyeza kuti Atate awo amawakonda. Taonani zimene Baibulo limanena: “Yehova Mulungu anadzala munda ku Edeni, chakum’mawa, ndipo m’mundamo anaikamo munthu amene anamuumba uja.” (Genesis 2:8) Kodi munayamba mwapitako kumalo enaake okongola kwambiri? N’chiyani chinakusangalatsani kwambiri kumeneko? Kodi kunali kuwala kwa dzuwa komwe kunkadutsa m’masamba a mitengo? Kapena kukongola kochititsa chidwi kwa maluwa osiyanasiyana? Kodi kanali kaphokoso kapansipansi ka madzi akuyenda mumtsinje, kapena kulira kwa mbalame ndi tizilombo tina? Kapenanso kanali kafungo kabwino ka mitengo, zipatso komanso maluwa? Kaya zinthu zinali bwanji, masiku ano kulibe malo okongola amene tingawayerekezere ndi munda wa Edeni. N’chifukwa chiyani tikutero?
21 Yehova anadzala yekha munda umenewo. Choncho uyenera kuti unali wokongola kwambiri. M’mundawo munali mitengo yonse yokongola komanso ya zipatso zokoma kwambiri. Mundawo unali waukulu, munali mitsinje komanso nyama zambiri zosangalatsa. Adamu ndi Hava anali ndi chilichonse chowachititsa kukhala osangalala ndiponso okhutira, kuphatikizapo ntchito yosangalatsa komanso banja labwino. Yehova ndi amene anayamba kuwakonda, choncho iwonso ankafunika kumukonda. Komatu analephera kuchita zimenezi. M’malo momvera Atate wawo wakumwamba chifukwa chomukonda, anamupandukira chifukwa chodzikonda.—Genesis, chaputala 2.
22. Kodi zimene Yehova anachita Adamu ndi Hava atamupandukira zinasonyeza bwanji kuti chikondi chake ndi chokhulupirika?
22 Zimenezi ziyenera kuti zinamupweteka kwambiri Yehova. Koma kodi zinamuchititsa kuti asiye kukonda anthu? Ayi. “Chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.” (Salimo 136:1) Choncho nthawi yomweyo anakonza njira yopulumutsira ana a Adamu ndi Hava omwe angakhale ndi mtima wabwino. Monga taonera, chinthu chimodzi chomwe Yehova anachita kuti apulumutse anthu ndi kupereka dipo la Mwana wake wokondedwa, ngakhale kuti zimenezi zinamupweteka kwambiri.—1 Yohane 4:10.
23. Kodi chimodzi mwa zinthu zomwe zimachititsa kuti Yehova akhale “Mulungu wachimwemwe” n’chiyani, nanga ndi funso lofunika kwambiri liti limene liyankhidwe m’mutu wotsatira?
23 N’zosachita kufunsa kuti kuchokera pachiyambi Yehova wakhala akuyamba ndi iyeyo kusonyeza chikondi kwa anthu. Yehova wasonyeza m’njira zosawerengeka kuti iye “ndi amene anayamba kutikonda.” Chikondi chimachititsa kuti anthu azigwirizana ndiponso azisangalala, choncho n’zosadabwitsa kuti Baibulo limati Yehova ndi “Mulungu wachimwemwe.” (1 Timoteyo 1:11) Komabe mwina mungamadzifunse kuti, ‘Kodi Yehova amandikonda ineyo pandekha?’ Mutu wotsatira uyankha funso limeneli.
a Mawu akuti phi·leʹo, amene amanena za kukonda mnzako kapena m’bale wako, amapezekanso m’mavesi ambiri m’Malemba a Chigiriki a Chikhristu. Mawu akuti stor·geʹ omwe amanena za kukonda anthu a m’banja lako, anagwiritsidwa ntchito pa 2 Timoteyo 3:3 pofotokoza kuti m’masiku otsiriza anthu ambiri sazidzakonda achibale awo. Mawu akuti eʹros, omwe amanena za chikondi cha pakati pa mwamuna ndi mkazi, sanagwiritsidwe ntchito m’Malemba a Chigiriki a Chikhristu, ngakhale kuti chikondi cha mtundu umenewu chimafotokozedwanso m’Baibulo.—Miyambo 5:15-20.
b M’Baibulo muli mawu ena omwe analembedwa mofanana ndi amenewa. Mwachitsanzo, timawerenga kuti “Mulungu ndiye kuwala” ndiponso kuti “Mulungu . . . ndi moto wowononga.” (1 Yohane 1:5; Deuteronomo 4:24) Koma mawuwa tiyenera kuwaona kuti ndi ophiphiritsa chifukwa akuyerekezera Yehova ndi zinthu zooneka. Yehova ali ngati kuwala, chifukwa ndi woyera ndiponso wolungama. Kwa iye kulibe “mdima,” kapena kuti chinthu chodetsedwa. Ndipo tingamuyerekezere ndi moto chifukwa amagwiritsa ntchito mphamvu zake zowononga.
-
-
Palibe Chimene ‘Chingatisiyanitse ndi Chikondi cha Mulungu’Yandikirani Yehova
-
-
MUTU 24
Palibe Chimene ‘Chingatisiyanitse ndi Chikondi cha Mulungu’
1. Kodi ndi maganizo ofooketsa ati omwe anthu ambiri, ngakhalenso Akhristu ena oona, amavutika nawo?
KODI Yehova Mulungu amakukondani inuyo panokha? Ena amavomereza kuti Mulungu amakonda anthu onse mogwirizana ndi zimene lemba la Yohane 3:16 limanena. Komabe amaganiza kuti: ‘Mulungu sangandikonde ineyo pandekha.’ Ngakhalenso Akhristu oona nthawi zina amamva choncho. Bambo wina atakumana ndi mavuto anati: “Zikundivuta kwambiri kukhulupirira kuti ineyo Mulungu amandiganizira.” Kodi inunso mumaona choncho nthawi zina?
2, 3. Kodi ndi ndani amafuna kuti tizikhulupirira kuti Yehova amationa kuti ndife osafunika kapenanso sangatikonde, nanga tingathetse bwanji maganizo amenewa?
2 Satana amafunitsitsa kuti tizikhulupirira kuti Yehova Mulungu satikonda ndiponso sationa ngati ofunika. N’zoona kuti nthawi zambiri Satana amapusitsa anthu powachititsa kukhala odzikuza komanso onyada. (2 Akorinto 11:3) Komabe amasangalala kuchititsa anthu kuti azidziona kuti ndi osafunika. (Yohane 7:47-49; 8:13, 44) Satana amagwiritsa ntchito kwambiri bodza limeneli makamaka ‘m’masiku otsiriza’ ovuta ano. Anthu ambiri anakulira m’mabanja omwe anthu ake ‘sakonda achibale awo.’ Anthu ena tsiku lililonse amakumana ndi anthu oopsa, odzikonda komanso omva zawo zokha. (2 Timoteyo 3:1-5) Chifukwa choti kwa zaka zambiri ena akhala akuwachitira nkhanza, kuwasala komanso kudana nawo, anthu oterowo angafike pokhulupirira kuti ndi osafunika komanso palibe angawakonde.
3 Ngati nanunso nthawi zina mumavutika ndi maganizo oterewa, musataye mtima. Ambirife nthawi zina sitimadziona moyenera. Koma muzikumbukira kuti Mawu a Mulungu analembedwa kuti ‘azikonza zinthu’ komanso “kugwetsa zinthu zozikika molimba.” (2 Timoteyo 3:16; 2 Akorinto 10:4) Baibulo limati: “Tidzatsimikizira mitima yathu kuti Mulungu sakutiimba mlandu pa chilichonse chimene mitima yathu ingatitsutse, chifukwa Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo amadziwa zonse.” (1 Yohane 3:19, 20) Tiyeni tione zinthu 4 zimene Malemba amanena zomwe zimatithandiza ‘kutsimikizira mitima yathu’ kuti Yehova amatikonda.
Yehova Amakuonani Kuti Ndinu Wofunika
4, 5. Kodi fanizo la Yesu la mpheta limasonyeza bwanji kuti Yehova amationa kuti ndife ofunika kwambiri?
4 Choyamba, Baibulo limaphunzitsa kuti Mulungu amaona kuti mtumiki wake aliyense ndi wofunika. Mwachitsanzo, Yesu ananena kuti: “Mpheta ziwiri amazigulitsa kakhobidi kamodzi kochepa mphamvu, si choncho? Koma palibe ngakhale imodzi imene idzagwa pansi Atate wanu osadziwa. Ndipotu ngakhale tsitsi lonse lam’mutu mwanu amaliwerenga. Choncho musachite mantha, ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta zambiri.” (Mateyu 10:29-31) Kodi anthu omwe ankamvetsera mawu amenewa anamva bwanji?
“Ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta zambiri”
5 Mwina mungadabwe kuti munthu ankagula mpheta chifukwa chiyani. N’chifukwa choti m’nthawi ya Yesu, mpheta inali mbalame yotchipa kwambiri yomwe anthu ankagula kuti akadye. Mutha kuona kuti munthu ankagula mpheta ziwiri ndi kakhobidi kamodzi. Koma pa nthawi ina Yesu anati munthu akapereka timakobidi tiwiri ankamupatsa mpheta 5 osati 4. Mbalame inayo ankangomupatsa ngati ya pulaizi. Mwina mbalamezi anthu ankaziona kuti ndi zosafunika kwenikweni, koma kodi Yehova ankaziona bwanji? Yesu anati: “Palibe ngakhale imodzi mwa mbalame zimenezi [ngakhalenso yapulaiziyo] imene Mulungu amaiiwala.” (Luka 12:6, 7) Tsopano tingayambe kumvetsa mfundo ya Yesu. Ngati Yehova amaona kuti mpheta ndi yofunika kwambiri, ndiye kuli bwanji munthu? Mogwirizana ndi zimene Yesu ananena, Yehova amadziwa chilichonse chokhudza ifeyo. Amadziwa ngakhalenso kuchuluka kwa tsitsi lam’mutu mwathu.
6. N’chifukwa chiyani sitikayikira kuti Yesu ankafotokoza zoona pomwe ananena kuti Mulungu amadziwa kuchuluka kwa tsitsi lathu?
6 Ena angakayikire kuti zimene Yesu ananena zoti Mulungu amadziwa kuchuluka kwa tsitsi lathu si zoona. Komabe, taganizirani za chiyembekezo chakuti akufa adzauka. Yehova ayenera kuti amatidziwa bwino kwambiri kuti adzathe kutilenganso. Amationa kuti ndife ofunika kwambiri moti amakumbukira chilichonse chokhudza ifeyo, kuphatikizapo malangizo omwe ali m’maselo a m’thupi mwathu, zonse zomwe timakumbukira komanso zimene zakhala zikutichitikira pa moyo wathu.a Choncho Yehova sizingamuvute kudziwa kuchuluka kwa tsitsi lathu, lomwe m’mitu ya anthu ambiri limangokwana pafupifupi 100,000.
N’chifukwa Chiyani Yehova Amationa Kuti Ndife Ofunika?
7, 8. (a) Kodi ndi makhalidwe ena ati amene Yehova amasangalala akawapeza pamene akufufuza mitima ya anthu? (b) Kodi ndi zinthu zina ziti zomwe timachita zimene Yehova amaona kuti ndi zamtengo wapatali?
7 Chachiwiri, Baibulo limatiuza chifukwa chake Yehova amaona kuti atumiki ake ndi ofunika. Mwachidule, iye amasangalala ndi makhalidwe athu abwino ndiponso khama lathu pomutumikira. Mfumu Davide anauza mwana wake Solomo kuti: “Yehova amafufuza mitima yonse ndipo amazindikira maganizo a munthu ndi zolinga zake zonse.” (1 Mbiri 28:9) Mulungu akamafufuza mitima ya anthu mabiliyoni m’dzikoli, lomwe anthu ambiri ndi achiwawa komanso amadana, ayenera kuti amasangalala kwambiri akapeza munthu wa mtima wokonda mtendere, choonadi ndiponso chilungamo. Kodi Mulungu amatani akapeza munthu amene amamukonda, yemwe akufuna kuphunzira za iye komanso kuuza ena zomwe akuphunzirazo? Yehova amatiuza kuti amachita chidwi ndi anthu omwe amauza ena zokhudza iyeyo. Moti ali ndi “buku la chikumbutso,” lonena za anthu onse ‘oopa Yehova ndiponso amene amaganizira za dzina lake.’ (Malaki 3:16) Iye amaona kuti zimene anthuwa amachita, ndi zamtengo wapatali.
8 Kodi zinthu zina zimene Yehova amaziona kuti ndi zamtengo wapatali ndi ziti? Zimene timachita poyesetsa kutsanzira Mwana wake Yesu Khristu. (1 Petulo 2:21) Mulungu amaonanso kuti ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wake ndi chinthu chamtengo wapatali kwambiri. Pa Aroma 10:15, timawerenga kuti: “Mapazi a anthu olengeza uthenga wabwino wa zinthu zabwino, ndi okongola kwambiri.” Nthawi zambiri sitiganiza zoti mapazi ndi okongola. Koma palembali akuimira khama limene atumiki a Yehova amachita polalikira uthenga wabwino. Yehova amaona kuti zonse zomwe atumiki ake amachitazi ndi zokongola komanso zamtengo wapatali.—Mateyu 24:14; 28:19, 20.
9, 10. (a) N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira kuti Yehova amayamikira tikamapirira pamene tikukumana ndi mavuto osiyanasiyana? (b) Kodi Yehova sachita chiyani akamafufuza mitima ya atumiki ake okhulupirika?
9 Yehova amayamikiranso tikamapirira. (Mateyu 24:13) Kumbukirani kuti Satana amafuna kuti tisiye kutumikira Yehova. Tsiku lililonse limene takhulupirika kwa Yehova, timakhala kuti tasonyeza nawo kuti Satana ndi wabodza. (Miyambo 27:11) Komatu nthawi zina kupirira kumakhala kovuta kwambiri. Tsiku lililonse tingamavutike ndi matenda, mavuto azachuma, nkhawa ndiponso mavuto ena. Tikhozanso kukhumudwa chifukwa choti zimene timayembekezera sizikuchitika. (Miyambo 13:12) Tikamapirira mavuto amenewa, Yehova amaona kuti ndi chinthu chamtengo wapatali kwambiri. N’chifukwa chake Mfumu Davide anapempha Yehova kuti amusungire misozi yake ‘m’thumba lachikopa’ ndipo ankakhulupirira kuti Yehovayo analemba misoziyo “m’buku” lake. (Salimo 56:8) Choncho Yehova amaona kuti misozi yathu ndi yamtengo wapatali ndipo amaikumbukira. Amakumbukiranso tikamapirira mavuto kuti tikhalebe okhulupirika kwa iye. Misoziyo ndiponso kupirirako amaziona kuti ndi zamtengo wapatali.
Yehova amayamikira tikamapirira pamene tikukumana ndi mayesero
10 Koma mtima wathu ukhoza kumatsutsabe mfundo yakuti Mulungu amationa kuti ndife ofunika. Tikhoza kumaganiza kuti: ‘Pali anthu ambiri abwino kuposa ineyo. Yehova ayenera kuti amakhumudwa kwambiri akandiyerekezera ndi amenewo.’ Komatu Yehova satiyerekezera ndi ena ndiponso sayembekezera kuti tizichita zomwe sitingakwanitse. (Agalatiya 6:4) Amafufuza mosamala zimene zili m’mitima mwathu ndipo amayamikira zabwino zilizonse zimene wapeza, ngakhale zitakhala zochepa.
Yehova Amafufuza Zabwino pa Zoipa
11. Kodi nkhani ya Abiya ikutiphunzitsa chiyani za Yehova?
11 Chachitatu, Yehova amatifufuza mosamala kwambiri kuti apeze zabwino mwa ife. Mwachitsanzo, atalamula kuti anthu onse a m’banja la Mfumu Yerobowamu omwe anali ampatuko aphedwe, analamulanso kuti mwana mmodzi wa mfumuyo dzina lake Abiya aikidwe m’manda m’njira yolemekezeka. N’chifukwa chiyani anatero? Chifukwa chakuti ‘Yehova Mulungu wa Isiraeli anapeza chinachake chabwino mwa yekhayu.’ (1 Mafumu 14:1, 10-13) Tinganene kuti Yehova anafufuza mosamala mumtima mwa mnyamatayo n’kupezamo “chinachake chabwino.” Kaya chabwinocho chinali chochepa bwanji, Yehova anaonabe kuti chinali choyenera kuchitchula m’Mawu ake. Ndiponso iye anapereka mphoto kwa Abiya pomusonyeza chifundo n’kulola kuti aikidwe m’manda mwaulemu.
12, 13. (a) Kodi nkhani ya Mfumu Yehosafati imasonyeza bwanji kuti Yehova amafufuza zabwino zimene timachita ngakhale pamene tachimwa? (b) Kodi Yehova amaona bwanji makhalidwe athu abwino komanso zabwino zimene timachita?
12 Chitsanzo chinanso chabwino kwambiri tingachione munkhani ya Yehosafati yemwe anali mfumu yabwino. Mfumuyi itachita zinthu zopanda nzeru, mneneri wa Yehova anaiuza kuti: “Chifukwa cha zimenezi Yehova wakukwiyirani.” Umenewutu unali uthenga wochititsa mantha. Komatu uthenga wa Yehovawu sunathere pomwepo. Mneneriyu ananenanso kuti: “Komabe, pali zinthu zabwino zimene zapezeka mwa inu.” (2 Mbiri 19:1-3) Ngakhale kuti Yehova anakwiyira Yehosafati, zimenezi sizinamulepheretse kuona zabwino zimene Yehosafatiyo anachita. Zimenezi n’zosiyana kwambiri ndi zimene anthu omwe si angwirofe timachita. Anthu ena akatikhumudwitsa, tingalephere kuona zabwino zomwe amachita. Ndipo tikachita tchimo tingakhumudwe, kuchita manyazi ndiponso kudziimba mlandu moti tingalephere kuona zabwino zimene timachita. Komabe tizikumbukira kuti tikalapa machimo athu n’kuyesetsa kuti tisawabwerezenso, Yehova amatikhululukira.
13 Yehova akamatifufuza, amataya machimowo ngati mmene munthu wofufuza golide amatayira zinthu zosafunika n’kusunga miyala yagolide yokhayokha. Ndi mmenenso Yehova amaonera makhalidwe athu abwino komanso zabwino zimene timachita. Makolo ena amakonda kwambiri zithunzi zimene ana awo anajambula kapena zinthu zina zomwe ankapanga kusukulu moti amazisunga kwa zaka zambiri ngakhale anawo ataziiwala. Yehova ndi Kholo lachikondi kwambiri. Tikamapitiriza kukhala okhulupirika kwa iye, saiwala zabwino zomwe timachita ndiponso makhalidwe athu abwino. Kuchita zimenezi angakuone kuti n’kupanda chilungamo chifukwa iye ndi Mulungu wachilungamo. (Aheberi 6:10) Koma Yehova amatifufuzanso m’njira ina.
14, 15. (a) N’chifukwa chiyani zimene timalakwitsa sizilepheretsa Yehova kuona zinthu zabwino zimene timachita? Perekani chitsanzo. (b) Kodi Yehova amachita chiyani akaona kuti tili ndi makhalidwe abwino, nanga anthu ake okhulupirika amawaona bwanji?
14 Yehova amaona zambiri kuposa zimene timalakwitsa ndipo amadziwa kuti tikhoza kukhala anthu abwino kwambiri. Taganizirani izi: Anthu amene amakonda zojambulajambula amayesetsa ndi mtima wonse kukonza zithunzi zomwe zawonongeka kwambiri. Mwachitsanzo, munthu wina yemwe anali ndi mfuti anawononga chithunzi cha ndalama pafupifupi madola 30 miliyoni. Chithunzichi chinajambulidwa ndi Leonardo da Vinci, ndipo chinali m’nyumba yosungiramo zithunzi ku London. Komabe zimenezi zitachitika, palibe amene ananena kuti chithunzicho akangochitaya chifukwa chawonongedwa. Nthawi yomweyo ntchito yokonzanso chithunzi chojambulidwa mwalusochi, chomwe chakhalapo kwa zaka pafupifupi 500 inayambika. N’chifukwa chiyani sanangochitaya? Chifukwa chakuti anthu okonda zojambulajambula ankachiona kuti n’chamtengo wapatali. Komatu inuyo ndi wofunika kwambiri kuposa chithunzi chongojambula. Ndinu wamtengo wapatali kwa Mulungu, ngakhale kuti nthawi zina chifukwa cha uchimo womwe tonsefe timabadwa nawo, mungamadzione kuti ndinu wosafunika. (Salimo 72:12-14) Yehova Mulungu, yemwe analenga anthu mwaluso, adzachita zonse zofunika kuti athetse mavuto obwera chifukwa cha uchimo ndipo adzathandiza anthu onse amene amamukonda komanso kumumvera kuti akhale angwiro.—Machitidwe 3:21; Aroma 8:20-22.
15 Yehova amaona makhalidwe abwino amene tili nawo omwe ifeyo sitingawaone. Ndipo pamene tikumutumikira, amatithandiza kuti tizisonyeza kwambiri makhalidwewo mpaka pamene tidzakhale angwiro. Kaya dziko la Satanali latichitira zoipa zotani, Yehova amaona kuti atumiki ake okhulupirika ndi amtengo wapatali.—Hagai 2:7.
Yehova Amachita Zinthu Zosonyeza Kuti Amatikonda
16. Kodi umboni waukulu kwambiri wosonyeza kuti Yehova amatikonda ndi uti, nanga timadziwa bwanji kuti mphatso imeneyi inaperekedwa kwa aliyense payekha?
16 Cha 4, Yehova amachita zambiri posonyeza kuti amatikonda. Zimene anachita popereka Mwana wake kuti atifere ndi umboni wamphamvu wosonyeza kuti Satana ndi wabodza akamanena kuti ndife anthu osafunika. Tisamaiwale kuti pamene Yesu anafa mozunzika pamtengo wozunzikirapo ndiponso pamene Yehova anapirira ululu waukulu kwambiri poona Mwana wake yemwe amamukonda akufa, ndi umboni wosonyeza kuti awiriwa amatikonda. N’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri amalephera kukhulupirira kuti mphatso imeneyi inaperekedwa kwa iwowo pawokha. Amadziona kuti ndi osayenera kupatsidwa mphatsoyi. Kumbukirani kuti mtumwi Paulo ankapha otsatira a Khristu. Komabe iye analemba kuti: “Mwana wa Mulungu . . . anandikonda n’kudzipereka yekha chifukwa cha ine.”—Agalatiya 1:13; 2:20.
17. Kodi Yehova amagwiritsa ntchito chiyani kuti atikokere kwa iyeyo ndi Mwana wake?
17 Yehova amatitsimikizira kuti amatikonda pothandiza aliyense payekha kuti apindule ndi nsembe ya Khristu. Yesu anati: “Palibe munthu amene angabwere kwa ine pokhapokha Atate amene anandituma atamukoka.” (Yohane 6:44) Yehova ndi amene amatikokera kwa Mwana wake ndiponso kutipatsa chiyembekezo cha moyo wosatha. Kodi amachita bwanji zimenezi? Kudzera mu ntchito yolalikira, iye anaonetsetsa kuti taphunzira choonadi. Amagwiritsanso ntchito mzimu wake woyera potithandiza kumvetsa mfundo za m’Baibulo n’kumazigwiritsa ntchito ngakhale kuti si ife wangwiro. Choncho ponena za ife, Yehova akhoza kulankhulanso zomwe ananena zokhudza Aisiraeli kuti: “Ine ndakukonda ndipo ndidzakukonda mpaka kalekale. N’chifukwa chake ndakukokera kwa ine ndi chikondi chokhulupirika.”—Yeremiya 31:3.
18, 19. (a) Kodi njira yaikulu imene Yehova amatisonyezera chikondi ndi iti, ndipo n’chiyani chikusonyeza kuti udindo umenewu sanaupereke kwa aliyense? (b) Kodi Baibulo limatitsimikizira bwanji kuti Yehova amamvetsera ndipo amamva chisoni?
18 Yehova amatipatsa mwayi woti tizipemphera kwa iye ndipo mwina imeneyi ndi njira yaikulu imene amasonyezera chikondi kwa munthu aliyense payekha. Baibulo limauza aliyense payekhapayekha kuti ‘azipemphera’ kwa Mulungu nthawi zonse. (1 Atesalonika 5:17) Iye amamvetsera. Ndipotu amatchulidwa kuti “Wakumva pemphero.” (Salimo 65:2) Udindo umenewu sanaupereke kwa wina aliyense, ngakhalenso Mwana wake. Tangoganizani: Mlengi wa chilengedwe chonse amatilimbikitsa kuti tizilankhula naye momasuka m’pemphero. Ndiye tikamapemphera, kodi iye amangotimvetsera koma osakhudzika ndi zomwe zikutichitikira? Ayi ndithu.
19 Yehova amamva chisoni. Kodi kumvera munthu chisoni n’kutani? Mkhristu wina wachikulire ndiponso wokhulupirika anati: “Kumvera munthu chisoni kumatanthauza kumva ululu wake mumtima mwanga.” Kodi Yehova zimamukhudza tikamavutika? Taonani mmene anamvera pamene anthu ake Aisiraeli ankavutika. Baibulo limati: “Pa nthawi yonse imene iwo ankavutika, iye ankavutikanso.” (Yesaya 63:9) Yehova sankangoona anthuwo akuvutika koma ankawamveranso chisoni. Posonyeza kuti amamvera chisoni kwambiri atumiki ake, iye anati: “Amene akukukhudzani, akukhudza mwana wa diso langa.”b (Zekariya 2:8) Zimenezitu zingakhale zopweteka kwambiri. Zoonadi, Yehova amatimvera chisoni. Tikamamva kuwawa, nayenso amamva kuwawa.
20. Kodi ndi maganizo olakwika ati amene tiyenera kupewa kuti tizitsatira malangizo apalemba la Aroma 12:3?
20 Palibe Mkhristu aliyense woganiza bwino amene angamadzikuze kapena kudziona kuti ndi wofunika kuposa ena chifukwa chodziwa kuti Mulungu amamukonda komanso amamuona kuti ndi wofunika. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu anandisonyeza, ndikuuza aliyense wa inu kumeneko kuti musamadziganizire kuposa mmene muyenera kudziganizira. Koma aliyense aziganiza mwanzeru n’kumadziweruza mogwirizana ndi chikhulupiriro chimene Mulungu wamupatsa. (Aroma 12:3) Baibulo lina limati: “Ndikuuza aliyense wa inu kuti asamadzione kuti ndi wofunika kwambiri kuposa mmene alili, koma azidziona moyenera.” (A Translation in the Language of the People, by Charles B. Williams) Choncho tikamasangalala kuti Atate wathu wakumwamba amatikonda, tiyeni tizikhala oganiza bwino n’kumakumbukira kuti sikuti Mulungu amatikonda ngati malipiro a zimene timachita koma chifukwa cha kukoma mtima kwake kwakukulu.—Luka 17:10.
21. Kodi ndi mabodza a Satana ati amene tiyenera kuyesetsa kuti tisamawakhulupirire, nanga tizikhulupirira mfundo ya m’Baibulo iti imene Yehova amatiuza?
21 Tiyeni tizichita zonse zimene tingathe pokana kukhulupira mabodza a Satana, kuphatikizapo bodza lakuti ndife osafunika kapena palibe amene angatikonde. Ngati zimene mwakumana nazo pa moyo zachititsa kuti muzidziona kuti ndinu woipa kwambiri moti Mulungu sangakukondeni, kapena ngati mumaona kuti Mulungu saona zabwino zimene mumachita, kapenanso kuti munachita machimo oipa kwambiri moti ngakhale imfa ya Mwana wa Mulungu singawafafanize, dziwani kuti limeneli ndi bodza. Yesetsani kuti musamakhulupirire mabodza amenewa. Tiyeni tizitsimikizira mitima yathu mawu ouziridwa amene Paulo analemba akuti: “Ndatsimikiza mtima kuti imfa, moyo, angelo, maboma, zinthu zimene zilipo, zinthu zimene zikubwera, mphamvu, msinkhu, kuzama kapena cholengedwa chilichonse, sizidzatha kutisiyanitsa ndi chikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.”—Aroma 8:38, 39.
a Mobwerezabwereza Baibulo limasonyeza kuti pali kugwirizana pakati pa chiyembekezo choti akufa adzauka ndi zimene Yehova amakumbukira. Munthu wokhulupirikayo Yobu anauza Yehova kuti: “Zikanakhala bwino mukanandiikira nthawi n’kudzandikumbukira.” (Yobu 14:13) Yesu anatchula za kuukitsidwa kwa “onse amene ali m’manda achikumbutso.” Izi zinali zoyenera chifukwa Yehova amawakumbukira bwino kwambiri akufa amene akufuna kudzawaukitsa.—Yohane 5:28, 29.
b Palembali, Mabaibulo ena anamasulira kuti munthu amene akukhudza anthu a Mulungu ndiye kuti akudzikhudza yekha diso lake kapena akukhudza diso la Aisiraeli, osati la Mulungu. Kulakwitsa kumeneku anakuyambitsa ndi anthu ena okopera Malemba amene ankaganiza kuti vesili likunyoza Mulungu. Koma maganizo awo olakwikawa anachititsa kuti mfundo yoti Yehova amachitira kwambiri chifundo anthu ake isaonekere.
-
-
“Chifundo Chachikulu cha Mulungu Wathu”Yandikirani Yehova
-
-
MUTU 25
“Chifundo Chachikulu cha Mulungu Wathu”
1, 2. (a) Kodi mayi amachita chiyani mwachibadwa mwana wake akayamba kulira? (b) Kodi ndi ndani amene amasonyeza chifundo kwambiri kuposa mayi?
MWANA wakhanda akulira pakati pa usiku. Nthawi yomweyo mayi ake akudzuka. Kungoyambira pamene mwana wake anabadwa, mayiyu sagona kwambiri ngati mmene ankagonera poyamba. Anaphunzira kusiyanitsa kaliridwe kosiyanasiyana ka mwana wakeyo. Choncho nthawi zambiri amadziwa ngati mwanayo akufuna kuyamwa, kunyamulidwa kapena kumusamalira mwa njira ina. Kaya mwanayo akulira chiyani, mayi akewo amachitapo kanthu. Chifukwa choti amamukonda kwambiri, sanganyalanyaze zimene mwanayo akufuna.
2 Anthu ambiri amadziwa kuti mayi amakhala wachifundo kwambiri kwa mwana wake. Komabe, Mulungu wathu Yehova ndi amene amasonyeza kwambiri khalidwe la chifundo. Kuphunzira zokhudza khalidwe labwinoli kungatithandize kuti tiyandikire kwambiri Yehova. Choncho tiyeni tikambirane zimene chifundo chimatanthauza ndiponso mmene Mulungu wathu amachisonyezera.
Kodi Chifundo N’chiyani?
3. Kodi mawu a Chiheberi amene anawamasulira kuti “kusonyeza chifundo” kapena “kumvera wina chisoni” amatanthauza chiyani?
3 M’Baibulo, mawu akuti chifundo amafanana ndi akuti chisoni. Mawu angapo a Chiheberi ndiponso Chigiriki amanena za kukhala ndi chifundo chachikulu. Mwachitsanzo, taganizirani za mawu a Chiheberi akuti ra·chamʹ, omwe nthawi zambiri amamasuliridwa kuti “kusonyeza chifundo” kapena “kumvera wina chisoni.” Buku lina limafotokoza kuti mawu akuti ra·chamʹ “amanena za kumva chisoni kwambiri ngati chimene munthu amamva akaona munthu wina amene amamukonda akuvutika kapena akufunika kumuthandiza.” Mawu a Chiheberiwa, omwe Yehova amawagwiritsa ntchito ponena za iyeyo, amafanana ndi mawu otanthauza “chiberekero” ndipo angamasuliridwenso kuti “chifundo cha mayi.”a—Ekisodo 33:19; Yeremiya 33:26.
“Kodi mayi angaiwale . . . mwana wochokera m’mimba mwake?”
4, 5. Kodi Baibulo limagwiritsa ntchito bwanji chifundo chimene mayi amasonyeza mwana wake potiphunzitsa za chifundo cha Yehova?
4 Baibulo limagwiritsa ntchito mfundo yoti mayi amasonyeza mwana wake chifundo, pofuna kutiphunzitsa tanthauzo la chifundo cha Yehova. Lemba la Yesaya 49:15 limati: “Kodi mayi angaiwale mwana wake woyamwa kapena kulephera kuchitira chifundo [ra·chamʹ] mwana wochokera m’mimba mwake? Ngakhale amayi amenewa ataiwala, ine sindingakuiwale.” Lemba limeneli likusonyeza kuti Yehova amasonyeza anthu ake chifundo chachikulu. Kodi amachita bwanji zimenezi?
5 N’zovuta kuganiza kuti mayi angaiwale kuyamwitsa kapena kusamalira mwana wake wakhanda. Ndipotu mwana wakhanda sangathe kudzisamalira yekha, nthawi zonse amafunika kuti mayi ake azimusamalira komanso kumukonda. Koma n’zomvetsa chisoni kuti azimayi ambiri sasamalira ana awo, makamaka ‘m’nthawi yapadera komanso yovuta’ ino pomwe anthu ambiri ‘sakonda achibale awo.’ (2 Timoteyo 3:1, 3) Koma Yehova akutiuza kuti: “Ine sindingakuiwale.” Yehova sasiya kusonyeza atumiki ake chifundo. Chifundo chake n’chachikulu kwambiri kuposa chimene mayi mwachibadwa amasonyeza mwana wake. Choncho n’zosadabwitsa kuti munthu wina ponena za lemba la Yesaya 49:15 anati: “Amenewa ndi amodzi mwa mawu amphamvu kwambiri, mwinanso tingati ndiye amphamvu kwambiri pa mawu onse onena za chikondi cha Mulungu m’Chipangano Chakale.”
6. Kodi nthawi zambiri anthu omwe si angwiro amaona kuti munthu wachifundo ndi wotani, koma kodi Yehova amatitsimikizira chiyani?
6 Kodi munthu akakhala wachifundo ndiye kuti ndi wofooka? Nthawi zambiri anthu omwe si angwiro amaganiza choncho. Mwachitsanzo, ku Roma kunali katswiri wina wa nzeru za anthu amenenso anali wotchuka dzina lake Seneca. Iyeyu anakhala ndi moyo pa nthawi imene Yesu anali padzikoli, ndipo ankaphunzitsa kuti “munthu akamamvera ena chisoni amasonyeza kuti ndi wofooka maganizo.” Seneca ankalimbikitsa chiphunzitso chakuti, kuti munthu akhale ndi moyo wabwino, azipewa kumva kuwawa, kumva chisoni ndiponso kukhala wosangalala. Iye ankati munthu wanzeru akhoza kuthandiza anthu amene akuvutika, koma iyeyo asamawamvere chisoni chifukwa kumva chisoni kungamuchititse kuti asakhale ndi mtendere wamumtima. Maganizo odzikondawa sankathandiza anthu kuti azisonyeza chifundo mochokera pansi pa mtima. Koma si mmene Yehova alili. M’Mawu ake, iye amatitsimikizira kuti “ndi wachikondi chachikulu komanso wachifundo.” (Yakobo 5:11) Monga mmene tionere, kukhala wachifundo si kufooka, koma ndi khalidwe lofunika kwambiri. Tiyeni tione mmene Yehova, yemwe ndi kholo lachikondi, amasonyezera khalidweli.
Yehova Anachitira Chifundo Mtundu wa Aisiraeli
7, 8. Kodi Aisiraeli anavutika bwanji ku Iguputo, nanga Yehova anawathandiza bwanji?
7 Zimene Yehova ankachitira Aisiraeli zimatithandiza kumvetsa bwino chifundo chake. Chakumapeto kwa zaka za m’ma 1500 B.C.E., Aisiraeli mamiliyoni anali akapolo ku Iguputo komwe ankazunzidwa kwambiri. Aiguputo “anasautsa moyo wa Aisiraeliwo powagwiritsa ntchito yowawa, yomwe inali yoponda matope ndi kuumba njerwa. Anawagwiritsa ntchito yaukapolo wa mtundu uliwonse.” (Ekisodo 1:11, 14) Chifukwa chovutika chonchi, Aisiraeli ankachonderera Yehova kuti awathandize. Kodi Mulungu yemwe ndi wachifundo anachita chiyani?
8 Yehova zinamukhudza mtima kwambiri. Iye anati: “Ndaona mmene anthu anga amene ali ku Iguputo akuvutikira, ndipo ndamva kulira kwawo chifukwa cha amene akuwagwiritsa ntchito mwankhanza. Ndikudziwa bwino ululu umene akumva.” (Ekisodo 3:7) Sikuti Yehova ankangoona kapena kumva anthu ake akuvutika koma ankawamveranso chisoni. M’Mutu 24 wa bukuli, tinaona kuti Yehova ndi Mulungu amene amamvera ena chisoni. Ndipotu chisoni, chomwe chimatanthauza kumva ululu womwe munthu wina akumva, n’chogwirizana ndi chifundo. Yehova sanangomvera chisoni anthu ake koma anawathandizanso. Lemba la Yesaya 63:9 limati: “Iye anawawombola chifukwa cha chikondi komanso chifundo chake.” Yehova anapulumutsa Aisiraeli ku Iguputo ndi “dzanja lamphamvu.” (Deuteronomo 4:34) Kenako ankawapatsa chakudya modabwitsa ndiponso anawapatsa Dziko Lolonjezedwa.
9, 10. (a) N’chifukwa chiyani Yehova ankapulumutsa Aisiraeli mobwerezabwereza m’Dziko Lolonjezedwa? (b) M’nthawi ya Yefita, kodi Yehova anapulumutsa Aisiraeli pamene ankaponderezedwa ndi ndani, ndipo n’chiyani chinamuchititsa zimenezi?
9 Yehova anapitirizabe kuwasonyeza chifundo. Atakhazikika m’Dziko Lolonjezedwa, Aisiraeli ankachita zinthu zosakhulupirika mobwerezabwereza, zomwe zinkachititsa kuti azikumana ndi mavuto. Koma akazindikira kulakwa kwawo, ankalapa n’kupempha Yehova kuti awathandize. Iye ankawapulumutsa mobwerezabwereza. N’chifukwa chiyani ankachita zimenezi? “Chifukwa ankamvera chisoni anthu akewo.”—2 Mbiri 36:15; Oweruza 2:11-16.
10 Taganizirani zomwe zinachitika m’nthawi ya Yefita. Aisiraeli atayamba kulambira mafano, Yehova analola kuti Aamoni awapondereze kwa zaka 18. Koma kenako Aisiraeli analapa. Baibulo limatiuza kuti: “Iwo anachotsa milungu yonse yachilendo imene anali nayo ndipo anayamba kutumikira Yehova, moti iye sanalole kuti Aisiraeli apitirize kuvutika.” (Oweruza 10:6-16) Anthu ake atalapa mochokera pansi pa mtima, Yehova sanalole kuti azingowaona akuvutika. Choncho Mulungu wachifundo chachikuluyu, anagwiritsa ntchito Yefita kuti apulumutse Aisiraeli kwa adani awo.—Oweruza 11:30-33.
11. Kodi tikuphunzira chiyani zokhudza chifundo tikaganizira mmene Yehova ankachitira zinthu ndi Aisiraeli?
11 Kodi tikuphunzira chiyani zokhudza chifundo tikaganizira mmene Yehova ankachitira zinthu ndi Aisiraeli? Mfundo imodzi yofunika kwambiri imene tikuphunzira ndi yakuti chifundo sichitanthauza kungodziwa mavuto amene ena akukumana nawo n’kumawamvera chisoni. Taganiziraninso chitsanzo cha mayi amene chifundo chake chimamuchititsa kuti athandize mwana wake yemwe akulira. Mofanana ndi zimenezi, Yehova akamva anthu ake akumupempha kuti awathandize pamavuto awo, chifundo chimamuchititsa kuti amve pemphero lawo n’kuwathandiza. Timaphunziranso kuti munthu amene amasonyeza chifundo si wofooka, chifukwa chifundo chinachititsa Yehova kumenya nkhondo kuti apulumutse Aisiraeli. Koma kodi Yehova amangochitira chifundo atumiki ake monga gulu?
Yehova Amachitira Chifundo Munthu Aliyense Payekha
12. Kodi Chilamulo chinkasonyeza bwanji kuti Yehova amachitira chifundo munthu aliyense payekha?
12 Chilamulo chimene Mulungu anapatsa Aisiraeli chinasonyeza kuti iye amachitira chifundo munthu aliyense payekha. Mwachitsanzo, taganizirani mmene anasonyezera kuti ankaganizira anthu osauka. Yehova ankadziwa kuti pakhoza kuchitika zinthu zosayembekezereka zomwe zikanachititsa kuti munthu wina wa Chiisiraeli akhale pa umphawi. Ndiye kodi Aisiraeli ankayenera kumachita bwanji zinthu ndi munthu wosauka? Yehova anawalamula mwamphamvu kuti: “Muzimupatsa mowolowa manja zimene akufunazo, ndipo musamamupatse zinthuzo monyinyirika. Mukamachita zimenezi, Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani pa chilichonse chimene mukuchita ndi ntchito zanu zonse.” (Deuteronomo 15:7, 10) Yehova analamulanso Aisiraeli kuti asamakolole m’mbali mwa minda yawo kapenanso kukatenga mbewu zomwe zatsala kumunda. Anthu ovutika ndi amene ankayenera kutenga zimenezo. (Levitiko 23:22; Rute 2:2-7) Aisiraeli akamatsatira lamulo limeneli, lomwe linkathandiza osauka, anthu osaukawo sankapemphetsa chakudya. Kodi zimenezi sizikusonyeza kuti Yehova ndi wachifundo chachikulu?
13, 14. (a) Kodi mawu a Davide amatitsimikizira bwanji kuti Yehova amadera nkhawa kwambiri munthu aliyense pa yekha? (b) Perekani chitsanzo chosonyeza kuti Yehova amakhala pafupi ndi “anthu a mtima wosweka” kapena “amene akudzimvera chisoni mumtima mwawo”?
13 Masiku anonso, Mulungu wathu wachikondi amadera nkhawa kwambiri munthu aliyense payekha. Sitikayikira kuti amadziwa bwino mavuto amene tikukumana nawo. Wolemba masalimo Davide analemba kuti: “Maso a Yehova ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva kufuula kwawo kopempha thandizo. Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Iye amapulumutsa anthu amene akudzimvera chisoni mumtima mwawo.” (Salimo 34:15, 18) Ponena za anthu amene afotokozedwa palembali, katswiri wina wa Baibulo ananena kuti “ndi anthu amene afooka chifukwa chodziona kuti ndi ochimwa komanso achabechabe.” Anthu oterewa akhoza kumaona kuti Yehova ali nawo kutali kwambiri komanso ndi anthu osafunika moti sawawerengera. Koma zimenezi si zoona. Mawu a Davidewa amatitsimikizira kuti Yehova sasiya anthu amene ‘amadziona kuti ndi achabechabe.’ Mulungu wathu wachifundo amadziwa kuti pa nthawi ngati imeneyi m’pamene timafunikira kwambiri kuti atithandize ndipo amakhala nafe pafupi.
14 Taganizirani zomwe zinachitika ku United States. Mayi wina anathamangira kuchipatala ndi mwana wake wazaka ziwiri yemwe ankabanika. Atamuyeza, madokotala anauza mayi akewo kuti ayenera kumugoneka m’chipatalamo. Ndiye kodi mayiyo anagona kuti usiku umenewo? Anagona m’chipinda chomwe anagoneka mwanayo pampando womwe unali pafupi ndi bedi lake. Mwana wakeyo ankadwala choncho ankafunika kukhala naye pafupi. Zimene anachitazi zinangosonyeza chifundo chimene Yehova ali nacho. Pajatu tinapangidwa m’chifaniziro chake. (Genesis 1:26) Choncho n’zosakayikitsa kuti Atate wathu wakumwamba angatichitire zambiri kuposa pamenepa. Mawu olimbikitsa a pa Salimo 34:18 amatiuza kuti pamene ‘tasweka mtima’ kapena ‘kudzimvera chisoni,’ Yehova yemwe ndi kholo lachikondi amakhala nafe “pafupi.” Izi zikutanthauza kuti nthawi zonse amatisonyeza chifundo ndipo amakhala wokonzeka kutithandiza.
15. Kodi Yehova amathandiza bwanji aliyense payekhapayekha?
15 Kodi Yehova amatithandiza bwanji aliyense payekhapayekha? Si nthawi zonse pamene amachotsa zomwe zikuyambitsa mavuto athu. Koma pali zinthu zambiri zimene wapereka kuti zizithandiza amene akumupempha kuti awathandize. Baibulo, lomwe ndi Mawu ake, lili ndi malangizo amene angatithandize kupirira mavuto alionse. Yehova watipatsanso akulu mumpingo omwe amayesetsa kutsanzira chifundo chake akamatithandiza. (Yakobo 5:14, 15) Monga “Wakumva pemphero,” iye amapereka “mzimu woyera kwa amene akumupempha.” (Salimo 65:2; Luka 11:13) Mzimu umenewo ungatipatse “mphamvu yoposa yachibadwa” kuti tizipirira mpaka pamene Ufumu wa Mulungu udzachotse mavuto onse. (2 Akorinto 4:7) Timathokoza kwambiri Yehova chifukwa watipatsa zonsezi kuti zitithandize. Ndipo tisamaiwale kuti zinthu zimenezi zimasonyeza kuti iye ndi wachifundo chachikulu.
16. Kodi ndi njira yaikulu kwambiri iti imene Yehova anatisonyezera chifundo chake, ndipo aliyense ayenera kukumbukira chiyani?
16 Komabe, njira yaikulu kwambiri imene Yehova anatisonyezera chifundo chake ndi kupereka Mwana wake kuti akhale dipo lotiwombola. Chifukwa chotikonda, Yehova anapereka nsembe imeneyi kuti tipulumutsidwe ku uchimo ndi imfa. Muzikumbukira kuti dipo limeneli linaperekedwa kwa aliyense payekha. M’pake kuti Zekariya, yemwe anali bambo a Yohane M’batizi, ananeneratu kuti mphatso imeneyi idzasonyeza bwino “chifundo chachikulu cha Mulungu wathu.”—Luka 1:78.
Nthawi Imene Yehova Angasiye Kusonyeza Chifundo
17-19. (a) Kodi Baibulo limasonyeza bwanji kuti Yehova amafika posiya kuchitira anthu chifundo? (b) N’chifukwa chiyani Yehova anasiya kuchitira chifundo anthu ake?
17 Kodi tiyenera kumaganiza kuti chifundo cha Yehova n’chopanda malire? Ayi, chifukwa Baibulo limasonyeza bwino kuti anthu amene amapitiriza kuchita zoipa, iye amasiya kuwachitira chifundo. (Aheberi 10:28) Kuti timvetse chifukwa chake, tiyeni tiganizirenso zimene Aisiraeli ankachita.
18 Ngakhale kuti Yehova ankapulumutsa Aisiraeli mobwerezabwereza, m’kupita kwanthawi anasiya kuwachitira chifundo. Anthu amenewa anapitiriza kulambira mafano moti mpaka anafika potenga mafano awo onyansawo n’kuwaika m’kachisi wa Yehova. (Ezekieli 5:11; 8:17, 18) Baibulo limatiuzanso kuti: “Iwo anapitiriza kunyoza atumiki a Mulungu woona, kunyoza mawu ake ndiponso kuseka aneneri ake. Anafika poti panalibenso chiyembekezo choti angathe kuchiritsidwa. Kenako Yehova anawakwiyira kwambiri n’kuwalanga.” (2 Mbiri 36:16) Aisiraeli anafika poipa kwambiri moti sizinali zoyenera kuti Yehova awachitire chifundo. Zochita zawo zinamukwiyitsa kwambiri. Ndiye kodi zotsatira zake zinali zotani?
19 Yehova anasiya kuchitira chifundo anthu ake. Iye ananena kuti: “Sindidzawakomera mtima, kuwamvera chisoni kapena kuwachitira chifundo. Palibe chimene chidzandilepheretse kuti ndiwawononge.” (Yeremiya 13:14) Choncho mzinda wa Yerusalemu komanso kachisi zinawonongedwa, ndipo Aisiraeli anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo. Zimakhala zomvetsa chisoni kwambiri anthu akasiya kumvera Yehova mpaka kufika poti sizingathekenso kuwachitira chifundo.—Maliro 2:21.
20, 21. (a) Kodi chidzachitike n’chiyani Mulungu akadzaona kuti wasonyeza chifundo mokwanira? (b) Nanga ndi njira ina iti imene Yehova amasonyezera chifundo yomwe tidzakambirane m’mutu wotsatira?
20 Nanga bwanji masiku ano? Yehova sanasinthe. Chifukwa cha chifundo, iye wauza Mboni zake kuti zilalikire ‘uthenga wabwino wa Ufumu’ padziko lonse lapansi. (Mateyu 24:14) Anthu a mtima wabwino akamvetsera, Yehova amawathandiza kumvetsa uthengawo. (Machitidwe 16:14) Koma sikuti ntchito yolalikira idzagwiridwa mpaka kalekale. Yehova sangakhale kuti akusonyeza chifundo ngati atalola kuti dziko loipali limodzi ndi mavuto ake onse zipitirire mpaka kalekale. Akadzafika poona kuti wasonyeza chifundo mokwanira, adzapereka chiweruzo. Ndipo akamadzachita zimenezi, adzakhalanso kuti akuchitira chifundo atumiki ake okhulupirika komanso adzaonetsetsa kuti ‘dzina lake loyera’ lalemekezedwa. (Ezekieli 36:20-23) Yehova adzachotsa zoipa zonse ndipo adzabweretsa dziko latsopano lolungama. Koma ponena za anthu oipa, iye anati: “Diso langa silimva chisoni ndipo sindiwasonyeza chifundo. Ndiwabwezera mogwirizana ndi zochita zawo.”—Ezekieli 9:10.
21 Komabe, panopa Yehova akupitiriza kusonyeza chifundo ngakhale kwa anthu amene akhoza kudzawonongedwa. Anthu ochimwa amene alapa mochokera pansi pa mtima, Yehova akhoza kuwasonyeza chifundo m’njira ina yaikulu. Iye akhoza kuwakhululukira machimo. M’mutu wotsatira, tidzakambirana mawu ena ochititsa chidwi amene Baibulo limagwiritsa ntchito pofuna kutithandiza kumvetsa kuti Yehova amakhululuka ndi mtima wonse.
a Komabe n’zochititsa chidwi kuti pa Salimo 103:13, mawu a Chiheberi akuti ra·chamʹ amanena za chifundo chimene bambo amasonyeza ana ake.
-
-
Mulungu “Wokonzeka Kukhululuka”Yandikirani Yehova
-
-
MUTU 26
Mulungu “Wokonzeka Kukhululuka”
1-3. (a) Kodi ndi katundu wolemera uti amene Davide anasenza, nanga n’chiyani chinamukhazika mtima pansi? (b) Kodi tikachimwa zimakhala ngati tanyamula katundu uti, koma kodi Yehova amatitsimikizira chiyani?
WOLEMBA masalimo Davide anati: “Zolakwa zanga zakwera kupitirira mutu wanga. Sindingathe kuzisenza chifukwa zikulemera kwambiri ngati katundu wolemera. Thupi langa lonse lachita dzanzi ndipo ndilibiretu mphamvu.” (Salimo 38:4, 8) Davide ankadziwa kuti tikamadziimba mlandu chifukwa chochita tchimo, zimakhala ngati tasenza katundu wolemera kwambiri. Koma panali chinthu china chimene chinkamukhazika mtima pansi. Anazindikira kuti ngakhale kuti Yehova amadana ndi machimo, iye sadana ndi munthu wochimwa amene walapa mochokera pansi pa mtima n’kusiya machimowo. Pokhala ndi chikhulupiriro chonse kuti Yehova ndi wofunitsitsa kuchitira chifundo anthu olapa, Davide anati: “Inu Yehova ndinu . . . wokonzeka kukhululuka.”—Salimo 86:5.
2 Ifenso tikachita tchimo, chikumbumtima chathu chikhoza kumativutitsa kwambiri ndipo zingakhale ngati tanyamula katundu wolemera. Kumva chisoni kotereku n’kwabwino. Kungatichititse kuti tiyesetse kukonza zomwe talakwitsazo. Komabe, nthawi zina tikhoza kumadziimba mlandu mopitirira malire mpaka kufika pomaganiza kuti Yehova sangatikhululukire ngakhale titalapa mochokera pansi pa mtima. Ngati ‘tingakhale ndi chisoni chopitirira malire,’ Satana angayesetse kutichititsa kuti tisiye kutumikira Yehova, potipangitsa kuganiza kuti Yehovayo amationa kuti ndife osafunika ndiponso osayenera kumutumikira.—2 Akorinto 2:5-11.
3 Koma kodi ndi zoona kuti Yehova amationa choncho? Ayi ndithu. Tikutero chifukwa kukhululuka ndi njira imodzi imene Yehova amasonyezera chikondi chake chachikulu. M’Mawu ake, iye amatitsimikizira kuti tikalapa mochokera pansi pa mtima, amakhala wokonzeka kutikhululukira. (Miyambo 28:13) Kuti tisamakayikire kuti Yehova akhoza kutikhululukira, tiyeni tikambirane chifukwa chake amatikhululukira komanso mmene amachitira zimenezi.
Chifukwa Chake Yehova Ndi “Wokonzeka Kukhululuka”
4. Kodi Yehova amakumbukira chiyani chokhudza mmene anatilengera, ndipo zimenezi zimakhudza bwanji mmene amachitira nafe zinthu?
4 Yehova amadziwa zimene sitingathe kuchita. Lemba la Salimo 103:14 limati: “Iye akudziwa bwino mmene anatipangira, amakumbukira kuti ndife fumbi.” Saiwala kuti tinapangidwa kuchokera kudothi komanso kuti nthawi zambiri timalakwitsa zinthu chifukwa choti ndife ochimwa. Mawu akuti amadziwa bwino “mmene anatipangira” akutikumbutsa zimene Baibulo limanena. Timayerekezera Yehova ndi woumba mbiya ndipo ifeyo limatiyerekezera ndi dongo loumbira zinthu. (Yeremiya 18:2-6) Woumba Wamkuluyu amachita nafe zinthu mokoma mtima poganizira kuti ndife ochimwa komanso potengera zimene timachita akatipatsa malangizo.
5. Kodi buku la Aroma limatithandiza bwanji kudziwa kuti uchimo umagwira anthu mwamphamvu kwambiri?
5 Yehova amadziwa kuti uchimo ndi wamphamvu kwambiri. Baibulo limafotokoza kuti anthufe uchimo umatigwira mwamphamvu kwambiri ndipo umachititsa kuti tizifa. Kodi timadziwa bwanji kuti uchimo ndi wamphamvu kwambiri? M’buku la Aroma, mtumwi Paulo anafotokoza kuti ‘timalamuliridwa ndi uchimo,’ ngati mmene zimakhalira ndi asilikali amene amalamuliridwa ndi mtsogoleri wawo (Aroma 3:9); uchimo ‘umalamulira’ anthu ngati mfumu (Aroma 5:21); ‘umakhala nafe’ (Aroma 7:17, 20) ndiponso “lamulo” lake limagwira ntchito m’thupi mwathu nthawi zonse, n’kumayesa kutichititsa zofuna za uchimowo. (Aroma 7:23, 25) Izitu zikungosonyezeratu kuti uchimo ndi wamphamvu kwambiri kwa anthu omwe si angwirofe.—Aroma 7:21, 24.
6, 7. (a) Kodi Yehova amawaona bwanji anthu amene alapa n’kupempha kuti awakhululukire? (b) N’chifukwa chiyani sitiyenera kuganiza kuti tikhoza kumachita machimo mwadala ndipo Mulungu atikhululukira chifukwa choti ndi wachifundo?
6 Choncho Yehova amadziwa kuti sitingathe kumumvera osalakwitsa chilichonse, ngakhale titayesetsa bwanji. Mwachikondi amatitsimikizira kuti tikalapa mochokera pansi pa mtima n’kupempha kuti atichitire chifundo, iye adzatikhululukira. Lemba la Salimo 51:17 limati: “Nsembe zimene Mulungu amasangalala nazo ndi kudzimvera chisoni mumtima. Inu Mulungu, simudzakana mtima wosweka ndi wophwanyika.” Yehova sakana munthu yemwe ali ndi “mtima wosweka ndi wophwanyika” chifukwa chodziimba mlandu kwambiri.
7 Komabe, kodi zimenezi zikutanthauza kuti popeza tinabadwa ndi uchimo tikhoza kumachimwa mwadala n’kumaganiza kuti Mulungu ndi wachifundo atikhululukira? Ayi ndithu. Yehova sachita zinthu pongotengera mmene akumvera. Chifundo chake chili ndi malire. Iye sakhululukira anthu amene amachita machimo mwadala koma osalapa n’kuwasiya. (Aheberi 10:26) Komabe, akaona kuti wina ali ndi mtima wolapa amamukhululukira. Tsopano tiyeni tikambirane mawu ena ochititsa chidwi amene Baibulo limagwiritsa ntchito pofotokoza mmene Yehova amasonyezera chikondi chake m’njira yapaderayi.
Kodi Yehova Amakhululuka Mpaka Pati?
8. Kodi tingati Yehova amachita chiyani akatikhululukira, nanga timamva bwanji chifukwa cha zimenezi?
8 Davide atalapa ananena mawu ananena kuti: “Pamapeto pake ndinaulula tchimo langa kwa inu, sindinabise cholakwa changa. . . . Ndipo inu munandikhululukira zolakwa zanga ndi machimo anga.” (Salimo 32:5) Mawu akuti “munandikhululukira” anamasuliridwa kuchokera ku mawu a Chiheberi amene kwenikweni amatanthauza “kunyamula” kapena “kutenga.” Palembali anawagwiritsa ntchito ponena za kuchotsa “cholakwa, tchimo kapena choipa.” Choncho tingati Yehova ananyamula machimo a Davide n’kuwachotsa. N’zosakayikitsa kuti zimenezi zinathandiza Davide kuti asamadziimbe mlandu kwambiri. (Salimo 32:3) Ifenso tingakhulupirire ndi mtima wonse kuti Mulungu akhoza kutichotsera machimo athu ngati titamupempha kuti atikhululukire pogwiritsa ntchito nsembe ya dipo ya Yesu.—Mateyu 20:28.
9. Kodi Yehova amaika machimo athu kutali bwanji ndi ife?
9 Davide anagwiritsanso ntchito mawu ena amphamvu ofotokoza kukhululuka kwa Yehova. Iye anati: “Mofanana ndi mmene kotulukira dzuwa kwatalikirana ndi kolowera dzuwa, Mulungu waikanso zolakwa zathu kutali ndi ife.” (Salimo 103:12) Dzuwa limatuluka kum’mawa n’kukalowa kumadzulo. Kodi kum’mawa n’kotalikirana bwanji ndi kumadzulo? Nthawi zonse kum’mawa kumakhala kotalikirana kwambiri ndi kumadzulo ndipo mbali ziwirizi sizingakumane. Katswiri wina wa Baibulo anati mawuwa amatanthauza “kutali kwambiri koti sitingakuyerekezere.” Mawu a Davide ouziridwawa amatithandiza kudziwa kuti Yehova akakhululuka, amatenga machimo athu n’kukawataya kutali kwambiri.
“Machimo anu . . . adzayera kwambiri”
10. Yehova akatikhululukira, n’chifukwa chiyani sitifunika kumamva kuti ndife othimbirira ndi machimo kwa moyo wathu wonse?
10 Kodi munayesapo kuchapa chovala choyera chomwe chathimbirira? Mwina munayesetsa kuti muchotse zothimbirirazo koma sizinatheke. Koma taonani zimene Yehova amachita pa nkhani yokhululuka. Iye anati: “Ngakhale kuti machimo anu ndi ofiira kwambiri, adzayera kwambiri. Ngakhale kuti ndi ofiira ngati magazi, adzayera ngati thonje.” (Yesaya 1:18)a Patokha sitingathe kuchotsa uchimo womwe tingati unatithimbiriritsa. Koma Yehova akhoza kuchotseratu kuthimbirira kumeneku. Iye akatikhululukira machimo athu, sitifunikanso kumamva kuti ndife othimbirira ndi machimowo kwa moyo wathu wonse.
11. Kodi Yehova amaponya machimo athu kumbuyo kwake m’njira yotani?
11 Hezekiya atachiritsidwa matenda omwe akanafa nawo, analemba nyimbo yosangalatsa kwambiri. Iye anauza Yehova kuti: “Machimo anga onse mwawaponyera kumbuyo kwanu.” (Yesaya 38:17) Lembali likusonyeza kuti Yehova amatenga machimo a munthu wochimwa yemwe walapa n’kuwaponya kumbuyo kwake kumene iye sawaonanso kapena kuwaganiziranso. Mogwirizana ndi zimene buku lina linanena zokhudza lembali, tikhoza kunenanso kuti lembali limanena kuti: “Mwachititsa [machimo anga] kukhala ngati sanachitike.” Kodi zimenezi si zolimbikitsa kwambiri?
12. Kodi mneneri Mika anasonyeza bwanji kuti Yehova akatikhululukira amataya kutali machimo athu ndipo sawaganiziranso?
12 Ponena za lonjezo la Mulungu lobwezeretsa zinthu, Mika anasonyeza kuti ankakhulupirira kuti Yehova adzakhululukira anthu ake omwe alapa. Iye anati: “Kodi pali Mulungu winanso wofanana ndi inu, amene amakhululukira zolakwa . . . anthu ake otsala omwe ndi cholowa chake? . . . Machimo athu onse mudzawaponya m’nyanja pamalo ozama.” (Mika 7:18, 19) Taganizirani zimene mawu amenewa anatanthauza kwa atumiki a Yehova pa nthawiyo. Kodi zikanatheka kuvuula chinthu chimene chamira “m’nyanja pamalo ozama”? Choncho zimene Mika ananena zikusonyeza kuti Yehova akakhululuka, amataya kutali machimo athu ndipo sawaganiziranso.
13. Kodi mawu a Yesu akuti “mutikhululukire zolakwa zathu” amatanthauza chiyani?
13 Pofuna kutithandiza kumvetsa zimene Yehova amachita akakhululuka, Yesu anafotokoza chitsanzo cha zomwe zimachitika pakati pa munthu wokongoza zinthu ndi wokongola. Iye anatilimbikitsa kupemphera kuti: “Mutikhululukire zolakwa zathu.” (Mateyu 6:12) Mawu a chilankhulo choyambirira omwe anawamasulira kuti “zolakwa,” ankatanthauza ngongole. Choncho Yesu anayerekezera machimo ndi ngongole. (Luka 11:4) Tikachita tchimo timakhala ndi “ngongole” yoti tipereke kwa Yehova. Ponena za mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti “mutikhululukire,” buku lina linati amatanthauza “kukhululukira ngongole n’kusiya osadzailonjereranso.” Zimenezi n’zimene Yehova amachita akatikhululukira. Iye amakhala ngati wathetsa ngongole imene timafunika kumubwezera. Izitu n’zolimbikitsa kwambiri kwa anthu ochimwa omwe alapa. Yehova sangalonjerere ngongole imene anaithetsa.—Salimo 32:1, 2.
14. Kodi mawu akuti “machimo anu afafanizidwe” amatithandiza bwanji kumvetsa bwino zimene Yehova amachita akatikhululukira?
14 Zimene Yehova amachita pokhululuka zafotokozedwanso bwino pa Machitidwe 3:19 kuti: “Choncho lapani ndi kutembenuka kuti machimo anu afafanizidwe.” Mawu akuti “afafanizidwe” anamasuliridwa kuchokera ku mawu a Chigiriki amene akhoza kutanthauza “kupukuta, . . . kufufuta kapena kuwononga.” Mogwirizana ndi zimene akatswiri ena a Baibulo amanena, mawuwa amafotokoza za kufufuta zimene munthu walemba. Kodi zimenezi zinkatheka bwanji? Inki imene kale ankaigwiritsa ntchito, nthawi zambiri ankaipanga posakaniza makala, manthova a mitengo, madzi ndiponso zinthu zina. Munthu akangomaliza kulemba ndi inkiyo, ankatha kutenga siponji yonyowa n’kufufuta zimene analembazo. Zimenezitu zikutithandiza kumvetsa bwino chifundo cha Yehova. Iye akatikhululukira machimo athu, zimakhala ngati watenga siponji n’kuwafufuta.
15. Kodi Yehova amafuna kuti tidziwe zinthu ziti zokhudza iyeyo?
15 Tikaganizira mawu ochititsa chidwi osiyanasiyana amenewa, n’zodziwikiratu kuti Yehova amafuna kuti tidziwe kuti iye ndi wokonzeka kutikhululukira akaona kuti talapa mochokera pansi pa mtima. Choncho tisamaope kuti m’tsogolo adzatiimbanso mlandu pa machimo omwewo. Zimenezi zikuonekera bwino mu mfundo inanso imene Baibulo limanena yokhudza chifundo chachikulu cha Yehova, yakuti: Akakhululuka, amaziiwala.
Yehova amafuna kuti tidziwe kuti ndi “wokonzeka kukhululuka”
“Machimo Awo Sindidzawakumbukiranso”
16, 17. Kodi Baibulo limatanthauza chiyani likamati Yehova amaiwala machimo athu, ndipo n’chifukwa chiyani mukuyankha choncho?
16 Ponena za anthu amene ali m’pangano latsopano, Yehova analonjeza kuti: “Ine ndidzawakhululukira zolakwa zawo ndipo machimo awo sindidzawakumbukiranso.” (Yeremiya 31:34) Kodi izi zikutanthauza kuti Yehova akakhululuka sathanso kukumbukira machimowo? Ayi si choncho. Baibulo limatiuza za anthu amene anachita machimo omwe Yehova anawakhululukira, mwachitsanzo Davide. (2 Samueli 11:1-17; 12:13) N’zodziwikiratu kuti Yehova akudziwabe machimo amene anthuwo anachita. Machimo awo, kulapa kwawo ndiponso mmene Mulungu anawakhululukirira, zonsezi zinalembedwa m’Baibulo kuti zizitithandiza. (Aroma 15:4) Ndiye kodi Baibulo limatanthauza chiyani likamati Yehova ‘sakumbukira’ machimo a anthu amene anawakhululukira?
17 Mawu a Chiheberi amene anawamasulira kuti “sindidzawakumbukiranso,” amatanthauza zambiri osati kungokumbukira zinthu zakale. Buku lina limati mawuwa amatanthauzanso “kuchitapo kanthu pa zimene zinachitika.” (Theological Wordbook of the Old Testament) Choncho, ‘kukumbukira’ machimo kukuphatikizapo kulanga wochimwayo. (Hoseya 9:9) Koma pamene Mulungu ananena kuti “machimo awo sindidzawakumbukiranso” akutitsimikizira kuti akakhululukira ochimwa amene alapa, ndiye kuti m’tsogolo sadzawapatsanso chilango chifukwa cha machimo awowo. (Ezekieli 18:21, 22) Choncho Yehova amaiwala m’njira yakuti samangokhalira kutikumbutsa machimowo n’cholinga chakuti azitiimba mlandu kapena kutilanga. N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Mulungu wathu amakhululuka n’kuiwala.
Nanga Bwanji Zotsatira Zake?
18. N’chifukwa chiyani kukhululukidwa machimo sikutanthauza kuti wochimwa amene walapayo sakumana ndi zotsatira zoipa za machimo akewo?
18 Kodi Yehova akakhululukira wochimwa yemwe walapa, ndiye kuti munthuyo sakumana ndi zotsatira za tchimo lakelo? Ayi si choncho. Sitingachite tchimo n’kumayembekezera kuti sitikumana ndi vuto lililonse. Paulo analemba kuti: “Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.” (Agalatiya 6:7) Tingakumane ndi mavuto ena chifukwa cha zimene tinachita. Zimenezi sizikutanthauza kuti Yehova amatibweretsera mavuto pambuyo poti watikhululukira. Mkhristu akayamba kukumana ndi mavuto, asamaganize kuti, ‘Mwina Yehova akundilanga chifukwa cha machimo amene ndinachita.’ (Yakobo 1:13) Tizikumbukira kuti Yehova samatiteteza ku mavuto onse obwera chifukwa cha machimo omwe tinachita. Kutha kwa banja, mimba yosafunika, matenda opatsirana pogonana, anthu kusiya kukukhulupirira kapena kukulemekeza, zonsezi zingakhale zotsatira zomvetsa chisoni ndiponso zosapeweka za tchimo lomwe munthu anachita. Kumbukirani kuti ngakhale kuti Yehova anakhululukira Davide machimo ake okhudzana ndi Bati-seba ndi Uriya, sanamuteteze ku zotsatira zoipa za machimowo.—2 Samueli 12:9-12.
19-21. (a) Kodi lamulo la pa Levitiko 6:1-7 linkathandiza bwanji wolakwiridwa ndiponso wolakwa? (b) Ngati machimo athu achititsa kuti anthu ena akumane ndi mavuto, kodi Yehova amasangalala tikachita zinthu ziti?
19 Machimo athu angakhale ndi zotsatira zinanso, makamaka ngati zimene tinachitazo zakhudzanso anthu ena. Mwachitsanzo taganizirani zimene zafotokozedwa m’buku la Levitiko, chaputala 6. M’chaputalachi, Chilamulo cha Mose chikufotokoza zimene zinkayenera kuchitika munthu akaba kapena kulanda katundu wa Mwisiraeli mnzake kapenanso kumuchitira zachinyengo kenako n’kukana kuti sanachite zimenezo, mwinanso mpaka kulumbira. Nkhaniyi inkakhala yoti palibe munthu wina amene angapereke umboni. Koma kenako mwina wolakwayo ankavutika ndi chikumbumtima n’kuvomera tchimo lake. Kuti Mulungu amukhululukire, ankafunika kuchita zinthu zinanso zitatu izi: Kubweza zimene anabazo, kupereka chindapusa kwa mwini katunduyo chokwana magawo 20 a magawo 100 alionse a zomwe anabazo ndiponso kupereka nkhosa yamphongo kuti ikhale nsembe yakupalamula. Ndiyeno Chilamulo chinkati: “Wansembe aziphimba machimo a munthuyo pamaso pa Yehova, ndipo adzakhululukidwa.”—Levitiko 6:1-7.
20 Lamulo limeneli linkasonyeza kuti Mulungu ndi wachifundo. Linkathandiza woberedwa chifukwa katundu wake ankabwezedwa komanso ankasangalala kuti wakubayo wavomereza tchimo lake. Lamuloli linkathandizanso munthu wochimwayo, amene chikumbumtima chake chinkamuchititsa kuti avomereze kulakwa kwake n’kukonza zolakwikazo. Ngati akanakana kuchita zimenezi, Mulungu sakanamukhululukira.
21 Ngakhale kuti sititsatira Chilamulo cha Mose, Chilamulochi chimatithandiza kudziwa maganizo a Yehova pa nkhani yokhululuka. (Akolose 2:13, 14) Ngati machimo athu achititsa kuti anthu ena akumane ndi mavuto, Mulungu amasangalala tikachita zomwe tingathe kuti tikonze zolakwazo. (Mateyu 5:23, 24) Zimenezi zingaphatikizepo kuvomera kuti tinachita tchimo, kuvomereza kuti tinalakwa komanso kupepesa munthu amene tinamulakwirayo. Kenako tingapemphe Mulungu kuti atikhululukire pogwiritsa ntchito nsembe ya Yesu ndipo tingayambe kumva kuti watikhululukira.—Aheberi 10:21, 22.
22. Kodi n’chiyani chingachitike ngakhale kuti Yehova watikhululukira?
22 Mofanana ndi kholo lililonse lachikondi, Yehova akatikhululukira akhoza kutipatsanso chilango. (Miyambo 3:11, 12) Ngakhale kuti Mkhristu analapa, akhoza kuluza mwayi womwe anali nawo wokhala mkulu, mtumiki wothandiza kapena kusiya utumiki wa nthawi zonse. Zingakhale zopweteka kwambiri kuti kwa kanthawi sazichitanso utumiki womwe ankaukonda. Komabe chilango chimenechi sichitanthauza kuti Yehova sanamukhululukire. Tizikumbukira kuti Yehova akatipatsa chilango ndi umboni wakuti amatikonda. Kuvomereza chilango chomwe tapatsidwa n’kusintha kumatithandiza kwambiri.—Aheberi 12:5-11.
23. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuganiza kuti Yehova sangatichitire chifundo, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kutsanzira Yehova pa nkhani yokhululukira ena?
23 N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Mulungu wathu ndi “wokonzeka kukhululuka.” Kaya tachita zolakwa zotani, tisamaganize kuti Yehova sangatichitire chifundo. Tikalapa ndi mtima wonse, kuchita zonse zofunika kuti tikonze zolakwikazo ndiponso kupemphera mochokera pansi pa mtima kuti Yehova atikhululukire pogwiritsa ntchito magazi a Yesu, tisamakayikire kuti watikhululukira. (1 Yohane 1:9) Tiyeni tizitsanzira Yehova pa nkhani yokhululukira anzathu. Ngati Yehova amene sachimwa amatikhululukira mwachikondi, kodi si zoyenera kuti anthu ochimwafe tiziyesetsa mmene tingathere kukhululukira ena?
a Katswiri wina wa Baibulo anati kufiira kotchulidwa palembali sikunkasuluka ngakhale pang’ono. Chinthu chamtunduwu sichinkasintha maonekedwe ngakhale atachiika pamame, pamvula, kuchichapa kapena kuchigwiritsa ntchito kwa nthawi yaitali.
-
-
“Ubwino Wake Ndi Waukulu Kwambiri!”Yandikirani Yehova
-
-
MUTU 27
“Ubwino Wake Ndi Waukulu Kwambiri!”
1, 2. Kodi ndi ndani amene amapindula chifukwa choti Yehova ndi wabwino, nanga Baibulo limafotokoza zotani zokhudza ubwino wa Yehova?
MUNTHU wina ndi anzake apamtima akudyera limodzi chakudya panja pomwe dzuwa likulowa. Anthuwa akucheza komanso kuseka pamene akuona kukongola kwa dzuwalo. Kudera lina lakutali, mlimi akuyang’ana munda wake mosangalala chifukwa mvula yayamba kugwa, pambuyo poti mbewu zake zinafota ndi dzuwa. Kudera linanso, mwamuna ndi mkazi wake akusangalala kuona mwana wawo akuyamba kuyenda.
2 Kaya anthuwa akudziwa kapena ayi, onsewa akusangalala ndi zinthu zimenezi chifukwa choti Yehova ndi wabwino. Anthu ambiri opemphera amakonda kunena kuti “Mulungu ndi wabwino.” Koma Baibulo limanena zoposa pamenepa. Limati: “Ubwino wake ndi waukulu kwambiri.” (Zekariya 9:17) Koma zikuoneka kuti masiku ano pali anthu ochepa okha omwe amadziwa zimene mawuwa amatanthauza. Ndiye kodi mfundo yoti Yehova ndi wabwino imatanthauza chiyani, nanga tonsefe timapindula bwanji ndi khalidwe la Mulungu limeneli?
Khalidwe Lomwe Limasonyeza Kuti Yehova Ndi Wachikondi
3, 4. Kodi ubwino n’chiyani, nanga n’chifukwa chiyani tinganene kuti mfundo yoti Yehova ndi wabwino imasonyeza kuti iye ndi wachikondi?
3 M’zilankhulo zambiri masiku ano, mawu akuti “ubwino” amangowagwiritsa ntchito pa zilizonse. Komabe, Baibulo limasonyeza kuti ubwino ndi khalidwe palokha. Nthawi zambiri limatanthauza kukhala ndi makhalidwe abwino kwambiri. Choncho tikhoza kunena kuti Yehova ndi wabwino kwambiri pa chilichonse. Mphamvu zake, chilungamo chake, nzeru zake ndiponso makhalidwe ake ena onse ndi abwino kwambiri. Komabe, tinganene kuti mfundo yoti Yehova ndi wabwino imasonyeza kuti iye ndi wachikondi. N’chifukwa chiyani tikutero?
4 Munthu yemwe ndi wabwino amachitira zinthu zabwino anthu ena. Mtumwi Paulo anasonyeza kuti anthu amasangalala kwambiri ndi munthu wabwino kuposa wolungama. (Aroma 5:7) Munthu wolungama amatsatira malamulo mokhulupirika, koma munthu wabwino amachita zoposa pamenepo. Amayamba ndi iyeyo kuchitapo kanthu ndipo amafufuza njira zothandizira ena. Monga tionere, Yehova ndi wabwino m’njira imeneyi. N’zodziwikiratu kuti iye amasonyeza khalidwe la ubwino chifukwa cha chikondi chake chopanda malire.
5-7. N’chifukwa chiyani Yesu anakana kutchulidwa kuti “Mphunzitsi Wabwino,” ndipo kodi pamenepa anaphunzitsa mfundo ya choonadi yofunika iti?
5 Yehova ndi wabwino kuposa aliyense. Kutatsala nthawi yochepa kuti Yesu aphedwe, munthu wina anapita kukamufunsa funso. Munthuyo anatchula Yesu kuti “Mphunzitsi Wabwino.” Yesu anamuyankha kuti: “Nʼchifukwa chiyani ukunditchula kuti wabwino? Palibe wabwino, koma Mulungu yekha.” (Maliko 10:17, 18) Mwina yankho limeneli lingakudabwitseni kwambiri. N’chifukwa chiyani Yesu anamukonza munthuyo? Kodi m’mesa Yesu analidi “Mphunzitsi Wabwino”?
6 N’zodziwikiratu kuti munthuyo anatchula Yesu kuti “Mphunzitsi Wabwino” popereka ulemu wabodza. Modzichepetsa, Yesu anapereka ulemerero umenewu kwa Atate ake akumwamba, omwe ndi abwino kwambiri kuposa aliyense. (Miyambo 11:2) Koma pamenepa Yesu anaphunzitsanso mfundo yofunika kwambiri. Popeza ndi Wolamulira Wamkulu Kwambiri, Yehova yekha ndi amene ali ndi ufulu wotiuza zinthu zomwe ndi zabwino kapena zoipa. Pamene Adamu ndi Hava sanamvere Mulungu n’kudya zipatso za mtengo wodziwitsa zabwino ndi zoipa, anasonyeza kuti ankafuna kukhala ndi ufulu umenewu. Koma mosiyana ndi iwowo, modzichepetsa Yesu anavomereza kuti Atate ake okha ndi amene ali ndi ufulu wouza anthu kuti ichi n’chabwino, ichi n’choipa.
7 Ndiponso, Yesu ankadziwa kuti chinthu chilichonse chabwino chimachokera kwa Yehova. Ndi iyeyo amene amapereka “mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro.” (Yakobo 1:17) Tiyeni tione mmene Yehova amasonyezera kuti ndi wabwino pokhala wowolowa manja.
Umboni Woti Yehova Ndi Wabwino Kwambiri
8. Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti ndi wabwino kwa anthu onse?
8 Munthu aliyense amene anakhalako ndi moyo anapindulako ndi ubwino wa Yehova. Lemba la Salimo 145:9 limati: “Yehova ndi wabwino kwa aliyense.” Kodi zitsanzo zina zosonyeza kuti iye ndi wabwino kwa anthu onse ndi ziti? Baibulo limati: “Iye sanangokhala wopanda umboni wakuti anachita zabwino. Anakupatsani mvula kuchokera kumwamba ndi nyengo zimene zokolola zanu zimakhala zambiri. Anadzaza mitima yanu ndi chakudya komanso chisangalalo.” (Machitidwe 14:17) Kodi munadyapo chakudya chokoma chomwe munasangalala nacho kwambiri? Zikanakhala kuti Yehova si wabwino ndipo sanakonze zoti padzikoli pazigwa mvula komanso pazikhala ‘nyengo zimene zokolola zimakhala zambiri,’ bwenzi kulibe zakudya. Yehova amachitira aliyense zabwinozi, osati anthu amene amamukonda okha. Yesu anati: “Iye amawalitsira dzuwa lake anthu abwino ndi oipa omwe, ndipo amagwetsera mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.”—Mateyu 5:45.
9. Kodi maapozi amasonyeza bwanji kuti Yehova ndi wabwino?
9 Chifukwa chakuti nthawi zonse timakhala ndi dzuwa, mvula ndiponso nyengo ya zipatso, ambiri saona kuti m’pofunika kumayamikira zinthu zimene Yehova amatipatsa mosaumira. Mwachitsanzo, taganizirani za maapozi. Zipatso zimenezi zimapezeka kwambiri m’madera otentha padzikoli. Komatu ndi zipatso zokongola, zokoma komanso zimakhala ndi madzi ambiri ndiponso zinthu zofunika m’thupi. Kodi mukudziwa kuti padzikoli pali mitundu pafupifupi 7,500 ya maapozi owoneka mosiyanasiyana? Ena ndi ofiira, ena agolide, ayelo ndiponso agirini. Maapoziwa amasiyananso kukula kwake, ena amakhala akuluakulu pomwe ena amakhala ang’onoang’ono. Mukatenga kanjere ka apozi m’manja mwanu, zimangokhala ngati palibe chimene mwagwira. Koma kanjereka kakamera, kamakula n’kukhala umodzi wa mitengo yosangalatsa kwambiri. (Nyimbo ya Solomo 2:3) Chaka chilichonse mitengo ya maapozi imachita maluwa okongola ndipo kenako imabereka zipatso. Pa chaka, mtengo wa maapozi umabereka zipatso zokwana makatoni 20, katoni iliyonse yolemera makilogalamu 19 ndipo umachita zimenezi kwa zaka 75.
Yehova ‘amakupatsani mvula kuchokera kumwamba ndi nyengo zimene zokolola zanu zimakhala zambiri’
Kanjere kakang’ono aka kamamera n’kukhala mtengo umene zipatsa zake anthu amadya komanso kusangalala nazo kwa zaka zambiri
10, 11. Kodi mmene thupi lathu linapangidwira zimasonyeza bwanji kuti Mulungu ndi wabwino?
10 Chifukwa cha ubwino wake wosatha, Yehova anatipatsa thupi ‘lopangidwa modabwitsa,’ limene limatha kuzindikira zomwe Mulungu analenga n’kumasangalala nazo. (Salimo 139:14) Taganiziraninso zitsanzo zomwe tafotokoza m’ndime yoyamba zija. Mukanakhala kuti inuyo munalipo, kodi ndi zinthu ziti zomwe mukanasangalala mutaziona? Kodi ndi kumwetulira kwa mwana yemwe akusangalala, mvula ikugwa m’minda, kapena mitundu yosiyanasiyana imene dzuwa limaonetsa likamalowa? Diso la munthu linapangidwa kuti lizitha kusiyanitsa mitundu ya zinthu mahandiredi masauzande, mwinanso mpaka mamiliyoni. Ndiponso makutu athu amatha kuzindikira mawu abwino amene tikumva kuchokera kwa munthu yemwe timam’konda, kuseka kwa mwana yemwe wasangalala kapenanso kaphokoso kamphepo yomwe ikudutsa m’mitengo. Kodi n’chifukwa chiyani timatha kuona komanso kumva zinthu zimenezi? Baibulo limati: “Khutu lakumva ndiponso diso loona, zonsezi anazipanga ndi Yehova.” (Miyambo 20:12) Koma pali zinthu zinanso zomwe timachita zomwe zimatithandiza kuti tizisangalala ndi moyo.
11 Umboni wina woti Yehova ndi wabwino ndi woti timatha kumva fungo. Mphuno ya munthu ikhoza kusiyanitsa mitundu yosiyanasiyana ya fungo yofika mpaka 1 thililiyoni. Mwachitsanzo, taganizirani za fungo lomwe mumamva wina akamaphika chakudya chomwe mumachikonda, la maluwa, la masamba ouma omwe athothoka komanso la utsi umene ukuchokera pamoto wonyeka bwino. Thupi lathu limazindikiranso kuti lakhudza kapena lakhudzidwa ndi chinthu chinachake. Mwachitsanzo, timamva kamphepo kayaziyazi kakatiwomba kumaso, timamva bwino wokondedwa wathu akatihaga komanso tikagwira chipatso chosalala. Mukamadya chipatsocho mumamva kukoma kwambiri ndipo kukomako kumamveka mosiyanasiyana m’kamwamu. N’zosachita kufunsa kuti tili ndi zifukwa zomveka zotamandira Yehova kuti: “Ubwino wanu ndi wochuluka kwambiri! Ubwino umenewu mwasungira anthu amene amakuopani.” (Salimo 31:19) Koma kodi zikutanthauza chiyani tikamati Yehova wasungira ubwino anthu amene amamuopa?
Zinthu Zabwino Zomwe Zidzatithandize Mpaka Kalekale
12. Kodi ndi zinthu ziti zimene Yehova amatipatsa zomwe ndi zofunika kwambiri, ndipo n’chifukwa chiyani?
12 Yesu anati: “Malemba amati: ‘Munthu sangakhale ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu alionse ochokera mʼkamwa mwa Yehova.’” (Mateyu 4:4) Zoonadi, zinthu zauzimu zomwe Yehova amatipatsa zingatithandize kwambiri kuposa zakuthupi, chifukwa zauzimuzi zingatithandize kudzapeza moyo wosatha. M’Mutu 8 wa bukuli, tinaona kuti m’masiku otsiriza ano Yehova akugwiritsa ntchito mphamvu zake zobwezeretsa zinthu, pokhazikitsa paradaiso wauzimu. Mbali yaikulu ya paradaisoyu, ndi chakudya chauzimu chochuluka.
13, 14. (a) Kodi mneneri Ezekieli anaona chiyani m’masomphenya, nanga zimenezo zimatanthauza chiyani? (b) Kodi ndi zinthu ziti zothandiza kudzapeza moyo zimene Yehova akupatsa anthu ake okhulupirika?
13 Mu ulosi wina wofunika kwambiri wonena za kubwezeretsa zinthu, mneneri Ezekieli anaona masomphenya a kachisi waulemerero yemwe anabwezeretsedwa. Madzi ankayenda kuchokera kukachisiyo ndipo ankawonjezereka mpaka anakhala mtsinje. Kulikonse kumene mtsinjewo unkapita, unkabweretsa madalitso. M’mbali mwake munamera mitengo yomwe inkabereka zipatso komanso inkachiritsa anthu. Mtsinjewo unachititsanso Nyanja Yakufa, imene inali yamchere komanso munalibe zamoyo, kuti ikhale ndi zamoyo. (Ezekieli 47:1-12) Koma kodi zonsezi zinkatanthauza chiyani?
14 Masomphenya okhudza kachisiwa ankatanthauza kuti Yehova adzabwezeretsa kulambira koona ndipo anthu azidzamulambiranso mogwirizana ndi mfundo zake zolungama. Ankatanthauzanso kuti mofanana ndi mtsinje wa m’masomphenya uja, zinthu zothandiza kudzapeza moyo wosatha zimene Mulungu adzapatse anthu ake zizidzawonjezereka. Yehova wakhala akuchita zimenezi kungoyambira pamene kulambira koona kunabwezeretsedwa mu 1919. Kodi akuzichita bwanji? Pogwiritsa ntchito Baibulo, mabuku othandiza kumvetsa Baibulo komanso misonkhano ya mpingo ndi ikuluikulu, anthu mamiliyoni ambiri aphunzira choonadi. Yehova amagwiritsa ntchito zinthu zimenezi pophunzitsa anthu mfundo zofunika kwambiri, makamaka yokhudza nsembe ya dipo ya Khristu. Nsembeyi imathandiza anthu amene amakonda komanso kuopa Mulungu kuti Mulunguyo aziwaona kuti ndi olungama ndiponso adzapeze moyo wosatha.a Choncho m’masiku onse otsiriza ano, pamene dzikoli likuvutika ndi njala yauzimu, anthu a Yehova akhala akusangalala ndi phwando lauzimu.—Yesaya 65:13.
15. Mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu, kodi Yehova adzasonyeza bwanji ubwino wake kwa anthu okhulupirika?
15 Koma mtsinje umene Ezekieli anaona m’masomphenya sudzasiya kuyenda dziko loipali likadzawonongedwa. Udzapitiriza kuyenda komanso kukula mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu. Pa nthawi imeneyi, kudzera mu Ufumu wa Mesiya, Yehova adzagwiritsa ntchito nsembe ya Yesu pothandiza anthu okhulupirika mpaka anthuwo atakhala angwiro. Zikadzatero tidzasangalalatu kwambiri ndi ubwino wa Yehova.
Mbali Zinanso za Ubwino wa Yehova
16. Kodi Baibulo limasonyeza bwanji kuti Yehova alinso ndi makhalidwe ena abwino, nanga ena mwa makhalidwewa ndi ati?
16 Kuwonjezera pa kukhala wowolowa manja, Yehova amasonyeza kuti ndi wabwino m’njira zinanso. Iye anauza Mose kuti: “Ineyo ndidzakuonetsa ubwino wanga wonse, ndipo ndidzalengeza dzina langa lakuti Yehova kwa iwe.” Kenako nkhaniyi imati: “Yehova anadutsa pamaso pa Mose akulengeza kuti: ‘Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wosakwiya msanga ndiponso wachikondi chokhulupirika chochuluka komanso choonadi.’” (Ekisodo 33:19; 34:6, mawu a m’munsi) Choncho popeza Yehova ndi wabwino, alinso ndi makhalidwe ena abwino. Tiyeni tikambirane awiri okha.
17. Kodi munthu wachisomo amakhala wotani, nanga Yehova amasonyeza bwanji khalidweli kwa anthu omwe si angwirofe?
17 “Wachisomo.” Khalidwe limeneli, lomwe limamasuliridwanso kuti “wokoma mtima,” limatiuza zambiri za mmene Yehova amachitira zinthu ndi ena. Nthawi zambiri anthu audindo amakhala aukali komanso ankhanza. Koma Yehova nthawi zonse amachita zinthu modekha ndiponso mokoma mtima. Mwachitsanzo, iye anauza Abulamu kuti: “Takweza maso ako kuchokera pamene ulipo. Uyangʼane kumpoto ndi kumʼmwera, komanso kumʼmawa ndi kumadzulo.” (Genesis 13:14) Akatswiri a Baibulo amanena kuti m’Chiheberi choyambirira, mawu amulembali amasonyeza kuti Yehova ankapempha mwaulemu osati kulamula. Palinso malemba ena omwe Yehova anasonyeza kuti akupempha. (Genesis 31:12; Ezekieli 8:5) Tangoganizani, Wolamulira wa chilengedwe chonse amalankhula mwaulemu kwa anthu wamba. M’dzikoli anthu ambiri ndi olusa, ankhanza ndiponso achipongwe koma n’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Mulungu wathu, Yehova, ndi wachisomo.
18. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova ndi ‘wachoonadi chochuluka,’ nanga n’chifukwa chiyani zimenezi ndi zolimbikitsa?
18 ‘Wachoonadi chochuluka.’ Masiku ano anthu ambiri sachita zinthu moona mtima. Koma Baibulo limatikumbutsa kuti: “Mulungu sali ngati munthu amene amanena mabodza.” (Numeri 23:19) Ndipotu lemba la Tito 1:2 limati ‘Mulungu sanganame.’ Iye ndi wabwino kwambiri moti sangachite zimenezo. Choncho malonjezo a Yehova ndi odalirika kwambiri ndipo zimene wanena nthawi zonse zimachitika. Yehova amatchedwa “Mulungu wa choonadi.” (Salimo 31: 5) Sikuti amangopewa kunena zabodza, koma amatiuzanso mfundo zambiri za choonadi. Sabisa zimene amadziwa kapenanso kuchita zinthu mwachinsinsi. Koma mosaumira amauza atumiki ake nzeru zake zopanda malire.b Ndiponso amawauza zimene angachite kuti azitsatira choonadi chimene amawaphunzitsa n’cholinga choti ‘apitirize kuyendabe m’choonadicho.’ (3 Yohane 3) Ndiye kodi tiyenera kutani chifukwa chodziwa kuti Yehova ndi wabwino?
Muzisangalala “Chifukwa cha Ubwino wa Yehova”
19, 20. (a) Kodi Satana anachititsa bwanji kuti Hava azikayikira zoti Yehova ndi wabwino, nanga zotsatira zake zinali zotani? (b) Kodi mumamva bwanji mukaganizira za ubwino wa Yehova, ndipo n’chifukwa chiyani?
19 Pamene Satana ankayesa Hava m’munda wa Edeni, mochenjera kwambiri anamuchititsa kuti ayambe kukayikira kuti Yehova ndi wabwino. Yehova anali atauza Adamu kuti: “Zipatso za mtengo uliwonse wa mʼmundamu uzidya mmene ungafunire.” Pa mitengo yonse yambirimbiri imene inali m’mundawo, Yehova anangowaletsa mtengo umodzi wokha. Koma taonani funso loyamba limene Satana anafunsa Hava. Anati: “Eti nʼzoona kuti Mulungu ananena kuti musadye zipatso za mtengo uliwonse wamʼmundamu?” (Genesis 2:9, 16; 3:1) Satana anapotoza mawu a Yehova n’cholinga choti Hava aziganiza kuti Yehova sankafuna kumupatsa zinthu zina zabwino. N’zomvetsa chisoni kuti zimene ankafunazi zinachitikadi. Mofanana ndi anthu ambiri amene pambuyo pake anachitanso zomwezi, Hava anayamba kukayikira zoti Mulungu, yemwe anali atamupatsa chilichonse, ndi wabwino.
20 Tikudziwa kuti kukayikira kumeneku kunabweretsa mavuto ambirimbiri. Choncho tisamaiwale mawu a pa Yeremiya 31:12 akuti: “Nkhope zawo zidzawala chifukwa cha ubwino wa Yehova.” Zoonadi, nkhope zathu ziyenera kumawala, kapena kuti tiyenera kumasangalala kwambiri chifukwa cha zinthu zabwino zimene Yehova amatichitira. Tisamakayikire zolinga za Mulungu wathu yemwe ndi wabwino pa chilichonse. Tingamudalire ndi mtima wonse chifukwa nthawi zonse amafunira zabwino anthu amene amamukonda.
21, 22. (a) Kodi mukufuna kumachita zinthu ziti potsanzira ubwino wa Yehova? (b) Kodi m’mutu wotsatira tidzakambirana khalidwe liti, nanga limasiyana bwanji ndi ubwino?
21 Timasangalalanso tikapeza mwayi wouza ena za ubwino wa Mulungu. Ponena za anthu a Mulungu lemba la Salimo 145:7 limati: “Iwo azidzalankhula mosangalala akadzakumbukira ubwino wanu wochuluka.” Tsiku lililonse timapindula ndi ubwino wa Yehova m’njira inayake. Bwanji osakonza zoti tsiku lililonse muzithokoza Yehova pa zabwino zimene wakuchitirani, n’kumatchula mwachindunji zinthuzo? Kuganizira ubwino wa Yehova, kumuthokoza tsiku lililonse komanso kumauzako ena zokhudza khalidweli, kungatithandize kuti tizitsanzira Mulungu wathu wabwinoyu. Ndipo tikamayesetsa kuchita zabwino ngati Yehova, ubwenzi wathu ndi iye umalimba. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Wokondedwa, usamatsanzire anthu ochita zoipa, m’malomwake uzitsanzira anthu amene amachita zabwino. Amene amachita zabwino amayendera maganizo a Mulungu.”—3 Yohane 11.
22 Palinso makhalidwe ena amene amayendera limodzi ndi ubwino wa Yehova. Mwachitsanzo, Mulungu ndi “wachikondi chokhulupirika chochuluka.” (Ekisodo 34:6) Mosiyana ndi ubwino, khalidwe limeneli ndi lapadera chifukwa Yehova amalisonyeza kwa atumiki ake okhulupirika okha. M’mutu wotsatira, tidzaphunzira mmene amachitira zimenezi.
a Dipo ndi chitsanzo chachikulu kwambiri chosonyeza kuti Yehova ndi wabwino. Pa angelo mamiliyoni ambiri omwe alipo, iye anasankha Mwana wake wokondedwa ndiponso wobadwa yekha kuti adzatifere.
b N’chifukwa chake Baibulo limagwirizanitsa choonadi ndi kuwala. Wolemba masalimo anaimba kuti: “Tumizani kuwala kwanu ndi choonadi chanu.” (Salimo 43:3) Yehova amapereka kuwala kwakukulu kwauzimu kwa anthu amene amafuna kuti iye awaunikire, kapena kuti awaphunzitse.—2 Akorinto 4:6; 1 Yohane 1:5.
-
-
‘Inu Nokha Ndinu Wokhulupirika’Yandikirani Yehova
-
-
MUTU 28
‘Inu Nokha Ndinu Wokhulupirika’
1, 2. N’chifukwa chiyani tinganene kuti sizinali zachilendo kwa Mfumu Davide kuona anthu ena akusiya kukhala okhulupirika kwa iye?
SIZINALI zachilendo kwa Mfumu Davide kuona anthu ena akusiya kukhala okhulupirika kwa iye. Pa nthawi ina anthu a mtundu wake omwe, anaukira ulamuliro wake umenenso unkakumana ndi mavuto ambiri. Pa nthawi inanso anzake ena apamtima anasonyeza kusakhulupirika. Taganizirani za Mikala, mkazi wake woyamba. Poyamba, iye “ankakonda Davide” ndipo ayenera kuti ankamuthandiza. Koma patapita nthawi Mikala “anayamba kumunyoza mumtima mwake” mpaka kufika pomamuona kuti anali “munthu wopanda nzeru.”—1 Samueli 18:20; 2 Samueli 6:16, 20.
2 Ndiye panalinso Ahitofeli yemwe anali mlangizi wa Davide. Anthu ankaona kuti malangizo ake ndi mawu ochokera kwa Yehova. (2 Samueli 16:23) Koma kenako mnzake wapamtima ameneyu anagwirizana ndi gulu limene linaukira ufumu wa Davide. Kodi ndi ndani amene anayambitsa gulu limeneli? Anali Abisalomu, mwana weniweni wa Davideyo. Abisalomu “anapitiriza kukopa anthu mu Isiraeli” ndipo anadziika kukhala mfumu m’malo mwa Davide. Anthu ambiri anakhala kumbali ya Abisalomu moti Mfumu Davide inakakamizika kuthawa poopa kuphedwa.—2 Samueli 15:1-6, 12-17.
3. Kodi Davide sankakayikira za chiyani?
3 Koma kodi panalibe aliyense amene anapitiriza kukhala wokhulupirika kwa Davide? M’mavuto ake onse, Davide ankadziwa kuti panali winawake yemwe anali wokhulupirika kwa iye. Ameneyu anali Yehova Mulungu. Ponena za Yehova, Davide anati: “Munthu wokhulupirika, mumamuchitira mokhulupirika.” (2 Samueli 22:26) Kodi kukhulupirika n’kutani, nanga n’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhaniyi?
Kodi Munthu Wokhulupirika Amatani?
4, 5. (a) Kodi munthu “wokhulupirika” amatani? (b) Kodi kukhala wokhulupirika kumasiyana bwanji ndi kudalirika?
4 M’Malemba a Chiheberi, mawu akuti “kukhulupirika,” amatanthauza kumamatira munthu amene umamukonda n’kumapitirizabe kumuthandiza. Munthu amachita zimenezi osati chifukwa chongoti n’zimene ayenera kuchita koma chifukwa cha chikondi.a Choncho kukhala wokhulupirika n’kosiyana ndi kungokhala wodalirika. Mwachitsanzo, wolemba masalimo anati mwezi ndi “mboni yokhulupirika yamumlengalenga” chifukwa nthawi zonse umakhalapo. (Salimo 89:37) Choncho tinganene kuti mwezi ndi wokhulupirika, kapena kuti wodalirika. Koma sikuti mwezi umasonyeza kukhulupirika kofanana ndi kumene munthu amasonyeza. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa choti mwezi sungasonyeze chikondi.
Mwezi umatchulidwa kuti mboni yokhulupirika, koma anthu ndi angelo okha ndi omwe angasonyeze kukhulupirika kofanana ndi kumene Yehova amasonyeza
5 Baibulo limasonyeza kuti munthu wokhulupirika amakhalanso wachikondi. Ndipotu munthu akakhala wokhulupirika kwa munthu wina, zimasonyeza kuti munthu winayo ndi mnzake. Munthu woteroyo amakhala wokhulupirika nthawi zonse ndipo sakhala ngati mafunde apanyanja amene amangokankhika ndi mphepo iliyonse. Munthu wokhulupirika, kapena kuti wachikondi chokhulupirika, samasintha zivute zitani.
6. (a) Kodi masiku ano zinthu zili bwanji m’dzikoli pa nkhani ya kukhulupirika, nanga Baibulo linasonyeza bwanji kuti zimenezi zizidzachitika? (b) Kodi njira yabwino yomwe ingatithandize kumvetsa tanthauzo la kukhulupirika ndi iti, ndipo n’chifukwa chiyani?
6 N’zoona kuti masiku ano anthu si okhulupirika chonchi. Nthawi zambiri anthu amene amagwirizana amakhala “okonzeka kuchitirana zoipa.” Timamvanso za anthu amene athawa akazi kapena amuna awo. (Miyambo 18:24; Malaki 2:14-16) Anthu ambiri amachita zachinyengo moti tinganenenso mawu amene mneneri Mika ananena akuti: “Anthu okhulupirika atha padziko lapansi.” (Mika 7:2) Ngakhale kuti nthawi zambiri anthu amalephera kukhala okhulupirika, Yehova amasonyeza kwambiri khalidwe lapadera limeneli. Ndipotu njira yabwino yomwe ingatithandize kumvetsa tanthauzo la kukhulupirika, ndi kuphunzira mmene Yehova amasonyezera khalidweli lomwe ndi logwirizana kwambiri ndi chikondi chake.
Yehova Ndi Wokhulupirika Kuposa Aliyense
7, 8. N’chifukwa chiyani Baibulo limanena kuti Yehova yekha ndiye wokhulupirika?
7 Baibulo limati: “Inu nokha Yehova ndinu wokhulupirika.” (Chivumbulutso 15:4) N’chifukwa chiyani limanena zimenezi? Kodi anthu ndiponso angelo ena sanasonyezepo m’njira yapadera kuti ndi okhulupirika? (Yobu 1:1; Chivumbulutso 4:8) Nanga bwanji Yesu Khristu? Pajatu iye ndi “wokhulupirika” wa Mulungu. (Salimo 16:10) Ndiye n’chifukwa chiyani Baibulo limati Yehova yekha ndiye wokhulupirika?
8 Choyamba, kumbukirani kuti kukhulupirika ndi mbali imodzi ya chikondi. Popeza “Mulungu ndi chikondi” ndipo iye ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yosonyeza chikondi, ndaninso angakhale wokhulupirika kwambiri kuposa iyeyo? (1 Yohane 4:8) N’zoona kuti angelo komanso anthu akhoza kusonyeza makhalidwe a Mulungu, komatu Yehova yekha ndi amene ali wokhulupirika kwambiri kuposa aliyense. Popeza ndi “Wamasiku Ambiri,” iye wakhala akusonyeza kukhulupirika kwa nthawi yaitali kuposa zolengedwa zonse. (Danieli 7:9) Choncho Yehova ndi amene amasonyeza kwambiri kukhulupirika kuposa aliyense ndipo palibe angafanane naye. Taonani zitsanzo izi.
9. Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti ndi “wokhulupirika pa chilichonse chimene amachita”?
9 Yehova ndi “wokhulupirika pa chilichonse chimene amachita.” (Salimo 145:17) Kodi amachita bwanji zimenezi? Yankho likupezeka mu Salimo 136. Salimo limeneli limatchula zinthu zingapo zimene Yehova anachita populumutsa anthu ake, kuphatikizapo kupulumutsa Aisiraeli pa Nyanja Yofiira. N’zochititsa chidwi kuti vesi lililonse la mu salimoli limamaliza ndi mawu akuti: “Chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.” Salimo limeneli lilinso m’bokosi lakuti “Mafunso Ofunika Kuwaganizira” lomwe lili patsamba 289. Tikamawerenga Salimoli timachita chidwi kwambiri ndi njira zosiyanasiyana zimene Yehova anasonyezera anthu ake chikondi chokhulupirika. Inde, Yehova amasonyeza kuti ndi wokhulupirika kwa atumiki ake powamvetsera akamapempha kuti awathandize ndipo amawathandizadi pa nthawi yoyenera. (Salimo 34:6) Yehova sasiya kusonyeza atumiki ake chikondi chokhulupirika ngati iwo akupitirizabe kukhala okhulupirika.
10. Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti ndi wokhulupirika pa nkhani yotsatira mfundo zake?
10 Njira inanso imene Yehova amasonyezera kuti ndi wokhulupirika kwa atumiki ake, ndi yoti mfundo zake sizisintha. Mosiyana ndi anthu amene chifukwa chotengeka maganizo amasinthasintha pa nkhani yokhudza chabwino ndi choipa, Yehova sasintha. Mwachitsanzo, iye sanasinthe mmene amaonera kukhulupirira zamizimu, kulambira mafano komanso kupha munthu. Kudzera mwa mneneri wake Yesaya, iye anati: “Ngakhale mudzakalambe, ine ndidzakhala chimodzimodzi.” (Yesaya 46:4) Choncho, sitikayikira kuti zinthu zidzatiyendera bwino tikamatsatira malangizo omveka bwino opezeka m’Mawu a Mulungu.—Yesaya 48:17-19.
11. Perekani zitsanzo zosonyeza kuti Yehova amakwaniritsa malonjezo ake.
11 Yehova amasonyezanso kuti ndi wokhulupirika pokwaniritsa zimene walonjeza. Akanena kuti chinachake chidzachitika, chimadzachitikadi. Choncho iye anati: “Mawu otuluka pakamwa panga sadzabwerera kwa ine popanda kukwaniritsa cholinga chake, koma adzachitadi chilichonse chimene ine ndikufuna, ndipo zimene ndinawatumizira kuti achite zidzachitikadi.” (Yesaya 55:11) Akamachita zimene walonjeza, Yehova amasonyeza kuti ndi wokhulupirika kwa anthu ake. Sawachititsa kuti azidikirira zinthu zomwe akudziwa kuti sizichitika. Pa nkhaniyi, Yehova ali ndi mbiri yabwino moti mtumiki wake Yoswa ananena kuti: “Palibe lonjezo limene silinakwaniritsidwe, pa malonjezo onse abwino amene Yehova analonjeza nyumba ya Isiraeli. Onse anakwaniritsidwa.” (Yoswa 21:45) Choncho timakhulupirira kuti sitidzagwiritsidwa fuwa lamoto chifukwa choti Yehova walephera kukwaniritsa malonjezo ake.—Yesaya 49:23; Aroma 5:5.
12, 13. Kodi chikondi chokhulupirika cha Yehova chidzakhalapo mpaka kalekale m’njira ziti?
12 Monga taonera kale, Baibulo limatiuza kuti chikondi chokhulupirika cha Yehova “chidzakhalapo mpaka kalekale.” (Salimo 136:1) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Choyamba, zikukhudza zimene Yehova amachita akatikhululukira machimo. Monga tinaonera m’Mutu 26, Yehova akakhululukira munthu, m’tsogolo sakumbutsanso zimene anakhululukazo. Popeza “anthu onse ndi ochimwa ndipo amalephera kusonyeza bwinobwino ulemerero wa Mulungu,” tiyenera kumayamikira kuti chikondi chokhulupirika cha Yehova chimakhalapo mpaka kalekale.—Aroma 3:23.
13 Koma Yehova amasonyeza m’njira inanso kuti chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale. Mawu ake amanena kuti wolungama “adzakhala ngati mtengo wodzalidwa mʼmbali mwa ngalande za madzi, umene umabereka zipatso mʼnyengo yake, umenenso masamba ake safota. Ndipo zonse zimene amachita zimamuyendera bwino.” (Salimo 1:3) Taganizirani za mtengo waukulu womwe masamba ake ndi wobiriwira ndipo safota. Nafenso tikamakonda Mawu a Mulungu, timakhala ndi moyo wautali, wamtendere komanso zinthu zimatiyendera bwino. Yehova amapatsa atumika ake madalitso osatha ndipo amachita zimenezi mokhulupirika. Ndithudi, m’dziko latsopano, anthu omvera Yehova adzawasonyeza chikondi chake chokhulupirika mpaka kalekale.—Chivumbulutso 21:3, 4.
Yehova “Sadzasiya Anthu Ake Okhulupirika”
14. Kodi Yehova amamva bwanji atumiki ake akamamutumikira mokhulupirika?
14 Yehova wakhala akusonyeza mobwerezabwereza kuti ndi wokhulupirika. Ndipo popeza iye sasintha, sadzasiya kukhala wokhulupirika kwa atumiki ake. Wolemba masalimo anati: “Ndinali mwana ndipo tsopano ndakula, koma sindinaonepo munthu aliyense wolungama atasiyidwa, kapena ana ake akupemphapempha chakudya. Chifukwa Yehova amakonda chilungamo, ndipo sadzasiya anthu ake okhulupirika.” (Salimo 37:25, 28) N’zoona kuti timayenera kulambira Yehova popeza ndi Mlengi. (Chivumbulutso 4:11) Komabe chifukwa choti ndi wokhulupirika, amayamikira kwambiri tikamamutumikira mokhulupirika.—Malaki 3:16, 17.
15. Kodi zimene Yehova anachitira Aisiraeli zimasonyeza bwanji kuti ndi wokhulupirika?
15 Chifukwa choti ali ndi chikondi chokhulupirika, Yehova amathandiza anthu ake akakhala pa mavuto. Wolemba masalimo anati: “Iye amateteza moyo wa anthu ake okhulupirika. Amawapulumutsa mʼmanja mwa oipa.” (Salimo 97:10) Taganizirani zimene anachitira Aisiraeli. Atawapulumutsa modabwitsa pa Nyanja Yofiira, iwo anaimbira Yehova kuti: “Munasonyeza chikondi chanu chokhulupirika potsogolera anthu amene munawawombola.” (Ekisodo 15:13) Apatu Yehova anasonyeza chikondi chokhulupirika. Choncho Mose anauza Aisiraeliwo kuti: “Sikuti Yehova anakusonyezani chikondi ndi kukusankhani chifukwa chakuti munali ochuluka kuposa mitundu yonse, chifukwatu mtundu wanu unali waungʼono mwa mitundu yonse. Koma Yehova anakutulutsani ndi dzanja lamphamvu kuti akulanditseni mʼnyumba yaukapolo, mʼmanja mwa Farao mfumu ya Iguputo, chifukwa chakuti Yehova anakukondani, komanso chifukwa chosunga lumbiro lake limene analumbirira makolo anu.”—Deuteronomo 7:7, 8.
16, 17. (a) Kodi Aisiraeli anasonyeza bwanji kuti anali osayamika ngakhale pang’ono, komabe Yehova anawasonyeza bwanji chifundo? (b) Kodi Aisiraeli ambiri anasonyeza bwanji kuti panalibenso “chiyembekezo choti angathe kuchiritsidwa,” nanga tikuphunzirapo chiyani?
16 N’zoona kuti monga mtundu, Aisiraeli analephera kusonyeza kuti ankayamikira chikondi chokhulupirika cha Yehova, chifukwa atapulumutsidwa “anapitiriza kumuchimwira popandukira Wamʼmwambamwamba.” (Salimo 78:17) Kwa zaka mahandiredi ambiri, ankapandukira Yehova mobwerezabwereza ndipo ankalambira mafano komanso kuchita miyambo yachikunja yomwe inkachititsa kuti akhale odetsedwa. Komabe Yehova anapitiriza kusunga pangano lake. Kudzera mwa mneneri Yeremiya, Yehova anachonderera anthu ake kuti: “Bwerera Isiraeli wopanduka iwe. Sindidzakuyangʼana mokwiya chifukwa ndine wokhulupirika.” (Yeremiya 3:12) Komabe monga tinaonera m’Mutu 25, Aisiraeli ambiri anakana kutsatira malangizowa. Ndipotu iwo “anapitiriza kunyoza atumiki a Mulungu woona, kunyoza mawu ake ndiponso kuseka aneneri ake.” Ndiye kodi zotsatira zake zinali zotani? “Iwo anafika poti panalibenso chiyembekezo choti angathe kuchiritsidwa. Kenako Yehova anawakwiyira kwambiri nʼkuwalanga.”—2 Mbiri 36:15, 16.
17 Kodi tikuphunzirapo chiyani? Tikuphunzira kuti ngakhale kuti Yehova ndi wokhulupirika, salekerera zolakwa komanso n’zosatheka kumupusitsa. N’zoona kuti Yehova ndi “wachikondi chokhulupirika chochuluka” ndipo amasangalala kuchitira ena chifundo pakakhala zifukwa zomveka. Koma kodi iye amatani munthu akakhala woipa kwambiri moti sangasinthe? Zikatero amatsatira mfundo zake zolungama ndipo amalanga munthuyo. Mogwirizana ndi zimene anauza Mose, iye ‘salekerera wolakwa osamʼpatsa chilango.’—Ekisodo 34:6, 7.
18, 19. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova akalanga anthu ochita zoipa amasonyeza kuti ndi wokhulupirika? (b) Kodi Yehova adzasonyeza bwanji kuti ndi wokhulupirika kwa atumiki ake amene amazunzidwa mpaka kuphedwa?
18 Mulungu akalanga anthu ochita zoipa umakhalanso umboni wakuti iye ndi wokhulupirika. N’chifukwa chiyani tikutero? Mfundo imeneyi yafotokozedwa m’buku la Chivumbulutso pamene Yehova analamula angelo 7 kuti: “Pitani, kathireni mbale 7 za mkwiyo wa Mulunguzo padziko lapansi.” Mngelo wachitatu atathira mbale yake “pamitsinje ndi pa akasupe amadzi,” zonse zinasanduka magazi. Ndiyeno mngeloyo anauza Yehova kuti: “Inu Mulungu amene mulipo ndi amene munalipo, inu Wokhulupirika, ndinu wolungama chifukwa mwapereka ziweruzo zimenezi, chifukwa iwo anakhetsa magazi a oyera ndi a aneneri ndipo inu mwawapatsa magazi kuti amwe. Iwo akuyeneradi kulandira chiweruzo chimenechi.”—Chivumbulutso 16:1-6.
19 N’chifukwa chiyani pamene ankapereka uthenga wachiweruzo, mngeloyo ananena kuti Yehova ndi “wokhulupirika”? N’chifukwa choti powononga anthu oipa, Yehova akusonyeza kuti ndi wokhulupirika kwa atumiki ake omwe akhala akuzunzidwa mpaka kuphedwa. Yehova amasonyeza kukhulupirika popitirizabe kuwakumbukira anthu amenewa. Iye amalakalaka ataonanso anthu okhulupirika amene anamwalirawa, ndipo Baibulo limatitsimikizira kuti adzawaukitsa. (Yobu 14:14, 15) Ngakhale kuti atumiki ake okhulupirikawo anamwalira, Yehova sanawaiwale. “Kwa iye onsewa ndi amoyo.” (Luka 20:37, 38) Yehova amafuna kudzapatsanso moyo anthu amene akuwakumbukira ndipo umenewu ndi umboni wamphamvu wakuti ndi wokhulupirika.
Yehova adzakumbukira ndiponso kuukitsa anthu amene anakhala okhulupirika mpaka kuphedwa
Bernard Luimes (pamwamba) ndi Wolfgang Kusserow (pakati) anaphedwa ndi a chipani cha Nazi
Gulu la ndale linabaya Moses Nyamussua ndi mkondo mpaka kumupha
Chikondi Chokhulupirika cha Yehova Chikuthandiza Kuti Tidzapulumuke
20. Kodi “anthu oyenera kuwachitira chifundo” ndi ndani, ndipo Yehova amasonyeza bwanji kuti ndi wokhulupirika kwa anthuwa?
20 Yehova wakhala akusonyeza kuti ndi wokhulupirika kwa atumiki ake. Ndipotu kwa zaka masauzande ambiri, iye wakhala ‘akulekerera moleza mtima kwambiri anthu oyenera kuwonongedwa.’ Chifukwa chiyani? “Kuti asonyeze kukula kwa ulemerero wake kwa anthu oyenera kuwachitira chifundo, omwe anawakonzeratu kuti alandire ulemerero.” (Aroma 9:22, 23) “Anthu oyenera kuwachitira chifundo” amenewa, ndi Akhristu omwe amadzozedwa ndi mzimu woyera kuti akalamulire limodzi ndi Khristu mu Ufumu wake. (Mateyu 19:28) Pokonza zoti anthuwa adzapulumutsidwe, Yehova anasonyeza kuti ndi wokhulupirika kwa Abulahamu, yemwe anachita naye pangano lakuti: “Kudzera mwa mbadwa yako, mitundu yonse yapadziko lapansi idzapeza madalitso chifukwa chakuti wamvera mawu anga.”—Genesis 22:18.
Chifukwa chakuti Yehova ndi wokhulupirika, atumiki ake onse okhulupirika ali ndi chiyembekezo chodalirika
21. (a) Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti ndi wokhulupirika kwa “khamu lalikulu” limene lidzapulumuke “chisautso chachikulu”? (b) Kodi mukufunitsitsa kuchita chiyani chifukwa chodziwa kuti Yehova ndi wokhulupirika?
21 Yehova amasonyezanso kuti ndi wokhulupirika kwa “khamu lalikulu” limene lidzapulumuke pa “chisautso chachikulu” n’kudzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padzikoli. (Chivumbulutso 7:9, 10, 14) Ngakhale kuti atumiki ake si angwiro, mokhulupirika Yehova akuwapatsa mwayi wodzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso. Kodi akuchita bwanji zimenezi? Akuzichita pogwiritsa ntchito dipo, lomwe ndi njira yaikulu kwambiri imene anasonyezera kuti ndi wokhulupirika. (Yohane 3:16; Aroma 5:8) Chifukwa choti Yehova ndi wokhulupirika, anthu amene akufunafuna chilungamo amakopeka naye. (Yeremiya 31:3) Kodi mukumva bwanji mukaganizira mfundo yoti Yehova wakhala akusonyeza kuti ndi wokhulupirika kwambiri ndipo adzapitirizabe kusonyeza khalidweli? Popeza timafunitsitsa kuyandikira Mulungu, tiyeni tizisonyeza kuti timayamikira chikondi chake pokhala otsimikiza mtima kuti tizimutumikira mokhulupirika.
a N’zochititsa chidwi kuti mawu amene anawamasulira kuti “mokhulupirika” pa 2 Samueli 22:26, m’malo ena anawamasulira kuti “chikondi chokhulupirika.”
-
-
“Mudziwe Chikondi cha Khristu”Yandikirani Yehova
-
-
MUTU 29
“Mudziwe Chikondi cha Khristu”
1-3. (a) Kodi n’chiyani chinachititsa Yesu kuti azifuna kutsanzira Atate ake? (b) Kodi tikambirana njira zitatu ziti zimene Yesu anasonyezera chikondi?
KODI munaonapo kamnyamata kakuyesera kukhala ngati bambo ake? Mwanayo angatsanzire mmene bambowo amayendera, amalankhulira komanso mmene amachitira zinthu. Akamakula, angatengerenso makhalidwe abwino a bambo akewo ndiponso zimene amakhulupirira. Chifukwa choti mnyamatayo amakonda bambo ake komanso amawalemekeza, amafuna atakhala ngati iwowo.
2 Nanga bwanji za Yesu ndi Atate ake akumwamba? Pa nthawi ina iye anati: “Ndimakonda Atate.” (Yohane 14:31) Palibe aliyense amene angakonde Yehova kwambiri kuposa Mwanayu, yemwe anakhala naye kwa zaka zambiri zinthu zina zonse zisanakhalepo. Chikondi chimenecho chinachititsa Mwana wokhulupirikayu kuti azifuna kukhala ngati Atate ake.—Yohane 14:9.
3 Mitu yoyambirira ya bukuli yafotokoza mmene Yesu anatsanzirira mphamvu, chilungamo ndiponso nzeru za Yehova. Nanga anasonyeza bwanji kuti amatsanzira chikondi cha Yehova? Tiyeni tikambirane njira zitatu zimene Yesu anasonyezera chikondi, zomwe ndi mtima wodzipereka, chifundo chake chachikulu ndiponso mtima wokhululuka.
Anasonyeza “Chikondi Chachikulu”
4. Kodi Yesu anasonyeza bwanji chikondi chachikulu kuposa chimene munthu aliyense anasonyezapo?
4 Yesu anapereka chitsanzo chapadera kwambiri pa nkhani yosonyeza chikondi chololera kuvutikira ena. Kuti munthu asonyeze chikondi chimenechi amafunika kukhala wosadzikonda n’kuika patsogolo zofuna za ena osati zake. Ndiye kodi anachita bwanji zimenezi? Iye anafotokoza kuti: “Palibe amene ali ndi chikondi chachikulu kuposa cha munthu amene wapereka moyo wake chifukwa cha anzake.” (Yohane 15:13) Mofunitsitsa Yesu anapereka moyo wake wangwiro chifukwa cha ife. Chimenechi chinali chikondi chachikulu kwambiri kuposa chimene munthu aliyense anasonyezapo. Komabe Yesu anasonyeza chikondi chololera kuvutikira ena m’njira zinanso.
5. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Mwana wa Mulungu anasonyeza chikondi pamene analolera kubwera padzikoli?
5 Mwana wobadwa yekha wa Mulungu asanakhale munthu padzikoli, anali ndi udindo wapadera komanso waukulu kumwamba. Ankagwirizana kwambiri ndi Yehova komanso angelo ambirimbiri. Ngakhale kuti anali ndi mwayi waukulu chonchi, Mwana wokondedwayu “anasiya zonse zimene anali nazo nʼkukhala ngati kapolo ndipo anakhala munthu.” (Afilipi 2:7) Mofunitsitsa, iye anabwera kudzakhala limodzi ndi anthu ochimwa m’dzikoli, lomwe “lili mʼmanja mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Pamenepatu Mwana wa Mulungu anasonyeza chikondi chachikulu pololera kusiya zinthu zambiri.
6, 7. (a) Pamene ankachita utumiki wake padzikoli, kodi Yesu anasonyeza chikondi chololera kuvutikira ena m’njira ziti? (b) Kodi ndi chitsanzo chabwino kwambiri chiti chokhudza chikondi chololera kuvutikira ena chomwe chili pa Yohane 19:25-27?
6 Pa nthawi yonse imene ankachita utumiki wake padzikoli, Yesu ankasonyeza chikondi chololera kuvutikira ena. Iye sankachita zinthu modzikonda. Maganizo ake onse anali pa utumiki wake moti sankalakalaka zinthu zapamwamba zimene anthu ambiri amafuna atakhala nazo. Iye anati: “Nkhandwe zili ndi mapanga ndipo mbalame zamumlengalenga zili ndi zisa, koma Mwana wa munthu alibiretu poti nʼkutsamiritsa mutu wake.” (Mateyu 8:20) Popeza Yesu anali kalipentala waluso, akanatha kusiya kaye ntchito yolalikira n’kumanga nyumba yabwino yoti azikhalamo kapena kupanga zinthu zokongola zamatabwa n’kugulitsa kuti apeze ndalama. Koma iye sanagwiritse ntchito luso lake kuti akhale ndi katundu wambiri.
7 Chitsanzo chabwino kwambiri cha chikondi cha Yesu chololera kuvutikira ena chili pa Yohane 19:25-27. Taganizani zinthu zambirimbiri zimene zinkayenda m’mutu mwa Yesu masana a tsiku limene anaphedwa. Pamene ankavutika pamtengo wozunzikirapo, ankadera nkhawa ophunzira ake, ntchito yolalikira ndiponso makamaka mmene kukhulupirika kwake kukanathandizira kuti dzina la Atate ake lilemekezedwe. Tsogolo lonse la anthu linkadalira pa zimene iye akanachita. Komatu atatsala pang’ono kufa, Yesu anasonyeza kuti ankadera nkhawa amayi ake, Mariya, omwe pa nthawiyi ayenera kuti anali amasiye. Yesu anapempha mtumwi Yohane kuti azisamalira Mariya ngati mayi ake enieni ndipo kenako Yohaneyo anatenga Mariya n’kupita naye kunyumba kwake. Choncho Yesu anakonza zoti amayi ake azipeza zofunika pa moyo komanso zowathandiza pa ubwenzi wawo ndi Yehova. Apatu Yesu anasonyeza chikondi chachikulu.
“Anawamvera Chisoni”
8. Kodi mawu a Chigiriki amene Baibulo limagwiritsa ntchito pofotokoza chifundo cha Yesu amatanthauza chiyani?
8 Mofanana ndi Atate ake, Yesu anali wachifundo. Malemba amanena kuti Yesu zinkamukhudza akaona anthu akuvutika ndipo ankayesetsa kuwathandiza. Pofotokoza chifundo cha Yesu, Baibulo limagwiritsa ntchito mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “anawamvera chisoni.” Katswiri wina wa Baibulo anati ‘mawuwa amanena za munthu amene wakhudzidwa kwambiri ndi zinazake n’kuchita zinthu kuchokera pansi pa mtima. Amenewa ndi mawu a Chigiriki amphamvu kwambiri onena za chifundo.’ Tiyeni tione zochitika zina zomwe zinachititsa Yesu kugwidwa chifundo kwambiri n’kuchitapo kanthu.
9, 10. (a) Kodi n’chiyani chinachititsa kuti Yesu ndi atumwi ake afune kukhala kwaokha? (b) Pamene anthu anawalepheretsa kukhala kwaokha, kodi Yesu anatani, ndipo n’chifukwa chiyani?
9 Anathandiza anthu kuphunzira za Mulungu. Nkhani yopezeka pa Maliko 6:30-34 imasonyeza chifukwa chachikulu chimene chinachititsa Yesu kuti asonyeze chifundo. Taganizirani zimene zinachitika. Atumwi anali osangalala chifukwa anali atangomaliza kulalikira m’madera ambiri. Anabwerera kwa Yesu n’kumufotokozera zinthu zosangalatsa zimene anakumana nazo. Koma panabwera anthu ambiri moti Yesu ndi atumwi ake sanapeze nthawi yoti adye. Popeza nthawi zonse ankachita chidwi ndi atumwiwo, Yesu anazindikira kuti atopa. Choncho anawauza kuti: “Inuyo bwerani kuno, tipite kwatokha kopanda anthu kuti mukapume pangʼono.” Kenako anakwera ngalawa ndipo ankawoloka Nyanja ya Galileya n’kumalowera chakumpoto kuti akapeze malo opanda anthu. Koma gulu la anthu lija linaona kuti akuchoka. Enanso anamva za nkhaniyi. Anthu onsewa anathamangira kumene Yesu ndi atumwi ake ankapita ndipo iwowo ndi amene anayamba kukafika.
10 Kodi Yesu anakhumudwa chifukwa choti anthuwa anawalepheretsa kukhala kwaokha? Ayi ndithu. Zinamukhudza kwambiri ataona kuti anthuwa, omwe analipo masauzande ambiri, akumudikira. Maliko analemba kuti ‘ataona gulu lalikulu la anthu anawamvera chisoni, chifukwa anali ngati nkhosa zimene zilibe mʼbusa. Ndiye anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.’ Yesu anaona kuti ankafunika kuwathandiza mwauzimu. Anali ngati nkhosa zosochera zopanda m’busa woziyang’anira. Yesu ankadziwa kuti atsogoleri achipembedzo ouma mtima, amene ankayenera kukhala abusa abwino, sankakonda komanso kusamalira anthuwo. (Yohane 7:47-49) Anawamvera chisoni moti anayamba kuwaphunzitsa “za Ufumu wa Mulungu.” (Luka 9:11) Kodi mwaona kuti Yesu anawamvera chisoni asanaone n’komwe zimene anthuwo achite akawaphunzitsa? M’mawu ena tinganene kuti, sikuti Yesu anagwidwa chifundo ataona kuti anthuwo akumvetsera zimene ankawaphunzitsa, koma chifundo n’chimene chinamuchititsa kuti awaphunzitse.
“Anatambasula dzanja lake nʼkumukhudza”
11, 12. (a) Kodi kale anthu akhate ankawaona bwanji, koma Yesu anachita chiyani atakumana ndi munthu wina “wakhate thupi lonse”? (b) Kodi wakhate amene Yesu anamukhudza ayenera kuti anamva bwanji, nanga zimene zinachitikira dokotala wina zikutithandiza bwanji kumvetsa zimenezi?
11 Anathandiza wodwala. Anthu odwala matenda osiyanasiyana ankadziwa kuti Yesu ndi wachifundo, choncho ankapita kwa iye kuti akawathandize. Umboni wa zimenezi ndi zomwe zinachitika pamene munthu wina “wakhate thupi lonse” anafika kwa Yesu, Yesuyo ali ndi gulu la anthu lomwe linkamutsatira. (Luka 5:12) Kale, anthu akhate ankawaika kwaokha kuti asapatsire ena. (Numeri 5:1-4) Koma patapita nthawi, atsogoleri ena omwenso anali Arabi, ankachititsa kuti anthu asamachitire chifundo akhate ndipo anapanga malamulo awoawo opondereza.a Koma taonani zimene Yesu anachitira wakhate uja. Baibulo limati: “Munthu wina wakhate anafika kwa iye ndipo anagwada pansi nʼkumuchonderera kuti: ‘Ndikudziwa kuti ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.’ Yesu atamva zimenezo, anagwidwa chifundo moti anatambasula dzanja lake nʼkumukhudza ndipo anamuuza kuti: ‘Inde ndikufuna. Khala woyera.’ Nthawi yomweyo khate lakelo linatha.” (Maliko 1:40-42) Yesu ankadziwa kuti zinali zosaloledwa kuti wakhateyo apezeke pagulupo. Komatu m’malo momuuza kuti achoke, anamva chisoni kwambiri moti anachita zinthu zimene anthu sankayembekezera. Iye anakhudza wakhateyo.
12 Kodi mukuganiza kuti wakhateyo anamva bwanji Yesu atamukhudza? Taganizirani chitsanzo ichi. Dokotala wina wa anthu akhate, dzina lake Paul Brand, anafotokoza za mnyamata wina wakhate amene anamuchiritsa ku India. Pamene ankamuyeza, dokotalayo anagwira phewa la wodwalayo. Kenako kudzera mwa munthu wina womasulira, anamufotokozera mankhwala amene ankafunika kulandira. Mwadzidzidzi, wodwalayo anayamba kulira. Dokotalayo anafunsa kuti: “Kodi ndalankhula zinazake zolakwika?” Womasulirayo anafunsa mnyamatayo m’chilankhulo chake, ndiyeno anayankha dokotalayo kuti: “Ayi adokotala. Akuti akulira chifukwa choti mwamugwira paphewa. Akuti patha zaka zambiri munthu aliyense asanamugwireko.” Choncho kwa wakhate amene anakumana ndi Yesu uja, kumukhudza kunatanthauza zambiri. Atangokhudzidwa kamodzi kokhako, matenda amene ankachititsa kuti anthu azimusala, anatheratu.
13, 14. (a) Kodi Yesu atatsala pang’ono kulowa mumzinda wa Nayini anakumana ndi anthu akupita kuti, nanga n’chiyani chinachititsa kuti zimenezi zikhale zomvetsa chisoni kwambiri? (b) Popeza Yesu anali wachifundo, kodi anathandiza bwanji mayi wamasiye wa ku Nayini?
13 Anathandiza anthu omwe anali ndi chisoni. Yesu zinkamukhudza kwambiri akaona anthu ali ndi chisoni chifukwa choti aferedwa. Mwachitsanzo, taganizirani nkhani yopezeka pa Luka 7:11-15. Inachitika Yesu atatsala pang’ono kufika mumzinda wina wa ku Galileya wotchedwa Nayini, chapakatikati pa utumiki wake. Atafika pafupi ndi geti la mzindawo, anakumana ndi anthu akukaika maliro. Koma maliro ake anali omvetsa chisoni kwambiri. Womwalirayo anali mnyamata yemwe anali mwana yekhayo wa mayi wina wamasiye. N’kutheka kuti pa nthawi ina, mayiyu analinso ndi anthu atanyamula maliro a mwamuna wake kupita kumanda. Koma pa nthawi imene anakumana ndi Yesuyi n’kuti akukaika maliro a mwana wake, yemwe n’kutheka kuti anali munthu yekhayo amene ankamuthandiza. Mwina pagululo panalinso anthu ena amene ankaimba nyimbo zapamaliro. (Yeremiya 9:17, 18; Mateyu 9:23) Komabe, Yesu ankayang’anitsitsa mayi woferedwayo yemwe mosakayikira anali ndi chisoni chachikulu ndipo ankayenda pafupi ndi chithatha chimene ananyamulirapo malirowo.
14 Yesu “anamvera chisoni” mayiyo. Kenako anamulimbikitsa ndi mawu akuti: “Tontholani mayi.” Ngakhale kuti palibe amene anamupempha, Yesu anapita pafupi ndi chithathacho n’kuchigwira. Anthu amene ananyamula chithathacho anaima, ndipo mwina gulu lonselo linaimanso. Kenako Yesu analankhula mwamphamvu kwa mnyamata womwalirayo kuti: “Mnyamata iwe, ndikunena ndi iwe, dzuka!” Zitatero, mnyamatayo “anadzuka nʼkuyamba kulankhula.” Ndipo zinangokhala ngati anagona tulo tofa nato ndiye amudzutsa. Kenako Baibulo limanena mawu olimbikitsa akuti: “Yesu anamupereka kwa mayi ake.”
15. (a) Kodi nkhani za m’Baibulo zofotokoza za Yesu kuti ankamvera ena chisoni zimasonyeza kuti pali kugwirizana kotani pakati pa chifundo ndi kuchitapo kanthu? (b) Kodi tingatsanzire bwanji Yesu pa nkhaniyi?
15 Kodi nkhani zimenezi zikutiphunzitsa chiyani? Kodi mwaona kuti munkhani iliyonse chifundo chikuyendera limodzi ndi kuchitapo kanthu? Nthawi zonse Yesu akaona ena akuvutika ankawamvera chisoni, ndipo akatero ankawathandiza. Ndiye kodi tingamutsanzire bwanji? Akhristufe, tili ndi udindo wolalikira uthenga wabwino ndiponso kuthandiza anthu kuti akhale ophunzira a Yesu. Chifukwa chachikulu chimene timachitira zimenezi ndi choti timakonda Mulungu. Komabe tizikumbukira kuti chifukwa china n’chakuti timamvera chisoni anthu. Tikamamvera chisoni anthu ngati mmene Yesu ankachitira, timayesetsa kuchita zonse zimene tingathe kuti tiwauze uthenga wabwino. (Mateyu 22:37-39) Nanga bwanji za Akhristu anzathu amene akuvutika kapena amene ali ndi chisoni? Sitingachiritse anthu modabwitsa kapena kuukitsa akufa. Komabe, tingasonyeze chifundo poyesetsa kupeza njira zowathandizira komanso kuwatsimikizira kuti timawakonda.—Aefeso 4:32.
“Atate, Akhululukireni”
16. Pamene Yesu anali pamtengo wozunzikirapo, kodi anasonyeza bwanji kuti anali wofunitsitsa kukhululuka?
16 Yesu anasonyezanso chikondi cha Atate ake m’njira ina yofunika kwambiri. Iye anali “wokonzeka kukhululuka.” (Salimo 86:5) Umboni wa zimenezi ndi zimene anachita pamene anali pamtengo wozunzikirapo. Kodi Yesu analankhula zotani ngakhale kuti anali atatsala pang’ono kufa imfa yochititsa manyazi komanso ankamva ululu chifukwa choti anali atamukhoma ndi misomali? Kodi anapempha Yehova kuti alange amene ankamuphawo? Ayi. Ena mwa mawu omalizira amene Yesu analankhula, anali akuti: “Atate, akhululukireni, chifukwa sakudziwa zimene akuchita.”—Luka 23:34.b
17-19. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anakhululukira mtumwi Petulo ngakhale kuti anamukana katatu?
17 Mwina chitsanzo chogwira mtima chosonyeza kuti Yesu anali wokhululuka tingachione tikaganizira zimene anachitira mtumwi Petulo. N’zosakayikitsa kuti Petulo ankakonda kwambiri Yesu. Pa Nisani 14, usiku womaliza wa Yesu, Petulo anamuuza kuti: “Ambuye, ndine wokonzeka kupita nanu limodzi kundende kapena kufa nanu limodzi.” Koma patangotha maola ochepa, Petulo anakana katatu kuti sankamudziwa Yesu. Baibulo limatiuza zimene zinachitika pamene Petulo ankamukana kachitatu. Limati: “Ambuye anacheuka nʼkuyangʼana Petulo.” Atazindikira kuti walakwitsa kwambiri, “Petulo anatuluka panja nʼkuyamba kulira mopwetekedwa mtima kwambiri.” Yesu atamwalira madzulo a tsikulo, mwina mtumwiyu ankadzifunsa kuti, ‘Kodi Ambuye anandikhululukira?’—Luka 22:33, 61, 62.
18 Koma pasanapite nthawi yaitali anapeza yankho. Yesu anaukitsidwa pa Nisani 16 m’mawa, ndipo zikuoneka kuti tsiku lomwelo anakumana ndi Petulo. (Luka 24:34; 1 Akorinto 15:4-8) N’chifukwa chiyani Yesu anaonetsetsa kuti akumane ndi mtumwiyu, yemwe anamukanitsitsa? N’kutheka kuti ankafuna kutsimikizira Petulo, yemwe anali atalapa, kuti ankamukondabe komanso ankamuonabe kuti ndi wofunika. Koma Yesu anachitanso zinthu zina kuti amutsimikizire kuti wamukhululukira.
19 Patapita nthawi, Yesu anaonekera kwa ophunzira ake ku Nyanja ya Galileya. Pa nthawiyi, anafunsa Petulo katatu ngati ankamukonda (paja Petulo anakana Ambuye katatu). Atamufunsa kachitatu, Petulo anati: “Ambuye, inu mumadziwa zinthu zonse. Mukudziwanso bwino kuti ndimakukondani kwambiri.” Yesu, yemwe ankatha kudziwa za mumtima mwa munthu, ankadziwadi kuti Petulo amamukonda. Komabe iye anamupatsa mwayi wotsimikizira zimenezo. Kuwonjezera pamenepo, Yesu anamupatsanso ntchito yoti ‘azidyetsa’ komanso ‘kuweta’ “ana a nkhosa” ake. (Yohane 21:15-17) M’mbuyomo, Petulo anapatsidwa ntchito yolalikira. (Luka 5:10) Koma tsopano, posonyeza kuti ankamudalira kwambiri, Yesu anamupatsa udindo wina waukulu woti azidzasamalira otsatira a Khristu. Patapita nthawi yochepa, anamugwiritsanso ntchito m’njira yapadera pa ntchito imene ophunzira ankagwira. (Machitidwe 2:1-41) Petulo ayenera kuti anasangalala kwambiri atadziwa zoti Yesu anamukhululukira ndipo ankamudalirabe.
Kodi ‘Mumadziwa Chikondi cha Khristu’?
20, 21. Kodi tingatani kuti ‘tidziwe bwino chikondi cha Khristu’?
20 Kunena zoona, Mawu a Mulungu amafotokoza bwino chikondi cha Khristu. Koma kodi tiyenera kuchita chiyani podziwa kuti Yesu amatikonda? Baibulo limatiuza kuti ‘tidziwe chikondi cha Khristu chimene chimaposa kudziwa zinthu.’ (Aefeso 3:19) Monga taonera, nkhani za m’Mauthenga Abwino zonena za moyo wa Yesu ndiponso utumiki wake zimatiphunzitsa zambiri zokhudza chikondi cha Khristu. Komabe, ‘kudziwa bwino chikondi cha Khristu’ kumafuna zambiri osati kungophunzira nkhani zokhudza iyeyo zimene Baibulo limanena.
21 Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “kudziwa” amatanthauza kuchidziwa chinthu “kuchokera pa zimene ukudziwa kale komanso zomwe wakumana nazo pa moyo.” Tikamasonyeza chikondi ngati mmene Yesu ankachitira, mwachitsanzo tikamadzipereka kuthandiza ena, kuwachitira chifundo komanso kukhululuka ndi mtima wonse, tidzadziwa maganizo a Khristu. Tikamachita zimenezi ‘timadziwa chikondi cha Khristu chimene chimaposa kudziwa zinthu.’ Ndipo tisaiwale kuti tikamayesetsa kutsanzira Khristu, timayandikira kwambiri Yehova Mulungu wathu wachikondi amenenso Yesuyo amamutsanzira.
a Malamulo a Arabi ankanena kuti munthu azitalikirana ndi wakhate pafupifupi mamita awiri. Ndipo ngati kukuwomba mphepo, wakhate ankafunika kutalikirana ndi anthu pafupifupi mamita 45. Buku lina limanena za Rabi wina yemwe ankabisala akaona akhate ndiponso wina amene ankawathamangitsa powagenda ndi miyala. (Midrash Rabbah) Choncho anthu akhate ankadziwa mmene zimapwetekera ukamakanidwa, kunyozedwa komanso kuona kuti anthu sakukufuna.
b M’mipukutu ina yakale, mulibe mawu oyambirirawa apalemba la Luka 23:34. Koma chifukwa chakuti mawuwa amapezeka m’mipukutu ina yambiri yodalirika, anaikidwa mu Baibulo la Dziko Latsopano komanso m’Mabaibulo ena ambiri. Yesu ayenera kuti ankanena za asilikali a Chiroma amene anamupachika. Iwo sankadziwa zimene ankachita chifukwa sankadziwa kuti Yesu anali ndani. Mwinanso Yesu ankaganizira za Ayuda omwe anapempha kuti iye aphedwe koma patapita nthawi anayamba kumukhulupirira. (Machitidwe 2:36-38) Koma atsogoleri achipembedzo amene anachititsa kuti Yesu aphedwe, anali ndi mlandu waukulu chifukwa ankadziwa zimene akuchita ndipo anachita zimenezo chifukwa chongodana naye. Ambiri mwa anthu amenewa sanakhululukidwe.—Yohane 11:45-53.
-
-
“Pitirizani Kusonyeza Chikondi”Yandikirani Yehova
-
-
MUTU 30
“Pitirizani Kusonyeza Chikondi”
1-3. Kodi chimachitika n’chiyani tikamatsanzira Yehova pa nkhani yosonyeza ena chikondi?
“KUPATSA kumatichititsa kukhala osangalala kwambiri kuposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Mawu a Yesuwa, amatiphunzitsa mfundo yofunika kwambiri iyi: Tikamasonyeza chikondi chenicheni, zotsatira zake zimakhala zabwino. Ngakhale kuti timasangalala ena akamatikonda, koma timasangalala kwambiri ifeyo tikamasonyeza ena chikondi.
2 Palibe amene amadziwa bwino mfundo imeneyi kuposa Atate wathu wakumwamba. Monga taonera m’mitu yapitayi ya gawo lino, chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yosonyeza chikondi, ndi Yehova. Palibe amene wasonyezapo chikondi kwambiri kapenanso kwa nthawi yaitali kuposa iyeyo. Choncho n’zosadabwitsa kuti Yehova akutchulidwa kuti “Mulungu wachimwemwe”—1 Timoteyo 1:11.
3 Mulungu wathu wachikondi amafuna tiziyesetsa kumutsanzira, makamaka pa nkhani yosonyeza chikondi. Lemba la Aefeso 5:1, 2 limati: “Muzitsanzira Mulungu, monga ana ake okondedwa, ndipo pitirizani kusonyeza chikondi.” Tikamatsanzira Yehova pa nkhani yosonyeza chikondi, timasangalala kwambiri chifukwa kumeneku n’kupatsa. Timasangalalanso podziwa kuti tikusangalatsa Yehova, chifukwa Mawu ake amatiuza kuti tiyenera “kukondana.” (Aroma 13:8) Komabe palinso zifukwa zina zotichititsa kuti ‘tipitirize kusonyeza chikondi.’
Chikondi N’chofunika Kwambiri
Chikondi chimatichititsa kuti tizikhulupirira abale athu
4, 5. N’chifukwa chiyani n’zofunika kwambiri kuti tizisonyeza Akhristu anzathu chikondi chololera kuvutikira ena?
4 N’zofunika kwambiri kuti tizikonda Akhristu anzathu. N’chifukwa chiyani tikutero? Mwachidule, chifukwa chakuti chikondi ndi khalidwe lofunika kwambiri kwa Akhristu oona. Popanda chikondi sitingagwirizane kwambiri ndi Akhristu anzathu komanso Yehova sangatigwiritse ntchito. Tiyeni tione zimene Mawu a Mulungu amanena pa nkhaniyi.
5 Pa usiku womaliza wa moyo wake padzikoli, Yesu anauza otsatira ake kuti: “Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mofanana ndi mmene ine ndakukonderani, inunso muzikondana choncho. Onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga ngati mukukondana.” (Yohane 13:34, 35) Ponena kuti “mofanana ndi mmene ine ndakukonderani,” Yesu akutilamula kuti tizisonyeza chikondi chofanana ndi chimene iye anasonyeza. M’Mutu 29 tinaona kuti Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yosonyeza chikondi chololera kuvutikira ena. Nafenso tiyenera kukhala ndi chikondi chimenechi ndipo tiyenera kuchisonyeza m’njira yoti anthu amene satumikira Yehova azitha kuona kuti timakondanadi. Ndithudi, chikondi chololera kuvutikira ena ndi chizindikiro chathu monga otsatira enieni a Khristu.
6, 7. (a) Kodi tikudziwa bwanji kuti Baibulo limatsindika kufunika kokhala ndi chikondi? (b) Kodi mawu a Paulo a pa 1 Akorinto 13:4-8 akunena za chikondi chiti?
6 Nanga bwanji ngati tilibe chikondi? Mtumwi Paulo ananena kuti: “Ngati . . . ndilibe chikondi, ndili ngati belu longolira kapena chinganga chosokosera.” (1 Akorinto 13:1) Ziwiri zonsezi, chinganga komanso belu longolira, zimasokosa kwambiri. Chimenechi ndi chitsanzo choyenera. Munthu wopanda chikondi amafanana ndi chida choimbira chimene chimasokosera ndipo sichisangalatsa. Munthu wotereyu sangakhale ndi anzake apamtima. Paulo ananenanso kuti: “Ngati . . . ndili ndi chikhulupiriro cholimba moti ndingathe kusuntha mapiri, koma ndilibe chikondi, zomwe ndimachita zilibe ntchito.” (1 Akorinto 13:2) Tangoganizani, zinthu zonse zimene munthu wopanda chikondi amachita n’zopanda ntchito. Ndiyetu m’pake kuti Baibulo limati tizikhala anthu achikondi.
7 Komabe, kodi tingasonyeze bwanji chikondi tikamachita zinthu ndi anthu? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyeni tikambirane zimene Paulo ananena pa 1 Akorinto 13:4-8. Mavesiwa sakunena za chikondi chimene Mulungu amatisonyeza kapenanso chikondi chimene timamusonyeza. Koma akunena za chikondi chimene timasonyeza anthu ena. Paulo anafotokoza zimene chikondi chimachita ndiponso zimene sichichita.
Zimene Chikondi Chimachita
8. Kodi kuleza mtima kungatithandize bwanji tikamachita zinthu ndi ena?
8 “Chikondi nʼcholeza mtima.” Munthu wachikondi amakhala wololera ndipo amachita zimenezo moleza mtima. (Akolose 3:13) Mwina mungavomereze kuti timafunikadi kukhala oleza mtima. Popeza ifeyo komanso Akhristu anzathu si ife angwiro ndipo timatumikira limodzi, timadziwa kuti nthawi zina tikhoza kulakwirana kapena kukhumudwitsana. Koma ngati ndife oleza mtima ndiponso ololera, tingathe kupirira zokhumudwitsa zing’onozing’ono zimene zingakhalepo tikamachita zinthu ndi ena, ndipo sitingasokoneze mtendere mumpingo.
9. Kodi tingasonyeze kukoma mtima m’njira ziti?
9 “Chikondi . . . nʼchokoma mtima.” Timasonyeza kuti ndife okoma mtima pochita zinthu zothandiza ena komanso polankhula mawu osonyeza kuti timawaganizira. Chikondi chimachititsa kuti tizifufuza njira zoti tisonyeze ena kukoma mtima, makamaka amene akufunika kuwathandiza. Mwachitsanzo, Mkhristu wachikulire angamasowe wocheza naye ndipo angafunike kumulimbikitsa. Mayi yemwe akulera yekha ana kapena mlongo amene mwamuna wake si Mboni angafunike kumuthandiza zinthu zina. Munthu amene akudwala kapena amene akukumana ndi mavuto enaake angafune kumva mawu abwino ochokera kwa mnzake wokhulupirika. (Miyambo 12:25; 17:17) Tikamayamba ndife kusonyeza kukoma mtima m’njira ngati zimenezi, timasonyeza kuti ndifedi achikondi.—2 Akorinto 8:8.
10. Kodi chikondi chimatithandiza bwanji kukhala kumbali ya choonadi komanso kulankhula zoona ngakhale pamene kuchita zimenezo kuli kovuta?
10 “Chikondi . . . chimasangalala ndi choonadi.” Baibulo lina limati: “Chikondi . . . chimasangalala kukhala kumbali ya choonadi.” Chikondi chimatichititsa kuti tizikhala kumbali ya choonadi ‘n’kumauzana zoona.’ (Zekariya 8:16) Mwachitsanzo, ngati munthu yemwe timamukonda wachita tchimo lalikulu, kukonda Yehova ndiponso wolakwayo kudzatithandiza kutsatira mfundo za Yehova m’malo moyesa kubisa tchimolo, kulichepetsa kapena kunena zabodza. N’zoona kuti zingakhale zovuta kuvomereza zomwe zachitikazo. Koma ngati timafunira zabwino munthuyo, tidzafuna kuti alandire chilango chochokera kwa Mulungu, womwe ndi umboni woti amamukonda. (Miyambo 3:11, 12) Komanso popeza ndife Akhristu, timafuna “kuchita zinthu zonse moona mtima.”—Aheberi 13:18.
11. Popeza chikondi ‘chimakwirira zinthu zonse,’ kodi tiyenera kutani ndi zimene Akhristu anzathu amalakwitsa?
11 “Chikondi . . . chimakwirira zinthu zonse.” Baibulo lina limati chikondi “chimaphimba zinthu zonse.” (Kingdom Interlinear) Lemba la 1 Petulo 4:8 limati: “Chikondi chimakwirira machimo ochuluka.” Kunena zoona, Mkhristu wachikondi sakonda kulankhula zimene Akhristu anzake amalakwitsa n’cholinga choti ena azidziwe. Nthawi zambiri, zolakwa za Akhristu anzathu zimakhala zazing’ono moti tikhoza kungozikwirira kapena kuziphimba ndi chikondi.—Miyambo 10:12; 17:9.
12. Kodi mtumwi Paulo anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira kuti Filimoni achita zabwino, nanga tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Paulo?
12 “Chikondi . . . chimakhulupirira zinthu zonse.” Baibulo limene anamasulira Moffatt limati chikondi “nthawi zonse chimafunitsitsa kukhulupirira zabwino kwambiri.” Timayesetsa kukhulupirira Akhristu anzathu ndipo timapewa kukayikira zolinga zawo popanda zifukwa zomveka. Chikondi chimatithandiza kuti tisamakayikire abale athu ndipo timakhulupirira kuti amachita “zabwino kwambiri.”a Timaona chitsanzo cha zimenezi m’kalata imene Paulo analembera Filimoni. Paulo analemba kalatayi pofuna kulimbikitsa Filimoni kuti amulandire bwino kapolo wake Onesimo amene anathawa, yemwe pa nthawiyi anali Mkhristu. Iye sanakakamize Filimoni kuti achite zimenezi, koma anamupempha mwachikondi. Ankakhulupirira kuti Filimoni achita zoyenera. Ananena kuti: “Ndikukulembera zimenezi chifukwa ndikukhulupirira kuti uzichitadi. Ndikudziwanso kuti uchita ngakhale zoposa zimene ndanenazi.” (Vesi 21) Tikamakhulupirira abale athu chifukwa chowakonda, zimawathandiza kuti azichita zinthu zabwino.
13. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayembekezera zabwino kwa abale athu?
13 “Chikondi . . . chimayembekezera zinthu zonse.” Monga mmene zilili kuti munthu wachikondi amakhulupirira kuti ena achita zabwino, iye amayembekezeranso zabwino. Chikondi chimatichititsa kuti tiziyembekezera kuti abale athu achita zabwino. Mwachitsanzo, ngati m’bale “wapatuka nʼkuyamba kulowera njira yolakwika mosazindikira,” timakhulupirira kuti atsatira malangizo achikondi omwe angapatsidwe. (Agalatiya 6:1) Timakhulupiriranso kuti anthu amene afooka ayambiranso kutumikira Yehova mwakhama. Timawalezera mtima ndipo timachita zonse zomwe tingathe powathandiza kuti akhalenso ndi chikhulupiriro cholimba. (Aroma 15:1; 1 Atesalonika 5:14) Munthu amene timamukonda akasiya choonadi, sititaya mtima ndipo timakhulupirira kuti tsiku lina nzeru zidzamubwerera ndipo adzabwerera kwa Yehova ngati mwana wolowerera wa m’fanizo la Yesu uja.—Luka 15:17, 18.
14. Kodi nthawi zina tingafunike kupirira mayesero ati mumpingo, nanga chikondi chingatithandize bwanji?
14 “Chikondi . . . chimapirira zinthu zonse.” Kupirira kumatithandiza kukhalabe olimba tikakumana ndi zokhumudwitsa kapena mavuto. Sikuti mayesero amachokera kwa anthu osalambira Yehova okha. Nthawi zina amachokera kwa abale ndi alongo athu. Popeza anthufe si angwiro, nthawi zina abale athu angatikhumudwitse. Mwina angalankhule mawu olasa ngati lupanga. (Miyambo 12:18) Mwinanso tingaone kuti nkhani ina mumpingo sinasamaliridwe ngati mmene ifeyo timaganizira. Kapena zochita za m’bale wina amene anthu amamulemekeza zingatikhumudwitse ndipo tingamadzifunse kuti, ‘Mkhristu angachitirenji zimenezi?’ Tikakumana ndi zinthu ngati zimenezi, kodi tidzachoka mumpingo n’kusiya kutumikira Yehova? Ngati tili ndi chikondi sitingachite zimenezo. Chikondi chimatithandiza kuti tisamangoona zimene Mkhristu wina amalakwitsa n’kulephera kuona zabwino zomwe iyeyo kapena abale ndi alongo athu amachita. Chifukwa cha chikondi, timakhalabe okhulupirika kwa Mulungu n’kumathandiza mpingo, kaya m’bale kapena mlongo wina wachita kapena kulankhula zotani.—Salimo 119:165.
Zimene Chikondi Sichichita
15. Kodi munthu wansanje amatani, nanga chikondi chimatithandiza bwanji kupewa khalidwe loipali?
15 “Chikondi sichichita nsanje.” Sitiyenera kuchitira ena nsanje chifukwa choti ali ndi katundu, luso linalake kapena chifukwa cha madalitso amene alandira. Munthu wansanje amakhala wodzikonda ndipo nsanje imabweretsa mavuto kwa iyeyo ndiponso anthu ena. Ngati munthu wotereyu sangasinthe, akhoza kusokoneza mtendere mumpingo. Ndiye kodi n’chiyani chingatithandize kupewa mtima wansanje? (Yakobo 4:5) Chikondi. Khalidwe lofunika kwambiri limeneli lingatithandize kuti tizisangalala ndi amene akuoneka kuti ali ndi zinthu zina zabwino zomwe ife tilibe. (Aroma 12:15) Chikondi chimatithandizanso kuti tisakhumudwe ngati wina watamandidwa chifukwa cha luso lake lapadera kapena chifukwa cha zimene wakwanitsa kuchita.
16. Ngati timakondadi abale athu, n’chifukwa chiyani timapewa kudzitama chifukwa cha zimene tikuchita m’gulu la Yehova?
16 “Chikondi . . . sichidzitama, sichidzikuza.” Chikondi chimatichititsa kuti tisamadzitame chifukwa cha maluso athu kapena zinthu zimene takwanitsa kuchita. Ngati timakondadi abale athu, kodi pali chifukwa choti tizidzitama chifukwa cha udindo wathu mumpingo kapena zinthu zikatiyendera bwino mu utumiki? Zimenezo zingafooketse ena ndipo angamadzione kuti ndi opanda pake poyerekezera ndi ifeyo. Ngati tili ndi chikondi sitingamadzitame chifukwa cha zimene Mulungu watilola kuchita m’gulu lake. (1 Akorinto 3:5-9) Ndipotu chikondi “sichidzikuza,” kapena mogwirizana ndi Baibulo lina, “sichisangalala ndi maganizo odzimva chifukwa choona kuti ndiwe wofunika.” (The New Testament in Modern English) Choncho chikondi chimatichititsa kuti tisamadzione kuti ndife apamwamba kuposa ena.—Aroma 12:3.
17. Ngati tili ndi chikondi, kodi timachita chiyani, nanga timapewa zinthu ziti?
17 “Chikondi . . . sichichita zosayenera.” Munthu amene amachita zosayenera amachita zinthu zochititsa manyazi komanso zosonyeza kupanda ulemu. Kuchita zimenezi ndi kupanda chikondi chifukwa zimasonyeza kuti munthuyo saganizira ena. Mosiyana ndi zimenezi, chikondi chimathandiza kuti tizikhala okoma mtima kwa ena komanso kuwasonyeza kuti timawaganizira. Chikondi chimatichititsa kuti tizisonyeza makhalidwe abwino, tizichita zinthu zimene Yehova amasangalala nazo komanso tizilemekeza Akhristu anzathu. Ngati tili ndi chikondi, tidzapewa khalidwe lililonse lochititsa manyazi, lomwe lingakhumudwitse kwambiri Akhristu anzathu.—Aefeso 5:3, 4.
18. N’chifukwa chiyani munthu wachikondi sakakamira kuti chilichonse chizichitika mmene iye akufunira?
18 “Chikondi . . . sichisamala zofuna zake zokha.” Baibulo lina limati: “Chikondi sichiumirira maganizo ake.” (Revised Standard Version) Munthu wachikondi sakakamira kuti chilichonse chizichitika mmene iye akufunira, ngati kuti nthawi zonse maganizo ake ndi amene amakhala olondola. Sakakamiza ena omwe ali ndi maganizo osiyana ndi ake kuti agwirizane ndi maganizo ake komanso kuti achite zinthu mmene iye akufunira. Ngati atamachita zimenezo, angasonyeze kuti ndi wonyada ndipo Baibulo limati: “Kunyada kumachititsa kuti munthu awonongeke.” (Miyambo 16:18) Ngati timakondadi abale athu, timalemekeza maganizo awo ndipo timakhala ololera ngati pakufunika kutero. Kukhala ololera n’kogwirizana ndi mawu a Paulo akuti: “Aliyense asamangofuna zopindulitsa iyeyo basi, koma zopindulitsanso ena.”—1 Akorinto 10:24.
19. Kodi chikondi chimatithandiza kuchita chiyani ena akatilakwira?
19 “Chikondi . . . sichikwiya ndipo sichisunga zifukwa.” Munthu wachikondi safulumira kupsa mtima ndi zimene ena anena kapena kuchita. N’zoona kuti mwachibadwa anthu ena akatichitira zoipa, timakhumudwa. Koma ngakhale titakwiya pa zifukwa zomveka, chikondi chimatithandiza kuti tisapitirize kukhala okwiya. (Aefeso 4:26, 27) Sitisunga zinthu zoipa zimene ena anatinenera kapena kutichitira ngati kuti tinazilemba m’buku kuti tisaziiwale. Chikondi chimatichititsa kuti tizitsanzira Mulungu wathu. Monga tinaonera m’Mutu 26, Yehova amatikhululukira pakakhala zifukwa zomveka. Akatero amaiwala, kutanthauza kuti pa nthawi ina m’tsogolo satiimbanso mlandu chifukwa cha machimo omwe anatikhululukirawo. Timathokozatu kwambiri kuti Yehova satisungira zifukwa.
20. Kodi tiyenera kutani Mkhristu mnzathu akachita tchimo kenako n’kumavutika ndi zotsatira zake?
20 “Chikondi . . . sichisangalala ndi zosalungama.” Baibulo lina limati: “Chikondi . . . sichinyadira anthu ena akachita machimo.” (New English Bible) Baibulo lomasuliridwa ndi Moffatt limati: “Chikondi sichisangalala ena akalakwitsa.” Munthu wachikondi sasangalala ndi zosalungama, choncho pakachitika khalidwe loipa lililonse sitisangalala. Ndiye kodi timatani Mkhristu mnzathu akachita tchimo kenako n’kumavutika ndi zotsatira zake? Ngati ndife achikondi sitingasangalale chifukwa zingakhale ngati tikunena kuti, ‘Zakhala bwino! Akhaule.’ (Miyambo 17:5) Koma timasangalala m’bale yemwe wachita tchimo akayamba kuchita zoyenera kuti akonzenso ubwenzi wake ndi Yehova.
“Njira Yopambana”
21-23. (a) Kodi Paulo ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti “chikondi sichitha?” (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’mutu womaliza?
21 “Chikondi sichitha.” Kodi Paulo ankatanthauza chiyani ponena mawu amenewa? Tikawerenga nkhani yonse, zikuoneka kuti ankafotokoza zokhudza mphatso za mzimu zimene Akhristu oyambirira anali nazo. Mphatso zimenezo zinali chizindikiro chosonyeza kuti Yehova wayamba kugwiritsa ntchito mpingo wa Chikhristu womwe unali utangokhazikitsidwa kumene. Koma si Akhristu onse omwe ankachiritsa odwala, kulosera kapena kulankhula malilime. Komabe imeneyi sinali nkhani yofunika kwambiri, chifukwa mphatso zochita zodabwitsa zinali zoti pakapita nthawi zidzatha. Koma panali chinthu china choti chidzapitiriza kukhalapo, chomwe Mkhristu aliyense akanatha kuyesetsa kuti akhale nacho. Chinali chapadera kwambiri ndiponso chokhalitsa kuposa mphatso yochita zodabwitsa iliyonse. Ndipotu Paulo anachitchula kuti “njira yopambana.” (1 Akorinto 12:31) Kodi “njira yopambana” imeneyi inali chiyani? Inali njira yachikondi.
22 Zoonadi, chikondi cha Akhristu chimene Paulo anafotokoza “sichitha” ndipo chidzakhalapo mpaka kalekale. Mpaka pano, otsatira oona a Yesu amadziwika kuti amasonyezana chikondi chololera kuvutikira ena. Chikondi chimenechi chimaoneka pakati pa atumiki a Yehova padziko lonse ndipo sichidzatha chifukwa Yehova analonjeza kuti adzapatsa atumiki ake okhulupirika moyo wosatha. (Salimo 37:9-11, 29) Tiyeni tizichita zonse zomwe tingathe kuti ‘tipitirize kusonyeza chikondi.’ Tikamachita zimenezi timasangalala kwambiri chifukwa chokhala wopatsa. Kuwonjezera pamenepo, tidzapitiriza kukhala ndi moyo ndiponso kusonyeza chikondi mpaka kalekale potsanzira Mulungu wathu wachikondi, Yehova.
Anthu a Yehova amadziwika ndi chikondi
23 M’mutuwu, womwe ndi womaliza pa gawo lonena za chikondi, takambirana mmene tingasonyezere ena chikondi. Chikondi cha Yehova chimatithandiza m’njira zambiri. N’chimodzimodzinso ndi mphamvu zake, chilungamo chake komanso nzeru zake. Tikaganizira zimenezi ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndingamusonyeze bwanji Yehova kuti ndimamukondadi?’ Tidzakambirana funso limeneli m’mutu womaliza.
a Komabe, ngakhale kuti chikondi “chimakhulupirira zinthu zonse,” sizikutanthauza kuti tizilola anthu ena kutinamiza. Baibulo limatichenjeza kuti: “Musamale ndi amene amagawanitsa anthu ndiponso kuchita zinthu zokhumudwitsa . . . choncho muziwapewa.”—Aroma 16:17.
-