MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Muziwalandira ndi Manja Awiri
Kodi ndi ndani omwe tiyenera kuwalandira ndi manja awiriwa? Ndi aliyense amene amabwera kumisonkhano yathu. (Aroma 15:7; Aheb. 13:2) Angakhale atsopano, Mkhristu mnzathu yemwe wachokera kudziko lina kapenanso Mkhristu amene anasiya kusonkhana kwa nthawi yaitali. Taganizirani muli inuyo, kodi simungathokoze ena atakulandirani ndi manja awiri? (Mat. 7:12) Choncho, bwanji osayesa kuchita khama kuti muzipereka moni mu Nyumba ya Ufumu, misonkhano isanayambe komanso ikatha? Izi zimathandiza kuti onse mumpingo azikondana ndiponso Yehova amalemekezedwa. (Mat. 5:16) N’zoona kuti sizingatheke kulankhulana ndi aliyense. Komabe tikamayesetsa, aliyense amaona kuti walandiridwa.a
Tiyenera kulandira bwino anthu nthawi zonse osati pa nthawi ya Chikumbutso yokha. Atsopano akaona chikondi pakati pathu, amalemekeza Mulungu ndipo zimawalimbikitsa kuti ayambe kulambira nafe limodzi.—Yoh. 13:35.
a Tiyenera kukumbukira kuti Baibulo limaletsa kulankhulana ndi anthu ochotsedwa kapena odzilekanitsa.—1 Akor. 5:11; 2 Yoh. 10.