Kodi Nthawi Zonse Mumaona Zimene Zili pa Bolodi la Chidziwitso?
Akulu, atumiki othandiza ndiponso ena amene amachita mbali zosiyanasiyana mumpingo amakonda kuona zimene zili pabolodi la chidziwitso kuti aone ngati ali ndi mbali iliyonse yoti achite. Komabe, tonsefe tikulimbikitsidwa kumaona zimene zili pabolodi limeneli chifukwa pamakhala zinthu zofunika zoti tizidziwe. Mwachitsanzo, kodi mukudziwa tsiku limene mudzayeretse Nyumba ya Ufumu? Kodi woyang’anira dera kapena ofesi ya nthambi inatumiza kalata iliyonse yofunika kumpingo wanu yomwe inaikidwa pabolodi? Kodi mukudziwa mutu wa nkhani ya onse mlungu uno kuti muthe kuitanira wophunzira Baibulo wanu? Kodi pali kusintha kulikonse kwa nthawi ya misonkhano kapena m’kagulu kanu ka utumiki wakumunda? Nkhani ngati zimenezi sizilengezedwanso pa misonkhano. Komanso n’zosatheka kuti akulu aziuza wofalitsa aliyense zinthu zimenezi. Choncho, tiyenera kukhala ndi chizolowezi choona zimene zili pabolodi la chidziwitso. Ngati titamaona zimenezi pabolodi, ndiye kuti zinthu zonse zizichitika “moyenera ndi mwadongosolo.”—1 Akor. 14:40.