Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 11/08 tsamba 3
  • Bokosi la Mafunso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Bokosi la Mafunso
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Nkhani Yofanana
  • Zomwe Mungachite Kuti Tsiku la Ukwati Wanu Likhale Losangalatsa ndi Lolemekezeka Kwambiri
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Maukwati Osangalatsa Amene Amalemekeza Yehova
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Maukwati Olemekeza Yehova
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Ukwati Wolemekezeka kwa Mulungu ndi kwa Anthu
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
km 11/08 tsamba 3

Bokosi la Mafunso

◼ Ngati m’bale ndi mlongo akufuna kugwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu pa ukwati wawo, kodi ndi zinthu ziti zimene ayenera kukambirana ndi akulu?

Maukwati amene amachitika mogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo amalemekeza Yehova. Zimenezi zili choncho ndi maukwati amene amachitikira pa Nyumba za Ufumu. Chifukwa chake n’chakuti anthu amaona kuti zinthu zimene zimachitika kumeneko zimasonyeza mmene gulu lathu liliri. Kuti ‘zinthu zonse zichitike moyenera ndi mwadongosolo,’ akulu ayenera kukambirana ndi akwati ngati iwo apempha kudzagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu panthawi ya ukwati wawo.—1 Akor. 14:40.

Akwati amene akufuna kudzagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu panthawi ya ukwati wawo, ayenera kulemba kalata yopempha Nyumba ya Ufumuyo ku komiti ya utumiki ya mpingo umene umasonkhana panyumbayo. Kalatayo, iyenera kuperekedwa mwamsanga ndipo isonyeze deti ndi nthawi imene akwatiwo adzafuna kugwiritsa ntchito nyumbayo. Iwo ayenera kukumbukira kuti, akulu sadzasintha nthawi ya misonkhano chifukwa cha ukwati wawo. Ndiponso, mkwati ndi mkwatibwi ayenera kukhala ndi mbiri yabwino, ndipo moyo wawo uyenera kugwirizana ndi mfundo za m’Baibulo ndi malamulo olungama a Yehova.

Pofuna kuonetsetsa kuti ukwati wawo ukupereka ulemu kwa Mulungu wathu wolemekezeka, akwatiwo ayenera kukambirana za dongosolo lonse ndi komiti ya utumiki asanamalizitse kukonza dongosolo la ukwati wawolo. Akulu sayenera kukakamiza akwati kuti atsatire maganizo a akuluwo, komabe ngati pa zinthu zimene akwatiwo akukonza pali zinthu zina zosayenera, akwatiwo ayenera kulola kusintha zimenezo. Nyimbo zimene ayenera kugwiritsa ntchito zikhale zochokera mu Kingdom Melodies kapena m’buku lathu la nyimbo basi. Ngati akufuna kukongoletsa Nyumba ya Ufumu kapena kusintha kayalidwe ka mipando, ayeneranso kulandira chilolezo. Ngati padzakhala kujambula zithunzi kapena vidiyo, zimenezi siziyenera kuchotsera ulemu mwambo wa ukwati. Akulu angaloleze akwatiwo kudzayeserera zimene akonza pa Nyumba ya Ufumu malinga ngati zimenezo sizidzasokoneza zochitika zina za mpingo. Makalata oitanira anthu ku ukwati sayenera kuikidwa pa bolodi la chidziwitso. M’malo mwake, akulu angapereke chilengezo chachidule pa Msonkhano wa Utumiki kuuza mpingo za ukwati umene udzachitikire pa Nyumba ya Ufumupo.

Ngakhale kuti si lamulo kuti onse operekeza akwati azikhala obatizidwa, sikoyenera kuikapo anthu amene zochita zawo zimaphwanya mfundo za m’Baibulo kapena amene makhalidwe awo angabweretse mafunso m’maganizo a anthu oitanidwa. Ngati mkulu alipo, ndi amene ayenera kuyendetsa mwambo wa ukwati. Akulu ndiwo aphunzitsi oyenerera a Mawu a Mulungu, choncho iwo ndi amene ali ndi ziyeneretso zonse zofotokoza mfundo za m’Malemba zogwirizana ndi mwambo wofunika kwambiri umenewo.—1 Tim. 3:2.

Popeza kuti mwambo wa ukwati ungakhudze mbiri ya mkulu amene adzayendetse mwambowo, mkuluyo afunika kuuzidwa za dongosolo lonse la ukwati. Iye ayenera kukumana ndi akwatiwo kuti adziwe ngati iwo anali odzisunga panthawi imene anali pachibwenzi. Akwatiwo sayenera kuchita manyazi, ayenera kumufotokozera zonse moona mtima. Ngati mkwatibwi kapena mkwati anakwatirapo m’mbuyomo, ayenera kupereka umboni wakuti iye mwa Malemba ndiponso mwalamulo ali ndi ufulu wokwatiwa kapena kukwatiranso. (Mat. 19:9) Zimenezi zikuphatikizapo kusonyeza mkuluyo chikalata chakuboma cha chisudzulo.

Ngati akwatiwo angakambirane momasuka ndi akulu ndiponso kugwirizana nawo bwinobwino, mwambo wa ukwati udzakhala wosangalatsa kwa onse.—Miy. 15:22; Aheb. 13:17.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena