MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kodi Mungachite Upainiya kwa Chaka Chimodzi?
Kodi mungapeze madalitso otani ngati mutachita upainiya?—Miy. 10:22.
MUKAMACHITA UPAINIYA, MUKHOZA KUPEZA MADALITSO OTSATIRAWA:
Mukhoza kukhala ndi luso lolalikira ndipo mungamasangalale mu utumiki.
Mungamakonde kwambiri Yehova. Mukamauza ena zokhudza Yehova m’pamenenso mumaganizira kwambiri za makhalidwe ake abwino.
Mungaone ubwino woika zinthu za Ufumu pamalo oyamba m’malo mwa zofuna zanu. Mungakhalenso osangalala mukamagwiritsa ntchito nthawi komanso zinthu zanu pothandiza ena mu utumiki.—Mat. 6:33; Mac. 20:35
Mukhoza kulowa Sukulu ya Apainiya, kuchita nawo msonkhano wa apainiya womwe umachitika msonkhano wadera ukayandikira komanso womwe woyang’anira dera amachititsa akamachezera mpingo.
Mungapeze anthu ambiri oti muziphunzira nawo Baibulo.
Mungamakhale nthawi yaitali muli ndi abale ndi alongo, omwe angakulimbikitseni komanso kukuthandizani.—Aroma 1:11, 12