Muzilimbikitsa Mnzanu Amene Mwalowa Naye mu Utumiki
1. Kodi tingatsanzire bwanji mtumwi Paulo tikamalalikira ndi munthu wina?
1 Mtumwi Paulo akakhala ndi Akhristu anzake, ankaona kuti imeneyo ndi nthawi yabwino ‘yolimbikitsana.’ (Aroma 1:12) Mukakhala mu utumiki, kodi mumaona kuti mungagwiritse ntchito nthawi imeneyi kulimbikitsa komanso kuthandiza munthu amene mwayenda naye? M’malo mongokhala chete, ndi bwino kumakambirana ndi mnzanuyo zimene zakuthandizani inuyo kuti muzilalikira mogwira mtima.
2. Kodi tingathandize bwanji amene tayenda naye mu utumiki kuchotsa mantha, ndipo n’chifukwa chiyani kuchita zimene n’kofunika?
2 Muthandizeni Kuchotsa Mantha: Ofalitsa ena amakhala ndi mantha ndipo izi zimaonekera pankhope yawo komanso mmene mawu awo akumvekera. Tingawathandize kuchotsa mantha powayamikira kuchokera pansi pa mtima. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Woyang’anira dera wina amakonda kuuza amene walowa naye mu utumiki zimene zimamuchititsa mantha. Kenako amafotokoza kuti amapemphera pafupipafupi kuti Mulungu amuthandize kuthetsa manthawo. M’bale wina anafotokoza zimene zimamuthandiza kuti asamaoneke zoti ali ndi mantha. Iye anati: “Ndimayesetsa kumwetulira. Nthawi zina ndimafunika kupemphera kuti ndithe kuchita zimenezi.” Kodi inunso pali zina zimene zimakuthandizani kuti musamakhale ndi mantha mu utumiki? Mungachite bwino kufotokozera zimenezi mnzanu amene mwayenda naye.
3. Kodi ndi zinthu ziti zimene tingauze munthu amene tayenda naye mu utumiki, zomwe zingamuthandize kuti azilalikira mogwira mtima?
3 Muuzeni Njira Zimene Mumagwiritsa Ntchito Polalikira: Kodi pali mawu oyamba enaake kapena funso logwirizana ndi anthu a m’dera lanu limene mumaona kuti limathandiza poyamba kukambirana ndi anthu? Kapena kodi munaona kuti kusintha mwina ndi mwina zitsanzo za ulaliki, kumathandiza kuti anthu achite chidwi ndi uthenga wa m’Baibulo? Mungachite bwino kufotokozera zimenezi munthu amene mwayenda naye. (Miy. 27:17) Mukamapita ku ulendo wobwereza, mungamufotokozere zimene mwakonzekera ndi mmene mukazinenere. Kapena mukamaliza phunziro, mungafotokozere mnzanuyo chifukwa chimene mwagwiritsira ntchito njira inayake pophunzitsa. Mungamufotokozerenso chifukwa chimene mwatchulira mfundo inayake kapena kuwerenga lemba lina.
4. N’chifukwa chiyani tiyenera kuthandiza ofalitsa anzathu?
4 Akhristu a nthawi ya atumwi sankangothandiza anthu osakhulupirira okha. Iwo ankadziwanso kufunika kothandiza komanso kulimbikitsa Akhristu anzawo. (Mac. 11:23; 15:32) Mtumwi Paulo anaphunzitsa Timoteyo ndipo anamulimbikitsa kuti nayenso aphunzitse ena zimene waphunzirazo. (2 Tim. 2:2) Tikamakumbukira kuchitira zabwino Akhristu anzathu tikakhala mu utumiki, timawathandiza kuti azisangalala komanso kuti azilalikira mogwira mtima. Tikamachita zimenezi timasangalatsanso Atate wathu wakumwamba.—Aheb. 13:15, 16.