Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb17 December tsamba 8
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki​—Muzilalikira Munthu Aliyense wa M’gawo Lanu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki​—Muzilalikira Munthu Aliyense wa M’gawo Lanu
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
  • Nkhani Yofanana
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Muzilalikira Anthu Oyankhula Chinenero China
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
  • N’zotheka Kulalikira kwa Aliyense
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Njira Zolalikirira Uthenga Wabwino
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Tizichita Zinthu Mogwirizana Tikamalalikira M’gawo la Zinenero Zambiri
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
mwb17 December tsamba 8
Mlongo wa ku Namibia ali ndi mayi wachikulire

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki​—Muzilalikira Munthu Aliyense wa M’gawo Lanu

KODI ZIMENEZI N’ZOFUNIKA BWANJI? Zekariya analosera kuti anthu a zilankhulo komanso mitundu yosiyanasiyana adzamvetsera uthenga wabwino. (Zek. 8:23) Koma kodi adzawaphunzitse anthuwa ndi ndani? (Aroma 10:13-15) Ifeyo ndi amene tili ndi udindo wolalikira uthenga wabwino kwa munthu aliyense wa m’gawo lathu.​—od 84 ¶10-11.

KODI TINGACHITE BWANJI ZIMENEZI?

  • Tizikonzekera. Kodi tikamalalikira m’gawo lathu timakumana ndi anthu a zinenero zina? Ngati ndi choncho tingathe kugwiritsa ntchito pulogalamu ya JW Language kuti tiphunzire mmene tingalalikirire mwachidule anthuwo m’zinenero zawo. Tikhozanso kugwiritsa ntchito foni kapena tabuleti yathu kuwasonyeza mmene angapezere mabuku ndi zinthu zina pa jw.org

  • Tizikhala tcheru. Tizilalikira anthu amene tingakumane nawo mumsewu tikamachoka kunyumba ina kupita kunyumba ina komanso anthu amene ali m’magalimoto omwe angoima. Ngati tikulalikira m’malo opezeka anthu ambiri, maganizo athu onse azikhala pa ntchito yolalikirayo

  • Tizichita khama. Ngati sitinapeze anthu pakhomo linalake, tizibwererakonso. Tikhoza kusintha nthawi kapena tsiku loti tipiteko n’cholinga choti tikawapeze. Anthu ena omwe sakupezekabe pakhomo, tikhoza kuwalembera kalata, kuwaimbira foni, kapenanso tingathe kungochita ulaliki wa mumsewu

  • Tizibwererako mwachangu. Ngati munthu wasonyeza chidwi tizibwererako mofulumira. Ngati munthuyo amalankhula chinenero china, tizifufuza munthu woyenerera woti aziphunzira naye m’chinenero chakecho. Sitiyenera kusiya kupitako kufikira atayamba kuphunzira ndi ofalitsa amene amayankhula chinenero chake.​—od 94 ¶39-40

ONERANI VIDIYO YAKUTI KULALIKIRA MPAKA “KUMALEKEZERO A DZIKO LAPANSI” KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kagulu ka ku Namibia kakukonzekera ulendo wopita kukalalikira

    Kodi abale ndi alongo a m’vidiyoyi anakonzekera bwanji popita kukalalikira kugawo lakutali (1 Akor. 9:22, 23)

  • Magalimoto omwe atenga anthu popita kukalalikira kugawo lakutali la ku Namibia

    Kodi anakumana ndi mavuto otani?

  • Ana a ku Namibia akuonera mavidiyo a pa jw.org

    Kodi anapeza madalitso otani?

  • Kodi ndi zinthu ziti zimene tikufuna kuchita kuti tizilalikira anthu ambiri m’gawo lathu?

Woyang’anira utumiki ayenera kuonetsetsa kuti gawo lonse la mpingo likulalikidwa mokwanira. Mabungwe ena a akulu amakonza zoti pa masiku ena mwezi ulionse, ofalitsa azilalikira tsiku lonse m’magawo omwe salalikidwa kawirikawiri.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena