Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Muziphunzitsa Anthu Amene Mumaphunzira Nawo Baibulo Kuti Azikonda Kuphunzira Paokha
N’chifukwa Chiyani Kuchita Zimenezi N’kofunika? Kuti anthu amene timaphunzira nawo Baibulo azikonda kwambiri Yehova, ayenera kuphunzira paokha zinthu zozama zopezeka m’Mawu a Mulungu, osati mfundo zoyambirira zokha basi. (Aheb. 5:12-14; 6:1) Koma pamafunika khama kuti munthu aziphunzira payekha. Kuti munthu amvetse zimene akuphunzira, amayenera kugwirizanitsa zimene akuphunzirazo ndi zimene akudziwa kale n’kuona mmene angazigwiritsire ntchito pa moyo wake. (Miy. 2:1-6) Wophunzira wathu akadziwa kufufuza zinthu m’mabuku athu, akhoza kumayankha mosavuta mafunso amene anthu angamufunse mu utumiki. Akamachita khama kuphunzira komanso kutsatira zimene akuphunzirazo, zingamuthandize kuti akakumana ndi mayesero asamagonje.—Luka 6:47, 48.
Tayesani Kuchita Izi Mwezi Uno:
Mukamaliza kuphunzira kamutu kapena mutu wonse, muzipempha wophunzira wanu kuti afotokoze mwachidule zimene waphunzira. Ngati simukuphunzira Baibulo ndi aliyense, yesererani kufotokoza mwachidule mfundo zimene mwawerenga m’mavesi angapo a m’Baibulo kapena mu ndime ya mu Nsanja ya Olonda. Zimenezi zingakuthandizeni kuti nanunso muzitha kufotokoza mfundo m’mawu anuanu.