Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo—Gawo 4:
Kuphunzitsa Ophunzira Kuti Adziwe Kukonzekera
1 Wophunzira amene amawerengeratu zimene adzaphunzire, kuduliratu mizere kunsi kwa mayankho, ndi kulingalira mmene angadzawafotokozere m’mawu akeake, sachedwa kupita patsogolo mwauzimu. Ndiye mukangoti mwakhazikitsa phunziro, mufunika kukonzekera phunziro muli limodzi ndi wophunzirayo kuti mumusonyeze mmene angakonzekerere. Ophunzira ambiri, zimawathandiza kukonzekera nawo limodzi mutu wonse wathunthu.
2 Kudula Mizere ndi Kulemba Notsi: Fotokozani mmene angapezere mayankho a mafunso amene aperekedwa pa nkhaniyo. Muonetseni wophunzirayo buku lanu lophunzirira limene munadula mizere kunsi kwa mawu okhawo amene ali ofunika. Pamene mukukambirana nkhaniyo, angafune kutsatira chitsanzo chanu mwa kudula mizere kunsi kwa mawu okhawo amene ali ofunika kuti am’thandize kukumbukira mayankho. (Luka 6:40) Ndiyeno m’pempheni kupereka mayankho m’mawu akeake. Kuchita zimenezi kudzakuthandizani kuti muone mmene waimvetsetsera nkhaniyo.
3 Mbali yofunika kwambiri kwa wophunzira pokonzekera phunziro ndi kupenda mosamala malemba osagwidwa mawu. (Mac. 17:11) Choncho, m’thandizeni kuona kuti lemba lililonse losagwidwa mawu limachirikiza mfundo inayake ya m’ndimemo. Muonetseni mmene angalembere notsi zachidule m’mphepete mwa buku lake lophunzirira. Muuzeni motsindika mfundo yakuti gwero lalikulu la zonse zimene akuphunzirazo ndi Baibulo. Mukamaphunzira mulimbikitseni kugwiritsa ntchito kwambiri malemba osagwidwa mawu poyankha.
4 Kupenda Nkhani Yonse Mwachidule ndi Kubwereramo: Wophunzira asanayambe kukonzekera mwa ndondomeko yake nkhani imene adzaphunzire, zingam’thandize kuyamba waipenda kaye nkhani yonseyo mwachidule. Muuzeni kuti akhoza kupenda nkhaniyo mwa kuganizapo mwachidule pa mutu wakewo, timitu ta m’kati, ndi zithunzi. M’fotokozereni kuti asanamalize kukonzekerako, angachite bwino pamapeto pake kukhala ndi nthawi yobwereramo mu mfundo zikuluzikulu zimene zili mu nkhaniyo, ndipo mwina angachite zimenezi pogwiritsa ntchito bokosi la mafunso obwereza ngati lilipo. Kubwereza koteroko kungamuthandize kuti mfundo zimene wapeza mu nkhaniyo zikhazikike m’maganizo mwake.
5 Kuphunzitsa wophunzira kukonzekera bwino phunziro lake kudzamuthandiza kupereka ndemanga zogwira mtima pa misonkhano ya mpingo. Kudzamuthandizanso kukhala ndi chizolowezi chophunzira chimene chidzamuthandize m’tsogolo mukadzamaliza kuchita naye phunziro la Baibulo.