Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira December 13
Mph. 10: Zilengezo za pampingo limodzi ndi Zilengezo zina zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Fotokozani zimene zakonzedwa zoti padzakhale utumiki wa kumunda wapadera pa December 25 ndi pa January 1. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 8 kusonyeza chitsanzo cha mmene tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya December 15 ndi Galamukani! ya January 8. Mungathe kugwiritsanso ntchito maulaliki ena amene angakhale othandiza. M’chitsanzo chilichonse, sonyezani njira zosiyana za mmene tingachitire ndi munthu amene sakufuna kuti tikambirane naye ponena kuti ‘Inu ntchito yanu ndikuidziwa kale.’—Onani buku la Kukambitsirana, tsamba 20. (Ngati magazini ameneŵa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph. 15: “Thandizo Lanu Likufunika.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Funsani mkulu mmodzi mwachidule. M’pempheni kuti afotokoze chimene chinamulimbikitsa kuti akalamire udindo wotumikira mumpingo ndi zimene zinamuthandiza kuti afike poyenerera udindowo.
Mph. 20: “Mmene Tingalalikire Achibale.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Gwiritsani ntchito mafunso amene aperekedwawo. Pemphani omvera kupereka ndemanga zachidule kuti afotokoze zimene achita pokopa chidwi achibale ndiyeno n’kuwalalikira.
Nyimbo Na. 17 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira December 20
Mph. 5: Zilengezo za pampingo.
Mph. 15: “Mmene Timapindulira ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu.” Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira sukulu. Phatikizanipo ndemanga zochokera mu mphatika ya mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa October 2004. Konzani pasadakhale zoti munthu mmodzi kapena awiri adzafotokoze mmene akupindulira ndi sukulu imeneyi.
Mph. 25: “Kuthandiza Ena Kudzera mu Phunziro la Buku la Mpingo.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Ipatsidwe kwa mkulu yemwe ndi woyang’anira phunziro la buku wodziwa bwino. Limbikitsani onse kuti mlungu wamawa aliyense adzapezeke pomadzakambirana za njira yotithandiza kupewa magazi yomwe imaperekedwa chaka chilichonse.
Nyimbo Na. 50 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira December 27
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Kumbutsani ofalitsa onse kupereka malipoti awo a utumiki wa kumunda a mwezi wa December. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 8, sonyezani chitsanzo cha mmene tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya January 1 ndi Galamukani! ya January 8. (Ngati magazini ameneŵa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph. 20: “Zinthu Zotithandiza Kuti Tipewe Magazi.” Mafunso ndi mayankho. Gwiritsani ntchito mafunso amene aperekedwawo. Werengani Malemba onse amene aperekedwawo. Ikambidwe ndi mlembi. Pokambirana nkhani imeneyi pemphani atumiki otumikira kugawira makadi a MD ndi Makadi a Ana kwa amene ali oyenerera kupatsidwa.
Mph. 15: “Lemekezani Yehova ndi Chuma Chanu.” Nkhani yokambirana mwa mafunso ndi mayankho.
Nyimbo Na. 8 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira January 3
Mph. 5: Zilengezo za pampingo. Tchulani mabuku ogawira mu January.
Mph. 15: “Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo—Gawo 4.” Pambuyo pokamba mawu oyamba osapitirira mphindi imodzi kuchokera mu ndime 1, sonyezani chitsanzo cha mphindi 5 kuchokera mu ndime 2 ndi 3 chosonyeza wochititsa phunziro la Baibulo akuthandiza wophunzira mmene angakonzekerere phunziro. Posonyeza chitsanzochi, agwiritse ntchito ndime imodzi kuchokera m’buku la Chidziŵitso kapena kuchokera m’bulosha la Mulungu Amafunanji. Ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho ndime 2 mpaka 5, kutsindika mfundo zazikulu zimene azisonyeza m’chitsanzocho.
Mph. 25: “Thandizani Ana Kupindula Kwambiri ndi Misonkhano.” Nkhani ya mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo kufunsa ana mafunso. Kodi akhala akuphunzira zotani pa misonkhano kapena pa phunziro lawo laumwini? Kodi akumana ndi zotani mu utumiki? Fotokozani ubwino wopita ku misonkhano limodzi ndi ana komanso kuphunzira nawo limodzi ndi kupita nawo limodzi mu utumiki wa kumunda.
Nyimbo Na. 79 ndi pemphero lomaliza.