Mmene Timapindulira ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
1 Monga anthu a Yehova tili ndi mwayi wapadera kwambiri wophunzitsidwa ndi iye. (Yes. 54:13; Yoh. 6:45) Koma mmene timapindulira ndi maphunziro amenewa, mbali yaikulu zimadalira khama lathu. Kodi mungafotokoze mmene Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ikukuthandizirani mwauzimu?
2 Ndemanga Zoyamikira: Oyang’anira sukulu ambiri aona kuti kuphunzirira limodzi mozama nkhani ya luso lakulankhula kwathandiza ambiri m’mipingo yawo kukhala ogwira mtima kwambiri mu utumiki wa kumunda. Kuwonjezeranso pamenepo, woyang’anira sukulu wina waona kuti kuyambira pamene ananena kuti omvera azitenga nawo mbali kupereka ndemanga zawo pa mfundo zazikulu za Baibulo, ambiri akutsatira ndandanda yowerengera Baibulo. Pa Nkhani Na. 2, abale ambiri anenapo zolimbikitsa chifukwa cha phindu limene amapeza mwa kungoona za nkhaniyo popanda kukonzekera za mawu oyamba ndi omaliza. Panopa amene amapatsidwa nkhani imeneyi amaika kwambiri chidwi chawo pa kuwongolera luso lawo la kuwerenga.—1 Tim. 4:13.
3 Aliyense Akhoza Kupindula: Kupereka ndemanga pa misonkhano kumasangalatsa. (Miy. 15:23) Kukhala ndi mafunso a kubwereza kwa pakamwa nthawi yake isanafike kumatithandiza kuti tikonzekere ndi kudzatenga nawo mbali mokwanira bwino pomadzabwereramo. Kuwonjezeranso apo, kuyambira ndi Nsanja ya Olonda ya January 1, 2004, pakutuluka nkhani za mfundo zazikulu za mabuku a m’Baibulo zimene zikumayenderana ndi kuwerenga Baibulo kwa mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Nkhani zimenezi zathandiza anthu ambiri kupereka ndemanga zogwira mtima pokambirana mfundo zazikulu za Baibulo.
4 Aliyense amene analembetsa sukuluyi ali ndi mwayi wapadera wokonzekera ndi kukamba nkhani. Tonsefe tingapindule ndi ndemanga zoyamikira zimene woyang’anira sukulu amapereka kupulatifomu. Aliyense amene wapatsidwa nkhani amapindulanso ndi malangizo a mseri amene woyang’anira sukulu amapereka kwa aliyense pambuyo pa misonkhano. Zochita zimene zimakhalapo zokhudza luso la kulankhula pambuyo pa mutu uliwonse m’buku la Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu zimaperekanso thandizo lowonjezera.
5 Ngati mwapeza mfundo zina za m’Malemba zothandiza zimene azitchula m’kati mwa sukuluyi kapena pambuyo pake, zilembeni m’buku lanu la Sukulu ya Utumiki. Sinkhasinkhani zimene mwaphunzira, ndi kuona mmene maphunziro a Mulungu amenewa akukuthandizirani pamoyo wanu wauzimu.