Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Masitayelo—Kodi Ndiyenera Kuwasusukira?
‘NDIWE shasha eti!’ ‘Komatu ndiye watchena!’ Ausinkhu wanu angakuyamikireni kwambiri pamene mutsatira sitayelo yatsopano. Inde, masitayelo amakopa anthu ndi kutengetsa maganizo awo.
Komabe, masitayelo nawonso amasintha ngati mphepo ndipo amakhala kanthaŵi chabe. Malinga ndi kufufuza kwina pa zamalonda, choyamba sitayelo imapeza malo pang’ono pakati pa timagulu ta anyamata ndi atsikana osimbwa ndi opanda khalidwe. Pamene iyamba kufalikira, opanga zinthu ndi osatsa malonda amaichirikiza mwa kusatsa malonda ake m’magazini, pa TV, ndi pa wailesi. Kuti ikhale yolemekezeka ndi yotchuka, oimba nyimbo ndi anthu otchuka amalipidwa kuti aivomereze. Anyamata ndi atsikana mwa iwo okha amaichirikiza ndi changu chachikulu. Itafalikira, imakhala yonyanyula kwa “unyinji waukulu wa achinyamata.”
Komabe, sitayelo imataya chikoka chake m’kupita kwa nthaŵi ndipo imazimiririka. (American Demographics) Koma pamene kuli kwakuti sitayelo yatsopano, kavinidwe, kapena chiŵiya zili zonyanyula chabe, mungakakamizike kugonja. Ambiri amamva monga mmene amamvera Kim wazaka 15: “Ukasiyana ndi ena, iwo amakuchititsa kuona ngati ndiwe wosafunika.”
Kususukira masitayelo kungakhale kowonongetsa ndalama. Mwachitsanzo, talingalirani sitayelo yovala timapini imene inafala pakati pa anyamata ndi atsikana Achifalansa zaka zingapo zapitazo. Malinga ndi kunena kwa nkhani ya mu 1991 ya mu The New York Times, “kuvala kapusi yanu ya baseball kapena kumamatiza timapini tambiri ta mitu yaing’ono tamaonekedwe osiyanasiyana okongola pakolala ya jekete kuli de rigueur [kofunika].” Sitayeloyo inaoneka kukhala yosatayitsa zambiri—koma munthu anafunikira kulipira ndalama zambiri zokwanira $12 pa phini iliyonse yolinganizidwa ndi wolinganiza wotchuka.
Mnyamata kapena mtsikana angapezenso kuti kukhala “shasha” kumafuna zochuluka m’malo mwa kuwononga chabe ndalama zambiri. Kwa magulu ena, amene amaona kuvala kapusi ya baseball monga fashoni, munthuwe ufunikira kusankha kapusi yamaonekedwe oyenera, oimira timu loyenera, ndipo sitayeloyo imaphatikizapo mmene munthuwe umavalira kapusiyo.
Nkhani imeneyi ili yaikulu kwa anyamata ndi atsikana ambiri. Iwo amaona kuti kutsatira masitayelo akutiakuti ndiko njira yopezera kutchuka kapena chiyanjo cha ena. Ngakhale kuti zili choncho, mudzapeza kuti si nthaŵi zonse pamene kumakhala koyenera kususukira masitayelo.
Kusamalira Mayendedwe Anu
Baibulo silimatsutsiratu masitayelo pa iwo okha. Machitachita ena ofala angakhale oyenera mosasamala kanthu ndi kukhala kwawo asitayelo. Mwachitsanzo, pamene kuthamanga kunafalikira zaka zingapo zapitazo, ena anakuona monga sitayelo wamba. Koma kodi ndani angakane kukhalapo kwa mapindu ake a kulimbitsa thupi kwachikatikati ndi koyenera?—Yerekezerani ndi 1 Timoteo 4:8.
Komabe, masitayelo ena ali opusa ndi angozi kwambiri. Chotero chenjezo la mwambi wina wakale lili loyenera: “Wachibwana akhulupirira mawu onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.” (Miyambo 14:15) Munthu wochenjera ali wanzeru ndi wozindikira. Iye samangotsatira mkhalidwe watsopano kokha chifukwa chakuti uli wofala. Mwanzeru, amapenda zotsatirapo za zimene amachita.
China cha zimene ziyenera kulingaliridwa ndicho mtengo wake. Magazini ena a ku Canada akusimba za mtsikana wina amene amagwira ntchito pa lesitilanti ya zakudya zamwamsanga. Ndalama zake zoposa theka la zimene amapeza movutikira amaziwonongera pa mafashoni atsopano a zovala. Baibulo limati, “Ndalama zichinjiriza,” kutanthauza kuti, zili chipangizo chofunika ndi chothandiza. (Mlaliki 7:12) Kodi mungafune kutayira ndalamazo pa zinthu zimene, malinga ndi kunena kwa wolemba wina, zili “zolinganizidwa kukhala zachikale panyengo imodzi kapena ziŵiri”?
Chinanso chimene chiyenera kulingaliridwa ndicho kuvulala kwa kuthupi. Si kale kwambiri pamene break dance inali yotchuka. Koma inachititsa ambiri kuvulala msana. Bwanji nanga za lerolino? Nkhani ina m’magazini a Rolling Stone imanena za mavinidwe autsiru m’makalabu ovinira ndi m’makonsati a rock, mavinidwe onga “stage-diving” (kulumpha papulatifomu kugwera m’manja mwa ochemerera), “slamming,” ndi “moshing”—“mavinidwe” amene alidi chiwawa choyendera limodzi ndi maliridwe a nyimbo. “Zimenezi zakhala zosalamulirika konse. Ndikunenetsa,” akudandaula motero mtsikana wina. Iye akufotokoza mmene ovina “moshing” otengeka maganizo “amatengera bwalo lovinira ndi kuvina mosadziletsa, akumavina mozungulirazungulira, mosasamala akumagunda aliyense wochita tsoka amene waima pafupi.” Ausinkhu wanu ena angachite chidwi ndi khalidwe limenelo. Koma kodi kukhala pamalo otero kapena kuchita zinthu zotero kungadzetse chiyanjo cha Mulungu, amene amalamula Akristu ‘kukana chisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, kukhala ndi moyo [ndi kulama maganizo, NW]’?—Tito 2:12.
Bwanji za upandu pa thanzi umene ungadzetsedwe ndi kuboola thupi ndi kusindikiza mawu kapena zithunzi pathupi—kumenenso kukufala pakati pa anyamata ndi atsikana? Madokotala akunena kuti kusindikiza mawu kapena zithunzi pathupi kungayambitse matenda, onga kutupa chiŵindi ndipo mwinamwake AIDS, ngati palibe ukhondo. Ndiponso nkotheka kuti zosindikizidwazo zingakhaliretu patapita nthaŵi yaitali kuyambira pamene sitayeloyo yachoka m’fashoni. Zoona, mawu kapena zithunzi zina zingachotsedwe ndi laser. Koma kugwiritsira ntchito laser kuli m’magawo angapo opweteka, lililonse likumawononga ndalama madola mazana ambiri.
Kuvulala kwauzimu kumene masitayelo ena amadzetsa ndiko koipa koposa zonse. Ambiri amasumika maganizo pa anthu otchuka—oseŵera, othamanga, oimba nyimbo, ndi ena otero. Munthu amakhala “shasha” ngati avala ndi kuchita mofanana ndi munthu wina wotchuka panthaŵiyo. Koma kodi Yehova Mulungu amakuona motani kulambira ngwazi koteroko? Ndiko mtundu wa kulambira mafano. Chifukwa chake Baibulo limachenjeza kuti: “Thaŵani kupembedza mafano.” (1 Akorinto 10:14) Anthu ambiri otchuka samalemekeza konse miyezo ya Baibulo ya makhalidwe. (1 Akorinto 6:9-11) Popeza kuti zili choncho, kodi nzotheka kuti Mulungu angakondwere ngati muchita kapena kuvala m’njira imene, kwenikweni, imalemekeza anthu otero?
Chithunzi Chimene Mumapereka kwa Ena
Baibulo limalamulanso anyamata ndi atsikana kulemekeza makolo awo. (Aefeso 6:2) Kodi sikungakhale kuwanyoza ngati mungafike panyumba mutavala zigwinjiri kapena mutasindikiza mawu kapena zithunzi pathupi? Bwanji nanga za ena, onga anzanu a m’kalasi? Ngati muli Mkristu, kodi zingawavute kukhulupirira zimene mumanena ngati pambuyo pake mungayese kuwauza za chikhulupiriro chanu?—Yerekezerani ndi 2 Akorinto 6:3.
Tinganene zofananazo ponena za kuvala masitayelo ena otchukitsidwa ndi oimba nyimbo za rap. Nzoona kuti m’madera ambiri kapusi ya baseball ili chongovala kumutu. Koma m’madera ena a m’tauni, “maunansi a m’chitaganya tsopano akuthandiza kwambiri kutchukitsa zipeŵa zina zake.” (Entertainment Weekly) Kodi kuvala makapusi ena, majekete, ma sneaker, kapena zovala zina za hip-hop kungakhale kukupereka chithunzi chakuti mukutsatira moyo wa rap? Kumbukirani, chikondi Chachikristu “sichichita zosayenera” kapena zonyansitsa.—1 Akorinto 13:5.
Talingalirani zimene zinachitikira kagulu kena ka atsikana m’tauni ina yosunga mwambo, amene, malinga ndi kunena kwa magazini a People, ananyalanyaza zolingalira za anthu akumaloko mwa kupita kusukulu atavala “zovala zamasitayelo a hip-hop.” Mmodzi wa atsikanawo anafotokoza kuti: “Zovalazi timaziona pa MTV [cable TV yosonyeza mavidiyo a nyimbo]. Ine ndinaziona kukhala zabwino.” Komabe, zovala zamakonozo zinabutsa mkangano—ndi kumenyana kwa mafuko.
Chifukwa chake ifeyo monga Akristu tifunikira ‘kudziveka tokha ndi manyazi ndi [kulama maganizo, NW].’ (1 Timoteo 2:9) Zimenezi zikuphatikizapo kulingalira mtima wa ena ndi maganizo awo ndi kusaumirira pa zokonda zaumwini. Ndiponso zikutanthauza kupeŵa masitayelo a zovala ndi khalidwe limene ena angaone kukhala lonkitsa.
Kufunika Kwake kwa Kusamala
Ndithudi, sitayelo iliyonse iyenera kupendedwa malinga ndi mmene ilili. Komabe, kumbukirani kuti Satana Mdyerekezi ali wolamulira wa dziko lino ndipo cholinga chake ndicho ‘kulikwira wina.’ (1 Petro 5:8; Yohane 12:31; 1 Yohane 5:19) Mosakayikira Satana wagwiritsira ntchito masitayelo ena ofala kucheutsa anyamata ndi atsikana ndi kuwachotsa kwa Mulungu. Chotero kusamala nkoyenera.
Kaŵirikaŵiri sikwanzeru kukhala pakati pa oyamba kutsatira mkhalidwe kapena sitayelo yatsopano; kuli bwinopo kukhala wosatengeka. Komabe, Baibulo limachenjezanso kuti “usapambanitse kukhala wolungama.” (Mlaliki 7:16) Ndithudi, simufunikira kukana kusintha masitayelo kwakuti muyambe kuoneka ngati wachikale kwambiri, wachilendo, kapena waubulutu.
Pamene sitayelo iwombana moonekeratu ndi malamulo a mkhalidwe a Baibulo kapena luntha, pamenepo chinthu chanzeru kuchita ndicho kuipeŵa. Zoona, nkovuta kukhala wosiyana ndi ausinkhu wanu. Koma m’buku lake lakuti How to Say No and Keep Your Friends, wolemba Sharon Scott akufunsa kuti: “Kodi muli ndi mabwenzi anzeru kwambiri amenenso amakudziŵani bwino kwambiri kwakuti iwo ayenera kumakupangirani inu zosankha? Mwachionekere ayi!” Kodi sizingakhale bwino kutsogozedwa ndi zofuna za makolo anu ndi chikumbumtima chanu chophunzitsidwa Baibulo? Mwina kuchita zimenezo sikungakupezereni chiyanjo cha ausinkhu wanu, koma kudzakupezerani chiyanjo cha Yehova chimene, mosiyana ndi sitayelo yakanthaŵi, chili chosatha!—Salmo 41:12; Miyambo 12:2.
[Chithunzi patsamba 18]
Kodi makolo anu adzamva bwanji ngati mwatengera sitayelo yakutiyakuti?