Mfumu Idetsa Malo Opatulika a Yehova
“Koma anthu akudziŵa Mulungu wawo adzalimbika mtima.”—DANIELI 11:32.
1, 2. Kodi ndimpikisano wamphamvu wotani umene wakhala m’mbiri ya anthu kwa zaka zoposa 2,000?
MAFUMU aŵiri opikisana ali munkhondo yotheratu yolimbirana ulamuliro. Yoyamba igonjetsedwa, ndiyeno inayo ikuyamba kulamulira, kwazaka zoposa zikwi ziŵiri nkhondoyo ikupitirizabe. M’tsiku lathu kulimbanako kwayambukira anthu ochuluka padziko lapansi ndipo kwayesa umphumphu wa anthu a Mulungu. Kukuthera m’chochitika chosaonedweratu ndi maulamuliro onsewo. Mbiri yosangalatsa yolembedwa pasadakhale imeneyi inavumbulidwa kwa mneneri wakale Danieli.—Danieli, machaputala 10 mpaka 12.
2 Ulosiwo ngwonena za udani wopitirizabe pakati pa mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kummwera ndipo unafotokozedwa mwatsatanetsatane m’buku lakuti “Your Will Be Done on Earth.”a M’buku limenelo munasonyezedwa kuti mfumu ya kumpoto poyambirira inali Suriya, wokhala kumpoto kwa Israyeli. Pambuyo pake, malowo anatengedwa ndi Roma. Poyamba, mfumu ya kummwera inali Igupto.
Kulimbana m’Nthaŵi za Mapeto
3. Malinga nkunena kwa mngelo, kodi ndiliti pamene ulosi wonena za mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kummwera ukazindikiridwa, ndipo motani?
3 Mngelo wovumbula zinthuzi kwa Danieli anati: “Koma iwe Danieli, tsekera mawu awa, nukhomere chizindikiro buku, mpaka nthaŵi ya [mapeto, NW]; ambiri adzathamanga chauko ndi chauko, ndi chidziŵitso chidzachuluka.” (Danieli 12:4) Inde, ulosiwo ngwonena za nthaŵi ya mapeto—nyengo imene inayamba mu 1914. Kuyambira nthaŵi yoikidwa chizindikiro imeneyo, ambiri ‘akathamanga chauko ndi chauko’ m’Malemba Opatulika, ndipo ndi chithandizo cha mzimu woyera, chidziŵitso chowona, kuphatikizapo kuzindikira ulosi wa Baibulo, zikachuluka. (Miyambo 4:18) Pamene tiloŵa mozama m’nthaŵiyo, maumboni owonjezereka a maulosi a Danieli afotokozedwa bwino. Nangano, kodi ndimotani mmene tiyenera kumvera ulosi wa mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kummwera tsopano lino mu 1993, pambuyo pa zaka 35 buku la “Your Will Be Done on Earth” litafalitsidwa?
4, 5. (a) Kodi ndipati pamene chaka cha 1914 chimapezedwa muulosi wa Danieli wonena za mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kummwera? (b) Malinga nkunena kwa mngeloyo, kodi nchiyani chikachitika mu 1914?
4 Chiyambi cha nthaŵi ya mapeto mu 1914 chinasonyezedwa ndi nkhondo yadziko yoyamba ndi masautso ena adziko amene Yesu ananeneratu. (Mateyu 24:3, 7, 8) Kodi tingapeze chaka chimenecho muulosi wa Danieli? Inde. Chiyambi cha nthaŵi ya mapeto ndicho “nthaŵi yoikika” yotchulidwa pa Danieli 11:29. (Onani “Your Will Be Done on Earth,” pamasamba 269-70.) Inali nthaŵi yoikidwiratu ndi Yehova m’tsiku la Danieli, popeza kuti inadza pamapeto a zaka 2,520 zosonyezedwa m’zochitika zatanthauzo zaulosi wa m’buku la Danieli chaputala 4.
5 Zaka 2,520 zimenezo, zoyambira pakuwonongedwa kwa Yerusalemu mu 607 B.C.E. muubwana wa Danieli kufikira 1914 C.E., zinatchedwa “nthaŵi zawo za anthu akunja.” (Luka 21:24) Kodi nzochitika zandale zotani zimene zikazindikiritsa kutha kwawo? Mngelo anavumbulira Danieli zimenezi. Mngeloyo anati: “Panthaŵi yoikika [mfumu ya kumpoto] adzabwera, nadzaloŵa kummwera; koma sikudzakhala monga nthaŵi yoyamba ija, kapena yotsirizayi.”—Danieli 11:29.
Mfumu Igonja m’Nkhondo
6. Kodi ndani amene anali mfumu ya kumpoto mu 1914, ndipo kodi ndani amene anali mfumu ya kummwera?
6 Pofika mu 1914 malo a mfumu ya kumpoto anali atatengedwa ndi Germany, amene mtsogoleri wake anali Kaiser Wilhelm. (“Kaiser,” dzina lotengedwa kudzina Lachiroma laulemu lakuti “Kaisara.”) Kubuka kwa mikangano mu Ulaya kunali mpambo winanso wa kulimbana pakati pa mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kummwera. Malo a mfumu yotsirizayo, mfumu ya kummwera, tsopano anatengedwa ndi Britain, amene analanda mofulumira Igupto, ulamuliro wa mfumu yoyamba ya kummwera. Pamene nkhondo inapitiriza, dziko limene kale linali pansi pa Britain, United States of America, linagwirizana naye. Mfumu ya kummwera inakhala ulamuliro wa dziko wa Britain ndi America, ufumu wamphamvu koposa m’mbiri.
7, 8. (a) M’nkhondo yadziko yoyamba, kodi ndimotani mmene zinthu sizinakhalire “monga nthaŵi yoyamba ija”? (b) Kodi nchiyani chimene chinali chotulukapo cha nkhondo yadziko yoyamba, koma malinga nkunena kwa ulosi, kodi ndimotani mmene mfumu ya kumpoto inachitira?
7 M’kulimbana kwa pakati pa mafumu aŵiri kwapitako, ulamuliro wa Roma, monga mfumu ya kumpoto, unali kupambana mosalekeza. Panthaŵiyi, ‘zinthu sizinakhale monga nthaŵi yoyamba ija.’ Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti mfumu ya kumpoto inagonja m’nkhondo. Chifukwa chimodzi chinali chakuti “zombo za ku Kitimu” zinayambana ndi mfumu ya kumpoto. (Danieli 11:30) Kodi zombo zimenezi zinali chiyani? M’nthaŵi ya Danieli, Kitimu anali Kupro (Cyprus), ndipo kuchiyambiyambi kwa nkhondo yadziko yoyamba, Kupro anatengedwa ndi Britain. Ndiponso, malinga nkunena kwa The Zondervan Pictorial Encyclopedia of the Bible, dzina lakuti Kitimu “limaphatikizapo K[umadzulo] konse, koma m[akamaka] K[umadzulo] kwa maulendo a panyanja.” New International Version imamasulira mawu akuti “zombo za ku Kitimu” kukhala “zombo za maiko a kugombe la kumadzulo.” M’nkhondo yadziko yoyamba, zombo za Kitimu zinakhaladi zombo za Britain, zikumakhala kugombe la kumadzulo kwa Ulaya. Pambuyo pake Gulu Lankhondo la Pamadzi la Britain linachilikizidwa ndi zombo zochokera kudziko la kumadzulo la North America.
8 M’kuukiridwa kumeneku, mfumu ya kumpoto ‘inaipidwa mtima’ nivomereza kugonja kwake mu 1918. Komatu sinagonje kotheratu. “Nadzabwerera, nadzaipidwa mtima ndi chipangano chopatulika, nadzachita chifuniro chake [“mwamphamvu,” NW]; adzabweranso, nadzasamalira otaya chipangano chopatulika.” (Danieli 11:30) Mngeloyo analosera motero, ndipo zinaterodi.
Mfumuyo Ichita Mwamphamvu
9. Kodi nchiyani chimene chinachititsa Adolf Hitler kutenga mphamvu, ndipo ndimotani mmene iye ‘anachitira mwamphamvu’?
9 Nkhondo itatha, mu 1918, maiko Ogwirizana m’Nkhondo olakika anachita pangano lolanga Germany mwamtendere, mwachionekere lolinganizidwira kumana anthu a ku Germany pafupifupi chakudya chonse kunthaŵi yosadziŵika bwino. Monga chotulukapo chake, atadzandiradzandira kwazaka zingapo ndi mavuto aakuluwo, Germany anali wokonzeka kuukanso motsogozedwa ndi Adolf Hitler. Iye anapeza mphamvu yaikulu mu 1933 ndipo nthaŵi yomweyo anaukira mwankhanza “chipangano chopatulika,” choimiridwa ndi abale odzozedwa a Yesu Kristu. M’zimenezi iye anachita mwamphamvu polimbana ndi Akristu okhulupirika ameneŵa, akumazunza mwankhanza ambiri a iwo.
10. Pofunafuna chichilikizo, kodi Hitler anagwirizana ndi yani, ndipo ndi zotulukapo zotani?
10 Hitler anakhala ndi chipambano m’zachuma ndi kugwirizana ndi maiko ena, akumachita mbali imeneyonso mwamphamvu. M’zaka zoŵerengeka, anachititsa Germany kukhala dziko lodaliridwa ndi maiko ena, akumathandizidwa m’kuyesayesa kumeneku ndi “otaya chipangano chopatulika.” Kodi iwo anali ayani? Mwachionekere, atsogoleri a Dziko Lachikristu, amene ananena kuti anali muunansi wa chipangano ndi Mulungu koma anali ataleka kalekale kukhala ophunzira a Yesu Kristu. Mwachipambano, Hitler anapempha “otaya chipangano chopatulika” amenewo kumchilikiza. Papa ku Roma anachita naye pangano, ndipo Tchalitchi cha Roma Katolika, ndiponso matchalitchi a Protesitanti mu Germany, anachilikiza Hitler m’zaka zonse 12 za ulamuliro wake wankhalwe.
11. Kodi ndimotani mmene mfumu ya kumpoto ‘inadetsera malo opatulika’ ndi ‘kuchotsa nsembe yosalekezayo’?
11 Hitler anapambanadi kwakuti anamenya nkhondoyo, monga momwedi mngeloyo anali ataneneratu molondola. “Ndipo ankhondo adzamuimirira, nadzadetsa malo opatulika ndi linga lake; nadzachotsa nsembe yosalekezayo.” (Danieli 11:31a) Mu Israyeli wakale, malo opatulika anali mbali ya kachisi mu Yerusalemu. Komabe, pamene Ayuda anakana Yesu, Yehova anakana iwo ndi kachisi wawo. (Mateyu 23:37–24:2) Chiyambire zaka za zana loyamba, kachisi wa Yehova kwenikweni wakhala wauzimu, limodzi ndi malo ake opatulikitsa kumwamba ndi bwalo la kachisi lauzimu padziko lapansi mu limene abale odzozedwa a Yesu, Mkulu wa Ansembe, amatumikiramo. Kuyambira m’ma 1930, khamu lalikulu lalambira mogwirizana ndi otsalira odzozedwa; chifukwa chake, likunenedwa kuti likutumikira ‘m’kachisi wa Mulungu.’ (Chivumbulutso 7:9, 15; 11:1, 2; Ahebri 9:11, 12, 24) Bwalo la kachisi la padziko lapansi linadetsedwa ndi chizunzo chosalekeza pa otsalira odzozedwa ndi mabwenzi awo m’maiko amene mfumu ya kumpoto inalamulira. Chizunzocho chinali chachikuludi kwakuti nsembe yosalekezayo—nsembe yapoyera ya chitamando cha dzina la Yehova—inachotsedwa. (Ahebri 13:15) Komabe, mbiri imasonyeza kuti mosasamala kanthu za kuchitiridwa nkhanzako, Akristu odzozedwa okhulupirika, limodzi ndi “nkhosa zina,” anapitirizabe kulalikira mobisa.—Yohane 10:16.
“Chonyansa”
12, 13. Kodi nchiyani chimene chinali “chonyansa,” ndipo—monga momwe chinaonedweratu ndi kapolo wokhulupirika ndi wanzeru—kodi ndiliti ndiponso ndimotani mmene chinayambiranso kukhalako?
12 Pamene mapeto a nkhondo yadziko yachiŵiri anali kuyandikira, panali chochitika china. “Nadzaimitsa chonyansa chopululutsacho.” (Danieli 11:31b) “Chonyansa” chimenechi, chimene Yesu anatchulanso, chinali chitazindikiridwa kale kukhala Chigwirizano cha Mitundu, chilombo chofiiritsa chimene malinga nkunena kwa buku la Chivumbulutso, chinaloŵa m’phompho. (Mateyu 24:15; Chivumbulutso 17:8; onani Light, Buku Lachiŵiri, patsamba 94.) Zimenezi zinachitika pamene Nkhondo Yadziko II inaulika. Komabe, pa Msonkhano wa Mboni za Yehova wa Teokratiki ya Dziko Latsopano mu 1942, Nathan H. Knorr, prezidenti wachitatu wa Watch Tower Bible and Tract Society, anafotokoza ulosi wa pa Chivumbulutso 17 ndi kuchenjeza kuti chilombocho chikatulukanso m’phomphomo.
13 Mbiri inachitira umboni za kuwona kwa mawu ake. Pakati pa August ndi October 1944, ku Dumbarton Oaks mu United States, ntchito yolinganiza tchata cha gulu limene likatchedwa Mitundu Yogwirizana inayamba. Tchatacho chinalandiridwa ndi mitundu 51, kuphatikizapo yemwe kale anali Soviet Union, ndipo pamene linatenga mphamvu pa October 24, 1945, gulu la Chigwirizano cha Mitundu limene linali losagwira ntchitolo linatulukadi m’phompho.
14. Kodi ndiliti ndipo ndimotani mmene kudziŵika kwa mfumu ya kumpoto kunasinthira?
14 Germany anali atakhala mdani wamkulu wa mfumu ya kummwera m’nkhondo zonse ziŵiri zadziko. Pambuyo pa Nkhondo Yadziko II, mbali ina ya Germany inadzilinganiza ndi kugwirizana ndi mfumu ya kummwera. Koma mbali ina ya Germany inagwirizana ndi ulamuliro wina wamphamvu. Mgwirizano wa maiko a Chikomyunizimu, umene tsopano unaphatikizapo mbali inayo ya Germany, unatsutsa mwamphamvu mgwirizano wa Britain ndi America, ndipo mpikisano wa pakati pa mafumu aŵiriwo unakhala Nkhondo Yapakamwa.—Onani “Your Will Be Done on Earth,” patsamba 264-84.
Mfumu ndi Chipangano
15. Kodi ndayani amene “akuchitira choipa chipangano,” ndipo ndiunansi wotani umene akhala nawo ndi mfumu ya kumpoto?
15 Mngeloyo tsopano akuti: “Akuchitira choipa chipanganocho iye [adzawatsogolera kuloŵa mumpatuko mwanjira ya mawu osyasyalika, NW].” (Danieli 11:32a) Kodi ochitira choipa chipanganowo ndiwo ayani? Kachiŵirinso, iwo ndiwo atsogoleri a Dziko Lachikristu okha, amene amadzinenera kukhala Akristu koma mwa ntchito zawo amadetsa dzina lenilenilo la Chikristu. Mkati mwa nkhondo yadziko yachiŵiri, “Boma la Soviet [Union] linayesayesa kupeza chithandizo chakuthupi ndi cha malingaliro cha Matchalitchi kaamba ka chitetezo cha dziko lawo lobadwira.” (Religion in the Soviet Union, lolembedwa ndi Walter Kolarz) Pambuyo pankhondoyo, atsogoleri atchalitchi anayesayesa kuchititsa ubwenziwo kukhalapobe mosasamala kanthu za mchitidwe wa kusakhulupirira kukhalapo kwa Mulungu wa ulamulirowo umene tsopano unali mfumu ya kumpoto.b Motero, Dziko Lachikristu linakhaladi mbali yadziko koposa ndi kale lonse—mpatuko wonyansa m’maso mwa Yehova.—Yohane 17:14; Yakobo 4:4.
16, 17. Kodi ndayani amene ali “awo okhala ndi chidziŵitso,” ndipo kodi zinthu zawayendera motani muulamuliro wa mfumu ya kumpoto?
16 Komabe, bwanji ponena za Akristu owona? “Koma anthu akudziŵa Mulungu wawo adzalimbika mtima, nadzachita mwamphamvu. Ndipo [awo okhala ndi chidziŵitso pakati pa anthu, NW] adzalangiza ambiri, koma adzagwa ndi lupanga, ndi laŵi lamoto, ndi undende, ndi kufunkhidwa masiku ambiri.” (Danieli 11:32b, 33) Akristu okhala muulamuliro wa mfumu ya kumpoto, pamene kuli kwakuti ‘anamvera maulamuliro aakulu,’ sanakhale mbali ya dzikoli. (Aroma 13:1; Yohane 18:36) Posamala kupereka zinthu za Kaisara kwa Kaisara, iwo anapatsanso “Mulungu zake za Mulungu.” (Mateyu 22:21) Chifukwa cha zimenezi, umphumphu wawo unayesedwa.—2 Timoteo 3:12.
17 Chotulukapo chake? ‘Analimbika mtima’ ndi ‘kugwa’ komwe. Anagwa pakuti anazunzidwa ndi kuvutika kwambiri, ena akumaphedwadi. Koma analimbika mtima pakuti, kwakukulukulu, anakhalabe okhulupirika. Inde, analaka dziko, monga momwedi Yesu analakira dziko. (Yohane 16:33) Ndiponso, sanaleke kulalikira, ngakhale pamene anali m’ndende kapena mumsasa wachibalo. Mwakutero, ‘analangiza ambiri.’ Mosasamala kanthu za chizunzo, m’maiko ochuluka olamulidwa ndi mfumu ya kumpoto, ziŵerengero za Mboni za Yehova zinawonjezereka. Chifukwa cha kukhulupirika kwa “awo okhala ndi chidziŵitso,” mbali yomafutukuka mosalekeza ya “khamu lalikulu” yaonekera m’maiko amenewo.—Chivumbulutso 7:9-14.
18. Kodi ‘ndithandizo laling’ono’ lotani limene lalandiridwa ndi otsalira odzozedwa okhala muulamuliro wa mfumu ya kumpoto?
18 Ponena za chizunzo cha anthu a Mulungu, mngeloyo ananeneratu kuti: “Ndipo pakugwa iwo adzathandizidwa ndi thandizo laling’ono.” (Danieli 11:34a) Kodi zimenezi zinachitika motani? Choyamba, chipambano cha mfumu ya kummwera m’nkhondo yadziko yachiŵiri chinabweretsa mpumulo waukulu kwa Akristu okhala muulamuliro wa mfumu ya kumpoto. (Yerekezerani ndi Chivumbulutso 12:15, 16.) Ndiyeno, awo amene anazunzidwa ndi mfumu yotsatira ya kumpoto anali kupeza mpumulo kwanthaŵi ndi nthaŵi, ndipo pamene Nkhondo Yapakamwa inali kutha, atsogoleri ambiri anafikira pakuzindikira kuti Akristu okhulupirika sali chiwopsezo ndipo motero anawaloleza kuchita ntchito yawo mwalamulo.c Ndiponso, chithandizo chachikulu chadza m’ziŵerengero zowonjezereka za khamu lalikulu, limene lalabadira ulaliki wa odzozedwa okhulupirika ndipo lawathandiza, monga momwe zafotokozedwera pa Mateyu 25:34-40.
Kuyeretsedwa kwa Anthu a Mulungu
19. (a) Kodi ena ‘anaphatikizana nawo [motani] ndi mawu osyasyalika’? (b) Kodi nchiyani chimene chikutanthauzidwa ndi mawu akuti “mpaka nthaŵi ya mapeto”? (Onani mawu amtsinde.)
19 Sionse amene anasonyeza chikondwerero m’kutumikira Mulungu m’nthaŵi imeneyo anali ndi zolinga zabwino. Mngeloyo anachenjeza kuti: “Ambiri adzaphatikizana nawo ndi mawu osyasyalika. [Ndipo ena a awo okhala ndi chidziŵitso adzagwa ndi, NW] kuwayesa ndi moto, ndi kuwatsutsa, ndi kuwayeretsa, mpaka nthaŵi ya [mapeto, NW]; pakuti kukaliko kufikira nthaŵi yoikika.”d (Danieli 11:34b, 35) Ena anasonyeza chikondwerero m’chowonadi koma sanali ofunitsitsa kupanga kudzipatulira kowona kuti atumikire Mulungu. Ena amene anaonekera kukhala akulandira mbiri yabwino kwenikweni anali azondi a boma. Lipoti lochokera kudziko lina limati: “Ena a anthu onyenga ameneŵa anali ochilikiza Chikomyunizimu enieni amene anakwawira m’gulu la Ambuye, nasonyeza changu chachikulu koposa, ndipo ngakhale kuikidwa m’malo autumiki athayo.”
20. Kodi nchifukwa ninji Yehova analola Akristu ena okhulupirika ‘kugwa’ chifukwa cha anthu ozembera m’gulu onyenga?
20 Anthu ozembera m’guluwo anapereka okhulupirika ena m’manja mwa maboma. Kodi nchifukwa ninji Yehova analola zinthu zotero kuchitika? Kaamba ka kuyenga, kuyeretsa. Monga momwe Yesu ‘anaphunzirira kumvera ndi zimene adamva kuwawa nazo,’ chotero miyoyo yokhulupirika imeneyi inaphunzira kupirira chiyeso cha chikhulupiriro chawo. (Ahebri 5:8; Yakobo 1:2, 3; yerekezerani ndi Malaki 3:3.) Motero iwo ‘ayesedwa ndi moto, atsukidwa, ndi kuyeretsedwa.’ Okhulupirikawo akuyembekezera kudzasangalala pamene nthaŵi yoikidwiratu ifika kuti chipiriro chawo chifupidwe. Zimenezi zidzaonedwa pamene tifotokoza zowonjezereka ponena za ulosi wa Danieli.
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., ndipo lotulutsidwa m’Chingelezi mu 1958 pa Msonkhano wa Mitundu Yonse wa Mboni za Yehova wakuti “Chifuniro Chaumulungu.”
b Magazini a World Press Review a November 1992 anali ndi nkhani yochokera mu The Toronto Star imene inati: “M’zaka zingapo zapitazo, nzika za ku Russia zapenyereradi kuwonongeka kwa malingaliro onyenga amphamvu a mbiri ya dziko lawo. Koma kutulukiridwa kwa mgwirizano wa tchalitchi ndi boma la chikomyunizimu kwapereka nkhonya yowononga koposa.”
d Mawu akuti “mpaka nthaŵi ya mapeto” angatanthauze “m’nthaŵi ya chitsiriziro.” Liwu lotembenuzidwa pano kuti “mpaka” limaonekera m’malembo Achiaramu pa Danieli 7:25 ndipo pamenepo limatanthauza kuti “m’nthaŵi” kapena “kwa.” Liwulo lili ndi tanthauzo lofananalo m’malembo Achihebri pa 2 Mafumu 9:22, Yobu 20:5, ndi Oweruza 3:26. Komabe, m’matembenuzidwe ochuluka a Danieli 11:35, limamasuliridwa kuti “mpaka,” ndipo ngati liwuli lili lolondola, pamenepo “nthaŵi ya mapeto” yotchulidwa pano iyenera kukhala nthaŵi ya mapeto a chipiriro cha anthu a Mulungu.—Yerekezerani ndi “Your Will Be Done on Earth,” patsamba 286.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi nchifukwa ninji ife lerolino tiyenera kuyembekezera kukhala ndi tanthauzo lomvekera bwino la ulosi wa Danieli?
◻ Kodi ndimotani mmene mfumu ya kumpoto ‘inaipidwira mtima ndi chipangano chopatulika ndi kuchita mwamphamvu’?
◻ Kodi kuonekeranso kwa “chonyansa” kowonedweratu ndi kagulu ka kapolo kunali kotani?
◻ Kodi ndimotani mmene otsalira odzozedwa ‘anagwera, kulimbika mtima, ndi kulandira thandizo laling’ono’?
[Chithunzi patsamba 15]
Pansi pa Hitler, mfumu ya kumpoto inapezanso nyonga yokwana kuchokera pakugonjetsedwa kwake mu 1918 ndi mfumu ya kummwera
[Chithunzi patsamba 16]
Atsogoleri a Dziko Lachikristu anayesayesa kukulitsa unansi ndi mfumu ya kumpoto
[Mawu a Chithunzi]
Zoran/Sipa Press