Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Tinasangalala kuphunzira za maulosi a Danieli monga momwe alongosoledwera mu “Nsanja ya Olonda.” Komabe, kodi nchifukwa ninji madeti a nthaŵi zitatu ndi nusu za Chivumbulutso 11:3 akusiyana ndi a m’buku la “Revelation Climax”?
Inde, Nsanja ya Olonda ya November 1, 1993, inapereka masinthidwe pang’ono ponena za madeti a kukwaniritsidwa kwamakono kwa Chivumbulutso 11:3. Chifukwa ninji?
Choyamba tiyeni tione pa Chivumbulutso 11:2, pamene mapeto ake amatchula za “miyezi makumi anayi mphambu iŵiri.” Timapitiriza mu vesi 3 kuti: “Ndidzalamulira mboni zanga ziŵiri, ndipo zidzanenera masiku chikwi chimodzi ndi mazana aŵiri mphambu makumi asanu ndi limodzi, zovala chiguduli.” Kodi zimenezo zimagwira ntchito liti?
Chabwino, Mboni za Yehova kwanthaŵi yaitali zazindikira kuti ulosi umenewu unakwaniritsidwa ndi Akristu odzozedwa ndi mzimu pambuyo pa kutha kwa “nthaŵi zoikidwiratu za amitundu” (Nthaŵi za Akunja) mu 1914. (Luka 21:24, NW; 2 Akorinto 1:21, 22) Poperekera ndemanga nkhaniyi, buku la Revelation—Its Grand Climax At Hand!a (1988) limati pa tsamba 164: “Panali nyengo yodziŵika ya zaka zitatu ndi nusu pamene zokumana nazo zovuta za anthu a Mulungu zinagwirizana ndi zochitika zoloseredwa pano—kuyambira pa kuulika kwa nkhondo ya dziko yoyamba kumapeto kwa 1914 kupitirira kufikira kumayambiriro kwa 1918.”
Onani kuti madeti operekedwawo anali “pa kuulika kwa nkhondo ya dziko yoyamba kumapeto kwa 1914 [mpaka] kumayambiriro kwa 1918.” Zimenezi zimagwirizana bwino ndi madeti operekedwa kaŵirikaŵiri, monga ngati mu “Then Is Finished the Mystery of God,” masamba 261-4, (1969).b
Komabe, Nsanja ya Olonda inasumika chisamaliro pa maulosi a m’Danieli, buku limene limatchula kaŵiri nyengo zofanana ndi zija zotchulidwa pambuyo pake m’Chivumbulutso—zaka 3 1/2, kapena miyezi 42. Kunena molondola, Danieli 7:25 amanena kuti opatulika a Mulungu akasautsidwa “nthaŵi imodzi ndi nthaŵi zina, ndi nthaŵi yanusu,” kapena nthaŵi 3 1/2. Pambuyo pake, Danieli 12:7 amaneneratu za “nthaŵi, ndi nthaŵi zina, ndi nusu,” kapena nthaŵi 3 1/2, zimene zikachititsa “kumwaza mphamvu ya anthu opatulikawo.”
Chotero tili ndi maulosi onena za nyengo zofanana za pa Danieli 7:25, Danieli 12:7 ndi Chivumbulutso 11:2, 3, ndiponso pa Chivumbulutso 13:5. Zofalitsidwa zathu zasonyeza kuti onsewa anakwaniritsidwa m’nyengo ya 1914-18. Koma polongosola uliwonse wa ulosi umenewu pawokha, madeti a kuyambika ndi mapeto ake anasiyana pang’ono.
Komabe, Nsanja ya Olonda ya November 1, 1993, inafunsa kuti: “Kodi maulosi oyendera limodzi ameneŵa anakwaniritsidwa motani?” Inde, maulosi a nthaŵi 3 1/2 a pa Danieli 7:25, Danieli 12:7, ndi Chivumbulutso 11:3 anazindikiridwa kukhala “maulosi oyendera limodzi.” Chifukwa chake, ayenera kugwirizana ponena za chiyambi ndi mapeto awo.
Ponena za mapeto ake, magaziniwo anasonyeza mmene nsautso ya odzozedwa a Mulungu (Danieli 7:25) inafikira pachimake mu June 1918 pamene J. F. Rutherford ndi akuluakulu ena a Watch Tower Bible and Tract Society “anapatsidwa chilango cha kukhala m’ndende kwa nthaŵi yaitali pazinenezo zonama.” Chochitikacho chinalidi cha “kumwaza mphamvu ya anthu opatulikawo,” monga momwe kwasonyezedwera pa Danieli 12:7.
Kuŵerenga chifuta mbuyo kuyambira June 1918 kumatifikitsa ku December 1914 kukhala chiyambi cha nthaŵi 3 1/2. M’mwezi wotsiriza umenewo wa 1914, odzozedwa a Mulungu padziko lapansi anaphunzira lemba la chaka china chomadzacho lakuti: “‘Kodi mukhoza kumwa chikho Changa?’—Mateyu 20:20-23.” Nkhani yake yolilengeza inachenjeza kuti: “Kodi ndani adziŵa kuti pangakhale chiyeso chapadera, chikho cha kuvutika kapena kunyazitsidwa, kwa otsatira okhulupirika a Mwanawankhosa mkati mwa 1915!” Monga momwe Danieli 7:25 ananeneratu za nyengo imeneyi ya nthaŵi 3 1/2, ‘kulemetsa opatulika a Wam’mwambamwamba kunapitiriza.’ Mitundu inali kumenya Nkhondo Yadziko I, imene inawapeputsira zinthu kuti apereke nsautso yosayenera. Mapeto ake n’ngakuti: Maulosi onse oyendera limodzi atatuwo—Danieli 7:25, 12:7, ndi Chivumbulutso 11:3—anakwaniritsidwa m’zaka 3 1/2, kapena miyezi 42, kuyambira December 1914 kufikira June 1918.
Zimenezi zikufotokoza kuwongolera kwakung’ono m’madeti a kukwaniritsidwa kwa Chivumbulutso 11:3. Kuwongolera kumeneku kuli kanthu kena kamene tingakumbukire pamene tiphunzira ndi kugwiritsira ntchito buku la Revelation Climax mtsogolomu.
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
b Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.