Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 12/1 tsamba 23-26
  • Okonzekera Kuyamba Ntchito Yaikulu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Okonzekera Kuyamba Ntchito Yaikulu
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Uphungu Womaliza wa Aphunzitsi
  • Amishonale Akalekale Achimwemwe
  • Kuchoka pa Ophunzira Okhoza Bwino Kukhala Amishonale Okhoza Bwino
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Kufunitsitsa ndi Mtima Wonse Kumachititsa Anthu Kupita ku Sukulu ya Gileadi
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Amishonale Owonjezereka Kaamba ka Kututa Kwapadziko Lonse
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Madalitso a Maphunziro a Gileadi Afalikira Padziko Lonse
    Nsanja ya Olonda—1992
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 12/1 tsamba 23-26

Okonzekera Kuyamba Ntchito Yaikulu

“MUNALIBE kupikisana. Aliyense ankafuna kuti aliyense achite bwino,” anatero Richard ndi Lusia, posimba za ophunzira anzawo a m’kalasi ya 105 ya Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower. “Tonsefe ndife osiyana kwambiri, koma kwa ife, wophunzira aliyense ngwofunika kwambiri.” Mnzawo wa m’kalasi, Lowell, anavomereza, nawonjezera kuti: “Kusiyana kwathuko kwatipangitsa kukhala mabwenzi.”

Kalasilo, limene linamaliza maphunziro ake pa September 12, 1998, linalidi ndi anthu osiyanasiyana. Ophunzira ena anali atachita upainiya kumadera kumene kukufunikira ofalitsa Ufumu ambiri; ena anatumikira kwawo mokhulupirika. Angapo, monga Mats ndi Rose-Marie anayenera kulimbikira zedi kuti aphunzire kulankhula bwino Chingelezi asanabwere kusukulu. Ophunzira ambiri anayamba kuganiza za utumiki waumishonale adakali ana aang’ono. Mwamuna wina ndi mkazi wake anafunsira kuloŵa sukuluyo nthaŵi 12; iwo anakondwera kwambiri kuitanidwa ku kalasi ya nambala 105!

Milungu 20 ya maphunziro othinana inangodeluka. Mwadzidzidzi, ophunzira anangopeza kuti alemba kale mayeso awo omaliza, ndipo apereka kale lipoti lawo lomaliza loŵerenga ndipo linali tsiku lokondwerera kumaliza maphunziro.

Tcheyamani wa pologalamu imeneyo, Albert Schroeder, wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, anakumbutsa a m’kalasilo kuti anali okonzekera “kuyamba ntchito yaikulu yophunzitsa Baibulo,” kutsatira enanso oposa 7,000 amene analoŵa kale Gileadi. Anatchula kuti m’chilimwecho, ophunzirawo anali ndi mwayi wapadera woonana ndi amishonale akalekale amene anachezera likulu ladziko lonse panthaŵi ya misonkhano ya mitundu yonse.

Kenako Mbale Schroeder anaitana Max Larson wa mu Bethel Operations Committee (Komiti Yoyang’anira Beteli). Iye anakamba nkhani yakuti “Maphunziro Amene Amatsogolera ku Moyo Wosatha.” Mbale Larson anagwira mawu Miyambo 1:5, yomwe imati: “Kuti wanzeru amve, nawonjezere kuphunzira; ndi kuti wozindikira afikire kuuphungu.” Pafunikira kuzindikira bwino kuti munthu akhale mmishonale wabwino. Anthu ochita ntchito yawo mwaluso amaima pamaso pa mafumu. (Miyambo 22:29) Atalangizidwa kwa miyezi isanu, ophunzirawo anali okonzekera bwino kuimira Mafumu aŵiri aakulu koposa, Yehova Mulungu ndi Kristu Yesu.

Kenako, David Olson wa mu Service Department (Dipatimenti Yoyang’anira Utumiki) anakamba nkhani yamutu wakuti “Thandizani Kukondweretsa Mtima wa Yehova.” Anafunsa kuti: “Kodi anthu opanda ungwiro ayenera kuchitanji kuti akondweretse mtima wa Mulungu?” Yankho lake? Ayenera kumtumikira mokhulupirika ndiponso mwachimwemwe. Yehova amafuna kuti anthu ake azikondwera pomtumikira. Tikamachita chifuniro cha Mulungu mwachimwemwe, timakondweretsa mtima wake. (Miyambo 27:11) Mbale Olson anaŵerenga kalata imene linalemba banja lina omwe ndi amishonale omwe anamaliza maphunziro m’kalasi ya nambala 104 ya Gileadi. Kodi iwo akusangalala kugawo lawo latsopano? “Tili ndi ofalitsa ngati 140,” iwo analemba motero ponena za mpingo wawo, “ndipo pamisonkhano pamapezeka avareji ya anthu 250 mpaka 300. Utumiki wakumunda ndiyo mbali yosangalatsa kwambiri. Tonse aŵirife tili ndi maphunziro anayi aliyense, ndipo ena ayamba kale kufika pamisonkhano.”

Lyman Swingle, wa m’Bungwe Lolamulira, analankhula pamutu wakuti “Nthaŵi Yosinkhasinkha ndi Kuŵerenga Madalitso Anu.” Maphunziro a Gileadi anadzetsa madalitso ambiri. Anathandiza ophunzirawo kuwonjezera chidziŵitso chawo, kulidziŵa bwino kwambiri gulu la Yehova, ndi kukulitsa mikhalidwe yofunika kwambiri, monga kudzichepetsa. “Kubwera kuno ndi kukhala pansi kumamvetsera malangizo kumapangitsa munthu kukhala wodzichepetsa,” anatero Mbale Swingle, nawonjezera kuti: “Mukuchoka kuno muli wokonzekera bwino kwambiri kulemekeza Yehova.”

“Muli ndi Chimwemwe Chachikulu Kwambiri​—Choncho Nkuderanji Nkhaŵa?” ndiwo unali mutu wa nkhani ya Daniel Sydlik, nayenso wa m’Bungwe Lolamulira. Pakabuka mavuto, funafunani chitsogozo m’Malemba, anawalimbikitsa motero. Pogwiritsa ntchito mavesi ena ndi ena a mu chaputala chachisanu ndi chimodzi cha Mateyu, Mbale Sydlik anasonyeza mmene iwo angachitire zimenezi. Kusoŵa chikhulupiriro kungatipangitse kumada nkhaŵa ndi zinthu zakuthupi, monga chakudya ndi zovala. Komabe, Yehova amadziŵa zimene tikufunikira. (Mateyu 6:25, 30) Nkhaŵa idzangowonjeza mavuto a tsiku ndi tsiku. (Mateyu 6:34) Komanso, kukonzekera nkofunika. (Yerekezerani ndi Luka 14:28.) “Zimene Yesu akuletsa si kuganiza mwanzeru za m’tsogolo, koma kudera nkhaŵa mopanda nzeru za m’tsogolo,” anatero Mbale Sydlik pofotokoza. “Kuchitapo kanthu ndiko chimodzi mwa zinthu zimene zimathetsa nkhaŵa msanga. Tikayamba kuda nkhaŵa, kuli bwino kuti tiziyamba kulankhula za choonadi.”

Uphungu Womaliza wa Aphunzitsi

Panatsatira nkhani za aphunzitsi atatu a Gileadi. Karl Adams ndiye anayamba kulankhula, pamutu wakuti “Kodi Mudzambwezeranji Yehova?” Nkhani yake inazikidwa pa Salmo la 116, limene Yesu ayenera kuti anaimba usiku woti akufa maŵa. (Mateyu 26:30, NW, mawu amtsinde) Kodi Yesu anali kuganizanji pamene anali kuimba mawu akuti: “Ndidzabwezera Yehova chiyani chifukwa cha zokoma zake zonse anandichitira”? (Salmo 116:12) Mwina anali kuganiza za thupi langwiro limene Yehova anamkonzera. (Ahebri 10:5) Tsiku lotsatira, anali kudzapereka thupi limenelo monga nsembe, kupereka umboni wa chikondi chake chachikulu. Ophunzira a m’kalasi ya nambala 105 analaŵa ubwino wa Yehova pamiyezi isanu yapitayo. Tsopano ayenera kusonyeza chikondi chawo pa Mulungu mwa kugwira ntchito molimbikira m’magawo awo aumishonale.

Mark Noumair, mphunzitsi wa Gileadi wachiŵiri kukamba nkhani, analangiza ophunzirawo kuti ‘Apitirize Kuchita Zoyenera.’ Yosefe, atagulitsidwa monga kapolo ku Igupto, anapirira zaka 13 akusautsidwa popanda chifukwa. Kodi iye analola zolakwa za ena kumfooketsa? Iyayi, iye anapitirizabe kuchita zoyenera. Kenako, panthaŵi yoikidwiratu ya Mulungu, Yosefe analanditsidwa m’mayesero ake. Mosayembekezereka, anachoka m’ndende nakakhala m’nyumba ya mfumu. (Genesis, machaputala 37-50) Mphunzitsiyo anafunsa ophunzira ake kuti: “Ngati zinthu sizichitika monga momwe munkayembekezera m’gawo lanu laumishonale, kodi mudzasiya? Kodi mudzataya mtima? Kapena kodi mudzapirira, monga anachitira Yosefe?”

Pomalizira pake, wosunga kaundula wa Sukulu ya Gileadi, Wallace Liverance, anachititsa makambitsirano osangalatsa kwambiri ndi a m’kalasilo pamutu wakuti “Lengezani Mfumu ndi Ufumuwo.” Ophunzira ena anasimba zimene anakumana nazo polalikira kunyumba ndi nyumba, kusitolo ndi sitolo, ndi m’misewu. Ena anasimba zimene anachita kuti achitire umboni kwa anthu olankhula chinenero china. Enanso anasonyeza njira yolalikira kwa anthu a zipembedzo zina. Omaliza maphunziro onsewo anali ofunitsitsa kuchita zambiri mu utumiki m’munda waumishonale.

Amishonale Akalekale Achimwemwe

Mbali yotsatira, yamutu wakuti “Zotsatirapo Zosangalatsa za Utumiki Waumishonale,” inakambidwa ndi Robert Wallen ndipo panali kufunsa abale anayi a palikulu amene posachedwapo anali ndi macheza olimbikitsa ndi amishonale ozoloŵera. Amishonalewo anavomerezadi kuti kuphunzira chinenero chatsopano, kutsatira chikhalidwe china, kapena kuzoloŵera nyengo zosiyana kunali kovuta. Ndiyeno anafunikiranso kupirira kupukwa kwawo. Nthaŵi zina panali matenda. Koma amishonalewo anakhalabe ndi chiyembekezo chabwino pazovuta zonsezo, ndipo anadalitsidwa chifukwa cha kulimbikira kwawo. Ena anathandiza anthu ambirimbiri kukhala ndi chidziŵitso chonena za Yehova. Ena anathandizira m’njira zosiyanasiyana kuti ntchito ya Ufumu iwonjezeke m’maiko awo.

Womalizira kukamba nkhani anali Carey Barber, wa m’Bungwe Lolamulira. Iye anapenda mfundo zazikulu za pologalamu ya msonkhano wachigawo wa “Njira ya Moyo ya Mulungu.” “Kodi pologalamu ya msonkhano wachigawo inaukhudza motani unansi wanu ndi Yehova?” anafunsa omvera ake. Wokamba nkhaniyo anasonyeza kusiyana pakati pa madalitso a kutsatira njira ya Mulungu ndi zotsatirapo zoopsa za aja amene akutsatira njira ya dziko. Ponena za tchimo la Mose pa Meriba, iye anachenjeza kuti: “Ngakhale kuti munthu watumikira mokhulupirika zaka zambirimbiri, Yehova sanyalanyazabe kuswa malamulo Ake olungama ngakhale pang’ono.” (Numeri 20:2-13) Atumiki a Mulungu kulikonse agwiritsitsetu mwayi wawo wamtengo wapatali wa utumiki!

Tsopano inali nthaŵi yoti ophunzirawo alandire madipoloma awo. Kenako, woimira kalasilo anaŵerenga kalata yoyamikira maphunziro amene ophunzirawo analandira. Pambuyo pa nyimbo ndi pemphero lomaliza lokhudza mtima, pologalamu yokondwerera kumaliza maphunziro inatha. Koma, kwa a m’kalasi la nambala 105, chimenechi chinali chiyambi, popeza kuti amishonale amenewo atsopano anali “okonzekera kuyamba ntchito yaikulu.”

[Bokosi patsamba 23]

Ziŵerengero za Kalasi

Chiŵerengero cha maiko kumene anachokera: 9

Chiŵerengero cha maiko kumene anatumizidwa: 17

Chiŵerengero cha ophunzira: 48

Chiŵerengero cha mabanja: 24

Avareji ya zaka zakubadwa: 33

Avareji ya zaka m’choonadi: 16

Avareji ya zaka mu utumiki wa nthaŵi zonse: 12

[Bokosi patsamba 24]

Anasankha Utumiki wa Nthaŵi Zonse

“Pamene ndinali wamng’ono, sindinali kuganiza zochita upainiya,” anatero Ben, womaliza maphunziro m’kalasi ya nambala 105. “Ndinali kuganiza kuti amene amachita upainiya ndi anthu a maluso apadera ndiponso amene ali mumkhalidwe wabwino,” anawonjezera motero. “Koma ndinaphunzira kukonda utumiki wakumunda. Ndiye tsiku lina ndinaona kuti kukhala mpainiya kumangotanthauza kukhala ndi mbali yaikulupo mu utumiki. Mpamene ndinazindikira kuti ndidzachita upainiya.”

“Atumiki a nthaŵi zonse anali okondeka nthaŵi zonse panyumba pathu,” anasimba motero Lusia. Iye amakumbukira chimwemwe chimene anthu ankakhala nacho mumpingo wawo nthaŵi zonse amishonale akabwera kudzacheza. “Pamene ndinali kukula,” anatero, “ndinadziŵa kuti ndidzafuna kuloŵa utumiki wa nthaŵi zonse.”

Amayi a Theodis anamwalira pamene iye anali ndi zaka 15 zakubadwa. “Panthaŵiyo, mpingo unandithandizadi,” anatero, “choncho ndinadzifunsa kuti, ‘Kodi ndidzatani kuti ndisonyeze kuyamikira?’” Zimenezi zinampangitsa kuloŵa utumiki wa nthaŵi zonse ndipo tsopano ntchito yaumishonale.

[Chithunzi patsamba 25]

Kalasi la 105 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower

M’ndandanda pansipa, mizera ikuŵerengedwa kuyambira kutsogolo kumka kumbuyo, ndipo maina andandalikidwa kuyambira kulamanzere kumka kulamanja mumzera uliwonse

(1) Sampson, M.; Brown, I.; Heggli, G.; Abuyen, E.; Desbois, M.; Pourthié, P. (2) Kassam, G.; Lindberg, R.; Dapuzzo, A.; Taylor, C.; LeFevre, K.; Walker, S. (3) Baker, L.; Pellas, M.; Woggon, E.; Böhne, C.; Asplund, J.; Haile, J. (4) Pourthié, T.; Whittaker, J.; Palmer, L.; Norton, S.; Gering, M.; Haile, W. (5) Walker, J.; Böhne, A.; Groenveld, C.; Washington, M.; Whittaker, D.; Abuyen, J. (6) Gering, W.; Washington, K.; Pellas, M.; Desbois, R.; Heggli, T.; Asplund, Å. (7) Woggon, B.; LeFevre, R.; Taylor, L.; Brown, T.; Groenveld, R.; Palmer, R. (8) Norton, P.; Sampson, T.; Baker, C.; Lindberg, M.; Kassam, M.; Dapuzzo, M.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena