Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 6/15 tsamba 4-7
  • “Utatu Wodalitsidwa”—Kodi Uli mu Baibulo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Utatu Wodalitsidwa”—Kodi Uli mu Baibulo?
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mzimu Woyera ndi Munthu?
  • Funso Lina Lofunika Kwambiri
  • Kodi Yesu ali Wokhalako Wamkulukulu?
  • Kodi Chiphunzitso cha Utatu Chiri Chovulaza?
  • Gawo 1—Kodi Yesu ndi Ophunzira Ake Anaphunzitsa Chiphunzitso cha Utatu?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Yesu Kristu—Mwana Wokondedwa wa Mulungu
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kodi Pali Mulungu Atate, Mulungu Mwana Ndi Mulungu Mzimu mwa Mulungu M’modzi?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Utatu Kodi Umaphunzitsidwa m’Baibulo?
    Nsanja ya Olonda—1993
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 6/15 tsamba 4-7

“Utatu Wodalitsidwa”​—Kodi Uli mu Baibulo?

IYE anatenthedwa ku imfa mu England mu 1550. Dzina lake? Joan Bocher. Mlandu wake? The Encyclopaedia Britannica (1964) imanena kuti: “Iye anazengedwa mlandu wa kuchitira mwano kwapoyera mukukana Utatu, mlandu umodzi umene matchali tchi onse anaulingalira kukhala wosakhululukidwa kuyambira pamene anayamba kukangana ndi Arianism.”

Utatu uli chiphunzitso choyamba cha matchalitchi ambiri. Koma kodi nchiyani kwenikweni chimene chiri Utatu? The Waverley Encyclopedia imalongosola uwo monga “chinsinsi cha Mulungu mmodzi mu anthu atatu​—Atate, Mwana, ndi Mzimu Woyera, ofanana ndi a moyo wofanana mu zinthu zonse.”Koma The New Encyclopcedia Britannica (1981) imanena kuti: “Palibe liwu lakuti Utatu, osatinso kulongosoledwa komveka kwa chiphunzitso chonga chimenecho, chimene chimawoneka mu Chipangano Chatsopano.” Ichi mwamsanga chimadzutsa mafunso ponena za chiphunzitsocho.

Kuvomereza nkhaniyo chiri chivomerezo chowona mtima chimene New Catholic Encyclopedia imapereka mu mkhalidwe wa funso limene ophunzira apa sukulu ya tchalitchi kaŵirikaŵiri amafunsa, “Koma kodi ndimotani mmene wina angalalikire Utatu?” Ntchito ya Chikatolika imeneyi ikupitiriza: “Ngati funsolo liri chizindikiro cha kusokonezeka kumbali ya ophunzira, mwinamwake ilo sirili lochepera chizindikiro cha kusokonezeka kofananako kumbali ya aphunzitsi awo. Ngati ‘Utatu’ pano umatanthauza nzeru ya chipembedzo ya Utatu, yankho labwino koposa lingakhale lakuti wina salalikira uwo nkomwe . . . chifukwa ulalikiwo, ndipo makamaka nkhani yolongosoledwa yozikidwa mu Baibulo, ali malo kaamba ka mawu a Mulungu, osati kulongosola kwa ziphunzitso za chipembedzo.”

Kodi ndi liti pamene “kulongosola kwa chiphunzitso cha chipembedzo” kumeneko kunayamba? Ikuyankha The New Encyclopcedia Britannica (1981): “Chiphunzitsocho chinayamba kukula pang’onopang’ono mkati mwa zaka mazana angapo ndipo kupyolera mu kutsutsana kosiyanasiyana.” Kodi chimenecho chikumvekera kukhala chachindunji kwa inu, vumbulutso lomvekera bwino kuchokera kwa Mulungu? Chotero kodi ndimotani mmene icho chingakhalire chivumbulutso cha Malemba Oyera, monga mmene chimanenedwera?

Mawu a Baibulo amene aphunzitsi amatchalitchi kawirikawiri amagwiritsira ntchito kuchirikiza Utatu liri lamulo la Yesu lakuti otsatira ake ayenera kupanga ophunzira, “kuwabatiza iwo mu dzina la Atate ndi la Mwana ndi la mzimu woyera.” (Mateyu 28:19) Tsamba limenelo mwachiwonekere limatchula zinthu zitatu, koma siritchula kuti iwo onse ali anthu atatu kapena kuti ali mmodzi. M’kuwonjezerapo, tikudziwa dzina la Atate (Yehova) ndi la Mwana (Yesu), koma kodi ndi liti limene liri dzina la mzimu woyera? Ichi chimatsogolera ku funso. . . 

Kodi Mzimu Woyera ndi Munthu?

Chenicheni chakuti Baibulo silimapereka chizindikiro cha mzimu woyera kukhala ndi dzina la umunthu chimapereka lingaliro lakuti sungakhale munthu. Mungadzifunsenso,‘kodi mzimu woyera unayamba wawonedwapo?, Chabwino, pa ubatizo wa Yesu uwo unasonyezedwa monga nkhunda ndipo pa Pentekoste unasonyezedwa monga malilime a moto. (Mateyu 3:16; Machitidwe 2:3, 4) Ngati iwo uli munthu, kodi nchifukwa ninji sunawoneke monga munthu? Ndipo ngati mzimu woyera suli munthu, kodi uwo nchiyani? Mosakaikira, iwo uli mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu imene pa Pentekoste ‘inatsanuliridwa’pa ophunzira. (Machitidwe 2:17, 18) Ndi mphamvu yogwira ntchito imeneyi, Yehova anapanga ntchito zake za chilengedwe​—“[Mphamvu yogwira ntchito NW] ya Mulungu inali kufungatira pamwamba pa madzi.”(Genesis 1:2) Mphamvu yogwira ntchito imodzimodziyo inauzira alembi a Baibulo.​—2 Timoteo 3:16.

Mmodzi wa olemba ouziridwa amenewa anali mneneri Danieli. Mu Danieli mutu 7 iye akulongosola masomphenya odabwitsa amene Yehova anampatsa iye: “Nkhalamba ya kale lomwe” pa mpando wake wachifumu wa kumwamba, ndi khamu la angelo likumtumikira iye. Danieli anawonanso “wina wake monga mwana wa munthu [Yesu],” amene anapatsidwa “ulamuliro ndi ulemerero ndi ufumu, kuti anthu onse ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, amtumikire.” (Danieli 7: 9, 10, 13, 14) Bwanji, ngakhale kuli tero, ponena za mzimu woyera? Iwo sunatchulidwe monga munthu mu chochitika chakumwamba chimenechi.

Bukhu lomalizira la Baibulo​—Chivumbulutso​—limalongosola masomphenya ena akumwamba owonekera. Wokhalako Wamkulukulu, Yehova, akusonyezedwa ali pa mpando wake wachifumu, ndi Mwanawankhosa, Yesu Kristu, ali limodzi naye. Koma, kachiwirinso, mzimu woyera sunatchulidwe monga munthu wozindikirika. (Chivumbulutso, mitu 4-6)Chotero ngakhale bukhu lomalizira la Baibulo silikuvumbula kuti pali anthu atatu mwa mulungu mmodzi. Ichi chimadzutsa . . 

Funso Lina Lofunika Kwambiri

Nthanthi ya Utatu yakhala iri kulongosoledwa monga Mchiphunzitso chapakati cha chipembedzo Chachikristu.” Ngati ichi chinali chowona kodi nchifukwa ninji Yesu sanavumbulutse icho pamene iye anali padziko lapansi? Ophunzira ake, kukhala Aisrayeli, anakhulupirira kuti Yehova ali wapadera. Kufikira lerolino, Ayuda akupitirizabe kukumbukira Deutronomo 6:4: “Imvani, Israyeli; Yehova Mulungu wathu, Yehova ndiye mmodzi.” Palibe lingaliro mu Malemba Achihebri kuti Wokhalako Wamkulukulu ali mwa anthu atatu. Inu mungadabwe, ’Ngati ichi chinali chowona, kodi nchifukwa ninji “chiphunzitso chapakati chimenechi” sichinakhale nthanthi kufikira mu zana lachinayi​—pakati pa mkangano wowopsya umene unayambitsa kufalikira kwa chisokonezo?’

Ena anganene kuti: ’Koma Yesu anati, “Ine ndi Atate tiri amodzi.” ’ (Yohane 10:30) Zowona. Kodi ndi mlingaliro lotani, ngakhale kuli tero, mmene iwo aliri amodzi? Yesu iye mwini anachimveketsa bwino pambuyo pake mwakunena mu pemphero: “Atate Woyera, [yang’anirani iwo, NW] [ophunzira ake] . . . kuti akhale m’modzi, monga ife tiri m’modzi” (Yohane 17:11, 22) Chotero, umodzi wa Atate ndi Mwana uli wofanana ndi umodzi umene ulipo pakati pa atsatiri owona a Kristu​—kugwirizana kwa cholinga ndi kuthandizana.

Komabe, ena angalingalire kuti ngakhale kuti Yesu sanatchule chiphunzitso cha Utatu, mtumwi Yohane anatero pa 1 Yohane 5:7, pamene, malinga ndi King James Version pamati: “Pakuti pali atatu akuchitira umboni kumwamba, Atate, Mawu, ndi Mzimu Woyera: ndipo atatu amenewa ali mmodzi.” Komabe, matanthauzidwe amakono kwambiri samagwiritsira ntchito mbali imeneyi. Nchifukwa ninji? Jerusalem Bible ya Chikatolika imalongosola mu mawu ake apansi kuti lemba limeneri silikupezeka mu malemba aliwonse akale a Chigriki kapena a Chilatini abwino koposa a Baibulo. Icho chiri chabodza. Chinawonjezeredwa, mosakaikira, kuyesa kuchirikiza Utatu.

Monga mmene mungafufuzire mu Baibulo lanu mtumwi Paulo m’mawu otsegulira amakalata ake kawirikawiri anagwiritsira ntchito mawu onga ngati awa: “Chisomo chikhale ndi inu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Kristu.” (Aroma 1:7) Kodi ndi chifukwa ninji iye sanatchule mzimu woyera monga munthu? Chifukwa Paulo sanadziwe chiri chonse ponena za “Utatu Woyera.” Yakobo, Petro, ndi Yohane anagwiritsira ntchito mawu ofananawo mu makalata awo kumene iwo mofananamo satchula konse mzimu woyera. Nchifukwa ninji? Chifukwa iwo sanalinso okhulupirira Utatu. Mzimu woyera si munthu monga mmene aliri Mulungu ndi Mwana wake. Koma popeza Mwana ali munthu, funso lingabuke. . . .

Kodi Yesu ali Wokhalako Wamkulukulu?

Okhulupirira mu Utatu amati inde. Komabe mudzakhala osangalatsidwa kwambiri mu zimene Yesu ananena: “Atate ali wamkulu [pa NW] ine.” (Yohane 14:28) “Sakhoza Mwana kuchita kanthu pa iye yekha, koma. chimene awona Atate achichita, ndicho.” (Yohane 5: 19) Paulo anawonjezera: “Mutu wa Kristu ndiye Mulungu.”​—1 Akorinto 11:3.

Lingalirani mosamalitsa, kachiŵirinso, ma funso awa: Kodi Yehova ali ndi Mulungu? Mwachidziwikire ayi, iye ali wamkulukulu, Wamphamvuyonse. Kodi Yesu ali ndi Mulungu? Pambuyo pa kuukitsidwa kwake Yesu ananena kwa Mariya wa Magadala: “Ndikwera kunka kwa Atate wanga ndi Atate wanu, ndi Mulungu wanga, ndi Mulungu wanu.” Mtumwi Petro analemba: “Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu.”​—Yohane 20:17; 1 Petro 1:3.

Kodi Mulungu anayamba wafapo? ’Ndithudi ayi,’ lingakhale yankho lanu lolondola. Mulungu ali wosakhoza kufa. Mneneri Habakuku ananena za Yehova: “Wopatulika Wanga, [simufa, NW].” (Habakuku 1:12) Mkusiyanitsa, Yesu anafa. Kenaka kodi ndani amene anamuukitsa iye kuchokera kwa akufa? Petro akuti: “Mulungu anaukitsa [Kristu] kuchokera kwa akufa.” Chimakhala chotsimikizirika, chotero kuti Yesu siali Wokhalako Wamkulukulu.​—Machitidwe 3:15; Aroma 5:8.

Mungapitebe patsogolo. Kodi Mulungu anayamba wawonedwapo? “Kulibe munthu anawona Mulungu nthawi zonse.” (Yohane 1:18) Koma zikwi zinawona Yesu padziko lapansi. Kodi Mulungu anayamba wapempherapo kwa winawake? Kodi ndi kwa ndani kumene iye akanapemphera? Iye ali “Wakumva pemphero Wamkulu.” (Masalmo 65:2) Nanga Yesu? Iye mobwerezabwereza anapemphera kwa Atate wake ngakhale kuchezera usiku wonse m’pemphero. Kodi Mulungu ali wansembe? Mwachidziwikire ayi. Nanga Yesu? Timawerenga: “Lingalirani mtumwi ndi mkulu wansembe wa chivomerezo chathu​—Yesu.”​—Ahebri 3:1.

Kodi sichiri chomvekera mokulira kuti Yesu sali Wokhalako Wamkulukulu?

Kodi Chiphunzitso cha Utatu Chiri Chovulaza?

Inde. Chiphunzitso chofala chimenechi chimasokoneza chowonadi chopepuka cha Baibulo chakuti Yehova yekha ali Wokhalako Wamkulukulu, ndi kuti Yesu ali Mwana wake, ndi kuti mzimu woyera uli mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu. Chiphunzitsocho chimayambitsanso msokonezo mwa kuphimba Mulungu mu ntambo wa chinsinsi, kutsogoleraku mdima wauzimu.

Inu, ngakhale kuli tero, simukafunikira kukhala mu mdima umenewo. Mungakhazikitse momvekera bwino mu maganizo nsonga zina:

Chiphunzitso cha Utatu sichinatchulidwe mu Baibulo. Icho chiri “kulongosola kwa phunziro la chipembedzo” komwe kunabuka mazana ambiri pambuyo pa tsiku la Yesu, ndipo chinakhazikitsidwa pansi pa chiwopsyezo cha imfa pa mtengo. Icho chachepsya kulambiridwa kwa Wokhalako Wamkulukulu, kuphunzitsa chikhulupiriro mu chinsinsi.

Ngati inu nthawi zonse mwakhala muli kukhulupirira Utatu, kodi nchiyani chimene muyenera kuchita tsopano? Tikufulumizani inu kuphunzira Mawu a Mulungu ndi zofalitsidwa zonga ngati ichi zimene zidzakuthandizani inu kumvetsetsa Baibulo. Kuchita tero kuli kofunika kwambiri. Yesu ananena kuti moyo wosatha umadalira pa kutenga chidziwitso cha iye ndi cha Yehova​—“Mulungu yekha wowona.”​—Yohane 17:3.

Bokisi/​Chithunzi patsamba 5

Chala cha Mulungu

“Chala cha Mulungu ichi!” ansembe amatsenga a mu Igupto anavomereza pamene analephera kutembenuza pfumbi kukhala nsabwe, monga mmene anachitira Mose. (Eksodo 8:18, 19) Pa Phiri la Sinayi, Yehova anamupatsa Mose “magome amiyala olembedwa ndi chala cha Mulungu.” (Eksodo 31:18) Kodi chimenechi chinali chala chenicheni? Ayi. Yehova mwachidziwikire, alibe zala zenizeni. Ndi chiyani, nanga? Olemba Baibulo Luka ndi Mateyu akutipatsa ife mfungulo. Mmodzi analemba kuti “ndi chala cha Mulungu,” Yesu anatulutsa ziwanda. Wina akulongosola kuti Yesu anachita ichi “mwa mzimu wa Mulungu.” (Luka 11:20; Mateyu 12:28) Chotero mzimu woyera uli “chala cha Mulungu,” chida chake cha kukwaniritsira chifuniro chake. Iwo suli munthu, koma uli mphamvu yaikulu yogwira ntchito ya Mulungu.

[Chithunzi patsamba 7]

Mzimu woyera unawoneka monga nkhunda ndi monga malilime a moto​—osati monga munthu

[Mawu a Chithunzi patsamba 4]

Choimira cha Utatu mu Tchalitchi cha Chikatolika cha mu Zana la 14 mu Tagnon, France

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena