Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 5/8 tsamba 30-31
  • Kodi Chaka cha 2,000 Chidzawakhudza Bwanji Anthu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Chaka cha 2,000 Chidzawakhudza Bwanji Anthu?
  • Galamukani!—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova, Wosunga Nthaŵi
  • “Zija Zidzaoneka Liti?”
  • Kodi Zaka za Chikwi Chachitatu Zidzayamba Liti?
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Kodi Chaka cha 2000 N’chapadera?
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Zaka Chikwi Zachitatu—Kodi Zidzakwaniritsa Ziyembekezo Zanu?
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Kodi N’kupupuluma Kapena Kuzengereza?
    Galamukani!—1999
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 5/8 tsamba 30-31

Lingaliro la Baibulo

Kodi Chaka cha 2,000 Chidzawakhudza Bwanji Anthu?

CHAKA chimene chidzakhala cha 2,000 ku maiko a Kumadzulo kuphatikizapo ena ambiri, anthu ochuluka sachigwirizanitsa ndi zachipembedzo. Mwachitsanzo, Ayuda, Asilamu, ndi Ahindu onseŵa ali ndi makalendala awo achipembedzo amene sagwirizana ndi ya maiko a Kumadzulo. Pa masiku a zachipembedzo ndi a za mwambo wakwawoko, anthu a ku China amatsatira kalendala yotsatira kayendedwe ka mwezi. Motero mabiliyoni ambiri a anthu lerolino, mwinamwake chiŵerengero chachikulu kwambiri padziko saona chaka cha 2,000 monga chokhala ndi tanthauzo lapadera.a

Komabe ambiri, makamaka m’maiko a Kumadzulo, akudikirira mwachidwi kuti aone kuyambika kwa zaka chikwi zotsatira monga mmene kalendala yokonzedwa ndi Papa Gregory imasonyezera. Kwa ena si chidwi chabe. Amaona ngati chaka cha 2,000 kudzakhala kuyambika kwa nthaŵi yatsopano, monga posinthira zinthu m’mbiri. Ambiri mwa amene amati amakhulupirira Baibulo amati maulosi adzakwaniritsidwa m’chaka cha 2,000. Ena akuyembekezera kuti anthu ambiri adzadzipereka pa zinthu zauzimu. Ena amaopa kuti kudzakhala tsoka lalikulu—mapeto a dziko. Koma kodi Baibulo limanenapo chilichonse chokhudza ziyembekezo zimenezi?

Yehova, Wosunga Nthaŵi

Mulungu wa m’Baibulo amatchedwa “nkhalamba ya kale lomwe.” (Danieli 7:9) Amalamulira nthaŵi bwino kwambiri, monga mmene timaonera kugwira ntchito kwa zinthu zimene analenga, kuyambira kuzungulira kwa mapulaneti mpaka mayendedwe a zinthu zing’onozing’ono zoposa atomu. Ali ndi ndandanda yake yochitira zinthu imene amaitsatira mosaphonyetsa. Baibulo linati: ‘Anapangiratu nyengo zawo, ndi malekezero a pokhala pawo,’ Yehova amasunga nthaŵi mosaphonyetsa.

Mogwirizana ndi zimenezi, Baibulo limapereka ndandanda yolongosoka ya nthaŵi imene zinthu zinachitika. Limapereka mbiri yogwirizana bwino mwakuti nzotheka kuŵerenga mpaka pamene mbiri ya munthu inayambira. Kuŵerengera kumeneko kumasonya 4026 B.C.E. kuti ndicho chaka chimene Mulungu analenga Adamu. Zaka 2,000 pambuyo pake, mpamene Abrahamu anabadwa. Panathanso zaka zina 2,000 kufika pamene Yesu anabadwa.

Ena mwa amene amaŵerenga mbiri za m’Baibulo ananena za masiku pamene zinthu zina zidzachitika mtsogolo. Mwachitsanzo, poyerekezera nthaŵi za zaka pafupifupi 2,000 zilizonse zimene zinapitapo kusiyanitsa Adamu, Abrahamu, ndi Yesu, amayembekezera kuti kudzachitika zoopsa pamapeto a chaka cha 2,000 kuyambira pamene Yesu anabadwa. Ichi nchitsanzo chimodzi chabe cha kuŵerengera nthaŵi kumene amati nkochokera pa ndandanda ya zochitika m’mbiri ya m’Baibulo.

Nzoonadi kuti Baibulo limanena nthaŵi pamene Yehova Mulungu adzaloŵererapo pa zochita za anthu mwakuchotsa kuipa ndi kubweretsa dziko latsopano. Ulosi wa m’Baibulo umanena za “nthaŵi ya chimariziro,” “mathedwe a nthaŵi ya pansi pano,” “masiku otsiriza,” ndi “tsiku la Mulungu.” (Danieli 8:17; Mateyu 24:3; 2 Timoteo 3:1; 2 Petro 3:12) Komabe mapeto otchulidwa m’Baibulo sagwirizana mwanjira iliyonse ndi chaka cha 2,000. Palibe kalikonse m’Malemba kamene kamasonyeza kuti padzachitika china chake pamapeto pa zaka za chikwi chachiŵiri tikaŵerenga ndi kalendala ya Gregory.

“Zija Zidzaoneka Liti?”

Atumwi a Yesu anachita chidwi ndi ndandanda yochitira zinthu ya Mulungu pamene anafunsa Yesu kuti: “Mutiuze ife zija zidzaoneka liti? ndipo chizindikiro cha kufika kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthaŵi ya pansi pano?” (Mateyu 24:3) Lerolino ambiri ali ndi chidwi chofananacho chofuna kudziŵa zamtsogolo. Nkwachibadwa kukhala ofunitsitsa kudziŵa ulosi wa m’Baibulo wofunika wotero ndi nthaŵi pamene udzakwaniritsidwa. Komabe, nkwanzeru kulolera ndi kulemekeza mmene Mulungu amaonera nkhaniyo.

Kupyolera mwa Mwana wake, Yehova anaulula zomwe akufuna kuchita ndipo anapereka yankho lachindunji pankhani imeneyi. Patangotsala pang’ono kuti Yesu akwere kumwamba, ophunzira ake anamfunsanso za nthaŵi pamene malonjezo a Mulungu adzakwaniritsidwa. Yesu anayankha kuti: ‘Sikuli kwa inu kudziŵa nthaŵi kapena nyengo, zimene Atate anaziika m’ulamuliro wake wa iye yekha.’ (Machitidwe 1:7) Panthaŵi ina poyambirira, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Koma za tsiku ilo ndi nthaŵi yake sadziŵa munthu aliyense, angakhale angelo a Kumwamba, kapena Mwana, koma Atate yekha.”—Mateyu 24:36.

Nzoonekeratu kuti “nthaŵi kapena nyengo,” makamaka pamene zikhudzana ndi kukwaniritsidwa kwa ulosi wa m’Baibulo, sizili m’manja mwa munthu. Mulungu anasankha kusatiululira zimenezo. (Mateyu 24:22-44) Kodi tingachitepo kanthu mwanjira ina iliyonse pa chifuno cha Mulungu mwakudziŵa “za tsiku ilo” patokha, motsutsana ndi chifuniro chake? Mwachionekere zimenezi nzosatheka. (Numeri 23:19; Aroma 11:33, 34) Baibulo limati: “Chiweruzo cha Yehova chikhazikika chikhazikikire.” (Salmo 33:11) Pokhala ndi Mulungu wamphamvu zonse, nthaŵi zonse salephera.—Yesaya 55:8-11.

Pokhala tilibe mphamvu yonga ya Mulungu yoti nkudziŵira “nthaŵi ndi nyengo zimene atate anaziika,” ambiri amangoganizira. Ena amadzipanga okha aneneri onenera za tsiku la chiwonongeko. Pachifukwa chimenechi mtumwi Paulo anapereka malangizo kwa Atesalonika ponena za kuopsa kwa kumvera amene amanena za masiku. Iye analemba kuti: “Tikupemphani . . . kuti musamagwedezeka mtima msanga ndi kutaya maganizo anu, kapena kuwopsedwa, mwa mzimu kapena mwa mawu; kapena mwa kalata, monga wolembedwa ndi ife, monga ngati tsiku la Ambuye lafika. Munthu asakunyengeni konse.”—2 Atesalonika 2:1-3.

Mboni za Yehova zimakhulupirira motsimikiza kuti zifuno za Mulungu za mtsogolo nzodalirika kuti zidzachitika panthaŵi yoikidwiratu, pali tsiku lenileni ndi ola limene anakhazikitsa. (Habakuku 2:3; 2 Petro 3:9, 10) Ndipo timakhulupirira kuti zimenezi zidzachitika osati kale kwambiri. (2 Timoteo 3:1-5) Komabe, sitimangonenanena kapena kugwirizana ndi zonenanena zomwe zikumveka masiku anozi.b Ndithudi, palibe chaka chilichonse kaya cha 2,000, kapena cha 2001, kaya nthaŵi ina iliyonse yokhazikitsidwa ndi anthu imene ingagwirizane ndi nthaŵi imene Mulungu anakhazikitsa.

[Mawu a M’munsi]

a Malinga ndi akatswiri odziŵa za zaka, chomwe chimatchedwa kuti zaka zachikwi chachitatu chidzayamba pa January 1, 2001. Zaka za chikwi choyamba sizinayambe ndi zilo, koma mmalo mwake zinayamba ndi 1. Komabe anthu wamba amaona kuti “zaka za chikwi chachitatu” zidzayamba m’chaka cha 2,000. Nkhani ino ikunena za zomwe anthu ambiri akuyembekeza m’chaka cha 2,000.

b Nsanja ya Olonda ya September 1, 1997, masamba 21-2, inati: “Mboni za Yehova zafunitsitsa kudziŵa pamene tsiku la Yehova lidzadza. Chifukwa cha kufunitsitsa kwawoko izo nthaŵi zina zayesa kupeza nthaŵi pamene lidzadza. Koma mwa kuchita zimenezo, izo zakhala zikulephera kulabadira chenjezo la Mbuye wawo lakuti ‘sitidziŵa nthaŵi yake,’ monganso anachitira ophunzira oyambirira a Yesu. (Marko 13:32, 33) Onyoza anyodola Akristu okhulupirika poyembekezera zinthu nthaŵi yake isanakwane. (2 Petro 3:3, 4) Ngakhale ndi tero, tsiku la Yehova lidzadza ndithu, akutsimikiza Petro, malinga ndi nthaŵi Yake yoikika.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena