Chidziŵitso pa Nyuzi
Anthabwala Kaamba ka Kristu?
“Anthabwala a Uthenga Wabwino ali pa Msewu” unali mutu wa nkhani womwe unawonekera mu Church Times, nyuzipepala ya Tchalitchi cha England. Iwo unkalengeza kuchezera kwa pachaka kwa Kusonyeza kwa pa Msewu kwa Church Army ku malo osankhidwa okhala kumbali kwa nyanja mu England ndi Wales. Chopezedwa kokha zaka zoposa zana limodzi zapitazo monga chiwalo cha Tchalitchi cha England, Church Army inkalengeza “pakati pa okanidwa ndi aupandu a m’malo osasamalidwa bwino a ku Westminster.”
Lerolino, atsogoleri a Church Army ali odera nkhaŵabe kuti “kulengeza kufunikira kupatsidwa malo ake olondola.” Kusonyeza kwawo kwa pa Msewu kumalunjika pa kupereka uthenga wabwino “m’njira yabwino kwa anthu omwe ali ndi kuzoloŵera kwa papitapo kochepera kwa Mulungu, ndi omwe alibe cholinga cha kupezeka pa chochitika chochitidwira ku tchalitchi kapena holo ya tchalitchi.” “Anthabwala a Uthenga Wabwino” okometseredwa m’kusonyeza kwa pa msewu amayembekeza kuti “kudzipereka kwawo kopusitsa mwinamwake kudzawapangitsa oyenda mu msewu kuimirira ndi kumvetsera kwa kanthaŵi,” yadziŵitsa tero Church Times.
Komabe, pamene kuli kwakuti kavalidwe kawo ka nthabwala, maseŵera, ndi maballoon aulere anakoka achichepere ambiri, achikulire anasiidwa akuzizwitsidwa ndi chimene kufikira kumeneku kunkachita ndi kulengeza koyambitsidwa ndi Yesu Kristu.
Zowona, mtumwi Paulo analemba kuti: “Pakuti takhala ife chowonetsera ku dziko lapansi . . . Tiri opusa ife chifukwa cha Kristu.” (1 Akorinto 4:9, 10) Koma kodi nchiyani chimene iye anali nacho m’malingaliro? Kupanga Nthabwala kapena “kudzipusitsa” ndi cholinga chofuna kukoka oyenda m’njira? Ayi. Paulo anali kuchitira chitsanzo mmene dziko limalingalirira Akristu kukhala opusa, “owunikiridwa ku kusekedwa kwapoyera ndi kunyazitsidwa,” monga mmene The New International Dictionary of New Testament Theology yachiikira icho, pa chifukwa cha chikhulupiriro chawo ndi chiphunzitso.
Mosiyana ndi “Anthabwala a Uthenga Wabwino” a Church Army, Yesu anaphunzitsa anthu “monga munthu wokhala ndi lamulo.” Utumiki wake unali wolunjika ndi wopanda kukometseredwa. Monga mmene iye analongosolela, “Monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi.” Kodi chotulukapo chake chinali chotani? “Ambiri anakhulupirira iye.”—Mateyu 7:29; Yohane 8:28, 30.
“Cholemetsa cha Chikumbumtima”
Eugene Stockwell, mtsogoleri wa Commission on World Mission and Evangelism ya Bungwe la Matchalitchi a Dziko Lonse, posachedwapa anavomereza malo achinyengo omwe atsogoleri a chipembedzo ndi matchalitchi a Chikristu cha Dziko akhala akutengamo mbali mkati mwa nkhondo zonse zadziko. “Icho chiri cholemetsa chokulira cha chikumbumtima cha Akristu kotero kuti nkhondo zadziko zazikulu ziŵiri za zana lino zinabweretsedwa pakati pa mitundu yomwe iri ndi miyambo yokulira ya Chikristu pakati pawo ndi imene kukantha kwa magulu ankhondo kaŵirikaŵiri kunadalitsidwa ndi atsogoleri a matchalitchi a Chikristu,” iye anauza bungwe la matchalitchi opezekapo mu Warsaw, Poland.
Stockwell anawonjezera kuti: “Mulungu mwachikondi analengezedwa kukhala kumbali imodzi ya kukanthana kapena ku inayo. . . . Ife Akristu mosavuta tinaika chikhulupiriro chathu pa ntchito ya chiwawa chathu.” Iye ananena kuti Nkhondo ya Dziko II inali “chisonyezero chokulira cha kulephera kwathu monga ‘mitundu ya Chikristu’ kukhalirira ku chikhulupiriro chathu, chikhulupiriro chomwe chimalankhulidwa kaŵirikaŵiri m’mawu ndi kukanidwa mowonekera m’ntchito.”
Koma kodi “cholemetsa cha chikumbumtima” chimenechi chathandiza otchedwa Akristu ndi atsogoleri awo a chipembedzo kuphunzira phunziro? Mogwirizana ndi Ecumenical Press Service, Mtsogoleri Stockwell wavomereza kuti: “Timalankhula za kukonda adani athu, ndipo timawapha iwo. Timalankhula za kutembenuza tsaya lina, ndipo timadzikonzekeretsa ife ndi mano athu. Timalankhula za mtendere womwe umakwaniritsa kumvetsetsa, ndipo timagawana m’nkhondo yomwe imapitirira kumvetsetsa kulikonse. Timalankhula za chikhulupiriro mwa Mulungu ndipo timaika chikhulupiriro chathu chowona m’zida zowononga.”
Atsogoleri a chipembedzo ochirikiza nkhondo a Chikristu cha Dziko ndi owatsatira awo amafanana mowonekera bwino ndi “olankhula zopanda pake” a m’masiku a mtumwi Paulo. Ponena za iwo, iye ananena kuti: “Avomereza kuti adziŵa Mulungu, koma ndi ntchito zawo amukana iye.”—Tito 1:10, 16.
Sitampu “Yolakwira”
Pa November 19, 1987, Postal Administration ya ku South Africa inakonzekera kutulutsa masitampu anayi okumbukira za m’Baibulo. Imodzi ya masitampuwo inali ndi kalongosoledwe kakuti “Mawu a Mulungu” m’Chigriki ndi “Mawu a Yehova” m’Chihebri. Panali kusindikiza konse pamodzi kwa makope 1,750,000 a sitampu imeneyi.
Komabe, mwamsanga tsiku lakuwatulutsa lisanakwane, mapositi ofesi analandira lamya kuwalangiza iwo kubweza kufalitsa kwawo kwa sitampu imeneyi. Chifukwa chake? “Chifukwa chakuti inapezedwa kukhala yoputa mlandu ndi bungwe la orthodox ya Chiyuda,” inasimba tero The Star, nyuzipepala ya ku Johannesburg. Iyo inawonjezera kuti: “Rabi David Hazdan wa ku Johannesburg ananena kuti dzina la Mulungu losindikizidwa lathunthu monga mmene linasindikizidwira pa sitampupo linasungidwa kaŵirikaŵiri kaamba ka kokha zochitika zapadera za chipembedzo.”
Chiri kaamba ka mwambo wofananawo Wachiyuda kuti otembenuza ambiri amakono a Baibulo apewa kugwiritsira ntchito dzina la Yehova ndipo alilowetsa m’malo ndi maina aulemu okha, monga ngati “Ambuye” kapena “Mulungu.” Nchosadabwitsa kuti Yesu ananena kwa atsogoleri a chipembedzo a m’tsiku lake kuti: “Inu mupeputsa mawu a Mulungu chifukwa cha miyambo yanu”!—Mateyu 15:6.