-
Kudziŵa “Mtima wa Kristu”Nsanja ya Olonda—2000 | February 15
-
-
Kudziŵa “Mtima wa Kristu”
“Wadziŵa ndani mtima wa Ambuye [“wa Yehova,” NW], kuti akam’langize Iye? Koma ife tili nawo mtima wa Kristu.”—1 AKORINTO 2:16.
1, 2. M’Mawu ake, kodi Yehova anaona kuti chofunika ndicho kuvumbula chiyani ponena za Yesu?
KODI Yesu ankaoneka motani? Kodi maonekedwe a tsitsi lake anali otani? nanga khungu lake? nanga maso ake? Kodi anali wamtali chotani? Kodi anali wonenepa kapena woonda chotani? M’zaka mazana onseŵa, zithunzithunzi za Yesu zajambulidwa mosiyanasiyana. Zina zooneka bwino, zinanso zokokomeza. Ena am’jambula monga mwamuna wamphamvu zake, pamene ena am’jambula monga munthu wofooka ndi wosakondwa.
2 Komano Baibulo silitchula zambiri zokhudza maonekedwe a Yesu. M’malo mwake, Yehova anaona kuti chofunika ndicho kuvumbula chinthu china chofunika kwambiri: mtundu wa munthu umene Yesu anali. Nkhani za m’Mauthenga Abwino sizimangosimba zimene Yesu ananena ndi kuchita komanso zimavumbula zenizeni zimene zinali mumtima mwake ndi m’maganizo mwake kuti anene mawu akewo ndi kuchita zinthu zimene anachita. Nkhani zouziridwa zinayizi zimatithandiza kusuzumira mu umene mtumwi Paulo anautcha kuti “mtima wa Kristu.” (1 Akorinto 2:16) M’pofunika kuti tidziŵe bwino malingaliro a Yesu, za mumtima mwake, ndi umunthu wake. Chifukwa chiyani? Pali zifukwa pafupifupi ziŵiri.
3. Kodi kudziŵa bwino mtima wa Kristu kudzatipangitsa kudziŵa chiyani?
3 Choyamba, mtima wa Kristu umatisonyeza zinazake ponena za mtima wa Yehova Mulungu. Yesu anali paunansi wathithithi ndi Atate wake moti Yesuyo anati: “Palibe munthu azindikira Mwana ali yani, koma Atate; ndipo Atate ali yani, koma Mwana, ndi iye amene Mwana afuna kumuululira Iye.” (Luka 10:22) Zili ngati kuti Yesuyo anali kunena kuti, ‘Ngati mukufuna kum’dziŵa Yehova kuti ndi wotani, yang’anani kwa ine.’ (Yohane 14:9) Chotero pamene tiphunzira zimene Mauthenga Abwino amavumbula ponena za malingaliro a Yesu ndi mmene ankamvera mumtima, kwenikweni timakhala tikuphunzira mmene Yehova amalingalirira ndi mmene amamvera mumtima. Chidziŵitso chimenechi chimatithandiza kuyandikira kwambiri kwa Mulungu wathu.—Yakobo 4:8.
4. Ngati tikufuna kuchitadi zinthu monga Kristu, kodi choyamba tiyenera kuphunzira chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?
4 Chifukwa chachiŵiri n’chakuti kudziŵa mtima wa Kristu kumatithandiza ‘kulondola mapazi ake.’ (1 Petro 2:21) Kulondola Yesu si nkhani yongobwereza mawu ake ndi kuchita zomwe anachita. Popeza kuti zonena ndi zochita zimakhala zotsatira za zimene munthu akulingalira ndi mmene akumvera mumtima, kulondola Kristu kumafuna kuti tikulitse “mtima” womwe iyeyo anali nawo. (Afilipi 2:5) M’mawu ena, ngati tikufuna kuchitadi zinthu monga Kristu, choyamba tiyenera kuphunzira kuganiza ndi kumva monga iye mumtima, komatu, monga momwe tingathere monga anthu opanda ungwiro. Chotero, tiyeni, mothandizidwa ndi olemba Mauthenga Abwino, tisuzumire mumtima wa Kristu. Choyamba tidzakambirana zinthu zimene zinapangitsa Yesu kuti azilingalira ndi kumva m’njira imeneyo mumtima mwake.
Moyo Wake Asanadzakhale Munthu wa Padziko Lapansi
5, 6. (a) Kodi mabwenzi athu angatisonkhezere motani? (b) Kodi ndi unansi wotani umene Mwana woyamba wa Mulungu anali nawo kumwamba asanadze padziko lapansi, ndipo kodi unansiwo unam’khudza motani?
5 Zochita za mabwenzi athu a ponda apa m’pondepo zingatikhudze, m’njira yabwino kapena yoipa, posonkhezera malingaliro athu, mmene timamvera mumtima, ndi zochita zathu.a (Miyambo 13:20) Talingalirani unansi umene Yesu anali nawo kumwamba asanadze padziko lapansi. Uthenga Wabwino wa Yohane umanena za Yesu asanadzakhale munthu wa padziko lapansi kuti anali “Mawu” a Mulungu kapena kuti Wom’lankhulira wake. Yohane amati: “Pachiyambi panali Mawu, ndipo Mawu anali kwa Mulungu, ndipo Mawu ndiye Mulungu. Aŵa anali pachiyambi kwa Mulungu.” (Yohane 1:1, 2) Popeza kuti Yehova analibe chiyambi, kukhala kwa Mawuwo ndi Mulungu kuyambira “pachiyambi” kukunena za chiyambi cha ntchito yolenga ya Mulungu. (Salmo 90:2) Yesu ndiye “wobadwa woyamba wa chilengedwe chonse.” Chotero, iye anakhalako zolengedwa zina zonse zauzimu ndi chilengedwe chonsechi zisanakhaleko.—Akolose 1:15; Chivumbulutso 3:14.
6 Malinga n’kunena kwa asayansi ena, thamboli lakhala lilipo kwa zaka zosachepera 12,000,000,000. Ngati zimenezo zingakhaledi zoona, Mwana woyamba wa Mulungu anali paunansi wathithithi ndi Atate wake kwa zaka mabiliyoni osaŵerengeka Adamu asanalengedwe. (Yerekezani ndi Mika 5:2.) Chotero pakati pa aŵiriwo panakhala unansi wachikondi kwambiri ndiponso wozama. Monga nzeru yolankhula ngati munthu, Mwana woyamba ameneyu asanakhale munthu wa padziko lapansi akusonyezedwa kuti akunena kuti: “Ndinakhala munthu amene [Yehova] anasangalala naye kwambiri tsiku ndi tsiku, pokhala wosangalala pamaso pake nthaŵi zonse.” (Miyambo 8:30, NW) Zoonadi, kukhalira pamodzi ndi Gwero la chikondi kwa zaka mabiliyoni osaŵerengeka kunali ndi chisonkhezero chachikulu kwambiri pa Mwana wa Mulungu! (1 Yohane 4:8) Mwana ameneyu anadziŵa malingaliro a Atate wake, kamvedwe kawo ka mumtima, ndi njira zawo ndipo anazisonyeza mosiyana ndi mmene wina aliyense akanachitira.—Mateyu 11:27.
Moyo Padziko Lapansi ndi Zisonkhezero Zina
7. Kodi chimodzi mwa zolinga zimene Mwana woyamba wa Mulungu anayenera kudzera padziko lapansi n’chotani?
7 Mwana wa Mulunguyo anali ndi zambiri zoti aphunzire, popeza chifuno cha Yehova chinali chakuti akonzekeretse Mwana wakeyo kukhala Mkulu wa Ansembe wachifundo, wokhoza “kumva chifundo ndi zofooka zathu.” (Ahebri 4:15) Kukwaniritsa ziyeneretso za ntchito imeneyi ndiko chimodzi mwa zolinga zimene Mwanayo anadzera padziko lapansi monga munthu. Padziko pano, monga munthu wokhala ndi thupi lanyama ndi magazi, Yesu anakumana ndi mikhalidwe ndi zisonkhezero zimene poyambapo anali kungoziona zikuchitika iye ali kumwamba. Koma tsopano anali kumva mmene anthu amamvera. Nthaŵi zina ankatopa, kumva ludzu, ndi njala. (Mateyu 4:2; Yohane 4:6, 7) Komanso, anapirira zovuta zamtundu uliwonse. Chotero “anaphunzira kumvera” ndipo anakhala ndi ziyeneretso zonse zofunika pantchito yake monga Mkulu wa Ansembe.—Ahebri 5:8-10.
8. Kodi tikudziŵapo chiyani ponena za ubwana wa Yesu padziko lapansi?
8 Nanga bwanji za zokumana nazo za Yesu pamene anali mwana padziko lapansi? Mbiri ya ubwana wake n’njaifupi kwambiri. Ndipotu, Mateyu ndi Luka okha ndi amene anasimba zochitika zokhudzana ndi kubadwa kwake. Olemba Mauthenga Abwino anadziŵa kuti Yesu anali kumwamba asanadze padziko lapansi. Kuposa china chilichonse, moyo wakewo asanakhale munthu wa padziko lapansi unafotokoza mtundu wa munthu amene iye anadzakhala. Komabe, Yesu anali munthu weniweni. Ngakhale kuti anali wangwiro, anayenerabe kukula kuchokera paukhanda kukhala mwana wamng’ono kenako kukhala mnyamata mpaka atakhala munthu wamkulu, nthaŵi yonseyi akuphunzira. (Luka 2:51, 52) Baibulo limanena zinthu zina zokhudza ubwana wa Yesu zimene mosakayikira zinam’khudza.
9. (a) Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti Yesu anabadwira m’banja losauka? (b) Kodi Yesu ayenera kuti anakulira m’mikhalidwe yotani?
9 Umboni ukusonyeza kuti Yesu anabadwira m’banja losauka. Zimenezi zikusonyezedwa ndi nsembe imene Yosefe ndi Mariya anabwera nayo ku kachisi masiku ngati 40 pambuyo pa kubadwa kwake. M’malo mobwera ndi mwana wa nkhosa monga nsembe yopsereza ndi mwana wa nkhunda kapena njiwa monga nsembe yauchimo, iwo anadza ndi “njiwa ziŵiri kapena maunda aŵiri.” (Luka 2:24) Malinga ndi Chilamulo cha Mose, nsembe imeneyi inkaperekedwa ndi osauka. (Levitiko 12:6-8) M’kupita kwa nthaŵi, banja lodzichepetsa limeneli linakula. Pambuyo pa kubadwa kozizwitsa kwa Yesu, Yosefe ndi Mariya anakhala ndi ana enanso mwa njira yachibadwa osachepera pa asanu ndi mmodzi. (Mateyu 13:55, 56) Chotero Yesu anakulira m’banja lalikulu, mwachionekere m’mikhalidwe yosauka.
10. N’chiyani chikusonyeza kuti Mariya ndi Yosefe anali anthu oopa Mulungu?
10 Yesu analeredwa ndi makolo oopa Mulungu amene anam’samalira bwino. Amayi wake, Mariya, anali mkazi wamikhalidwe yapadera. Kumbukirani kuti pom’lonjera, mngelo Gabrieli anati: “Tikuoneni, wochitidwa chisomo, Ambuye ali ndi iwe.” (Luka 1:28) Yosefe anali wopembedza kwambiri nayenso. Mokhulupirika, chaka chilichonse anali kuyenda ulendo wa makilomita 150 kupita ku Yerusalemu kukachita Paskha. Mariyanso anali kupita nawo, ngakhale kuti amuna okha ndiwo analamulidwa kutero. (Eksodo 23:17; Luka 2:41) Paulendo wina wotero, Yosefe ndi Mariya, atafufuza kwadzaoneni, anapeza Yesu wazaka 12 zakubadwayo ali m’kachisi pakatikati pa aphunzitsi. Poyankhula ndi makolo ake ogwidwa ndi nkhaŵawo, Yesu anati: “Simunadziŵa kodi kuti kundiyenera Ine ndikhale m’zake za Atate wanga?” (Luka 2:49) “Atate”—mawu amenewo ayenera kuti anali apamtima ndiponso osangalatsa kwa Yesu wachinyamatayo. Mfundo ndi yakuti, umboni ukusonyeza kuti iye anauzidwa kuti Yehova ndiye Atate wake weniweni. Ndiponso, Yosefe ayenera kuti anali atate wom’lera wabwino kwa Yesu. Ndithudi, Yehova sakanasankha mwamuna waukali kapena wankhanza kuti alere Mwana Wake wokondedwa!
11. Kodi Yesu anaphunzira ntchito yanji, ndipo m’nthaŵi ya Baibulo, kodi kuchita ntchito imeneyi kunkaphatikizapo chiyani?
11 Pazaka zimene anali ku Nazarete, Yesu anaphunzira ntchito yaukalipentala, mwachionekere kwa atate wake wom’lera, Yosefe. Yesu anakhala katswiri pantchitoyo moti ankatchedwa kuti “mmisiri wa mitengo.” (Marko 6:3) M’nthaŵi za Baibulo, akalipentala ankalembedwa ntchito pomanga nyumba, kupanga mipando (kuphatikizapo matebulo, mipando ing’onoing’ono, ndi mabenchi), ndi kupanga zida zolimira. M’buku lake lakuti Dialogue With Trypho, Justin Martyr, wa m’zaka za zana lachiŵiri C.E., analemba za Yesu kuti: “Pamene anali pakati pa anthu anali kugwira ntchito monga kalipentala, kupanga makasu olimira ndi ng’ombe ndi magoli.” Ntchito imeneyi siinali yofeŵa, popeza kuti kalipentala wakale sanali kuchita kugula matabwa. Zikuoneka kuti anali kuphothyola m’tchire ndi kusankha mtengo, kuudula ndi nkhwangwa, ndi kuunyamula kupita nawo kunyumba. Chotero Yesu ayenera kuti ankadziŵa kuvuta kwa kupeza zofunika panyumba, kuchita malonda ndi makasitomala, ndi kusamalira banja.
12. N’chiyani chikusonyeza kuti Yosefe ayenera kuti anamwalira Yesu asanamwalire, ndipo zimenezi ziyenera kuti zinatanthauzanji kwa Yesu?
12 Pokhala mwana woyamba m’banjamo, Yesu ayenera kuti anali kuthandiza kusamalira banjalo, makamaka popeza zikuoneka kuti Yosefe anamwalira Yesuyo asanamwalire.b Magazini ya Zion’s Watch Tower ya January 1, 1900, inati: “Mbiri ikusonyeza kuti Yosefe anamwalira Yesu adakali wamng’ono, ndikuti Yesuyo anayamba ntchito yaukalipentala nakhala wochirikiza banja lakelo. Umboni wina wa zimenezi ukupezeka m’Malemba mmene Yesu mwiniyo akutchedwa kuti mmisiri wa matabwa, ndipo amayi ake ndi abale ake akutchulidwa, koma Yosefe sakutchulidwa. (Marko 6:3) . . . Ndiyetu n’zoonekeratu kuti nthaŵi yaitaliyo ya zaka 18 za moyo wa Ambuye wathu, kuchokera panthaŵi ya chochitikacho [cholembedwa pa Luka 2:41-49] mpaka panthaŵi ya ubatizo wake, anaithera pa kusamalira maudindo wamba a m’moyo.” Mariya ndi ana ake, kuphatikizapo Yesu, ayenera kuti ankadziŵa chisoni chimene chimakhalapo pamene mwamuna wokondedwa wa m’banja ndiponso atate amwalira.
13. Pamene Yesu anayamba utumiki wake, n’chifukwa chiyani anali ndi chidziŵitso, nzeru, ndi malingaliro akuya zimene munthu wina aliyense sakanakhala nazo?
13 N’zodziŵikiratu kuti Yesu sanakulire m’moyo wa zinthu za mwana alirenji. M’malo mwake, iye anakhala moyo wa anthu wamba. Ndiyeno mu 29 C.E., nthaŵi inafika yoti Yesu achite ntchito ya Mulungu yomwe anayenera kuchita. Chakumapeto kwa chaka chimenecho, iye anabatizidwa m’madzi ndipo anabadwanso monga Mwana wauzimu wa Mulungu. ‘Kunam’tsegukira kuthambo,’ mwachionekere kusonyeza kuti tsopano anatha kukumbukira moyo wake wakumwamba asanadze padziko lapansi, kuphatikizapo malingaliro ndi momwe ankamvera mumtima. (Luka 3:21, 22) Chotero pamene Yesu anayamba utumiki wake, iye anali ndi chidziŵitso, nzeru, ndi malingaliro akuya zimene munthu wina aliyense sakanakhala nazo. Ndiye chifukwa chaketu zambiri zimene olemba Mauthenga Abwino analemba zinali zokhudza zochitika mu utumiki wa Yesu. Ngakhale zinali motero, iwo sanathe kulemba zonse zimene iye ananena ndi kuchita. (Yohane 21:25) Koma zomwe analembazo zimatitheketsa kusuzumira mumtima wa munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako.
Mmene Yesu Analili Monga Munthu
14. Kodi Mauthenga Abwino amam’sonyeza motani Yesu monga munthu wachikondi ndi wachifundo kwambiri?
14 Umunthu wa Yesu umene ukuonekera m’Mauthenga Abwino umam’sonyeza kukhala munthu wachikondi ndi wachifundo kwambiri. Anasonyeza mmene amamvera mumtima m’njira zosiyanasiyana: anachitira chifundo munthu wakhate (Marko 1:40, 41); anamva chisoni chifukwa cha anthu ouma khosi (Luka 19:41, 42); anasonyeza mkwiyo wolungama kwa osintha ndalama aumbombo (Yohane 2:13-17). Pokhala munthu wachifundo, Yesu ankatha kugwetsa misozi, ndipo sanabise mmene ankamvera mumtima. Bwenzi lake lapamtima Lazaro litamwalira, kungoona Mariya, mlongo wake wa Lazaro, akulira kunam’khudza kwambiri Yesu moti iyeyo anagwetsa misozi, kulira pamaso pa onse.—Yohane 11:32-36.
15. Kodi chikondi ndi chifundo cha Yesu chinaonekera motani mwa njira imene ankaonera ndi kukhalira ndi ena?
15 Chikondi ndi chifundo cha Yesu chinali kuonekera kwambiri mwa njira imene ankaonera ena ndiponso momwe ankakhalira nawo. Anafikira osauka ndi otsenderezedwa, kuwathandiza ‘kupeza mpumulo wa miyoyo yawo.’ (Mateyu 11:4, 5, 28-30) Sanali wotanganitsidwa kwambiri moti n’kulephera kuthandiza ovutika pamavuto awo, kaya mkazi wamatenda a kukha magazi yemwe anakhudza chovala chake mwakachetechete kapena wopemphapempha wakhungu amene sanalolere kukhala chete. (Mateyu 9:20-22; Marko 10:46-52) Yesu anali kuyang’ana pa ubwino wa ena ndipo anali kuwathokoza; komabe, anali wokonzekanso kupereka uphungu pamene uli wofunikira. (Mateyu 16:23; Yohane 1:47; 8:44) Panthaŵi imene akazi analibe ufulu wochuluka, Yesu anawasonyeza ulemu woyenerera. (Yohane 4:9, 27) Ndiyetu chifukwa chake gulu la akazi linam’tumikira ndi chuma chawo.—Luka 8:3.
16. N’chiyani chikusonyeza kuti Yesu anali ndi kaonedwe koyenera ka moyo ndi zinthu zakuthupi?
16 Yesu anali ndi kaonedwe koyenera ka moyo. Zinthu zakuthupi sizimene zinali zofunika kwambiri kwa iye. Zikuoneka kuti analibe zinthu zambiri zakuthupi. Iye ananena kuti ‘analibe potsamira mutu wake.’ (Mateyu 8:20) Panthaŵi imodzimodziyo, Yesu anali kuwonjezera chisangalalo cha ena. Pamene anapezeka paphwando laukwati, pamene nthaŵi zambiri pamakhala nyimbo, kuimba, ndi kusangalala, n’zoonekeratu kuti sanapezekepo kuti asokoneze chochitikacho. Ndithudi, Yesu anachita chozizwitsa chake choyamba pachochitikacho. Pamene vinyo anatha, iye anasandutsa madzi kukhala vinyo, chakumwa ‘chokondweretsa mtima wa munthu.’ (Salmo 104:15; Yohane 2:1-11) Chotero phwandolo linapitiriza, ndipo mosakayikira mkwati ndi mkwatibwi sanachititsidwe manyazi. Kaonedwe kake koyenerako kakusonyezedwabe ndi mfundo yakuti pali nthaŵi zambiri zotchulidwa pamene Yesu anagwira ntchito kwa nthaŵi yaitali ndiponso molimbikira mu utumiki wake.—Yohane 4:34.
17. N’chifukwa chiyani sizodabwitsa kuti Yesu anali Mphunzitsi Wamkulu, ndipo zophunzitsa zake zinasonyeza chiyani?
17 Yesu anali Mphunzitsi Wamkulu. Zambiri zomwe anaphunzitsa zinasonyeza zochitika zenizeni m’moyo wa tsiku ndi tsiku, zomwe ankazidziŵa bwino. (Mateyu 13:33; Luka 15:8) Kaphunzitsidwe kake kanali kapamwamba koposa—kotsatirika, kosavuta kumva, ndiponso kothandiza. Koma zofunika kwambiri ndi zimene anaphunzitsa. Ziphunzitso zake zinasonyeza chikhumbo chake cha pansi pa mtima cha kupangitsa omvetsera ake kudziŵa bwino malingaliro, mtima, ndi njira za Yehova.—Yohane 17:6-8.
18, 19. (a) Kodi Yesu anafotokoza Atate wake pogwiritsa ntchito mafanizo omveka otani? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?
18 Pogwiritsa ntchito zitsanzo nthaŵi zambiri, Yesu anafotokoza Atate wake mwa mafanizo omveka ndiponso osaiŵalika msanga. Kulankhula za chifundo cha Mulungu mwachisawawa ndi nkhani ina. Koma ndi nkhani inanso kuyerekezera Yehova ndi atate wokhululukira amene akumva chifundo kwambiri poona mwana wake amene wabwerera moti ‘akuthamanga, nam’kupatira pakhosi mwana wakeyo, nam’psompsonetsa.’ (Luka 15:11-24) Pokana mwambo wopanda chifundo wa atsogoleri achipembedzo omwe amanyozera anthu wamba, Yesu anafotokoza kuti Atate wake ndi Mulungu wofikirika amene anasankha kumvetsera mapempho a wamsonkho m’malo mwa pemphero lodzikweza la Mfarisi wodzitukumula. (Luka 18:9-14) Yesu anasonyeza Yehova kukhala Mulungu wosamala amene amadziŵa mpheta yaing’onong’ono ikagwa. “Musamaopa,” Yesu anatsimikizira ophunzira ake, “inu mupambana mpheta zambiri.” (Mateyu 10:29, 31) Ndiye chifukwa chaketu anthu anazizwa ndi “chiphunzitso” cha Yesu ndipo anayandikira kwa iye. (Mateyu 7:28, 29) Inde, panthaŵitu ina “khamu lalikulu” linakhala pafupi naye kwa masiku atatu, lopandanso chakudya!—Marko 8:1, 2.
19 Tiyenera kukhala okondwa kuti Yehova wavumbula mtima wa Kristu m’Mawu ake! Motero, kodi tingakulitse motani mtima wa Kristu ndi kuusonyeza pazochita zathu ndi ena? Tidzakambirana zimenezi m’nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
a Mfundo yonena kuti zolengedwa zauzimu zimasonkhezeredwa ndi mayanjano awo imaonekera pa Chivumbulutso 12:3, 4. Pamenepo Satana akusonyezedwa kukhala “chinjoka” chimene chinagwiritsa ntchito chisonkhezero chake kuti chipangitse “nyenyezi” zinanso, kapena kuti ana aamuna auzimu, kugwirizana nacho pachipanduko chake.—Yerekezani ndi Yobu 38:7.
b Nthaŵi yomaliza pamene Yosefe akutchulidwa mwachindunji ndiyo pamene Yesu wazaka 12 zakubadwa anapezeka m’kachisi. Sizikutchulidwa kuti Yosefe analipo paphwando laukwati ku Kana, kuchiyambiyambi kwa utumiki wa Yesu. (Yohane 2:1-3) Mu 33 C.E., atapachikidwa, Yesu anapereka Mariya m’manja mwa mtumwi wake wokondedwa Yohane kuti am’samalire. Zikuoneka kuti Yesu sakanachita zimenezo zikanakhala kuti Yosefe anali adakali moyo.—Yohane 19:26, 27.
-
-
Kodi Muli ndi “Mtima Wa Kristu”?Nsanja ya Olonda—2000 | February 15
-
-
Kodi Muli ndi “Mtima Wa Kristu”?
“Mulungu wa chipiriro ndi wa chitonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi . . . monga mwa Kristu Yesu.”—AROMA 15:5.
1. Kodi Yesu amasonyezedwa kukhala munthu wotani m’zithunzi zambiri za Matchalitchi Achikristu, ndipo n’chifukwa chiyani kumeneko si kum’sonyeza bwino Yesu?
“PALIBE munthu anamuonapo akuseka.” Ndi mmene buku linalake limene monyenga limanena kuti linalembedwa kalekale ndi mkulu wina wa boma la Roma, linam’fotokozera Yesu. Buku limeneli, limene ladziŵika monga momwe lilili lerolino chiyambire zaka za zana la 11, akuti lakhudza akatswiri ambiri ojambula zithunzi.a Pazithunzi zambiri, Yesu amaoneka kukhala munthu wachisoni amene nthaŵi zambiri sanali kumwetulira, ngati anali kumwetulira n’komwe. Koma kumeneko si kum’sonyeza bwino Yesu, amene Mauthenga Abwino amam’sonyeza kukhala munthu wosangalala, wokoma mtima ndi wachifundo kwambiri.
2. Kodi tingakulitse motani ‘mtima umodzi monga mwa Kristu Yesu,’ ndipo zimenezi zidzatikonzekeretsa kuchita chiyani?
2 Ndithudi, kuti tim’dziwedi Yesu, tiyenera kudzaza malingaliro athu ndi mitima yathu ndi chidziŵitso cholongosoka ponena za mtundu wa munthu amene Yesu analidi pamene anali padziko lapansi. Chotero tiyeni tisanthule nkhani zina za m’Mauthenga Abwino zimene zimatipatsa chidziŵitso ponena za “mtima wa Kristu,” kutanthauza, mmene ankamvera mumtima, nzeru zake, maganizo ake, ndi zifukwa zake zochitira zinthu m’njira imeneyo. (1 Akorinto 2:16) Pamene tikutero, tiyeni tizilingalira mmene tingakulitsire “mtima umodzi . . . monga mwa Kristu Yesu.” (Aroma 15:5) Chotero, tingakhale okonzeka bwino m’moyo wathu komanso pochita zinthu ndi ena kuti titsatire chitsanzo chimene anatipatsa.—Yohane 13:15.
Wofikirika
3, 4. (a) Kodi nkhani yolembedwa pa Marko 10:13-16 inali pachochitika chotani? (b) Kodi Yesu anatani pamene ophunzira ake anayesa kuletsa tiana kuti tisafike kwa iye?
3 Anthu ankakopeka naye Yesu. Panthaŵi zosiyanasiyana, anthu amisinkhu yosiyanasiyana komanso ochokera uku ndi uku anali kum’fikira mosavuta. Talingalirani za chochitikachi chomwe chinalembedwa pa Marko 10:13-16. Chinachitika chakumapeto kwa utumiki wake pamene anali kupita ku Yerusalemu nthaŵi yomaliza, kukafa imfa yopweteka zedi.—Marko 10:32-34.
4 Tayerekezani chochitikacho. Anthu akuyamba kubweretsa ana, ngakhalenso makanda, kuti Yesu awadalitse anawo.b Komano ophunzira akuyesa kutsekereza kuti tianato tisafike kwa Yesu. Mwinamwake ophunzirawo akuganiza kuti Yesu sangalolere ana kumam’sokoneza m’milungu yovutitsitsa ngati imeneyi. Koma ophunzirawo alakwitsa. Yesu ataona zimene ophunzira akuchita, sakusangalala. Yesu akuitana tianato kwa iye, nati: “Lolani tiana tidze kwa Ine; musatiletse.” (Marko 10:14) Kenako akuchita kanthu kena komwe kakusonyeza mtima wake wachifundo ndi wachikondi zedi. Nkhaniyo imasimba kuti: “Iye anatiyangata [tianato], natidalitsa.” (Marko 10:16) Mosakayikira tianato tikusangalala pamene Yesu akutiyangata mosamala.
5. Kodi nkhani ya pa Marko 10:13-16 imatiuzanji ponena za mtundu wa munthu amene Yesu anali?
5 Nkhani imeneyo ikutiuza zinthu zambiri ponena za mtundu wa munthu amene Yesu anali. Mutha kuona kuti anali wofikirika. Ngakhale kuti anali pamalo apamwamba kumwamba, iye sanali woopsa kapena wopeputsa anthu opanda ungwiro. (Yohane 17:5) Kodi sizochititsanso chidwi kuti ngakhale ana anali omasuka kukhala pafupi naye? Ndithudi sakanakopeka ndi munthu wamsunamo, wosasangalala amene sanali kumwetulira kapena kuseka! Anthu amisinkhu yonse anali omasuka naye Yesu chifukwa anaona kuti iye anali munthu wachifundo, wosamala za ena, ndipo ankadziŵa bwino lomwe kuti sadzawanyalanyaza.
6. Kodi akulu angadzipangitse motani kukhala ofikirika kwambiri?
6 Poganizira nkhani imeneyi, tingadzifunse kuti, ‘Kodi ndili ndi mtima wa Kristu? Kodi ndine wofikirika?’ M’nthaŵi zovutazi, nkhosa za Mulungu zimafuna abusa ofikirika, amuna amene ali ngati “pobisalira mphepo.” (Yesaya 32:1, 2; 2 Timoteo 3:1) Akulu, ngati mukulitsa chidwi chenicheni, chochokera pansi pa mtima, pa abale anu ndipo ndinu wofunitsitsa kudzipereka m’malo mwawo, iwo adzaona kuti mumawadera nkhaŵa. Adzaona zimenezo mwa kaonekedwe ka nkhope yanu, kamvekedwe ka mawu anu, ndiponso mwa kukoma mtima kwanu. Chifundo ndiponso nkhaŵa yeniyeni imeneyi zingayambitse unansi wokhulupirirana umene ungapangitse ena, kuphatikizapo ana, kukufikirani momasuka. Mkazi wina wachikristu anafotokoza chifukwa chimene anayankhulira momasuka ndi mkulu wina: “Anandiyankhula mokoma mtima, mosonyeza chifundo. Mwina sindikanatchula liwu ndi limodzi lomwe. Anandipangitsa kusaopa kalikonse.”
Woganizira Ena
7. (a) Kodi Yesu anasonyeza motani kuti anali kuganizira ena? (b) Kodi Yesu ayenera kuti anachiritsa munthu wakhungu pang’onopang’ono pachifukwa chiti?
7 Yesu anali woganizira ena. Anali kusamala za mmene ena akumvera mumtima. Kungoona anthu ovutika kunkam’mvetsa chisoni kwambiri moti anali kusonkhezereka kuwathetsera mavuto awo. (Mateyu 14:14) Anali kuganiziranso ena pa zofooka zawo kapena zosoŵa zawo. (Yohane 16:12) Panthaŵi inayake, anthu anabwera ndi munthu wakhungu ndi kupempha Yesu kuti am’chiritse. Yesu anam’chiritsadi, koma anam’chiritsa pang’onopang’ono. Poyamba, munthuyo anayamba kungoona anthu mwachimbuuzi—“ayendayenda ngati mitengo.” Kenako Yesu anam’chiritsiratu ndipo anaona bwino. N’chifukwa chiyani anachiritsa munthuyo pang’onopang’ono? Ayenera kuti anachita zimenezi pofuna kuthandiza munthu amene anazoloŵera kungoona mdima kuti azoloŵere kuona dziko lowala ndi dzuŵa ndiponso lokhala ndi zinthu zambiri.—Marko 8:22-26.
8, 9. (a) N’chiyani chinachitika Yesu ndi ophunzira ake atangoloŵa m’dera la Dekapoli? (b) Longosolani mmene Yesu anachiritsira munthu wogontha.
8 Lingaliraninso za chinachake chimene chinachitika pambuyo pa Paskha wa 32 C.E. Yesu ndi ophunzira ake anali ataloŵa m’dera la Dekapoli, kum’maŵa kwa Nyanja ya Galileya. Posapita nthaŵi, chinamtindi cha anthu chinawapeza kumeneko ndipo anthuwo anabweretsera Yesu anthu ambiri odwala ndi opuwala, ndipo anawachiritsa onsewo. (Mateyu 15:29, 30) Koma chochititsa chidwi n’chakuti, Yesu anapatulapo munthu mmodzi kuti amuone mwapadera. Wolemba Uthenga Wabwino Marko, yekhayo amene analemba za chochitikachi, akusimba zimene zinachitika.—Marko 7:31-35.
9 Mwamunayo anali wogontha komanso wosatha kuyankhula. Yesu ayenera kuti anazindikira kuti munthuyo akuchita mantha kapena manyazi. Kenako Yesu anachita kanthu kena kachilendo ndithu. Anam’tengera pambali mwamuna ameneyu, kutali ndi gulu, poduka mphepo. Ndiyeno Yesu anapanga zizindikiro zina pofuna kusonyeza mwamunayo zimene anali pafupi kuchita. “[A]nalonga zala zake m’makutu mwake, nalavula malovu, nakhudza lilime lake.” (Marko 7:33) Kenako, Yesu anayang’ana kumwamba ndi kupemphera mousa moyo. Zizindikiro zimenezi zinali kuuza mwamunayo kuti, ‘Zimene nditi ndikuchitire zidzachitika mwamphamvu ya Mulungu.’ Pomalizira pake, Yesu anati: “Tatseguka.” (Marko 7:34) Pomwepo, makutu a mwamunayo anatseguka, ndipo anayambanso kuyankhula bwino.
10, 11. Kodi tingasonyeze motani kuganizira malingaliro a ena mumpingo? m’banja?
10 N’kuganiziratu ena kwakukulu komwe Yesu anasonyeza! Anali wosamala za mmene iwo akumvera mumtima, ndipo kuwaganizira mwachifundo kumeneku kunam’pangitsa kuchita zinthu m’njira imene sinawakhumudwitse kapena kuwachititsa manyazi. Monga Akristu, timachita bwino kukulitsa ndi kusonyeza mtima wa Kristu pankhani imeneyi. Baibulo limatilangiza kuti: “Khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa.” (1 Petro 3:8) Ndithudi, zimenezi zimafuna kuti tizilankhula ndi kuchita zinthu moganizira malingaliro a anthu ena.
11 Mumpingo, tingasonyeze kuganizira malingaliro a ena mwa kuwalemekeza, kuwachitira mmene timafunira kuti azitichitira. (Mateyu 7:12) Zimenezo zingaphatikizepo kusamala zimene tikunena komanso mmene tikuzinenera. (Akolose 4:6) Kumbukirani kuti ‘kulankhula mwansontho kungapyoze ngati lupanga.’ (Miyambo 12:18) Nanga bwanji m’banja? Mwamuna ndi mkazi wake amene amakondanadi amasamala kwambiri za malingaliro a wina ndi mnzake. (Aefeso 5:33) Amapeŵa mawu aukali, kusuliza kopitirira muyeso, ndi mawu onyoza, zonse zimene zingapute nsautso ya mumtima yovuta kwambiri kuithetsa. Ananso nawo ali ndi malingaliro, ndipo makolo achikondi amasamala za mmene anawo amamvera mumtima. Ngati m’pofunika kuwawongolera, makolo otero amawawongolera mowalemekeza anawo ndi kusawachititsa manyazi.c (Akolose 3:21) Tikamaganizira ena motero, timasonyeza kuti tili ndi mtima wa Kristu.
Wokonzeka Kukhulupirira Ena
12. Kodi Yesu anali ndi kaonedwe kabwino komanso koyenera kotani ka ophunzira ake?
12 Yesu anali ndi kaonedwe kabwino ndiponso koyenera ka ophunzira ake. Anali kudziŵa bwino lomwe kuti ndi opanda ungwiro. Komansotu paja amatha kudziŵa za mumtima wa munthu. (Yohane 2:24, 25) Ngakhale zinali motero, sanali kuyang’ana zophophonya zawo koma mikhalidwe yawo yabwino. Iye anaonanso kuti amuna amene Yehova anawakoka ameneŵa angathe kuchita zabwino. (Yohane 6:44) Kaonedwe kabwino ka Yesu ka ophunzira ake kanaonekera m’njira imene anali kukhalira nawo ndi mmene anali kuwatengera. Chinthu chimodzi n’chakuti, anasonyeza kuti ndi wokonzeka kuwakhulupirira.
13. Kodi Yesu anasonyeza motani kuti amakhulupirira ophunzira ake?
13 Kodi Yesu anasonyeza motani kuti amawakukhulupirira? Atachoka padziko lapansi, anapatsa ophunzira ake odzozedwawo udindo waukulu. Anawasiyira ntchito yosamalira zinthu za Ufumu wake zapadziko lonse. (Mateyu 25:14, 15; Luka 12:42-44) Panthaŵi ya utumiki wake, anasonyeza kuti amawakhulupirira, ngakhale pa zinthu zazing’ono zosanunkha kanthu. Pamene anachulukitsa chakudya mozizwitsa kuti adyetse makamu, anapatsa ophunzira ake udindo wogaŵa chakudyacho.—Mateyu 14:15-21; 15:32-37.
14. Kodi mungalongosole motani mwachidule nkhani yolembedwa pa Marko 4:35-41?
14 Lingaliraninso za nkhani yolembedwa pa Marko 4:35-41. Panthaŵi imeneyo Yesu ndi ophunzira ake anakwera ngalaŵa ndi kuloŵera cha kum’maŵa modutsa Nyanja ya Galileya. Atangoyenda pang’ono, Yesu anagona tulo kumchira kwa ngalaŵayo. Koma posapita nthaŵi, “panauka namondwe wamkulu wa mphepo.” Anamondwe ngati ameneŵa ankachitikachitika pa Nyanja ya Galileya. Popeza kuti nyanjayo ili potsika (mamita ngati 200 kuchokera pomwe pali nyanja zonse zikuluzikulu), mpweya ndi wotentha pamenepo kusiyana ndi mpweya wa pamtunda wozungulira nyanjayo, ndipo zimenezi zimapangitsa kusinthasintha kwa mphepo. Kuwonjezera apo, mphepo yamphamvu imawomba Chigwa cha Yordano kuchokera ku Phiri la Hermoni, limene lili chakumpoto. Mphindi ya bata ingasinthe mwadzidzidzi kukhala mphindi ya mkuntho. Talingalirani izi: Yesu mosakayikira ankadziŵa za anamondwe ameneŵa, popeza anakulira ku Galileya. Komabe, anagona tulo mtima uli m’malo, pokhulupirira maluso a ophunzira ake, amene ena mwa iwo anali asodzi.—Mateyu 4:18, 19.
15. Kodi tingatsanzire motani kukhulupirira ophunzira ake kwa Yesu?
15 Kodi tingatsanzire kukhulupirira ophunzira ake kwa Yesu? Ena amavutika kugaŵira anthu ena maudindo. Nthaŵi zonse amafuna kuti ntchito aziichita okha. Angamaganize kuti, ‘Ngati ndikufuna kuti ntchitoyo ichitike bwino, ndiyenera kuichita ndekha!’ Koma tikamachita tokha ntchito zonse, ndiye kuti tili pangozi ya kudzitopetsa mwinanso kusapeza nthaŵi yocheza ndi banja lathu pamene tinayenera kucheza nalo. Komanso, ngati sitigaŵira ena ntchito zina ndi maudindo ena oti tingawagaŵire, tingakhale tikuwamana chidziŵitso ndi maphunziro ofunika. Kungakhale kwanzeru kuphunzira kukhulupirira ena, kuwagawira ntchito zina. Tingachite bwino kudzifunsa moona mtima kuti, ‘Kodi ndili ndi mtima wa Kristu pankhani imeneyi? Kodi ndimapatsa ena ntchito zina, ndichikhulupiriro chakuti adzazichita monga momwe angathere?’
Anasonyeza Kuti Ophunzira Ake Amawadalira
16, 17. Usiku womaliza wa moyo wake wapadziko lapansi, kodi Yesu anawatsimikizira motani atumwi ake, ngakhale kuti ankadziŵa kuti iwo adzam’thaŵa?
16 Yesu anasonyeza kaonedwe kabwino ka ophunzira ake m’njira inanso yofunika kwambiri. Anawasonyeza kuti amawadalira. Zimenezi zinali zoonekeratu m’mawu owatsimikizira amene analankhulira atumwi ake usiku womaliza wa moyo wake wapadziko lapansi. Taonani zimene zinachitika.
17 Madzulo amenewo Yesu anali ndi zochita zambiri. Anapatsa atumwi ake phunziro la chitsanzo mwa kuwasambitsa mapazi awo. Kenako, anayambitsa chakudya chamadzulo chomwe chinali kudzakhala chikumbutso cha imfa yake. Komano, atumwi ake anayambanso mkangano wadzaoneni wotsutsana za amene akuoneka kukhala wamkulu pakati pawo. Poleza mtima monga kale, Yesu sanawathire mphepo koma anayankhula nawo mwanzeru. Anawauza zimene zidzachitika: “Inu nonse mudzakhumudwa chifukwa cha Ine usiku uno; pakuti kwalembedwa, Ndidzakantha mbusa, ndipo zidzabalalika nkhosa za gulu.” (Mateyu 26:31; Zekariya 13:7) Anadziŵa kuti abwenzi ake apamtimawo adzam’thaŵa panthaŵi yomwe adzawafunitsitsa. Koma sanawadzudzule. M’malo mwake, anawauza kuti: “Koma nditauka ndidzatsogolera inu ku Galileya.” (Mateyu 26:32) Inde, anawatsimikizira kuti ngakhale kuti adzam’thaŵa, iye sadzawasiya. Nsautso imeneyi ikadzapita, iye adzakumananso nawo.
18. Ku Galileya, kodi Yesu anasiyira ophunzira ake ntchito yaikulu iti, ndipo atumwi anaichita motani ntchito imeneyo?
18 Yesu anasunga mawu ake. Pambuyo pake, m’Galileya, Yesu woukitsidwayo anaonekera kwa atumwi ake 11, amene mwachionekere anasonkhana ndi enanso ambiri. (Mateyu 28:16, 17; 1 Akorinto 15:6) Kumeneko, Yesu anawapatsa ntchito yaikulu: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 28:19, 20) Buku la Machitidwe limatipatsa umboni womveka wakuti atumwi anaichitadi ntchito imeneyo. Mokhulupirika, iwo anatsogolera ntchito yolalikira uthenga wabwino m’zaka za zana loyamba.—Machitidwe 2:41, 42; 4:33; 5:27-32.
19. Kodi zochita za Yesu pambuyo pa chiukiriro chake zikutiphunzitsa chiyani ponena za mtima wa Kristu?
19 Kodi nkhani yolongosola zonse imeneyi ikutiphunzitsanji ponena za mtima wa Kristu? Yesu anawaona atumwi ake ali panthaŵi yawo yovuta koposa, komabe “anawakonda kufikira chimaliziro.” (Yohane 13:1) Mosasamala kanthu za zophophonya zawo, anawasonyeza kuti amawadalira. Mutha kuona kuti chidaliro cha Yesu sichinali cholakwika. Chidaliro ndi chikhulupiriro zimene anawasonyeza mosakayikira zinawalimbitsa kuti akhale otsimikizira kwambiri kuchita ntchito imene anawalamula kuchita.
20, 21. Kodi tingasonyeze motani kuti okhulupirira anzathu timawaona bwino?
20 Kodi tingasonyeze motani mtima wa Kristu pankhaniyi? Musamakayikire okhulupirira anzanu. Ngati mumawakayikira, zolankhula zanu ndi zochita zanu zidzasonyeza zimenezo. (Luka 6:45) Komabe, Baibulo limatiuza kuti chikondi “chikhulupirira zinthu zonse.” (1 Akorinto 13:7) Chikondi chimafunira ena zabwino, osati zoipa. Chimamangirira osati kugwetsa. Anthu amachitapo kanthu mofunitsitsa ngati asonyezedwa chikondi ndi kulimbikitsidwa osati ngati aopsezedwa. Tingamangirire ndi kulimbikitsa ena mwa kuwasonyeza kuti timawadalira. (1 Atesalonika 5:11) Ngati, monga Kristu, timawaona bwino abale athu, tidzawatenga m’njira zimene zidzawamangirira ndi kuwalimbikitsa kuchita zinthu zabwino kwambiri zimene angathe.
21 Kukulitsa ndi kusonyeza mtima wa Kristu kumafuna zambiri, osati kungoyerekeza kuchita zinthu zina zimene Yesu anachita. Monga momwe tatchulira kale m’nkhani yoyambayo, ngati tikufuna kuchitadi zinthu monga Yesu, choyamba tiyenera kuphunzira kuona zinthu monga momwe iye ankazionera. Mauthenga Abwino amatithandiza kuona mbali inanso ya umunthu wake, malingaliro ake ndi mmene ankamvera mumtima ponena za ntchito imene anapatsidwa, monga momwe nkhani yotsatira idzalongosolera.
[Mawu a M’munsi]
a M’cholembedwa chachinyengo chimenecho, wolemba wakeyo akufotokoza amene akuti ndiwo anali maonekedwe a Yesu, kuphatikizapo maonekedwe a tsitsi lake, ndevu zake, ndi maso ake. Wotembenuza Baibulo Edgar J. Goodspeed anafotokoza kuti chinyengo chimenechi “chinakonzedwa kuti anthu avomereze mafotokozedwe opezeka m’mabuku a malangizo a ojambula zithunzi onena za maonekedwe a Yesu.”
b Zikuoneka kuti anawo anali amisinkhu yosiyanasiyana. Panopo liwu lotembenuzidwa kuti “tiana” likugwiritsidwanso ntchito potchula mwana wamkazi wa Yairo wazaka 12 zakubadwa. (Marko 5:39, 42; 10:13) Koma posimba nkhani yofananayo ya ana, Luka akugwiritsa ntchito liwu lomwe limatanthauzanso makanda.—Luka 1:41; 2:12; 18:15.
c Onani nkhani yakuti “Kodi Mumawalemekeza?” m’kope la April 1, 1998, la Nsanja ya Olonda.
-
-
Kodi Mwasonkhezeredwa Kukhala Monga Yesu?Nsanja ya Olonda—2000 | February 15
-
-
Kodi Mwasonkhezeredwa Kukhala Monga Yesu?
“[A]naona khamu lalikulu la anthu, nagwidwa chifundo ndi iwo, chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo anayamba kuwaphunzitsa.”—MARKO 6:34.
1. N’chifukwa chiyani zili zomveka kuti anthu ena amasonyeza mikhalidwe yosiririka?
M’MBIRI yonse ya anthu, anthu ambiri asonyeza mikhalidwe yosiririka. Mutha kumvetsa chifukwa chake. Yehova Mulungu ali ndi chikondi, ndi wokoma mtima, wowoloŵa manja, komanso ali ndi mikhalidwe ina imene amaisonyeza ndipo timaithokoza. Anthu analengedwa m’chifanizo cha Mulungu. Choncho titha kuona chifukwa chake ambiri amatha kusonyeza mkhalidwe wa chikondi, chifundo, ndi mikhalidwe ina yaumulungu, monga momwe ambiri amasonyezera kuti ali ndi chikumbumtima. (Genesis 1:26; Aroma 2:14, 15) Komano, mungaone kuti ena amasonyeza kwambiri mikhalidwe imeneyi kuposa ena.
2. Kodi ndi ntchito zina zotani zimene anthu angachite, mwinanso akumaona kuti akutsanzira Kristu?
2 Muyenera kuti mumadziŵa amuna ndi akazi amene nthaŵi zambiri amachezera kapena kuthandiza odwala, kusonyeza chifundo kwa anthu opuwala, kapena amene amapatsa osauka mowoloŵa manja. Talingaliraninso za anthu amene chifukwa cha chifundo chawo amadzipereka kukagwira ntchito m’nyumba za anthu akhate kapena m’nyumba zosungiramo ana amasiye, aja amene amachita ntchito yodzifunira m’zipatala kapena kuthandiza anthu odwala matenda osachiritsika, kapenanso anthu amene amayesetsa kuthandiza anthu opanda nyumba kapena othaŵa kwawo chifukwa cha mavuto. Mwachionekere, ena a iwo amaona kuti akutsanzira Yesu, amene anapatsa Akristu chitsanzo. Timaŵerenga m’Mauthenga Abwino kuti Kristu anachiritsa odwala ndi kudyetsa anjala. (Marko 1:34; 8:1-9; Luka 4:40) Pamene Yesu anasonyeza chikondi ndi chifundo, iye anasonyeza “mtima wa Kristu,” amenenso anali kutsanzira Atate wake wakumwamba.—1 Akorinto 2:16.
3. Kuti tikhale ndi kaonedwe koyenera ka ntchito zabwino za Yesu, kodi tiyenera kulingalira za chiyani?
3 Koma kodi mwaona kuti ambiri lerolino amene asonkhezeredwa ndi chikondi ndi chifundo cha Yesu amanyalanyaza mbali yofunika kwambiri ya mtima wa Kristu? Tingamvetse zimenezi mwa kupenda Marko chaputala 6 mosamalitsa. Pamenepo timaŵerenga kuti anthu anabwera ndi anthu odwala kwa Yesu kuti awachiritse. Nkhani imeneyo imatisonyezanso kuti ataona kuti anthu zikwi zambiri amene anadza kwa iye anamva njala, Yesu anawadyetsa mozizwitsa. (Marko 6:35-44, 54-56) Kuchiritsa odwala ndi kudyetsa anjala zinali zisonyezero zapadera za chikondi ndi chifundo, koma kodi ndizo zinali njira zofunika kwambiri zimene Yesu anathandizira ena? Ndipo ndi motani mmene tingatsanzirire bwino kwambiri chitsanzo chake changwirocho cha chikondi, kukoma mtima, ndi chifundo, monga momwenso iye anatsanzirira Yehova?
Anasonkhezeredwa Kuthandiza pa Zosoŵa Zauzimu
4. Kodi nkhani ya pa Marko 6:30-34 inachitika motani?
4 Yesu anamvera chisoni anthu om’zinga makamaka chifukwa cha zosoŵa zawo zauzimu. Zosoŵa zimenezo ndizo zinali zofunika koposa, kuposanso zosoŵa zakuthupi. Talingalirani nkhani ya pa Marko 6:30-34. Chochitika chosimbidwa pamenepo chinachitikira pagombe la Nyanja ya Galileya, kutangotsala pang’ono kuti Paskha achitike mu 32 C.E. Atumwi anali osangalala, ndipotu pachifukwa chabwino. Popeza anali atangomaliza kumene kuchezera madera ambiri, anadza kwa Yesu, mosakayikira akufunitsitsa kum’simbira zimene akumana nazo. Komabe, khamu lalikulu la anthu linasonkhana. Linali lalikulu zedi moti Yesu ndi atumwi ake sanadye kapena kupumula. Yesu anauza atumwiwo kuti: “Idzani inu nokha padera ku malo achipululu, mupumule kamphindi.” (Marko 6:31) Atakwera ngalaŵa, mwina chapafupi ndi Kapernao, anapita kutsidya lina la Nyanja ya Galileya kumalo achete. Koma khamulo linathamanga m’mbali mwa gombelo ndi kufika kumeneko ngalaŵayo isanafike. Kodi Yesu anatani? Kodi anakhumudwa kuti akum’sokoneza panthaŵi yake yopuma? Kutalitali!
5. Kodi Yesu anamva bwanji poona makamu amene anadza kwa iye, ndipo anachitanji powathandiza?
5 Mtima wa Yesu unakhudzidwa poona khamu la anthu zikwi zambiri, kuphatikizapo odwala, amene anali kum’dikira mwachidwi. (Mateyu 14:14; Marko 6:44) Polongosola zimene zinapangitsa Yesu kumva chifundo ndi zimene Iye anachita, Marko analemba kuti: “[A]naona khamu lalikulu la anthu, nagwidwa chifundo ndi iwo, chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.” (Marko 6:34) Yesu anaona zambiri m’khwimbi la anthulo. Anaona anthu osoŵa mwauzimu. Iwo anali monga nkhosa zotayika zopanda wozithandiza, zopanda mbusa woti azitsogolere kumabusa obiriŵira kapena kuziteteza. Yesu anadziŵa kuti atsogoleri achipembedzo ouma mtimawo, amene anafunikira kukhala abusa osamala, anali kunyansidwa ndi anthu wambawo m’malo mwake ndipo ananyalanyaza zosoŵa zawo zauzimu. (Ezekieli 34:2-4; Yohane 7:47-49) Yesu anafuna kuwatenga m’njira yosiyana, kuwachitira zabwino zonse zomwe angathe. Anayamba kuwaphunzitsa za Ufumu wa Mulungu.
6, 7. (a) Kodi n’chiyani chimene Mauthenga Abwino amasonyeza kuti chinali chofunika kwambiri pa zimene Yesu anachitira anthu pa zosoŵa zawo? (b) Kodi n’chiyani chinasonkhezera Yesu kulalikira ndi kuphunzitsa?
6 Onani ndondomeko yake ndiponso chimene chikuoneka kukhala chofunika koposa chomwe chikuonekera m’nkhani inanso yofanana ndi imeneyo. Imeneyi inalembedwa ndi Luka, amene anali dokotala komanso wosamala kwambiri za thanzi la ena. ‘Unyinji wa anthu . . . anam’tsata [Yesu]; ndipo Iye anawalandira, nalankhula nawo za Ufumu wa Mulungu, nachiritsa amene anasoŵa kuchiritsidwa.’ (Luka 9:11; Akolose 4:14) Ngakhale kuti sizili motero ndi nkhani iliyonse yonena za chozizwitsa, panopa, kodi n’chiyani chimene nkhani youziridwa ya Luka inatchula kaye? Inali mfundo yakuti Yesu anaphunzitsa anthu.
7 Zimenezi zikugwirizana ndi mfundo yaikulu imene tikupeza pa Marko 6:34. Vesi limenelo limasonyeza bwino lomwe chinthu chachikulu chimene chinasonkhezera Yesu kuti amve chisoni. Anaphunzitsa anthuwo, kuwathandiza pa zosoŵa zawo zauzimu. Kuchiyambi kwa utumiki wake, Yesu anali atanena kuti: “Kundiyenera Ine ndilalikire Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu ku midzi inanso.” (Luka 4:43) Komanso, tingakhale tikulakwitsa kuganiza kuti Yesu analengeza uthenga wa Ufumu chabe chifukwa chakuti anapatsidwa ntchitoyo, ngati kuti anali kulalikira chabe chifukwa chakuti anauzidwa kutero. Ayi, chikondi chake ndi chifundo chake pa anthu ndicho chinali chisonkhezero chachikulu chogaŵanira nawo uthenga wabwino. Chinthu chabwino koposa chimene Yesu akanachita, ngakhale kwa odwala, ogwidwa ndi ziŵanda, osauka, kapena anjala, chinali kuwathandiza kudziŵa, kulandira, ndi kukonda choonadi chonena za Ufumu wa Mulungu. Choonadi chimenecho chinali chofunika koposa chifukwa cha zimene Ufumu udzachita pokweza uchifumu wa Yehova ndi kupereka madalitso osatha kwa anthu.
8. Kodi Yesu anali kuiona motani ntchito yake yolalikira ndi yophunzitsa?
8 Kulalikira za Ufumu mokangalika kumene Yesu anachita ndiko kunali chimodzi mwa zifukwa zazikulu zimene anadzera padziko lapansi. Chakumapeto kwa utumiki wake wapadziko lapansi, Yesu anauza Pilato kuti: “Ndinabadwira ichi Ine, ndipo ndinadzera ichi kudza ku dziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi choonadi. Yense wakukhala mwa choonadi amva mawu anga.” (Yohane 18:37) M’nkhani ziŵiri zoyambazo, taona kuti Yesu anali munthu wachifundo, wosamala kwambiri za ena, anali wofikirika, woganizira ena, wokhulupirira ena, komanso chachikulu pa zonse, wachikondi. Tiyenera kudziŵa mbali zimenezo za umunthu wake ngati tikufuna kumvetsadi mtima wa Yesu. Momwemonso n’kofunika kudziŵa kuti mtima wa Kristu ukuphatikizapo kutsogoza ntchito yake ya kulalikira ndi kuphunzitsa imene anachita.
Analimbikitsa Ena Kuchitira Umboni
9. Kodi ndani anayenera kuika patsogolo ntchito ya kulalikira ndi kuphunzitsa?
9 Kuika ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa patsogolo, monga njira yosonyezera chikondi ndi chifundo, sikunali kwa Yesu yekha. Iye analimbikitsa otsatira ake kuti atsanzire zolinga zake, zinthu zimene anaziika patsogolo, ndi zochita zake. Mwachitsanzo, Yesu atasankha atumwi ake 12, kodi iwo anayenera kuchitanji? Marko 3:14, 15 amatiuza kuti: ‘Anaika khumi ndi aŵiri, kuti akhale ndi Iye, ndi kuti akawatume kulalikira, ndi kuti akhale nawo ulamuliro wakutulutsa ziŵanda.’ Kodi mukuona kuti atumwi anayenera kutsogoza chiyani pamenepa?
10, 11. (a) Potumiza atumwi, kodi Yesu anawauza kuchitanji? (b) Ponena za kutumiza atumwi, kodi cholinga chachikulu chinali chiyani?
10 M’kupita kwa nthaŵi, Yesu anapatsa mphamvu anthu 12 amenewo kuti azichiritsa ena ndi kutulutsa ziŵanda. (Mateyu 10:1; Luka 9:1) Kenako anawatumiza kuti akayendere “nkhosa zosokera za banja la Israyeli.” Kukatani? Yesu anawalangiza kuti: “Pamene mulikupita lalikani kuti, Ufumu wa Kumwamba wayandikira. Chiritsani akudwala, ukitsani akufa, konzani akhate, tulutsani ziŵanda.” (Mateyu 10:5-8; Luka 9:2) Kodi n’chiyanidi chimene anachita? “Ndipo anatuluka [1] nalalikira kuti anthu atembenuke mitima. Ndipo [2] anatulutsa mizimu yoipa yambiri, nadzoza mafuta anthu ambiri akudwala nawachiritsa.”—Marko 6:12, 13.
11 Popeza kuti si pena paliponse pamene kuphunzitsa kukutchulidwa choyamba, kodi kulingalira zapamwambazo ndiko kukokomeza nkhani yokhudza zinthu zofunika kuziika patsogolo choyamba kapena zolinga zomwe tingakhale nazo? (Luka 10:1-9) Tisanyalanyazetu kuchuluka kwa nthaŵi zimene kuphunzitsa kukutchulidwa kaye asanatchule kuchiritsa. Pankhani yapamwambayo, tapendani zochitika zonse. Kutangotsala pang’ono kuti atumize atumwi ake 12, Yesu anali atamva chisoni ndi mkhalidwe wa makamuwo. Timaŵerenga kuti: “Yesu anayendayenda m’mizinda yonse ndi m’midzi, namaphunzitsa m’masunagoge mwawo, nalalikira uthenga wabwino wa Ufumuwo, nachiritsa nthenda iliyonse ndi zofooka zonse. Koma iye, poona makamuwo, anagwidwa m’mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa. Pomwepo ananena kwa ophunzira ake, Zotuta zichulukadi koma antchito ali oŵerengeka. Chifukwa chake pempherani Mwini zotuta kuti akokose antchito kukututa kwake.”—Mateyu 9:35-38.
12. Kodi zozizwitsa za Yesu ndi atumwi zinagwiranso ntchito ina yotani?
12 Pokhala ndi iye, atumwi anaphunzirako mbali zina za mtima wa Kristu. Iwo anatha kuona kuti kukhala kwawo achikondi chenicheni ndi achifundo kwa anthu kunaphatikizapo kulalikira ndi kuphunzitsa za Ufumu, imeneyo ndiyo inayenera kukhala mbali yaikulu ya ntchito zawo zabwino. Mogwirizana ndi zimenezo, ntchito zabwino zakuthupi, monga kuchiritsa odwala, sizinangothandiza osoŵawo. Monga momwe mungaonere, anthu ena akanakopeka ndi machiritso ndiponso chakudya choperekedwa mozizwitsa. (Mateyu 4:24, 25; 8:16; 9:32, 33; 14:35, 36; Yohane 6:26) Koma koposa kungokhala thandizo lakuthupi, ntchito zimenezo zinasonkhezeranso anthu oziona zikuchitikawo kuzindikira kuti Yesu anali Mwana wa Mulungu komanso “mneneri” amene Mose anam’losera.—Yohane 6:14; Deuteronomo 18:15.
13. Kodi ulosi wa pa Deuteronomo 18:18 unagogomeza ntchito iti ya “mneneri” yemwe anali kudzayo?
13 N’chifukwa chiyani mfundo yonena kuti Yesu ndiye anali “mneneri” ameneyo inali yofunika? Eya, kodi ntchito yaikulu imene ameneyo analoseredwa kuti adzaichita inali yotani? Kodi “mneneri” ameneyo anali kudzatchuka ndi machiritso ozizwitsa kapena kupangira anjala chakudya mwachifundo? Deuteronomo 18:18 analosera kuti: “Ndidzawaukitsira mneneri wa pakati pa abale awo, wonga iwe [Mose]; ndipo ndidzam’patsa mawu anga m’kamwa mwake, ndipo adzanena nawo zonse ndimuuzazi.” Chotero pamene kuli kwakuti atumwi anaphunzira kukhala ndi chifundo ndi chikondi komanso kuzisonyeza, iwo anazindikira kuti mtima wa Kristu unayenera kusonyezedwanso mwa ntchito yawo ya kulalikira ndi kuphunzitsa. Zimenezo ndizo zinali zinthu zabwino kwabasi zimene akanachitira anthu. Mwakutero, odwala ndi osauka anali kudzapeza mapindu osatha, osati ongopindulitsa moyo waufupi wa munthu kapena ongopeza chakudya nthaŵi zingapo zokha iyayi.—Yohane 6:26-30.
Khalani ndi Mtima wa Kristu Lerolino
14. Kodi kukhala ndi mtima wa Kristu kumaloŵamo motani m’kulalikira kwathu?
14 Palibe aliyense wa ife amene ayenera kuona mtima wa Kristu kukhala chinthu cha m’zaka za zana loyamba lokha, cha Yesu ndi ophunzira oyambirira okha amene mtumwi Paulo analemba kuti: “Ife tili nawo mtima wa Kristu.” (1 Akorinto 2:16) Ndipo tingavomereze ndi mtima wonse kuti tikulamulidwa kulalikira uthenga wabwino ndi kupanga ophunzira. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Komano ndi bwino kupenda zolinga zathu zochitira ntchitoyo. Sitiyenera kuichita kungoti popeza ndi ntchito imene tinapatsidwa. Kukonda Mulungu ndicho chifukwa chachikulu chimene timachitira nawo utumiki, ndipo kukhaladi monga Yesu kumaphatikizapo kusonkhezeredwa ndi chifundo kuti tilalikire ndi kuphunzitsa.—Mateyu 22:37-39.
15. N’chifukwa chiyani chifundo chili mbali yofunika ya utumiki wathu wapoyera?
15 Inde, nthaŵi zina zimavuta kumvera chifundo anthu amene sakhulupirira zimene timakhulupirira, makamaka ngati ndi amphwayi, amatikana, kapena ndi otsutsa. Komabe, kutaya chikondi ndi chifundo chathu pa anthu kungakhale kutaya chinthu chofunika kwambiri chotisonkhezera kutengamo mbali mu utumiki wachikristu. Chotero, kodi chifundo tingachikulitse motani? Tingayese kuona anthu monga momwe Yesu ankawaonera, monga “okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.” (Mateyu 9:36) Kodi si mmene anthu ambiri alili lerolino? Atsogoleri onyenga achipembedzo awanyalanyaza ndi kuwachititsa khungu. Ndiye chifukwa chake, iwo sakudziŵa kuti m’Baibulo muli chitsogozo chabwino kapenanso sakudziŵa za Paradaiso amene Ufumu wa Mulungu adzadzetsa padziko lapansi posachedwapa. Tsiku ndi tsiku amakumana ndi mavuto a m’moyo, kuphatikizapo umphaŵi, kusagwirizana kwa pabanja, matenda, ndi imfa, popanda kukhala ndi chiyembekezo cha Ufumu. Ifeyo tili ndi chimene akuchifunacho: uthenga wabwino wopulumutsa moyo wonena za Ufumu wa Mulungu umene tsopano uli wokhazikitsidwa kumwamba!
16. N’chifukwa chiyani tiyenera kufuna kugaŵirako ena uthenga wabwino?
16 Choncho mukaganizira za zosoŵa zauzimu za anthu okuzingani, kodi mtima wanu sukukusonkhezerani kufuna kuti muchite zonse zomwe mungathe kuti muwauze za chifuno chachikondi cha Mulungu? Inde, ntchito yathu ndi ntchito ya chifundo. Tikamachitira anthu chifundo monga momwe Yesu anachitira, zimenezo zidzaonekeratu mwa kamvekedwe ka mawu athu, kaonekedwe ka nkhope yathu, ndi kaphunzitsidwe kathu. Zonsezo zidzapangitsa uthenga wathu kukhala wosangalatsa kwambiri kwa awo “ofuna moyo wosatha.”—Machitidwe 13:48, NW.
17. (a) Kodi chikondi ndi chifundo chathu tingachisonyeze m’njira zina ziti kwa ena? (b) N’chifukwa chiyani si nkhani yongosankhapo kuchita ntchito zabwino kapena kuchita nawo utumiki wapoyera?
17 Komano chikondi ndi chifundo chathu ziyenera kuonekeradi m’njira yathu yonse ya moyo. Zimenezi zimaphatikizapo kukhala okoma mtima kwa anthu ovutika, odwala, ndi osauka—kuchita zomwe tingathe kuti tiwathandize pamavuto awo. Zimafuna kuyesetsa kwathu kwa mawu apakamwa ndi zochita zathu kuti titonthoze awo amene atayikidwa okondedwa awo mu imfa. (Luka 7:11-15; Yohane 11:33-35) Koma kusonyeza chikondi, kukoma mtima, ndi chifundo m’njira imeneyo sikuyenera kukhala chimake cha ntchito zathu zabwino, monga momwe zilili ndi anthu ena othandiza anthu ovutika. Zoyesayesa zopereka thandizo lokhalitsa zosonkhezeredwanso ndi mikhalidwe yaumulungu imodzimodziyo zimasonyezedwa mwa kuchita nawo ntchito yachikristu yolalikira ndi kuphunzitsa. Kumbukirani mawu a Yesu ponena za atsogoleri achipembedzo achiyuda akuti: “Mupereka limodzi la magawo khumi la timbewu tonunkhira, ndi katsabola, ndi la chitowe, nimusiya zolemera za chilamulo, ndizo kuweruza kolungama, ndi kuchitira chifundo, ndi chikhulupiriro; koma zijazo munayenera kuzichita, osasiya izi zomwe.” (Mateyu 23:23) Yesu sanasankhe kungochitapo chinthu chimodzi chokha, kaya kungothandiza anthu pazosoŵa zawo zakuthupi kapena kuwaphunzitsa zinthu zauzimu zopereka moyo, iyayi. Yesu anachita zonse ziŵiri. Ngakhale zinali motero, n’zoonekeratu kuti ntchito yake yophunzitsa ndiyo inali yofunika koposa chifukwa chakuti zinthu zabwino zimene anakwaniritsa mwantchitoyo zinali kudzakhala zothandiza kosatha.—Yohane 20:16.
18. Kodi kuphunzira za mtima wa Kristu kuyenera kutisokhezera kuchitanji?
18 Ndife othokoza zedi kuti Yehova wativumbulira mtima wa Kristu! Mwa Mauthenga Abwino, tingadziŵe bwino lomwe maganizo, za mumtima, mikhalidwe, zochita, ndi zinthu zimene munthu wamkulu woposa onse amene anakhalapo anaziika patsogolo. Zili ndi ife kuŵerenga, kusinkhasinkha, ndi kutsatira zimene Baibulo limavumbula ponena za Yesu. Kumbukirani kuti ngati tikufuna kuchitadi zinthu monga Yesu, choyamba tiyenera kuphunzira kalingaliridwe, kamvedwe ka mumtima, ndi kupenda zinthu monga ankachitira iyeyo, pamlingo wokwanira womwe tingathe monga anthu opanda ungwiro. Chotero tiyeni tikhale otsimikizira mumtima kuti tidzakulitsa ndi kusonyeza mtima wa Kristu. Palibe njira inanso yabwino kuposa imeneyi yokhalira ndi moyo, palibe njira inanso yabwino kuposa imeneyi yokhalira ndi anthu, ndipo palibe njira inanso yabwino kuposa imeneyi yoyandikirira kwa uyo amene Yesuyo anam’tsanzira mwangwiro, Mulungu wathu wachikondi ndi wachifundo, Yehova.—2 Akorinto 1:3; Ahebri 1:3.
-
-
Kodi Mwasonkhezeredwa Kukhala Monga Yesu?Nsanja ya Olonda—2000 | February 15
-
-
[Chithunzi chachikulu patsamba 23]
-