CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 ATESALONIKA 1-3
Wosamvera Malamulo Adzaonekera
Kodi Paulo ankanena za chiyani m’mavesi amenewa?
‘Chinachititsa kuti asaonekere’ (vesi 6)—Zikuoneka kuti anali atumwi
‘Anaonekera’ (vesi 6)—Pambuyo poti atumwi onse amwalira, Akhristu ampatuko anayamba kuphunzitsa zinthu zabodza komanso ankachita zachinyengo
“Chinsinsi cha kusamvera malamulo” (vesi 7)—M’nthawi ya Paulo, anthu sankadziwa bwinobwino kuti “wosamvera malamuloyo” ndi ndani
‘Wosamvera malamulo’ (vesi 8)—Masiku ano, wosamvera malamulo ameneyu ndi atsogoleri azipembedzo onse pamodzi
“Ambuye Yesu adzamuthetsa [wosamvera malamuloyo] . . . pa nthawi imene kukhalapo kwa Yesuyo kudzaonekere” (vesi 8)—Yesu adzasonyeza kuti iyeyo ndi mfumu akadzayamba kupereka chiweruzo kudziko la Satanali kuphatikizapo ‘wosamvera malamulo’
Kodi mavesiwa akuthandizani bwanji kuti muzilalikira modzipereka komanso mwachangu?