Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 10/15 tsamba 21
  • Chidziŵitso pa Nyuzi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chidziŵitso pa Nyuzi
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Si Achikale
  • “Kulangika Koposa”
  • Kulemekeza Mulungu
  • Tchalitchi cha Anglican cha ku Australia Nyumba Yogaŵanika
    Galamukani!—1993
  • Phunzirani ndi Kuphunzitsa Ena Makhalidwe Abwino Achikristu
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Mtima Wodzipereka Umabweretsa Madalitso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Kodi Zipembedzo za Dziko Zikupereka Chitsogozo Choyenera?
    Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 10/15 tsamba 21

Chidziŵitso pa Nyuzi

Si Achikale

Anthu ambiri kwanthaŵi yaitali asunga kawonedwe kakuti maprinsipulo akakhalidwe kabwino ondandalitsidwa m’Baibulo ali achikale ndi osagwira ntchito. Ngakhale kuli tero, maphunziro aposachedwa apangitsa maulamuliro a zamankhwala ena kulingaliranso za phindu la uphungu wa Baibulo wakuchita zabwino kwa ena.

Mogwirizana ndi American Health, adokotala aŵiri anadzinenera kuti “kuchita zabwino kungakhale kwabwino kaamba ka mtima wanu, dongosolo lanu la thupi lochinjiriza​—ndi mphamvu zanu zonse.” Mu Michigan gulu lina la zamankhwala linachita kufufuza likumatenga nyengo ya zaka khumi kugamulapo kuti ndi ku ukulu wotani kumene unansi wa mayanjano umayambukirira umoyo. Chopeza chodabwitsa chinali chakuti kugwira ntchito kwaufulu m’chitaganya mozizwitsa kunawonjezera kuyembekezera kwa moyo ndiponso mphamvu. Ofufuzawo anavumbula kuti amuna anayambukiridwa mwapadera. Awo amene sanachite ntchito yaufulu ananenedwa kukhala nthaŵi ziŵiri ndi theka othekera kufa mkati mwa nyengo ya kufufuzako kuposa amuna amene anachita mtundu wina wa ntchito yaufulu chifupifupi kamodzi pa mlungu.

Dokotala mu California wasimba kuti kukonza kwake kaamba ka odwala aŵiri omwe sanakondane wina ndi mnzake kuchapirana zovala kunali ndi chotulukapo cha kuchepetsa mlingo wawo wa mafuta a m’thupi nd kupweteka kwa m’chifuŵa.

Zaka mazana angapo zapitazo mtumwi Paulo anauza Timoteo “kulamulira iwo achuma m’nthaŵi ino ya pansi pano kuti asadzikuze, kapena asayembekezere chuma chosadziŵika kukhala kwake,” koma “kuti achite zabwino, nachuluke ndi ntchito zabwino, nakondwere kugawira ena, nayanjane.” Iye anakumbutsanso Akristu a Chihebri kusaiwala “kuchita chokoma ndi kugawira ena.” Chifukwa chake? “Ulemerero ndi ulemu ndi mtendere kwa munthu aliyense wakuchita zabwino.” Akristu owona adziŵa kwa nthaŵi yaitali kuti kulabadira uphungu wa panthaŵi yake umenewu kumabweretsa mapindu ponse paŵiri akuthupi ndi auzimu.​—1 Timoteo 6:17, 18; Ahebri 13:16; Aroma 2:10.

“Kulangika Koposa”

Ziwalo za General Synod ya Tchalitchi cha Anglican posachedwapa zinadzipeza izo zeni ziri m’tsoka loipa. Iwo anakhala atalankhula movomereza m’chiyanjo cha “kuphunzitsa kwa mwambo pa chiyero ndi kukhulupirika m’maunsi aumwini.” Ngakhale kuli tero, pamene wansembe wa pa tchalitchipo Tony Higton anapereka lingaliro kufunsa likulu la tchalitchilo kulengeza kuti atsogoleri onse a chipembedzo ayenera kukhala “opereka chitsanzo m’mbali zonse za makhalidwe abwino, kuphatikizapo makhalidwe abwino a kugonana, monga mkhalidwe wa kukhala oikidwa kapena kukhalabe pa ntchito yawo,” ilo linakanidwa. Chifukwa chake? Ecumenical Press Service ikusimba kuti ziwalo za likulu la tchalitchilo zinapeza chifunsirocho “kukhala champhamvu kwambiri,” zikumawonjezera kuti “Michael Baughen, bishopo wa ku Chester, analingalira kuti chikafunikira kuleka kugwira ntchito kwa mwamsanga kwa a bishopo a tchalitchi onsewo ndi atsogoleri ena a chipembedzo.”

M’malomwake, lingaliro la Higton linasinthidwa kuitanira pa Akristu onse, “makamaka . . . atsogoleri Achikristu,” kukhala zitsanzo “m’mbali zonse za makhalidwe abwino, kuphatikizapo makhalidwe abwino a kugonana.” Press Service inadziŵitsanso kuti likulu la tchalitchilo linagonjetsa chiitano kaamba ka “chilango choyenera” pakati pa atsogoleri a chipembedzo m’nkhani za mkhalidwe woipa wa chisembwere.

Pamene kuli kwakuti miyezo yolanga imeneyo ingakhale “yamphamvu kwambiri” kaamba ka ambiri a atsogoleri a chipembedzo a lerolino, Mawu a Mulungu ali achimvekere: “chotsani woipayo pakati pa inu nokha.” (1 Akorinto 5:13) Mulungu akutsogoza kuti kachitidwe kamphamvu kayenera kutengedwa motsutsana ndi onse amene mosalapa amachita chimene chiri cholakwa kuti achinjirize chiyero cha makhalidwe abwino ndi chiyero chauzimu cha mpingo wa Chikristu. Ndithudi, chilango chiri chofunikira koposa kaamba ka atsogoleri Achikristu, popeza wophunzira Yakobo analemba kuti: “Musakhale aphunzitsi ambiri, abale anga, podziŵa kuti tidzalangika koposa.”​—Yakobo 3:1.

Kulemekeza Mulungu

“Mtundu wa kachitidwe ka othamanga ungavumbule mtundu wachikondi chake kaamba ka Mulungu.” Kodi kudzinenera kumeneku kwa Wes Neal, prezidenti wa IAP (Institute for Atheletic Perfection), monga mmene kunasimbidwira mu Christianity Today, nkowona? IAP, bungwe logwiritsiridwa ntchito ndi alaliki “kuyeretsa maseŵera opikisana,” lapititsa patsogolo lingaliro lakuti othamanga pa bwalo la za maseŵera ayenera kutsanzira kuyesetsa kofananako kumene Yesu anasonyeza kulinga ku “kukwaniritsa chifuno cha Atate wake.” Kulingalira koteroko kwakhala chiphunzitso chofala cha “chipembedzo cha m’chipinda chodzitsekera” cha alaliki, yadziŵitsa tero Christianity Today. M’chenicheni, nkhaniyo ikugwira mawu chitsanzo cha katswiri mmodzi woseŵera mpira wa chitanyu yemwe “analemba ndi utoto mitanda pa nsapato zake ndi zovala m’chiwuno monga chikumbutso chakuti iye anali kuseŵera kulemekeza Kristu.”

Ngakhale kuli tero, kodi chinganenedwe kuti kutenga mbali m’maseŵera opikisana mopambana kapena achiwawa kuli kulemekeza Mulungu? Kutalitali! Monga mmene Psychology Today yadziŵitsira: “Mtundu weniweniwo wa kupikisana umafunikira kuti chikondwerero chaumwini chitengedwe kwa kanthaŵi pamene wothamangayo akulalamira kupambana.” Komabe Baibulo limanena kuti Akristu ayenera “kumayang’anitsitsa, osati mokondwera ndi zinthu [zawo] zokha, komanso mokondwera ndi zija za ena.” (Afilipi 2:3,4, NW) Akristu owona amalemekeza Mulungu mwa kuchita chifuniro chake, osati chawo.​—Yerekezani ndi Ysaya 58:13, 14.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena