Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 1/15 tsamba 23-28
  • Kuthandiza Ena Kuphunzira Zimene Mulungu Amafuna

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuthandiza Ena Kuphunzira Zimene Mulungu Amafuna
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Nkovuta Koma si Mtolo Wolemetsa
  • Okonzekera Bwino Kuthandiza Ena
  • Kupenda Chiŵiya Chatsopano
  • Gwiritsani Ntchito Kabuku Kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Chiŵiya Chatsopano Chothandiza Nacho Anthu Kuphunzira Zimene Mulungu Amafuna
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Thandizani Osoŵa Chidziŵitso Kuti Azindikire
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Lengezani Uthenga Wabwino wa Ufumu ndi Mabrosha
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 1/15 tsamba 23-28

Kuthandiza Ena Kuphunzira Zimene Mulungu Amafuna

“Chondikakamiza ndigwidwa nacho; pakuti tsoka ine ngati sindilalikira Uthenga Wabwino.”​—1 AKORINTO 9:16.

1, 2. (a) Kodi ndi ntchito ya mbali ziŵiri iti imene Yehova akufuna kuti tigaŵanemo? (b) Kodi anthu oona mtima ayenera kuphunziranji kuti akhale nzika za Ufumu wa Mulungu?

YEHOVA ali ndi uthenga wabwino kwa anthu. Ali ndi Ufumu, ndipo akufuna kuti anthu kulikonse amve za ufumuwo! Titaphunzira uthenga wabwino umenewo, Mulungu amafuna kuti tiuze ena. Imeneyi ndi ntchito ya mbali ziŵiri. Choyamba, tiyenera kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Mu ulosi wake wonena za “mathedwe a nthaŵi ya pansi pano,” Yesu anati: “Uthenga uwu wabwino wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.”​—Mateyu 24:3, 14.

2 Mbali yachiŵiri ya ntchito imeneyi imaloŵetsamo kuphunzitsa awo amene amalabadira chilengezo cha Ufumu. Ataukitsidwa, Yesu anauza khamu lalikulu la ophunzira ake kuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.” (Mateyu 28:19, 20) ‘Zinthu zimene Kristu analamulira’ sizinachokere kwa iye; anaphunzitsa ena kusunga malamulo a Mulungu, kapena zofuna zake. (Yohane 14:23, 24; 15:10) Chotero, kuphunzitsa ena ‘kusunga zinthu zimene Kristu analamula’ kumaphatikizamo kuwathandiza kuphunzira zimene Mulungu amafuna. Anthu oona mtima ayenera kufika pa zofuna za Mulungu kuti akhale nzika za Ufumu wake.

3. Kodi Ufumu wa Mulungu nchiyani, ndipo udzachitanji chimene chimapangitsa uthenga wa Ufumuwo kukhala uthenga wabwino kwambiri?

3 Kodi Ufumu wa Mulungu nchiyani? Ndipo udzachitanji chimene chimapangitsa uthenga wa Ufumu kukhala wabwino kwambiri? Ufumu wa Mulungu ndi boma lakumwamba. Uli wamtengo wapatali kwa Yehova, pakuti ndiwo njira imene adzayeretsera dzina lake, kulichotsa chitonzo chonse. Ufumuwo ndiwo chiŵiya chimene Yehova adzagwiritsira ntchito kuti chifuniro chake chichitike padziko lapansi monga kumwamba. Nchifukwa chake Yesu anatiphunzitsa kupemphera kuti Ufumu wa Mulungu udze ndi kuuika patsogolo m’moyo wathu. (Mateyu 6:9, 10, 33) Kodi mukuona chifukwa chake zili zofunika kwambiri kwa Yehova kuti ife tiphunzitse ena za Ufumu wake?

Nkovuta Koma si Mtolo Wolemetsa

4. Kodi tingapereke chitsanzo chotani kusonyeza kuti thayo lathu la kulalikira uthenga wabwino si mtolo wolemetsa?

4 Kodi ndi mtolo wolemetsa kulalikira uthenga wabwino umenewu? Kutalitali! Tinene mwachitsanzo: Tate ali ndi thayo la kupezera banja lake zofunika zakuthupi. Kulephera kuchita zimenezo kumatanthauza kukana chikhulupiriro chachikristu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupira.” (1 Timoteo 5:8) Koma kodi thayo limenelo ndi mtolo wolemetsa kwa mwamuna wachikristu? Osati ngati amakonda banja lake, pakuti amafuna kuwasamalira.

5. Ngakhale kuti ntchito yolalikira ndi kupanga ophunzira ndi thayo, nchifukwa ninji tiyenera kukondwa pogaŵanamo?

5 Mofananamo, ntchito yolalikira ndi kupanga ophunzira ndi thayo, chofunika, chimene moyo wathu umadalirapo kwambiri. Paulo ananena motere: “Chondikakamiza ndigwidwa nacho; pakuti tsoka ine ngati sindilalikira uthenga wabwino.” (1 Akorinto 9:16; yerekezerani ndi Ezekieli 33:7-9.) Komabe, chimene chimatisonkhezera kulalikira ndicho chikondi, osati thayo chabe. Makamaka, timakonda Mulungu, koma timakondanso anansi athu, ndipo tidziŵa kuti kuli kofunika kwambiri kuti iwo amve uthenga wabwino. (Mateyu 22:37-39) Umawapatsa chiyembekezo cha mtsogolo. Ufumu wa Mulungu posachedwapa udzawongolera chisalungamo chonse, kuchotsa chitsenderezo chonse, ndi kubwezeretsa mtendere ndi umodzi​—zonsezo kaamba ka dalitso losatha kwa awo ogonjera ulamuliro wake wolungama. Kodi sitili okondwa, inde osangalala kuuza ena uthenga wabwino umenewo?​—Salmo 110:3.

6. Nchifukwa ninji ntchito yolalikira ndi kupanga ophunzira ili yovuta?

6 Komabe, ntchito yolalikira ndi yopanga ophunzira imeneyi ndi yovuta. Anthu amasiyana. Amakonda zosiyanasiyana ndipo ali ndi maluso osiyanasiyana. Ena ngophunzira kwambiri, pamene ena sali ophunzira kwenikweni. Kuŵerenga​—kumene panthaŵi ina kunali kosangulutsa popuma​—tsopano kukuonedwa kukhala ntchito. Mphwayi ya kuŵerenga ikukhala vuto lalikulu, ngakhale m’maiko omwe amadzitama kukhala ndi ophunzira ochuluka. Chotero, kodi tingawathandize motani anthu aziyambi ndi zokonda zosiyanasiyana kuti aphunzire zimene Mulungu amafuna?​—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 9:20-23.

Okonzekera Bwino Kuthandiza Ena

7. Kodi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” watikonzekeretsa motani kuti tithandize ena kuphunzira zimene Mulungu amafuna?

7 Ntchito yovuta imagwirika mosavuta ngati muli ndi ziŵiya kapena zipangizo zoyenera. Chiŵiya chimene chili choyenera pantchito ina lero, mmaŵa chingasinthidwe kapena kuchotsedwa chifukwa cha kusintha kwa mikhalidwe. Chimodzimodzi ndi ntchito yathu yolengeza uthenga wa Ufumu wa Mulungu. Pa zaka zambiri, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” watipatsa ziŵiya zoyenera, zofalitsa zogwiritsira ntchito pochititsa maphunziro a Baibulo apanyumba. (Mateyu 24:45) Chotero tili okonzekera kuthandiza anthu a “mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi . . . manenedwe” kuti aphunzire zimene Mulungu amafuna. (Chivumbulutso 7:9) Nthaŵi ndi nthaŵi, zipangizo zina zaperekedwa kusamalira zosoŵa zomasintha m’munda wa padziko lonse. Tiyeni tipende zitsanzo zingapo.

8. (a) Kodi buku lakuti “Mulungu Akhale Woona” linathandiza motani kuphunzitsa Baibulo? (b) Kodi ndi chipangizo chotani chophunzitsira Baibulo chimene chinaperekedwa mu 1968, ndipo cholinga chake makamaka chinali chiyani? (c) Kodi buku la Coonadi linathandiza motani pa ntchito yopanga ophunzira?

8 Kuchokera mu 1946 mpaka 1968, buku lakuti “Mulungu Akhale Woona” linagwiritsiridwa ntchito monga chipangizo champhamvu chophunzitsira Baibulo, ndipo makope 19,250,000 anafalitsidwa m’zinenero 54. Buku la Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya, lofalitsidwa mu 1968, linagwira bwino ntchito zaka zambiri kuphunzitsira okondwerera Baibulo. Kumbuyoku, sizinali zachilendo kuona anthu ena akuphunzira ndi Mboni za Yehova kwa zaka zambiri osabatizidwa. Koma chipangizo chimenechi chinakonzedwa moti nkuloŵetsamo wophunzirayo, kumlimbikitsa kugwiritsira ntchito zimene anali kuphunzira. Chotulukapo? Buku lakuti Jehovah’s Witnesses​—Proclaimers of God’s Kingdom limati: “Kwa zaka zitatu zautumiki kuyambira pa September 1, 1968, mpaka August 31, 1971, anthu okwanira 434,906 anabatizidwa​—oposa kuŵirikiza chiŵerengero cha obatizidwa pazaka zitatu zautumiki zapitazo!” Chitulukire chake, buku la Coonadi lafalitsidwa pa chiŵerengero chodabwitsa​—choposa 107,000,000 m’zinenero 117.

9. Kodi ndi mbali yapadera yotani imene buku la Kukhala ndi Moyo Kosatha lili nayo, ndipo linakhala ndi chotulukapo chotani kwa olengeza Ufumu?

9 Mu 1982 buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi linakhala buku lalikulu lochititsira maphunziro a Baibulo. Chiŵiya chimenechi chili ndi zithunzi zoposa 150, chilichonse ndi mawu ake omveketsa bwino mfundo yake ya zithunzizo. Utumiki Wathu Waufumu wachingelezi wa October 1982 unati: “Pa zaka pafupifupi 20 zimene ‘Mulungu Akhale Woona’ linali buku lathu lalikulu lophunzitsira (kuchokera mu 1946 mpaka chapakati pa ma 1960) olengeza Ufumu atsopano oposa 1,000,000 anawonjezeredwa kwa ife. Ndiyeno ofalitsa ena 1,000,000 anawonjezeredwa pamene Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya linakhala buku lalikulu lophunzitsira litatuluka mu 1968. Mwa kugwiritsira ntchito buku lathu lophunziramo latsopano, Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, kodi tidzaona chiwonjezeko chofananacho cha ofalitsa Ufumu? Tidzaterodi, ngati chimenechi chili chifuniro cha Yehova!” Mwachionekere, chinalidi chifuniro cha Yehova, chifukwa kuyambira mu 1982 mpaka 1995, oposa 2,700,000 anawonjezedwa pa alengezi a Ufumu!

10. Kodi ndi chiŵiya chatsopano chotani chimene chinaperekedwa mu 1995, ndipo nchifukwa ninji chiyenera kutheketsa ophunzira Baibulo kupita patsogolo mwauzimu mwamsanga?

10 “Zotuta zichulukadi koma antchito ali oŵerengeka,” anatero Yesu. (Mateyu 9:37) Zotutazo nzochulukadi. Padakali ntchito yaikulu. M’maiko ena anthu amachita kulembedwa pampambo woyembekeza maphunziro a Baibulo. Motero, pokhala ndi cholinga cha kufalitsa chidziŵitso chonena za Mulungu mofulumira kwambiri, mu 1995 “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” anapereka chiŵiya chatsopano, buku la masamba 192 la mutu wakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Chipangizo chothandiza kwambiri chimenechi sichimasumika pa ziphunzitso zonyenga. Chimafotokoza choonadi cha Baibulo m’njira yolimbikitsa. Tikhulupirira kuti chidzathandiza ophunzira Baibulo kupita patsogolo mofulumira m’zauzimu. Buku la Chidziŵitso layamba kale kukhala ndi chiyambukiro chachikulu pa munda wa dziko lonse ndi makope 45,500,000 osindikizidwa m’zinenero 125 ndipo lili mkati mwa kutembenuzidwa m’zinenero zina 21.

11. Kodi ndi chiŵiya chothandiza chotani chimene chinaperekedwa chothandizira osaphunzira kapena osatha kuŵerenga bwino, ndipo icho chathandiza motani pantchito yathu yophunzitsa ya padziko lonse?

11 Nthaŵi ndi nthaŵi, ‘kapolo wokhulupirika’ wapereka ziŵiya zothandizira anthu akutiakuti, kapena gulu lochepa la anthu. Mwachitsanzo, bwanji za anthu omwe angafunikire chithandizo chapadera chifukwa cha mwambo kapena chipembedzo chawo? Kodi tingawathandize bwanji kuphunzira zimene Mulungu amafuna? Mu 1982 tinalandira chimene tinafunikiradi​—brosha la masamba 32 lakuti Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! Chofalitsa cha zithunzi zochuluka chimenechi chakhala chiŵiya chothandiza pophunzitsa anthu osaphunzira kapena osadziŵa kuŵerenga bwino. Limalongosola mwa njira yosavuta ziphunzitso zoyambirira za Malemba. Chitulukire chake, brosha la Moyo pa Dziko Lapansi lathandiza kwambiri pantchito yathu yophunzitsa ya padziko lonse. Makope oposa 105,100,000 asindikizidwa m’zinenero 239, likumakhala chofalitsa cha Watch Tower Society chotembenuzidwa m’zinenero zambiri koposa china chilichonse kufikira lero!

12, 13. (a) Chiyambire 1990, “kapolo wokhulupirika” wapereka njira yatsopano yotani yofikira anthu ochuluka? (b) Kodi tingagwiritsire ntchito motani vidiyo ya Sosaite mu utumiki wathu wakumunda? (c) Kodi ndi chiŵiya chatsopano chotani chimene chinaperekedwa posachedwapa chotithandiza pantchito yathu yopanga ophunzira?

12 Kuwonjeza pa zofalitsa zosindikiza, kuyambira mu 1990 ‘kapolo wokhulupirika ndi wanzeru’ watipatsa njira yotilangizira imene imapereka njira yatsopano yofikira anthu ambiri​—mavidiyokaseti. Mu October chaka chimenecho, vidiyo ya mphindi 55 yakuti Jehovah’s Witnesses​—The Organization Behind the Name inatuluka​—vidiyo yoyamba kutulutsidwa ndi Watch Tower Society. Filimu yake yokongola ndi yopatsa chidziŵitso, yopezeka m’zinenero pafupifupi 35, imasonyeza kakonzedwe ka anthu odzipereka a Yehova akumakwaniritsa lamulo la Yesu la kulengeza uthenga wabwino padziko lonse lapansi. Cholinga cha vidiyoyo makamaka ndicho kutithandiza pantchito yathu yopanga ophunzira. Ofalitsa Ufumu sanataye nthaŵi iliyonse kuti ayambe kugwiritsira ntchito chiŵiya chatsopano chimenechi mu utumiki wakumunda. Ena anainyamula m’zola zawo za mabuku, ali okonzeka nthaŵi zonse kuisonyeza kapena kuibwereka kwa okondwerera. Itangotulutsidwa, woyang’anira woyendayenda wina analemba kuti: “Mavidiyo akhala njira ya m’zaka za zana la 21 yofikira maganizo ndi mitima ya anthu mamiliyoni ambiri, choncho tikhulupirira kuti vidiyo imeneyi idzangokhala yoyamba pampambo wautali wa mavidiyo omwe Sosaite idzagwiritsira ntchito kufutukula ntchito ya Ufumu padziko lonse.” Ndithudi, mavidiyo owonjezereka aperekedwa, kuphatikizapo ya mbali zitatu yakuti The Bible​—A Book of Fact and Prophecy ndi Jehovah’s Witnesses Stand Firm Against Nazi Assault. Ngati mavidiyo a Sosaite alipo m’chinenero chanu, kodi mwawagwiritsirapo ntchito mu utumiki wanu wakumunda?a

13 Posachedwapa chiŵiya chatsopano, brosha lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?, linaperekedwa kuti litithandize pantchito yathu yopanga ophunzira. Kodi nchifukwa ninji linafalitsidwa? Kodi lingagwiritsiridwe ntchito motani?

Kupenda Chiŵiya Chatsopano

14, 15. Kodi brosha lakuti Mulungu Amafunanji lakonzedwera ndani, ndipo lili ndi chiyani mkati mwake?

14 Chofalitsa chatsopanocho Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? chakonzedwera anthu okhulupirira kale Mulungu amene amalemekeza Baibulo. Oyang’anira oyendayenda limodzinso ndi amishonale a ku Gileadi omwe atumikira m’maiko omatukuka kwa zaka zambiri anathandiza kukonza brosha limeneli. Lili ndi kosi yokwanira bwino, yophunzitsa ziphunzitso zoyambirira za Baibulo. Mafotokozedwe ake ali osavuta kumva, ndipo olunjika. Ngakhale ndi choncho, mawu ake sali ofeŵa mopambanitsa. Limagaŵira osati “mkaka” wokha komanso “chakudya chotafuna” cha Mawu a Mulungu m’njira imene anthu ambiri akhoza kumva.​—Ahebri 5:12-14.

15 M’zaka zaposachedwapa ofalitsa Ufumu m’maiko osiyanasiyana anafunsira chofalitsa choterocho. Mwachitsanzo, nthambi ya Watch Tower Society ku Papua New Guinea inalemba kuti: “Anthu ali osokonezeka ndi ziphunzitso zowombana za zipembedzo. Amafuna mawu achidule a choonadi, ochirikizidwa ndi malemba angapo a m’Baibulo amene angadziŵerengere okha m’ma Baibulo awo. Amafuna malongosoledwe omveka ndi olunjika a zimene Mulungu amafuna kwa Akristu oona ndi kuwauza miyambo ndi machitachita amene iye samafuna.” Brosha la Mulungu Amafunanji ndilo lofunika kwa ife kuti tithandize oterowo kuphunzira zimene Mulungu amafuna.

16. (a) Kodi ndani makamaka amene angapindule ndi malongosoledwe osavuta a m’brosha latsopanolo? (b) Kodi a m’gawo lanu angapindule motani ndi brosha la Mulungu Amafunanji?

16 Kodi mungachigwiritsire ntchito motani chipangizo chatsopano chimenechi? Choyamba, mungachigwiritsire ntchito kuphunzira ndi anthu opeza vuto kuŵerenga kapena amphwayi ya kuŵerenga.b Anthu oterowo angapindule ndi mafotokozedwe osavuta kumva m’broshalo. Zitapenda kope loyambirira la chofalitsachi, nthambi za Watch Tower zinalemba kuti: “Broshali lidzakhala lothandiza kwambiri m’mbali zambiri za dziko kumene anthu samakonda kuŵerenga kwambiri.” (Brazil) “Pali alendo ambiri ochokera kumaiko ena osadziŵa kuŵerenga chinenero chawo komanso osatha kuŵerenga bwino Chifrenchi. Broshali lingagwiritsiridwe ntchito monga chothandiza pophunzira ndi anthu otero.” (France) Kodi mungaganizire anthu m’gawo lanu omwe angaphindule ndi brosha la Mulungu Amafunanji?

17. Kodi brosha latsopanoli lingagwiritsiridwe ntchito m’njira yotani m’maiko ambiri, ndipo chifukwa ninji?

17 Chachiŵiri, m’maiko ambiri broshalo lingathandize kuyambitsira maphunziro a Baibulo kwa anthu oopa Mulungu mosasamala kanthu za maphunziro awo. Inde, pafunikira khama kuti tiyambitse phunziro m’buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Koma nthaŵi zina kungakhale kopepuka kuyamba phunziro m’broshalo. Ndiyeno panthaŵi yoyenera, phunzirolo liyenera kusamukira m’buku la Chidziŵitso, buku lathu lalikulu lophunziramo ndi lokondeka kwambiri. Ponena za kugwiritsira ntchito brosha la Mulungu Amafunanji m’njira imeneyi, nthambi za Watch Tower zinalemba kuti: “Kuyamba maphunziro a Baibulo nkovuta, ndipo mipata yoyambitsira phunziro imaoneka kukhalapo yaikulu pamene ofalitsa ayamba ndi brosha.” (Germany) “Brosha la mtundu umenewu lidzakhala lothandiza kwambiri kuyambitsa maphunziro a Baibulo, amene pambuyo pake angapitirizidwe m’buku la Chidziŵitso.” (Italy) “Ngakhale kuti Ajapani ndi ophunzira kwambiri, ochuluka amadziŵa zochepa kwambiri za Baibulo ndi ziphunzitso zake zoyambirira. Broshalo liyenera kukhala ulalo wabwino wowolokera ku buku la Chidziŵitso.”​—Japan.

18. Kodi tiyenera kukumbukiranji za kukwaniritsa zimene Mulungu amafuna?

18 Nthambi za Sosaite kuzungulira dziko lonse zinapempha brosha limeneli, ndipo chivomerezo chapatsidwa kuti litembenuzidwe m’zinenero 221. Chofalitsa chatsopano chimenechi chikhaletu chotithandiza kuthandiza ena kuti aphunzire zimene Yehova Mulungu amafuna kwa iwo. Ifenso tikumbukire kuti kukwaniritsa zofuna za Mulungu, kuphatikizapo lamulo lakulalikira ndi kupanga ophunzira, kumatipatsa mwaŵi wapadera wakusonyeza Yehova mmene timamukondera. Inde, zimene Mulungu amafuna kwa ife si mtolo wolemetsa ayi. Ndiyo njira yabwino koposa ya moyo!​—Salmo 19:7-11.

[Mawu a M’munsi]

a Buku lakuti Jehovah’s Witnesses​—Proclaimers of God’s Kingdom limati: “Mavidiyokaseti sakuloŵa m’malo zosindikiza kapena ulaliki wa munthu mwini. Zofalitsa za Sosaite zikupitiriza kuchita mbali yaikulu pakulalikira uthenga wabwino. Ntchito ya kunyumba ndi nyumba ya Mboni za Yehova idakali mbali ya utumiki wawo yozikidwa zolimba m’Malemba. Komabe, mavidiyokaseti tsopano akuthandizira monga ziŵiya zokulitsira chikhulupiriro m’malonjezo amtengo wapatali a Yehova ndi kusonkhezera chiyamikiro pa zimene wachita padziko lapansi m’tsiku lathu.”

b Onani malongosoledwe a kachitidwe ka phunziro m’brosha la Mulungu Amafunanji, m’nkhani yakuti “Chiŵiya Chatsopano Chothandiza Nacho Anthu Kuphunzira Zimene Mulungu Amafuna,” pamasamba 16-17.

Kodi Mungafotokoze?

◻ Kodi ndi ntchito ya mbali ziŵiri iti imene Yehova amafuna kuti atumiki ake atengemo mbali?

◻ Kodi nchifukwa ninji thayo lathu la kulalikira ndi kupanga ophunzira silili mtolo wolemetsa kwa ife?

◻ Kodi “Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wapereka ziŵiya zotani zoti tigwiritsire ntchito pantchito yathu yolalikira ndi kupanga ophunzira?

◻ Kodi brosha la Mulungu Amafunanji lakonzedwera ndani, ndipo tingaligwiritsire ntchito motani mu utumiki wathu?

[Chithunzi patsamba 24]

Ntchito yathu yolalikira ndi kupanga ophunzira siili mtolo wolemetsa

[Zithunzi patsamba 26]

“Mulungu Akhale Woona” (1946, lokonzedanso mu 1952): 19,250,000 m’zinenero 54 (Losonyezedwali ndi Chingelezi)

Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya (1968): 107,000,000 m’zinenero 117 (Losonyezedwali ndi Chifrenchi)

Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi (1982): 80,900,000 m’zinenero 130 (Losonyezedwali ndi Chirasha)

Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha (1995): 45,500,000 m’zinenero 125 (Losonyezedwali ndi Chijeremeni)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena