Akazi Achikristu Ayenera Kuchitiridwa Ulemu
“Amuna inu, khalani nawo monga mwa chidziŵitso, ndi kuchitira mkazi ulemu, monga chotengera chochepa mphamvu.”—1 PETRO 3:7.
1, 2. (a) Kodi kukambitsirana kwa Yesu ndi mkazi Msamariya pachitsime kunasonkhezera nkhaŵa yotani, ndipo chifukwa ninji? (Onani mawu amtsinde.) (b) Mwa kulalikira kwa mkazi Msamariya, kodi Yesu anasonyezanji?
MASANA ena cha kumapeto kwa 30 C.E. pachitsime chakale pafupi ndi mzinda wa Sukari, Yesu anasonyeza malingaliro ake ponena za mmene akazi ayenera kuchitiridwa. Iye anali atathera mmaŵa wake paulendo wopyola dziko la zitunda la Samariya ndi kufika pachitsimepo ali wotopa, wanjala, ndi waludzu. Ali chikhalire pachitsimepo, mkazi wina Msamariya anafika kudzatunga madzi. “Undipatse ine ndimwe,” Yesu anatero kwa iye. Mkaziyo ayenera kukhala atamyang’ana modabwa. Anafunsa kuti: “Bwanji inu, muli Myuda, mupempha kwa ine kumwa, ndine mkazi Msamariya?” Pambuyo pake, pamene ophunzira ake anafika kuchokera kokagula chakudya, anazizwa, poona kuti Yesu “analinkulankhula ndi mkazi.”—Yohane 4:4-9, 27.
2 Kodi nchiyani chimene chinasonkhezera funso la mkazi ameneyu ndi nkhaŵa ya ophunzirawo? Iyeyo anali Msamariya, ndipo Ayuda sanali kudyerana ndi Asamariya. (Yohane 8:48) Koma mwachionekere panalinso chifukwa china chodera nkhaŵa. Panthaŵiyo, mwambo wachirabi unaletsa amuna kulankhula ndi akazi poyera.a Komabe, Yesu mwapoyera analalikira mkazi woona mtima ameneyu, akumamuululiradi kuti anali Mesiya. (Yohane 4:25, 26) Motero Yesu anasonyeza kuti sanamangidwe ndi miyambo yosachirikizidwa ndi malemba, kuphatikizapo ija imene inachepetsa akazi. (Marko 7:9-13) M’malo mwake, pa zimene anachita ndi zimene anaphunzitsa, Yesu anasonyeza kuti akazi ayenera kuchitiridwa ulemu.
Mmene Yesu Anachitira ndi Akazi
3, 4. (a) Kodi ndimotani mmene Yesu anachitira ndi mkazi amene anakhudza chovala chake? (b) Kodi ndimotani mmene Yesu anaperekera chitsanzo chabwino kwa amuna Achikristu, makamaka oyang’anira?
3 Chifundo cha Yesu kwa anthu chinasonyezedwa ndi mmene anachitira ndi akazi. Panthaŵi ina mkazi wina amene anadwala nthenda ya kukha mwazi kwa zaka 12 anafunafuna Yesu pakati pa khamu. Nthenda yake inampangitsa kukhala wodetsedwa mwamwambo, chotero anali wosayenera kukhala pamenepo. (Levitiko 15:25-27) Koma iye anafunitsitsa kuchira kwakuti anadza kumbuyo kwa Yesu. Pamene anakhudza chovala chake, anachira nthaŵi yomweyo! Ngakhale kuti Yesu anali paulendo wake wa kunyumba ya Yairo, amene mwana wake wamkazi anadwala kwakayakaya, Yesu anaima. Pomva mphamvu ikutuluka mwa iye, anaunguzaunguza kuti aone amene anamkhudza. Ndiyeno, mkaziyo anadza nagwada pamaso pake akunthunthumira. Kodi Yesu anamzazira chifukwa cha kukhala pakati pa khamulo kapena chifukwa cha kukhudza chofunda chake popanda chilolezo? Ayi, m’malo mwake iye anali wachikondi ndi wachifundo kwa mkaziyo. “Mwana wamkaziwe,” iye anatero, “chikhulupiriro chako chakuchiritsa.” Imeneyi inali nthaŵi yokha imene Yesu anatchula mkazi mwachindunji kukhala “mwana wamkazi.” Mawu amenewo ayenera kukhala atamkhazika mtima pansi chotani nanga mkaziyo!—Mateyu 9:18-22; Marko 5:21-34.
4 Yesu analingalira zoposa pa Chilamulo. Anaona mzimu umene unali kuseri kwake ndi kufunika kwa chisoni ndi chifundo. (Yerekezerani ndi Mateyu 23:23.) Yesu anaona mkhalidwe wa kuthedwa nzeru wa mkazi wodwalayo ndipo anaona kuti anasonkhezeredwa ndi chikhulupiriro. Chotero iye anapereka chitsanzo chabwino kwa amuna Achikristu, makamaka oyang’anira. Ngati mlongo Wachikristu akulimbana ndi vuto laumwini kapena mkhalidwe wina wovuta kwambiri kapena woyesa, akulu ayenera kuyesayesa kuona zoposa mawu ndi machitidwe apanthaŵiyo ndi kulingalira za mikhalidwe ndi zolinga zake. Luntha lotero lingasonyeze kuti mwina kuleza mtima, kumvetsetsa, ndi chifundo ndizo zimene zikufunika m’malo mwa kupereka uphungu ndi kuwongolera.—Miyambo 10:19; 16:23; 19:11.
5. (a) Kodi akazi anali omangika motani ndi miyambo yachirabi? (Onani mawu amtsinde.) (b) Kodi ndani amene anali oyamba kuona ndi kuchitira umboni za kuuka kwa Yesu?
5 Pokhala omangika ndi miyambo yachirabi, akazi okhalako pamene Yesu anali pa dziko lapansi analetsedwa kukhala mboni pamlandu.b Tangolingalirani zimene zinachitika Yesu atangoukitsidwa kwa akufa mmaŵa pa Nisani 16, 33 C.E. Kodi ndani amene anakhala oyamba kuona Yesu woukitsidwa ndi kuchitira umboni kwa ophunzira ena kuti Ambuye wawo anali atauka? Anali akazi amene anaimirira pafupi ndi malo opachikira kufikira pamene anamwalira.—Mateyu 27:55, 56, 61.
6, 7. (a) Kodi Yesu anawauzanji akazi amene anadza kumanda? (b) Kodi ophunzira a Yesu achimuna anachita motani poyamba ndi umboni wa akaziwo, ndipo tingaphunzirenji pa zimenezi?
6 Mmamaŵa pa tsiku loyamba la mlunguwo, Mariya wa Magadala ndi akazi ena anamka kumanda ndi zonunkhira kuti akadzoze thupi la Yesu. Atapeza mandawo ali apululu, Mariya anathamanga kukauza Petro ndi Yohane. Akazi enawo anatsala. Posapita nthaŵi, mngelo anaonekera kwa iwo ndi kuwauza kuti Yesu anali atauka. “Pitani msanga, muuze ophunzira ake,” mngeloyo analangiza motero. Pamene akazi ameneŵa anali kupita mofulumira kukapereka mbiriyo, Yesu mwiniyo anaonekera kwa iwo. “Pitani, kauzeni abale anga,” anawauza motero. (Mateyu 28:1-10; Marko 16:1, 2; Yohane 20:1, 2) Posadziŵa za kufika kwa mngeloko ndi kugwidwa ndi chisoni, Mariya wa Magadala anabwerera kumanda. Yesu anaonekera kwa iye kumeneko, ndipo potsirizira pake iyeyo atamzindikira, Yesu anati: “Pita kwa abale anga, ukati kwa iwo, Ndikwera kumka kwa Atate wanga, ndi Atate wanu, ndi Mulungu wanga, ndi Mulungu wanu.”—Yohane 20:11-18; yerekezerani ndi Mateyu 28:9, 10.
7 Yesu akanatha kuonekera choyamba kwa Petro, Yohane, kapena kwa mmodzi wa ophunzira ena achimuna. M’malo mwake, anasankha kuyanja akazi ameneŵa mwa kuwapanga mboni zoyamba zoona ndi maso za chiukiriro chake ndi mwa kuwatuma kukachitira umboni za icho kwa ophunzira ake achimuna. Kodi amunawo anachita motani poyamba? Nkhaniyo imati: “Mawu awa anaoneka pamaso pawo ngati nkhani zachabe, ndipo sanamvera akaziwo.” (Luka 24:11) Kodi chinali chifukwa chakuti anapeza umboniwo kukhala wovuta kuuvomereza chifukwa unachokera kwa akazi? Ngati ndi choncho, m’kupita kwa nthaŵi, iwo analandira umboni wochuluka wakuti Yesu anali atauka kwa akufa. (Luka 24:13-46; 1 Akorinto 15:3-8) Lerolino, amuna Achikristu amachita mwanzeru pamene alingalira pa malingaliro a alongo awo auzimu.—Yerekezerani ndi Genesis 21:12.
8. Kodi Yesu anasonyezanji ndi njira imene anachitira ndi akazi?
8 Nkokondweretsadi kuona njira imene Yesu anachitira ndi akazi. Pokhala wachifundo nthaŵi zonse ndi wochita zinthu moyenera ndi akazi, iye sanawakweze kapena kuwachepetsa. (Yohane 2:3-5) Anakana miyambo yachirabi imene inawalanda ulemu wawo ndi imene inapeputsa Mawu a Mulungu. (Yerekezerani ndi Mateyu 15:3-9.) Mwa kuchitira akazi ulemu, Yesu anasonyeza mwachindunji zimene Yehova Mulungu amafuna kuti iwo azichitiridwa. (Yohane 5:19) Yesu anaperekanso chitsanzo chabwino kwambiri kwa amuna Achikristu choti achitsanzire.—1 Petro 2:21.
Ziphunzitso za Yesu Zonena za Akazi
9, 10. Kodi Yesu anatsutsa motani miyambo yachirabi yonena za akazi, ndipo ananenanji Afarisi atadzutsa funso lonena za chisudzulo?
9 Yesu anatsutsa miyambo yachirabi ndi kulemekeza akazi osati ndi zochita zake zokha komanso ndi ziphunzitso zake. Mwachitsanzo, lingalirani zimene anaphunzitsa ponena za chisudzulo ndi chigololo.
10 Ponena za chisudzulo, Yesu anafunsidwa funso: “Kodi nkuloledwa kuti munthu achotse mkazi wake pa chifukwa chilichonse?” Malinga ndi kusimba kwa Marko, Yesu anati: “Munthu aliyense akachotsa mkazi wake [kosakhala chifukwa cha chigololo], nakakwatira wina, achita chigololo kulakwira mkaziyo; ndipo ngati mkazi akachotsa mwamuna wake, nakwatiwa ndi wina, achita chigololo iyeyu.” (Marko 10:10-12; Mateyu 19:3, 9) Mawu onenedwa amenewo anasoneyeza kuchitira ulemu akazi. Motani?
11. Kodi mawu a Yesu akuti “kosakhala chifukwa cha chigololo” amasonyezanji ponena za chomangira cha ukwati?
11 Choyamba, mwa mawu akuti “kosakhala chifukwa cha chigololo” (opezeka m’nkhani ya Uthenga Wabwino wa Mateyu), Yesu anasonyeza kuti chomangira cha ukwati sichiyenera kuonedwa mopepuka kapena kudulidwa mosavuta. Chiphunzitso chaurabi chimene chinalipo chinaloleza kusudzula mkazi pa zifukwa zazing’ono zonga kupsereretsa chakudya kapena kulankhula ndi mwamuna wachilendo. Eetu, chisudzulo chinkaloledwa ngakhale ngati mwamuna wapeza mkazi amene anali wokongola kwa iye! Katswiri wina wa Baibulo akunena kuti: “Pamene Yesu analankhula motero anali . . . kuchirikiza akazi mwa kufuna kubwezeretsa ukwati pamalo ake ofunika.” Indedi, ukwati uyenera kukhala mgwirizano wosatha mu umene mkazi angamve kukhala wotetezereka.—Marko 10:6-9.
12. Kodi Yesu anali kupereka lingaliro lotani mwa kunena mawu akuti “achita chigololo kulakwira mkaziyo”?
12 Chachiŵiri, mwa kunena kuti “achita chigololo kulakwira mkaziyo,” Yesu anasonyeza lingaliro limene linali losavomerezedwa ndi mabwalo amilandu achirabi—lingaliro lakuti mwamuna wochita chigololo alakwira mkazi wake. The Expositor’s Bible Commentary ikulongosola kuti: “M’Chiyuda cha chirabi mkazi wochita chigololo analakwira mwamuna wake; ndipo mwamuna, wogonana ndi mkazi wa mwini, analakwira mwamuna winayo. Koma mwamuna sanali kulakwira mkazi wake konse ndi chigololo, pa chilichonse chimene anachita. Yesu, mwa kuika mwamuna pansi pa thayo la kusunga makhalidwe mofanana ndi mkazi, anakweza malo ndi ulemu wa akazi.”
13. Ponena za chisudzulo, kodi ndimotani mmene Yesu anasonyezera kuti pansi pa dongosolo Lachikristu, padzakhala muyezo umodzi wa amuna ndi akazi omwe?
13 Chachitatu, mwa mawu akuti “akachotsa mwamuna wake,” Yesu anasonyeza kuyenera kwa mkazi kwa kusudzula mwamuna wosakhulupirika—mchitidwe umene mwachionekere unali wodziŵika komano wosafala pansi pa lamulo Lachiyuda m’tsikulo.c Kunanenedwa kuti “mkazi akhoza kusudzulidwa kaya afuna kapena safuna, koma mwamuna pamene iye yekha afuna.” Komabe, malinga ndi kunena kwa Yesu, pansi pa dongosolo Lachikristu, muyezo umodzimodziwo unagwira ntchito kwa amuna ndi akazi omwe.
14. Kodi Yesu anasonyezanji ndi ziphunzitso zake?
14 Ziphunzitso za Yesu zimasonyeza bwino kwambiri nkhaŵa yakuya kaamba ka ubwino wa akazi. Chotero, nkosavuta kumvetsa chifukwa chake akazi ena anakonda kwambiri Yesu kwakuti anachirikiza zosoŵa zake ndi chuma chawo. (Luka 8:1-3) “Chiphunzitso changa sichili changa,” Yesu anatero, “koma cha iye amene anandituma ine.” (Yohane 7:16) Yesu anasonyeza chisamaliro chachikondi cha Yehova kwa akazi mwa zimene anaphunzitsa.
‘Kuwachitira Ulemu’
15. Kodi nchiyani chimene mtumwi Petro analemba ponena za mmene amuna ayenera kuchitira ndi akazi awo?
15 Mtumwi Petro anadzionera ndi maso mmene Yesu anachitira ndi akazi. Zaka 30 pambuyo pake, Petro anapatsa akazi uphungu wachikondi ndiyeno analemba kuti: “Amuna inu, khalani nawo monga mwa chidziŵitso, ndi kuchitira mkazi ulemu, monga chotengera chochepa mphamvu, monganso woloŵa nyumba pamodzi wa chisomo cha moyo, kuti mapemphero anu angaletsedwe.” (1 Petro 3:7) Kodi Petro anatanthauzanji ndi mawuwo ‘kuwachitira ulemu’?
16. (a) Kodi tanthauzo la nauni Yachigiriki yotembenuzidwa kuti “ulemu” njotani? (b) Kodi Yehova analemekeza motani Yesu pa kusandulika, ndipo timaphunziranji pamenepa?
16 Malinga ndi kunena kwa wolemba dikishonale wina, nauni Yachigiriki yotembenuzidwa kuti “ulemu” (ti·meʹ) imatanthauza “mtengo, kuŵerengera, ufulu, kulemekeza.” Mipangidwe ina ya mawu Achigiriki ameneŵa imamasuliridwa kuti “mphatso” ndi “mtengo wake.” (Machitidwe 28:10, NW; 1 Petro 2:7) Timadziŵa tanthauzo la kuchitira ulemu munthu wina ngati tipenda mmene Petro anagwiritsirira ntchito mpangidwe wina wa mawu amodzimodziwo pa 2 Petro 1:17. Pamenepo iye anati potchula za kusandulika kwa Yesu: “Analandira kwa Mulungu Atate ulemu ndi ulemerero, pakumdzera iye mawu otere ochokera ku ulemerero waukulu, Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene ine ndikondwera naye.” Pa kusandulika kwa Yesu, Yehova anachitira ulemu Mwana wake mwa kunena mawu osonyeza kuyanja kwake Yesu, ndipo Mulungu anatero ena akumamva. (Mateyu 17:1-5) Pamenepo, mwamuna amene amachitira ulemu mkazi wake samamchititsa manyazi kapena kumtsitsa. M’malo mwake, iye amasonyeza mwa mawu ndi zochita zake—kuseri ndi poyera—kuti amamuŵerengera kwambiri.—Miyambo 31:28-30.
17. (a) Kodi nchifukwa ninji ulemu uli woyenerera kwa mkazi Wachikristu? (b) Kodi nchifukwa ninji mwamuna sayenera kulingalira kuti ali wofunika kwambiri pamaso pa Mulungu kuposa mmene mkazi alili?
17 Ulemu umenewu, Petro akutero, uyenera ‘kuchitidwa’ ndi amuna Achikristu kwa akazi awo. Uyenera kuperekedwa, osati monga kungowakomera mtima chabe, koma monga mangawa awo kwa akazi awo. Kodi nchifukwa ninji akazi amayenerera ulemu wotero? Chifukwa “[muli, NW] monganso woloŵa nyumba pamodzi wa chisomo cha moyo,” akufotokoza motero Petro. M’zaka za zana loyamba C.E., akazi ndi amuna amene analandira kalata ya Petro onse anaitanidwa kukhala oloŵa nyumba pamodzi ndi Kristu. (Aroma 8:16, 17; Agalatiya 3:28) Iwo sanasenze mathayo amodzimodziwo mumpingo, koma potsirizira pake anali kudzakhala ndi phande m’kulamulira ndi Kristu kumwamba. (Chivumbulutso 20:6) Lerolinonso, pamene ochuluka a anthu a Mulungu ali ndi chiyembekezo cha pa dziko lapansi, kukakhala kulakwa kwakukulu kwa mwamuna Wachikristu aliyense kulingalira kuti chifukwa cha mathayo omwe angakhale nawo mumpingo, ndiye kuti ali wofunika kwambiri pamaso pa Mulungu kuposa mmene akazi alili. (Yerekezerani ndi Luka 17:10.) Amuna ndi akazi ali ndi kaimidwe kauzimu kofanana pamaso pa Mulungu, pakuti imfa yansembe ya Yesu inatsegulira amuna ndi akazi omwe mwaŵi wofanana—uja wa kukhala omasulidwa pa chiweruzo cha uchimo ndi imfa, wokhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha.—Aroma 6:23.
18. Kodi ndi chifukwa chokakamiza chotani chimene Petro akupereka kwa mwamuna cha kuchitira ulemu mkazi wake?
18 Petro akupereka chifukwa china chokakamiza mwamuna kuchitira ulemu mkazi wake, “kuti mapemphero [ake] angaletsedwe.” Mawu akuti ‘kuletsedwa’ achokera m’verebu Yachigiriki (en·koʹpto) imene kwenikweni imatanthauza “kudula.” Malinga ndi kunena kwa Expository Dictionary of New Testament Words ya Vine, “inagwiritsiridwa ntchito pa anthu ochedwetsa mwa kuwononga msewu, kapena mwa kuika chopinga pakati pa njira.” Chifukwa chake, mwamuna amene amalephera kuchitira ulemu mkazi wake angapeze kuti pali chopinga pakati pa mapemphero ake ndi khutu la Mulungu. Mwamunayo angamve kukhala wosayenera kufikira Mulungu, kapena Yehova angakhale wosafuna kumvetsera. Mwachionekere, Yehova amadera nkhaŵa kwambiri ndi mmene amuna amachitira ndi akazi.—Yerekezerani ndi Maliro 3:44.
19. Kodi ndimotani mmene amuna ndi akazi mumpingo angatumikire pamodzi molemekezana?
19 Thayo la kusonyeza ulemu silili pa amuna pokha. Pamene kuli kwakuti mwamuna ayenera kuchitira ulemu mkazi wake mwa kumchitira mwachikondi ndi ulemu, mkazi ayenera kuchitira ulemu mwamuna wake mwa kukhala womvera ndi kusonyeza kuwopa. (1 Petro 3:1-6) Ndiponso, Paulo analangiza Akristu “kuchitira wina mnzake ulemu.” (Aroma 12:10) Limeneli ndi pempho kwa amuna ndi akazi mumpingo kuti azitumikira pamodzi molemekezana. Pamene mzimu wotero ukhalapo, akazi Achikristu samanena mawu onyoza ulamuliro wa awo amene amatsogolera. M’malo mwake amachirikiza akulu ndi kugwirizana nawo. (1 Akorinto 14:34, 35; Ahebri 13:17) Pochita mbali yawo, oyang’anira Achikristu adzachitira “akazi aakulu ngati amayi; akazi aang’ono ngati alongo, m’kuyera mtima konse.” (1 Timoteo 5:1, 2) Mwanzeru, akulu adzalingalira mokoma mtima pa mawu a alongo awo Achikristu. Motero, pamene mlongo asonyeza kulemekeza kwake umutu wateokrase nafunsa funso mwaulemu kapena ngakhale pamene asonyeza kanthu kena kofuna kukasamalira, akulu mwachimwemwe adzalingalira za funso lakelo kapena vutolo.
20. Malinga ndi mbiri ya m’Malemba, kodi akazi ayenera kuchitiridwa motani?
20 Chiyambire pamene uchimo unaloŵa mu Edene, akazi m’mafuko ambiri atsitsidwa ndi kusapatsidwa ulemu. Koma mkhalidwe umenewo sindiwo umene Yehova anawalinganizira pachiyambi. Mosasamala kanthu za malingaliro a miyambo amene angakhalepo kulinga kwa akazi, mbiri ya m’Malemba Achihebri ndi Achigiriki Achikristu imasonyeza bwino lomwe kuti akazi owopa Mulungu ayenera kuchitiridwa ulemu. Ndiwo mangawa awo amene Mulungu amafuna kuti azipatsidwa.
[Mawu a M’munsi]
a The International Standard Bible Encyclopedia imalongosola kuti: “Akazi sanadye ndi alendo achimuna, ndipo amuna analetsedwa kulankhula ndi akazi. . . . Kucheza ndi akazi poyera kunalidi konyansa.” Mishnah Yachiyuda, mpambo wa ziphunzitso zachirabi, unalangiza kuti: “Musalankhule kwambiri ndi akazi. . . . Munthu amene amalankhula kwambiri ndi akazi amadzibweretsera tsoka ndipo amanyalanyaza kuphunzira Chilamulo ndipo potsirizira adzaloŵa ku Gehena.”—Aboth 1:5.
b Buku lakuti Palestine in the Time of Christ likunena kuti: “M’zochitika zina, mkazi anali kuonedwa ngati kapolo. Mwachitsanzo, iye analetsedwa kupereka umboni m’bwalo lachiweruzo, kusiyapo kupereka umboni wa imfa ya mwamuna wake.” Ponena za Levitiko 5:1, The Mishnah ikufotokoza kuti: “[Lamulo lonena za] ‘lumbiro la umboni’ limagwira ntchito kwa amuna koma osati kwa akazi.”—Shebuoth 4:I.
c Wolemba mbiri Wachiyuda wa m’zaka za zana loyamba Josephus akusimba kuti mlongo wake wa Mfumu Herode, Salome anatumizira mwamuna wake “chikalata chothetsa ukwati wawo, chinthu chimene chinali chosagwirizana ndi lamulo Lachiyuda. Pakuti kwa ife mwamuna (yekha) ndiye amene amaloledwa kuchita zimenezi.”—Jewish Antiquities, XV, 259 [vii, 10].
Kodi Yankho Lanu Nlotani?
◻ Kodi ndi zitsanzo zotani zimene zimasonyeza kuti Yesu anachitira ulemu akazi?
◻ Kodi ziphunzitso za Yesu zinasonyeza bwanji kuchitira ulemu akazi?
◻ Kodi nchifukwa ninji mwamuna ayenera kuchitira ulemu mkazi wake Wachikristu?
◻ Kodi Akristu onse ali ndi thayo lotani la kusonyeza ulemu?
[Chithunzi patsamba 17]
Akazi owopa Mulungu anali oyamba kuona Yesu woukitsidwayo, amene anawauza kukachitira umboni kwa abale ake mokondwera