Khalani Aulemu Pamalo Olambirira Yehova
1 Pamene tili alendo m’nyumba ya munthu wina, timasamala katundu wa munthuyo, osachita chilichonse chomwe chingamuwononge, ndipo sitimadodometsa njira imene banjalo limachitira zinthu zake. Koposa kotani nanga pamene tili alendo m’nyumba ya Yehova! Tiyenera kudziŵa mmene tiyenera ‘kukhalira’ m’nyumba yake. (Sal. 15:1, NW; 1 Tim. 3:15) Kaya msonkhano wathu wachikristu ukuchitikira m’Nyumba ya Ufumu, m’nyumba ya munthu wina, m’holo kapena bwalo lamaseŵero, ambiri mwa ife amalemekeza malo athu olambirira, monga ngati malowo analidi nyumba ya Yehova, amene “ulemerero wake uli pamwamba pa dziko lapansi ndi thambo.”—Sal. 148:13.
2 Komabe, abale ena samasonyeza ulemu pamisonkhano mwa kukhala aphokoso kapena kuchita ngati kuti chidziŵitso chimene chikuperekedwacho nchosafunika. Achikulire angapo amapezeka akukambitsirana nkhani zosafunikira kwenikweni ali pakhomo, m’chimbudzi, kapena kunja kwa Nyumba ya Ufumu pamene msonkhano uli mkati. Pamene mwana asiyidwa kuti ayang’anire mng’ono wake, nthaŵi zina aŵiri onsewo amayamba kuseŵera ndipo samapindula konse ndi programuyo. Akuti anyamata ndi atsikana ena amakhala kunja kwa Nyumba ya Ufumu pambuyo pamisonkhano, akumaseŵera, namasokosera kwambiri, ndi kumapanga za makarate. Kumalo ena iwo akhala akumasokosera anansi kapena kudodometsa anthu ofuna kuimika galimoto poimika magalimoto kapena oyenda pamsewu.
3 Mmene Tingapeŵere Kukhala Opanda Ulemu: Tikamazindikira kuti kulambira kwathu nkolemekezeka ndiponso kopatulika, ndithudi tidzapeŵa kudodometsa ena mwa kunong’onanong’ona, kumadya zinthu, kutafuna chingamu, kupanga phokoso ndi mapepala, kupitapita kuchimbudzi mosafunikira, kapena kuzoloŵera kufika pamisonkhano mochedwa. Makolo aulemu ndi oyamikira samalola ana awo kuipitsa sementi, kapena makoma a Nyumba ya Ufumu kapena a m’nyumba imene amachitiramo phunziro la buku. Ndithudi, tonsefe tiyenera kuvomereza kuti sikoyeneradi konse kuti pamalo athu olambirira pazimveka “chinyanso, ndi kulankhula zopanda pake, kapena zopusa zimene siziyenera.”—Aef. 5:4.
4 Nthaŵi zonse tikamakumbukira cholinga cha misonkhano yathu yachikristu, tidzaonetsetsa kuti ifeyo limodzi ndi ana athu tikulambira Yehova mwaulemu pamalo amene ‘timakonda kukhala.’—Sal. 84:10.