Misonkhano Yautumiki ya January
Mlungu Woyambira January 5
Mph. 8 : Zilengezo zapamalopo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu.
Mph. 17: “Sangalalani ndi Kupereka Umboni Womveka Bwino.” Kambitsiranani nkhaniyo ndi omvetsera. Sonyezani mbali zofunika za ulaliki wogwira mtima: (1) Perekani moni waubwenzi, (2) nenani nkhani ina imene yafala posachedwapa kapena funsani za iyo, (3) tchulani Lemba lina loyenera, ndiponso (4) sonyezani buku limene mukugaŵiralo. Sankhani wofalitsa waluso kuti achitire chitsanzo ulaliki woyamba ndi ulendo wobwereza pankhani imodzimodziyo.
Mph. 20: Konzekerani Tsopanolino Kuchirikiza Lamulo la Mulungu Pankhani ya Mwazi. Mkulu woyeneretsedwa akukamba za kufunika kwa kudzaza khadi la Advance Medical Directive/Release. Malangizo ouziridwa m’Salmo 19:7 amasonyeza kuti mawu a Machitidwe 15:28, 29 ndiwo lamulo langwiro la Mulungu pankhani ya mwazi. Olambira okhulupirika amayesetsa kuchirikiza lamulo limenelo. Khadi limeneli limasonyeza kufunitsitsa kwanu kuchita chimenecho ndipo lidzakulankhulirani pamene inuyo simungathe kulankhula nokha. (Yerekezerani ndi Miyambo 22:3.) Khadi latsopano limasonyeza lumbiro lanu lapanthaŵiyo lakuti mukukana kuikidwa mwazi. Msonkhanowu utangotha, Mboni zobatizidwa zimene zikufuna khadi latsopano zingapatsidwe limodzi, ndipo amene ali ndi ana osabatizidwa adzalandira Identity Card ya mwana aliyense. Makhadiwo tisawadzaze pano ayi. Tikawadzazire kunyumba mosamala kwambiri, komabe TISAKAWASAINE AYI. Saini yathu, masaini a mboni, ndi deti zidzaikidwa pakhadipo pambuyo pa Phunziro la Buku la Mpingo. Wochititsa phunziro la buku adzayang’anira chochitikacho. Zimenezi zidzatheketsa kuti onse a m’kagulu kake omwe akufuna kugwiritsira ntchito khadi limeneli la medical directive, athandizidwe. Amene adzasaina maina awo monga mboni ayenera kuonadi mwini khadiyo akusaina khadi lakelo. Yemwe palibepo panthaŵiyo koma yemwe akufuna kudzaza khadilo ndi kulisaina adzathandizidwa ndi ochititsa maphunziro/akulu pa Msonkhano Wautumiki wotsatira, mpaka ofalitsa obatizidwa onse atalemba makhadi awo bwinobwino. (Pendani kalata ya November 16, 1991.) Mwa kusintha mawu a pakhadi limeneli kuti ayenerane ndi mikhalidwe yawo ndi zikhulupiriro zawo, ofalitsa osabatizidwa angalembe makhadi awoawo ogwiritsira ntchito iwo ndi ana awo. Tikukulimbikitsani kulidzaza khadi limeneli kuti mutetezeredwe bwino kwambiri mwa lamulo.
Nyimbo Na. 142 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira January 12
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Lipoti la maakaunti. Fotokozani za makonzedwe a kumunda a pa January 19.
Mph. 15: “Chenjerani ndi Chifundo Chosayenera!” Kukambitsirana ndi omvetsera.
Mph. 20: “Yehova Amapereka Mphamvu Yoposa Yaumunthu.” Mafunso ndi mayankho. (Onani w90-CN 7/15 19, ndime 15-16.) Linganizani kuti ena asimbe zokumana nazo zolimbikitsa zosonyeza mmene Yehova wawalimbikitsira.
Nyimbo Na. 81 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira January 19
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo.
Mph. 15: Zosoŵa zapamalopo.
Mph. 20: Phunziro la Banja Losangalatsa. Mwamuna ndi mkazi wake akukambitsirana zimene banja lawo likufunikira mwauzimu. Podera nkhaŵa kuti mzimu wadzikoli ukuyambukira ana awo moipa, akuganiza kuti afunikira kulimbikitsa ana awo mwauzimu komanso akuvomerezana kuti phunziro lawo la banja lakhala lodumphadumpha ndi kutinso silimasangalatsa. Onse pamodzi akupenda malangizo a mmene phunziro la banja lingapangidwire mopindulitsa, omwe ali mu Nsanja ya Olonda ya August 1, 1997, masamba 26-9. Onsewo akutsimikiza kukhala maso kuti atetezere mkhalidwe wauzimu wa ana awo.
Nyimbo Na. 146 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira January 26
Mph. 12: Zilengezo zapamalopo. Pendani chogaŵira cha February. Tchulani mfundo imodzi kapena ziŵiri za m’buku la Revelation Climax zimene zingakhale zothandiza poligaŵira.
Mph. 15: “Khalani Aulemu Pamalo Olambirira Yehova.” Mafunso ndi mayankho. Ikambidwe ndi mkulu, amene angasamale bwino kugwirizanitsa nkhaniyo ndi mkhalidwe wa kwanuko.
Mph. 18: Kupereka Lipoti la Ntchito Yathu Yapadziko Lonse Yochitira Umboni. (Yochokera mu buku la Uminisitala Wathu, masamba 100-102, 106-10) Nkhani yokambitsirana yokambidwa ndi mlembi. Atasonyeza chitsanzo cha m’Malemba choperekera lipoti ntchito yathu, akupempha atumiki otumikira aŵiri kuti akambitsirane nawo mutu waung’ono wakuti “Chifukwa Chake Timaperekera Lipoti Utumiki Wathu Wakumunda.” Kenako mlembiyo akugogomezera kuti nkofunika kumapereka msanga malipoti olongosoka. Akufotokoza zifukwa zake kudziikira zolinga kumapindulitsa, akumatsiriza ndi mawu olimbikitsa onena za madalitso omwe anthu amapeza pokhala ndi mbali mokwanira pantchito yochitira umboni.
Nyimbo Na. 189 ndi pemphero.