Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 2/1 tsamba 24-28
  • Malo a Nyimbo Pakulambira Kwamakono

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malo a Nyimbo Pakulambira Kwamakono
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Malo Akale a Nyimbo Pakulambira
  • Kuimba kwa Akristu a m’Zaka za Zana Loyamba
  • Chisonkhezero cha Kulambira Konyenga
  • Kubwezeretsa Nyimbo m’Malo Ake Oyenera Pakulambira
  • ‘Kuimbira Ambuye Mumtima Mwathu’
  • Muimbireni Yehova
  • Phindu la Kuimba m’Kulambira Kowona
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Tiziimba Mosangalala
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Imbirani Yehova Zitamando
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Kuimba Kwathu Kutamande Yehova
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 2/1 tsamba 24-28

Malo a Nyimbo Pakulambira Kwamakono

KUIMBA ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. Kuimba mofuula kungatisangalatse ifeyo ndi Mlengi wathu. Mwa kuimba, tingasonyeze malingaliro athu, ponse paŵiri achisoni ndi achisangalalo. Ndiponso, tingasonyeze chikondi chathu, ulemu wathu, ndi chitamando chathu kwa Woyambitsa nyimbo, Yehova.

Pamene Baibulo limatchula nyimbo nthaŵi ngati mazana atatu kaŵirikaŵiri limanena za kulambira Yehova. Kuimba kumapatsa chimwemwe​—osati kupatsa chabe chimwemwe oimbawo komanso Yehova. Wamasalmo analemba kuti: “Amuimbire . . . Popeza Yehova akondwera nawo anthu ake.”​—Salmo 149:3, 4.

Koma kodi kuimba nkofunika motani pakulambira kwamakono? Kodi anthu a Yehova lerolino angamkondweretse motani mwa kuimba mofuula? Kodi nyimbo ziyenera kukhala ndi malo otani pakulambira koona? Kupenda mbiri yakale ya nyimbo pakulambira kudzatithandiza kuyankha mafunsowa.

Malo Akale a Nyimbo Pakulambira

Nthaŵi yoyamba imene Baibulo limatchula nyimbo sipakulambira Yehova ayi. Pa Genesis 4:21, Yubala akutchulidwa kuti ndiye anapanga zimene tingati zoimbira zoyamba kapena mwinamwake amene anayambitsa luso linalake la zoimbaimba. Komabe, nyimbo zinali mbali ya kulambira Yehova ngakhale anthu asanalengedwe. Ma Baibulo angapo amanena kuti angelo amaimba. Yobu 38:7 amasimba za angelo amene anaimba ndi ‘kufuula ndi chimwemwe.’ Choncho, pali chifukwa cha m’Malemba chokhulupirira kuti kuimba polambira Yehova kunaliko kalekale munthu asanakhaleko.

Olemba mbiri ena anena kuti nyimbo zakale zachihebri zinali zatchuni chimodzi basi, zopanda tchuni china chogwirizana. Komabe, ankatha kuimba tchuni choposa chimodzi nthaŵi imodzi pazeze, choimbira chimene chimatchulidwa kaŵirikaŵiri m’Baibulo. Oimba zeze ayenera kuti anazindikira kugwirizana kumene kumakhalapo mwa kuimba tchuni chosiyanasiyana pachoimbiracho. M’malo mokhala zapansi, mosakayikira nyimbo zawo zinali zapamwamba ndithu. Ndipo mwa kungoona ndakatulo ndi kalembedwe ka Malemba Achihebri, tinganene kuti nyimbo zachiisrayeli zinali zapamwamba. Ndithudi, chowasonkhezera kupanga nyimbo chinali chapamwamba kwambiri kuposa chija cha mitundu yoyandikana nayo.

Makonzedwe apakachisi wakale anafuna kuti pazikhala oimba ndi zoimbira zamitundumitundu ndi oimba ndi mawu polambira m’kachisi. (2 Mbiri 29:27, 28) Panali ‘atsogoleri,’ ‘aphunzitsi,’ ‘ophunzira,’ ndi ‘akulu a oyimbira.’ (1 Mbiri 15:21; 25:7, 8; Nehemiya 12:46) Pothirira ndemanga paluso lawo lapamwamba loimba nyimbo, wolemba mbiri Curt Sachs analemba kuti: “Oimba pakamwa ndi oimba ndi zoimbira a m’Kachisi m’Yerusalemu ayenera kuti anali ndi mtundu wapamwamba wa maphunziro a zoimbaimba, luso lake, ndi chidziŵitso chake. . . . Ngakhale sitikudziŵa mamvekedwe a nyimbo zakalezo, umboni wonse wa mphamvu yake, ulemerero wake, ndi ukatswiri wake tili nawo.” (The Rise of Music in the Ancient World: East and West, 1943, masamba 48, 101-2) Nyimbo ya Solomo ili chitsanzo cha luso ndi mkhalidwe wa nyimbo zachihebri. Iyo ndi nkhani m’nyimbo, yofanana ndi mawu a opera. Nyimboyo m’malemba achihebri imatchedwa “Nyimbo ya Nyimbo,” ndiko kuti, nyimbo yabwino koposa. Kwa Ahebri akale, kuimba kunali mbali yofunika ya kulambira. Ndipo kunawachititsa kutamanda Yehova mwachimwemwe mochokera mumtima.

Kuimba kwa Akristu a m’Zaka za Zana Loyamba

Kuimba kunapitiriza kukhala mbali yokhazikika ya kulambira pakati pa Akristu oyambirira. Kuwonjezera pa Masalmo ouziridwa amene anali nawo, zikuchita ngati kuti iwo anapekanso nyimbo zawozawo ndi mawu ake zoimba polambira, kuika chitsanzo cha kupeka nyimbo zachikristu kwamakono. (Aefeso 5:19) Buku lakuti The History of Music, lolembedwa ndi Waldo Selden Pratt, limafotokoza kuti: “Unali mwambo wa Akristu oyambirira woimba onse pamodzi polambira ndipo aliyense payekha. Kwa otembenukira ku Chiyuda zimenezi zinali chabe kupitiriza kwa miyambo ya m’sunagoge . . . Kuwonjezera pa Masalmo achihebri . . . , chikhulupiriro chatsopanocho chinali kupeka nyimbo zatsopano nthaŵi zonse, poyamba zonga ma rhapsody.”a

Posonyeza kufunika kwa kuimba, pamene Yesu anayambitsa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye, iye ndi atumwi ayenera kuti anaimba ma Hallel. (Mateyu 26:26-30) Zimenezi zinali nyimbo zotamanda Yehova zolembedwa m’Masalmo ndipo zoimba paphwando la Paskha.​—Masalmo 113-118.

Chisonkhezero cha Kulambira Konyenga

Podzafika zimene amati Nyengo Zamdima, nyimbo zachipembedzo zinakhala nyimbo zachisoni. Cha ku ma 200 C.E., Clement wa ku Alexandria anati: “Tikufuna choimbira chimodzi basi: mawu amtendere achitamando, osati azeze kapena ng’oma kapena zitoliro kapena malipenga ayi.” Anaikapo ziletso, akumati nyimbo za tchalitchi ziyenera kuimbidwa pakamwa basi. Kaimbidwe kameneka kanadziŵika kuti chant kapena plainsong. “Zaka zosakwana makumi anayi Constantinople itamangidwa, Bungwe la ku Laodicea (A.D. 367) linaletsa zonse ziŵiri kuimba zoimbira ndi kutsagana ndi mpingo polambira. Kwa nthaŵi yaitali nyimbo zamwambo zangokhala zoimba pakamwa,” limatero buku lakuti Our Musical Heritage. (Kanyenye ngwathu.) Ziletso zimenezi zinalibe maziko m’Chikristu choyambirira.

M’Nyengo Zamdima, Baibulo linali buku losadziŵika kwa anthu wamba. Akristu amene analimba mtima moti nkukhala ndi Baibulo kapena kuliŵerenga anazunzidwa ndipo ngakhale kuphedwa. Choncho nkosadabwitsa kuti kuimbira Mulungu zitamando kunazimiririka kotheratu m’nyengo yamdima imeneyo. Choncho, ngati anthu wamba sanali kuwadziŵa Malemba, akanadziŵa bwanji kuti mbali imodzi mwa mbali khumi za Baibulo lonse ndi nyimbo? Ndani akanawauza kuti Mulungu analamula olambira ake ‘kumuimbira Yehova nyimbo yatsopano, ndi chilemekezo chake mumsonkhano wa okondedwa ake’?​—Salmo 149:1.

Kubwezeretsa Nyimbo m’Malo Ake Oyenera Pakulambira

Gulu la Yehova layesetsa kubwezeretsa nyimbo ndi kuimba m’malo ake oyenera pakulambira. Mwachitsanzo, kope la Zion’s Watch Tower la February 1, 1896, linali ndi nyimbo zokhazokha. Linali ndi mutu wakuti “Nyimbo za Ziyoni Zachimwemwe za Mmaŵa.”

Mu 1938 kuimba pamisonkhano yampingo kunaimitsidwa. Komabe, mwamsanga panakhala nzeru yotsatira chitsanzo ndi chitsogozo cha atumwi. Pamsonkhano wachigawo wa mu 1944, F. W. Franz anapereka nkhani yakuti “Nyimbo ya Utumiki wa Ufumu.” Iye anasonyeza kuti nyimbo zotamanda Yehova zinayamba kuimbidwa ndi zolengedwa zakumwamba za Mulungu kalekale munthu asanalengedwe ndipo anati: “Mulungu amaziona kukhala zoyenera ndipo amakondwa nazo ngati atumiki ake apadziko lapansi amuimbira nyimbo mofuula.” Atalongosola za kuimba polambira, analengeza kuti Kingdom Service Song Book (Buku la Nyimbo za Utumiki wa Ufumu) latuluka logwiritsira ntchito pamisonkhano ya utumiki ya mlungu ndi mlungu.b Ndiyeno Informant (imene tsopano ndiyo Utumiki Wathu Waufumu) ya December 1944 inalengeza kuti misonkhano ina idzakhalanso ndi nyimbo yotsegulira ndi yomaliza. Kuimba kunakhalanso mbali ya kulambira Yehova.

‘Kuimbira Ambuye Mumtima Mwathu’

Abale athu ku Eastern Europe ndi mu Afirika amene tsoka lawagwera ndipo azunzidwa zaka zambiri akusonyeza kufunika kwake kwa kuimba mochokera mumtima. Lothar Wagner anatha zaka zisanu ndi ziŵiri atambindikira kwayekha. Kodi anapirira motani? “Milungu ingapo ndinasumika maganizo pakuimba nyimbo zonse za Ufumu zomwe ndinali kukumbukira. Pamene sindinadziŵe mawu ake enieni ndinangopeka vesi limodzi kapena mavesi aŵiri. . . . Nyimbo zathu za Ufumu zili ndi malingaliro olimbikitsa ndi omangirira ochuluka chotani nanga!”​—1974 Yearbook of Jehovah’s Witnesses, masamba 226-8.

Pazaka zisanu atambindikira kwayekha chifukwa cha chikhulupiriro chake, Harold King anapeza chitonthozo mwa kupeka ndi kuimba nyimbo zotamanda Yehova. Nyimbo zingapo zimene anapeka Mboni za Yehova zikuzigwiritsira ntchito tsopano pakulambira kwawo. Chimwemwe chimene nyimbo zimadzetsa chimalimbikitsa. Koma sitiyenera kuzunzidwa kaye kuti titsimikize kuti kuimba zitamando kwa Mulungu nkofunika.

Anthu onse a Yehova angasangalale ndi nyimbo. Ngakhale kuti tingamavutike kufotokoza malingaliro athu mwa kulankhula, malingaliro athu kulinga kwa Yehova ayenera kumasuka pamene timawasonyeza m’nyimbo. Mtumwi Paulo anasonyeza mmene tingasangalalire ndi kuimba zitamando pamene analimbikitsa Akristu kupitirizabe “kudzilankhulira nokha ndi masalmo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuimbira ndi kuimba m’malimba Ambuye mumtima mwanu.” (Aefeso 5:19) Pamene mitima yathu yadzala ndi zinthu zauzimu, timaimba nyimbo mwamphamvu. Chotero mfungulo ya kuimba bwino ndiyo kukhala ndi maganizo abwino mumtima.

Kukhala ndi unansi wabwino ndi Yehova kumachititsanso mzimu wachimwemwe, wotisonkhezera kulankhula, kuimba, ndi kufuula zitamando za Yehova. (Salmo 146:2, 5) Timaimba mokondwa kwambiri pazinthu zimene zimatisangalatsa. Ndipo ngati nyimbo timaikonda kapena malingaliro ake, ndiye kuti tidzaiimba mokhudzika mtima kwambiri.

Munthu satofunikira kuimba mofuula kuti aimbe mokhudzika mtima. Sikuti kuimba bwino nkuimba mofuula; kapenanso kuimba mosamveka. Mawu ena amphamvu mwachibadwa angamveke pamwamba pa ena onse ngakhale kuti ndi maimbidwe ofeŵa. China chimene chimavuta kuimba bwino m’gulu ndicho kuphunzira kugwirizana ndi ena. Kaya mukuimba mogwirizana tchuni chosiyanasiyana kapena tchuni chimodzi, kulingana mphamvu ya mawu anu ndi a oyandikana nanu kumachititsa nyimbo kumveka yokondweretsa ndi yogwirizana. Kudekha kwachikristu ndi khutu lomvetsera zimamthandiza munthu kusamala poimba mwachimwemwe komanso mosapambanitsa ndi liwu lake. Komabe, awo amene amaimba mwaluso kapena amene ali ndi mawu abwino kwambiri sayenera kulefuka kuti asaimbe momveka. Liwu labwino lingalimbikitse kwambiri mpingo kuimbira Yehova zitamando.

Kuimba pamisonkhano yathu kumaperekanso mpata wabwino woimba tchuni chosiyanasiyana mogwirizana motsagana ndi nyimbo zamalimba. Awo amene angaimbe bwino tchuni chosiyanasiyana chogwirizana kapena amene angaŵerenge manotsi ake m’buku la nyimbo ndi kuwaimba akulimbikitsidwa kuwonjezeramo mawu awo m’nyimbo ndi kuwonjezera kukoma kwa nyimbo.c

Ena anganene kuti, ‘Sindimatsata bwino tchuni’ kapena ‘Ndili ndi liwu loipa kwambiri; limagoma nyimbo ikakwera.’ Choncho, iwo samaimba mwaufulu, ngakhale pa Nyumba ya Ufumu. Choonadi nchakuti kulibe mawu oimbira Yehova zitamando amene angakhale “oipa” kwa iye. Monga momwe liwu la munthu polankhula lingawongokere mwa kuyeseza ndi mwa kutsatira malingaliro othandiza a m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki, kuimba kwa munthu kungawongokerenso. Ena awongolera mawu awo mwa kungong’ung’udza nyimbo pochita ntchito. Kung’ung’udza nyimbo kumathandiza kusalaza mawu. Ndipo panthaŵi yoyenera pamene tili tokha kapena pamene tikugwira ntchito kumene sitingasokoneze ena, kuimba nyimbo za Ufumu ndiko njira yabwino kwambiri yoyesera mawu ndiponso yokhalira ndi malingaliro achimwemwe, ndi omasuka.

Tingalimbikitsenso kuimba nyimbo zingapo za Ufumu pamacheza. Kuimba kumeneku, motsagana ndi choimbira monga gitala kapena piyano kapena nyimbo za piyano za Sosaite, kumachititsa machezawo kukhala ndi mbali yauzimu. Kumaperekanso thandizo la kuphunzira nyimbo ndi kuziimba bwino pamisonkhano yampingo.

Kuti ithandize mipingo kukhala ndi mzimu woimba pamisonkhano, Sosaite yakonza nyimbo zotsagana nazo zojambula. Pamene akuziliza, wosamalira zokuzira mawu ayenera kudziŵa ukulu wake wa mawu. Ngati nyimbozo sizikumveka kwambiri, mpingo sungamasuke kuimba mofuula. Pamene mbale wosamalira zokuzira mawu aimbira limodzi ndi mpingo, adzatha kudziŵa ngati nyimbo zamalimba zikutsogolera bwino kapena sizikutero.

Muimbireni Yehova

Kuimba kumatipatsa mpata wofotokoza malingaliro athu kwa Mlengi wathu. (Salmo 149:1, 3) Sindiko kungotengeka mtima, koma kusonyeza chitamando chathu molamulirika, moyenerera, ndi mwachimwemwe. Kuimba mochokera mumtima mumpingo kungakonzekeretse maganizo athu ndi mtima wathu kaamba ka programu yotsatira ndipo kungatisonkhezere kuchita zambiri pakulambira Yehova. Ngakhale kuti kuimba kumakhudza mtima, mawu ake angatilangizenso. Choncho mwa kuimba tchuni chimodzi ndi tchuni chosiyanasiyana mogwirizana, timakonzekeretsa mitima yathu mofatsa ndi modzichepetsa kuti tiphunzire limodzi monga anthu osonkhanitsidwa.​—Yerekezerani ndi Salmo 10:17.

Kuimba kudzakhalabe mbali ya kulambira Yehova. Chotero tikuyembekezera kugwirizana kosatha ndi malingaliro a wamasalmo akuti: “Ndidzalemekeza Yehova m’moyo mwanga; ndidzaimbira zomlemekeza Mulungu wanga pokhala ndi moyo ine.”​—Salmo 146:2.

[Mawu a M’munsi]

a Rhapsody ndi nyimbo imene mbali zake zosiyanasiyana zimasinthasintha poimba chifukwa cha mzimu wake wa ufulu umene zimapereka. Kaŵirikaŵiri ma rhapsody ankatama zochitika zotchuka kapena anthu.

b Akorinto Woyamba 14:15 akuchita ngati akusonyeza kuti panali kuimba nthaŵi zonse pakulambira kwa Akristu a m’zaka za zana loyamba.

c Nyimbo zina m’buku lathu latsopano la nyimbo, Imbirani Yehova Zitamando, zili ndi mbali zinayi zogwirizana kuti awo amene amatha kuimba tchuni chosiyanacho asangalale nazo. Komabe, nyimbo zambiri azilinganiza kuti zizitsagana ndi piyano ndipo kaimbidwe kake kanakonzedwa kuti zikhalebe ndi tchuni chake cha kumaiko kumene zinachokera. Kudzikonzera manotsi m’nyimbo zolembedwa popanda mbali zake zinayi za tchuni kungachititse kuimba kwathu kumveka kokoma pamisonkhano.

[Bokosi patsamba 27]

Njira Zina Zoimbira Bwino

1. Tukulani buku lanu la nyimbo poimba. Zimenezi zidzakuthandizani kupuma mwachibadwa ndithu.

2. Kokani mpweya kwambiri pachiyambi cha mzera uliwonse.

3. Kutsegula kamwa poyamba kuposa mmene mumatsegulira nthaŵi zonse kudzakuza mawu ndi kamvekedwe kake mwachibadwa.

4. Koposa zonse, sumikani maganizo pamawu a nyimbo mukuimbayo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena