Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/04 tsamba 3
  • Kodi Mudzapezekapo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mudzapezekapo?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
  • Nkhani Yofanana
  • Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa 2006 Wakuti “Chipulumutso Chayandikira”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Zokumbutsa za Msonkhano Wachigawo wa 1998 Wakuti: “Njira ya Moyo ya Mulungu.”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Kodi Mudzapezekapo?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Kodi Mumayamikira Zinthu Zopatulika?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2000
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
km 5/04 tsamba 3

Kodi Mudzapezekapo?

1 Munthu wina amene wakhala Mboni kwa nthaŵi yaitali anati: “Ngati muphonya tsiku loyamba la msonkhano wachigawo, ndiye kuti mwaphonya zinthu zambiri zedi!” Chifukwa chiyani anatero? Chifukwa chakuti tsiku loyamba n’limene limakhala chiyambi cha phwando lalikulu lauzimu limene gulu la Yehova latikonzera. (Yes. 25:6) Kupezekapo kwathu kuyambira pachiyambi kumasonyeza kuti timavomereza mawu a wamasalmo akuti: “Ndinakondwera mmene ananena nane, tiyeni ku nyumba ya Yehova.”—Sal. 122:1.

2 Komabe, chaka chatha m’malo ena a Msonkhano Wachigawo wa “Patsani Mulungu Ulemerero,” chiŵerengero cha anthu patsiku Lachisanu chinali chochepa kwambiri poyerekezera ndi chiŵerengero cha tsiku Loŵeruka ndi Lamlungu. Zimenezi zikutanthauza kuti abale ambiri anaphonya mbali ya msonkhano imene inali ndi nkhani zofunika kwambiri zokhudza kupatsa Mulungu ulemerero. Komanso anadzimana mayanjano abwino ndi okhulupirira anzawo.

3 Musalole Ntchito Yakuthupi Kukulepheretsani: Kuopa kuchotsedwa ntchito chingakhale chifukwa chimene ena analepherera kupezeka pamsonkhano tsiku Lachisanu. Komabe, Mboni zambiri zaona kuti mabwana awo savuta pankhani imeneyi ngati apempheratu tchuthi nthaŵi ikadalipo. Bwana wina anachita chidwi kwambiri ndi mlongo wina amene anali mpainiya chifukwa cha chizoloŵezi chake chopezeka pamisonkhano yonse ya mpingo ndiponso yaikulu moti bwana wakeyo anakakhala nawo tsiku lathunthu pamsonkhano umene mlongoyu anapita!

4 Simuyenera kuganiza kuti abwana anu sangalole kukupatsani tchuthi, kapena kuganiza kuti kuphonya tsiku limodzi kulibe kanthu. Ndi chidaliro chonse, konzekerani kuwaonetsa mwaluso abwana anu kuchokera m’Malemba chifukwa chake kupezeka pamsonkhano kuli mbali yofunika kwambiri pa kulambira kwanu. (Aheb. 10:24, 25) Ndiyeno dalirani malonjezo a Yehova, pozindikira kuti zilizonse zimene mufuna zakuthupi zidzapatsidwa kwa inu ngati muika zinthu zauzimu pamalo oyamba m’moyo wanu.—Mat. 6:33; Aheb. 13:5, 6.

5 Chofunika kwambiri ndicho kuyamikira “zinthu zofunika kwambiri.” (Afil. 1:10, 11, NW; Sal. 27:4) Izi zimatipangitsa kukonzekera kuti tipindule mokwanira ndi makonzedwe ofunika a Yehova ameneŵa. Yambani kukonzekera lero, ndipo tsimikizani kuti mudzapezekepo masiku onse atatu!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena