Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo—Gawo 10
Kuphunzitsa Ophunzira Ulaliki wa Nyumba ndi Nyumba
1 Akulu akapenda wophunzira Baibulo n’kuona kuti akuyenerera kukhala wofalitsa wosabatizidwa, wophunzirayo angayambe kugwira nawo ntchito yolalikira limodzi ndi mpingo. (Onani buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova, tsa. 79 mpaka 81.) Kodi tingamuthandize bwanji wophunzira kuti athe kumalalikira nyumba ndi nyumba?
2 Kukonzekera Limodzi: Palibe chinthu chofunika kuposa kukonzekera bwino. M’sonyezeni wophunzirayo pamene angapeze zitsanzo za ulaliki mu Utumiki Wathu wa Ufumu ndi m’buku la Kukambitsirana. Mukatero m’thandizeni kusankha chitsanzo cha ulaliki wosavuta koma wogwirizana ndi gawo la kwanuko. Panthawi yoyamba yomweyo, m’limbikitseni kugwiritsa ntchito Baibulo mu utumiki wake.—2 Tim. 4:2.
3 Kuyeserera zimene mukachite mu utumiki n’kofunika kwambiri kwa wofalitsa watsopano. Pamene wophunzirayo akuyeserera ulalikiwo, m’sonyezeni mmene angayankhire mwanzeru mogwirizana ndi mmene anthu a m’gawolo amayankhira nthawi zambiri Mboni zikamawalalikira. (Akol. 4:6) M’tsimikizireni kuti atumiki achikristu sachita kufunika kuti adziwe yankho la funso lililonse limene mwininyumba angafunse. M’fotokozereni kuti nthawi zambiri zimakhala bwino kuyankha mafunso oterowo mwa kumuuza mwininyumbayo kuti mukufuna mukafufuze kaye ndipo mukabweranso kuti mudzapitirize kukambirana nkhaniyo.—Miy. 15:28.
4 Kulalikira Limodzi: Pamene mukupita koyamba ndi wophunzirayo mu ulaliki wa nyumba ndi nyumba, choyamba muuzeni kuti aonere mmene mugwiritsire ntchito chitsanzo cha ulaliki umene munakonzekera muli limodzi uja. Kenako muuzeni kuti atenge nawo mbali. Nthawi zina zimakhala bwino kwa wophunzira watsopano kuchita mbali yochepa ya ulalikiwo, monga kuwerenga lemba n’kuperekapo ndemanga. Zindikirani umunthu wa wophunzirayo ndiponso zimene angakwanitse kuchita ndi zimene sangakwanitse. (Afil. 4:5) Muzimuyamikira pamene mukupitirizabe kumuphunzitsa pang’onopang’ono mbali zosiyanasiyana za ntchito yolalikira.
5 Zimakhala bwino kwambiri kum’thandiza wofalitsa watsopano kukhala ndi ndandanda yopitira mu utumiki mokhazikika, mwina mlungu uliwonse ngati kungatheke. (Afil. 3:16) Konzani zopitira limodzi mu utumiki, ndipo m’limbikitseni kuti azilalikiranso limodzi ndi anthu ena omwe ndi achangu mu utumiki. Chitsanzo chawo ndiponso kucheza nawo zidzamuthandiza kukhala ndi luso ndi kupeza chimwemwe m’ntchito yolalikira nyumba ndi nyumba.