Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/07 tsamba 1
  • “Sindikufuna”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Sindikufuna”
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Nkhani Yofanana
  • Perekani Chisamaliro Chokhazikika ku Chiphunzitso Chanu
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kodi Amphwayi Mumachita Nawo Bwanji?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Sonyezani Ena Chidwi mwa Kukhala Wokhoza Kusintha
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Mmene Mungasungire Chimwemwe mu Utumiki wa Nthaŵi Zonse
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
km 1/07 tsamba 1

“Sindikufuna”

1 M’madera ena sizachilendo munthu kuyankha choncho tikafuna kumuuza uthenga wathu. Kodi n’chiyani chimene chingatithandize kuti tisataye mtima tikakumana ndi anthu opanda chidwi m’gawo? Ndiye kodi tingatani kuti tilimbikitse anthu kuti achite chidwi ndi uthenga wabwino?

2 Khalanibe Achimwemwe: Kukumbukira chifukwa chimene anthu ambiri safuna kumvetsera uthenga wathu, kungatithandize kukhalabe achimwemwe. Anthu amene anaphunzitsidwa kuti zamoyo sizinachite kulengedwa ndi Mulungu kapena amene anakulira pakati pa anthu amene amati kulibe Mulungu, sangadziwe kuti Baibulo n’lofunika. Ena angakhale kuti anasokonezeka chifukwa cha chinyengo chimene anaona m’chipembedzo. Anthu ena angakhale opanda chidwi chifukwa chokhumudwa ndiponso chifukwa choti alibe chiyembekezo chilichonse. (Aef. 2:12) Ena ‘sazindikira kanthu’ chifukwa alemedwa ndi nkhawa za moyo.—Mat 24:37-39.

3 Ngakhale kuti anthu ena sachita nazo chidwi, tingakhalebe achimwemwe mu utumiki, podziwa kuti khama lathu limalemekezetsa Yehova. (1 Pet. 4:11) Kuwonjezera apo, kuuza choonadi anthu, ngakhale amene panopo sachiona ngati chaphindu, kumalimbitsa chikhulupiriro chathu. Tiyeni tiyesetse kuona anthu a m’gawo lathu monga mmene Yehova amawaonera. Iye anamva chisoni ndi anthu a ku Nineve amene anali “osadziwa kusiyanitsa pakati pa dzanja lawo lamanja ndi lamanzere.” (Yona 4:11) Anthu amene akukhala m’gawo lathu akufunikira uthenga wabwino! Choncho sitiyenera kugwa mphwayi, koma tiyenera kufunafuna njira zowalimbikitsira kuti achite chidwi ndi uthenga wa m’Baibulo.

4 Kambiranani Zimene Zikudetsa Nkhawa Anthu a Kwanuko: Mwina, poyamba ulaliki wanu mungatchule zinthu zimene zikudetsa nkhawa anthu a kwanuko, ndi kufunsa mwininyumba kuti anenepo maganizo ake pa zinthuzo. Mvetserani pamene mwininyumbayo akulankhula, ndipo yankhani nkhawa zakezo pomusonyeza uthenga wotonthoza wa m’Baibulo. M’dera lina mutachitika tsoka, m’bale wina polalikira amapepesa moona mtima pa khomo lililonse. M’baleyu anati: “Nditangoyamba kuchita zimenezi, anthu anayamba kumasuka kulankhula nane. Tsiku limeneli, ndinalankhula bwinobwino ndi anthu ambiri chifukwa ndinasonyeza kuti ndikuwaganizira.”

5 Ufumu wa Mulungu udzathetsa vuto lililonse limene anthu amakumana nalo. Yesani kudziwa vuto limene mwininyumba akuda nalo nkhawa kwambiri. Iye angakuloleni kufotokoza uthenga wopatsa chiyembekezo wa m’Baibulo. Ngati sangatero, mwina angafune kudzamvetsera “nthawi ina.”—Mac. 17:32.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena