Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 1/07 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira January 8
  • Mlungu Woyambira January 15
  • Mlungu Woyambira January 22
  • Mlungu Woyambira January 29
  • Mlungu Woyambira February 5
Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
km 1/07 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira January 8

Nyimbo Na. 12

Mph.10: Zilengezo za pampingo. Gwiritsani ntchito malangizo amene ali pa tsamba 8 kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale wothandiza m’gawo lanu, kusonyeza chitsanzo cha mmene tingachitire pogawira Nsanja ya Olonda ya January 15 ndi Galamukani! ya January. M’chitsanzo chimodzi, sonyezani mmene tingayankhire munthu amene sakufuna kuti tipitirize kukambirana naye ponena kuti “Ndili wotanganitsidwa.”—Onani buku la Kukambitsirana, tsamba 19 ndi 20.

Mph.15: Pindulani ndi kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku. Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera kuchokera pa mawu oyamba a m’kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—2007. Fotokozani kufunika koti aliyense azipatula mphindi zochepa tsiku lililonse kuti awerenge Lemba la tsiku ndi ndemanga. Konzeranitu zoti munthu mmodzi kapena awiri adzafotokoze za chizolowezi chawo chochita lemba la tsiku ndi mmene apindulira. Malizani mwa kukambirana mwachidule lemba la chaka la 2007.

Mph.20: Fikirani Aliyense ndi Uthenga Wabwino. Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera kuchokera m’buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova, tsamba 92 mpaka pa kamutu komwe kali pa tsamba 102.

Nyimbo Na. 165 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira January 15

Nyimbo Na. 93

Mph.5: Zilengezo za pampingo. Musankhe zilengezo zina mu Utumiki Wathu wa Ufumu.

Mph.10: Kodi Pali Chinachake Chimene Chikukulepheretsani? Nkhani yokambidwa ndi mkulu kuchokera mu Nsanja ya Olonda ya April 1, 2002, masamba 13 mpaka 15.

Mph.15: “Sindikufuna.”a Mukamakambirana ndime yachinayi, funsani omvetsera kuti atchulepo zinthu zimene zimachititsa chidwi anthu a m’gawo la kwanuko. Khalani ndi zitsanzo ziwiri za ulaliki zosonyeza mmene tingayankhire munthu amene sakufuna kuti tikambiranane naye ponena kuti “Sindikufuna.”—Onani buku la Kukambitsirana, tsamba 16.

Mph.15: “Mtima Wodzipereka Umabweretsa Madalitso.”b Funsani wofalitsa mmodzi kapena awiri amene amadziwika kuti ali ndi mtima wodzipereka. Kodi asonyeza motani kuti ali ndi mtima wodzipereka? Kodi anayenera kusintha pa zinthu zotani ndipo anatha bwanji kusintha m’njira imeneyi? Kodi ndi madalitso otani amene apeza chifukwa cha mtima umenewu?

Nyimbo Na. 135 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira January 22

Nyimbo Na. 224

Mph.8: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndiponso ndalama zimene zaperekedwa mumpingomo zolembedwa pa sitetimenti. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 8 kapena mfundo zina zothandiza m’gawo lanu, posonyeza zitsanzo za mmene tingagawire Nsanja ya Olonda ya February 1 ndi Galamukani! ya February. M’chitsanzo chimodzi, asonyeze akuchita ulendo wobwereza kwa munthu amene amakam’patsira magazini.

Mph.17: “Kudziwa Kulemba ndi Kuwerenga Pakati pa Anthu a Mulungu.”c Nkhaniyi ikambidwe ndi mkulu. Anthu amene apindula ndi kalasi yophunzitsa kulemba ndi kuwerenga aperekepo ndemanga.

Mph.20: “Kodi Chithandizo Chamankhwala Chabwino Kwambiri N’chiti?”d Nkhaniyi ikambidwe ndi mkulu. Pomaliza werengani ndime yomaliza ndi kulimbikitsa onse kukabwereza mosamala nkhani zimene zatchulidwa zochokera mu Nsanja ya Olonda.

Nyimbo Na. 188 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira January 29

Nyimbo Na. 55

Mph.10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kuti apereke malipoti awo a utumiki wa kumunda a mwezi wa January. Tchulani mabuku ogawira mwezi wa February, ndipo onetsani chitsanzo chimodzi cha momwe tingagawire mabukuwo.

Mph.20: “Kodi Mwakonzekera Masoka Achilengedwe?”e Nkhaniyi ikambidwe ndi mkulu. Phatikizanipo ndemanga zochokera pa tsamba 3 la Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2005.

Mph.15: Mukalonjeza Kuti Mudzabweranso, Muzibweradi. Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera kuchokera mu Nsanja ya Olonda ya September 15, 1999, tsamba 11. Pemphani omvetsera kuti afotokoze zokumana nazo zosonyeza mmene anapindulira potsatira lonjezo lawo lobwererakonso.

Nyimbo Na. 137 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira February 5

Nyimbo Na. 3

Mph.10: Zilengezo za pampingo. Kambiranani mwachidule bokosi la mafunso

Mph.15: Inetu Ndine Wamboni! Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera. Achinyamata ena safuna kuzidziwikitsa kuti ndi Mboni za Yehova chifukwa amaganiza kuti anzawo awanyoza. Komabe, pali zifukwa zabwino zodzidziwikitsira kuti ndinu Mboni. Aphunzitsi amene akudziwa za zikhulupiriro zanu angalemekeze zikhulupirirozo mosavuta ndipo sangakukakamizeni kuchita nawo zinthu zina zosayenera. Achinyamata amene alibe khalidwe labwino angayambe kuganizira kaye asanakupempheni kuti muchite nawo khalidwe losayenera. Anthu ena angamvetse mosavuta zosankha zanu pankhani za zibwenzi ndiponso kuchita nawo masewera kusukulu, kapena zinthu zina zosakhudzana ndi maphunziro. Komanso simuchita mantha kuchitira umboni ku sukulu kapena kukumana ndi anzanu a m’kalasi pamene mukulalikira m’gawo. (g02 4/8 tsa. 16) Pemphani ofalitsa kuti anenepo mmene anapindulira atazidziwikitsa kusukulu kuti ndi a Mboni za Yehova. Konzeranitu pasadakhale ndemanga imodzi kapena ziwiri.

Mph.20: “Chikondi N’chofunika Kuti Utumiki Ukhale Wopindulitsa.”f Phatikizanipo ndemanga zochokera mu Nsanja ya Olonda ya February 1, 2003, tsamba 23, ndime 16 mpaka 17.

Nyimbo Na. 83 ndi pemphero lomaliza.

[Mawu a M’munsi]

a Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

b Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

c Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

d Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

e Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

f Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena