CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | NEHEMIYA 9-11
Anthu Okhulupirika Amatsatira Malangizo a Gulu la Yehova
Anthu okhulupirika anatsatira malangizo osiyanasiyana a gulu la Yehova
Anthu a Yehova anakonzekera Chikondwerero cha Misasa ndipo anachita motsatira malangizo
Tsiku lililonse anthu ankasonkhana kuti amvetsere Chilamulo cha Mulungu ndipo ankasangalala
Anthu anaulula machimo, anapemphera komanso anapempha Yehova kuti awadalitse
Anthu anavomereza kuti apitiriza kutsatira malangizo ochokera kwa Yehova
• Anatsatira malangizo a gulu la Yehova pochita zinthu izi:
Ankakwatirana ndi anthu okhawo amene ankalambira Yehova
Ankapereka ndalama zothandizira pa kulambira koona
Ankasunga Sabata
Ankapereka nkhuni zomwe ankazigwiritsa ntchito paguwa lansembe
Ankapereka kwa Yehova mbewu zoyamba kucha ndiponso ziweto zoyamba kubadwa