CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | ESITERE 6-10
Esitere Anasonyeza Kuti Sanali Wodzikonda
Esitere anasonyeza kuti ndi wolimba mtima komanso wosadzikonda poteteza anthu a Yehova
Moyo wa Esitere ndi Moredekai sunali pangozi. Koma lamulo la Hamani loti Ayuda onse aphedwe n’kuti likulengezedwa mu ufumu wonse wa Ahasiwero
Esitere anaika moyo wake pangozi pokaonekeranso pamaso pa mfumu asanaitanidwe. Iye analira n’kupempha mfumuyo kuti isinthe lamulo limene Hamani anakhazikitsa
Malamulo operekedwa m’dzina la mfumu sankasinthidwa. Choncho mfumuyo inapatsa mphamvu Esitere ndi Moredekai kuti apange lamulo latsopano
Yehova anathandiza anthu ake kuti apambane
Lamulo lachiwiri linalengezedwa ndipo linapatsa Ayuda mphamvu yoti adziteteze
Anthu okwera pa mahatchi anatumizidwa m’zigawo zonse za ufumuwo kuti akakonzekeretse Ayuda kumenya nkhondo
Anthu ambiri anaona kuti Yehova amakonda anthu ake ndipo ena anayamba kutsatira chipembedzo cha Ayuda