KUWONJEZERA LUSO LATHU MU UTUMIKI
Kukonza Ulaliki Wanuwanu wa Magazini
N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUCHITA ZIMENEZI?: Zitsanzo za ulaliki zomwe zimakhala mu Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ndi zothandiza, koma sitiyenera kuloweza chifukwa ndi zongotithandiza kudziwa zimene tinganene. Tiyenera kukonzekera m’mawu athuathu. Tingagwiritsenso ntchito ulaliki wina kapena nkhani ina yogwirizana ndi gawo lathu. Choncho tikawerenga magazini, kuona zitsanzo za ulaliki komanso kuonera vidiyo, tikhoza kugwiritsa ntchito mfundo zotsatirazi kuti tikonze ulaliki wathu.
KODI TINGACHITE BWANJI ZIMENEZI?
Dzifunseni kuti, ‘Kodi ineyo ndingakonde kugwiritsa ntchito chimodzi mwa zitsanzo za ulalikizi?’
INDE
Chikonzekereni m’mawu anuanu. Pambuyo popereka moni fotokozani cholinga chanu. (Mwachitsanzo, munganene kuti: “Ndabwera kuti . . .”)
Ganizirani zimene munganene pambuyo poti mwafunsa funso, pambuyo poti mwawerenga lemba komanso pambuyo poti mwapereka magazini. (Mwachitsanzo, pofuna kutchula lemba munganene kuti: “Yankho la funso limeneli tingalipeze palemba ili.”)
AYI
Sankhani nkhani imene yakusangalatsani komanso imene anthu a m’gawo lanu angasangalale nayo
Ganizirani funso limene lingachititse munthuyo kufotokoza maganizo ake. Koma funsolo lisakhale lochititsa manyazi. (Mwachitsanzo, mungasankhe funso limodzi pa mafunso amene ali patsamba 2 la magaziniyo.)
Sankhani lemba loti mukawerenge. (Ngati ndi Galamukani! mungasankhe kukawerenga lemba kapena ayi chifukwa magaziniwa amalembera anthu amene sadziwa bwino Baibulo komanso mwina amakayikira zochita za zipembedzo.)
Konzani mawu amene mungauze munthu amene mukumulalikirayo, omuthandiza kuona mmene angapindulire akawerenga magaziniyo
KAYA MWASANKHA INDE KAPENA AYI:
Konzani funso loti mudzayankhe pa ulendo wobwereza
Lembani mfundo zokuthandizani kukumbukira zimene mudzanene