Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb16 March tsamba 2
  • Tidzalandire Bwino Alendo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tidzalandire Bwino Alendo
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
  • Nkhani Yofanana
  • Alandireni Bwino
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Umboni Wamphamvu Udzaperekedwa
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Kodi Tingathandize Bwanji Anthu Obwera pa Chikumbutso?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Achititseni Kudzimva Olandiridwa pa Chikumbutso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
mwb16 March tsamba 2

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Tidzalandire Bwino Alendo

Pamwambo wa Chikumbutso womwe udzachitike pa 23 March, tikuyembekezera kudzakhala ndi alendo oposa 12 miliyoni. Iwo adzakhala ndi mwayi womva za mphatso ya dipo limene Yehova anapereka komanso madalitso ena omwe tidzapeze chifukwa cha mphatso imeneyi. (Yes. 11:6-9; 35:5, 6; 65:21-23; Yoh. 3:16) Komabe alendowa adzaphunziranso zinthu zambiri kuchokera kwa ena tonsefe osati kwa wokamba nkhani yekha. Tonsefe tili ndi udindo wodzalandira bwino alendowa. (Aroma 15:7) Mwina tingadzachite zotsatirazi:

Wamboni za Yehova akulandira mlendo amene wabwera pa Chikumbutso; Wamboni za Yehova akuona baibulo lake ndi mlendo amene wabwera pa Chikumbutso
  • M’malo mongokhala pampando wathu n’kumadikira kuti mwambo uyambe, tingadzachite bwino kulandira mwansangala alendo komanso anthu amene anasiya kusonkhana

  • Posamalira anthu amene tinawaitana, tisadzaiwale anthu enanso amene ndi alendo pamwambowo. Tingadzawapemphe kuti tikhale nawo pamodzi n’kumaona limodzi Baibulo ndi nyimbo

  • Mwambowu ukadzatha, tidzapeze nthawi yoyankha mafunso awo. Ngati tikufunika kupereka mpata kuti mpingo wina uchitenso Chikumbutso, tingadzakonze zoti tikumane nawo pasanathe masiku ambiri. Alendo amene sitikudziwa kumene amakhala tingadzawafunse kuti: “Kodi ndingakupezeni bwanji kuti tidzakambirane mmene mwaonera mwambowu?”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena