Nyimbo 147
Chuma Chapadera
Odzozedwa ndi mtundu,
Watsopano wa M’lungu.
Iye anawagula,
Padziko lapansi.
(KOLASI)
N’chuma chapadera,
Otchedwa dzina lanu
Amakukondani.
Amalengezadi za inu.
Ndi mtundu woyeradi,
Wophunzitsa cho’nadi.
Mulungu wawapatsa
Kuwala kwakedi.
(KOLASI)
N’chuma chapadera,
Otchedwa dzina lanu
Amakukondani.
Amalengezadi za inu.
Amasonkhanitsanso,
Nkhosa zina mwakhama.
Ndi okhulupirika.
Kwa Mwanawankhosa.
(KOLASI)
N’chuma chapadera,
Otchedwa dzina lanu
Amakukondani.
Amalengezadi za inu.
(Onaninso Yes. 43:20b; Mal. 3:17; Akol. 1:13.)