Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 4/06 tsamba 14-16
  • Ulendo wa Tsiku Limodzi wa ku Chernobyl

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ulendo wa Tsiku Limodzi wa ku Chernobyl
  • Galamukani!—2006
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Tchuthi Chomvetsa Chisoni Kwambiri
  • Nthawi Yoganizira Zinthu Mofatsa
  • Chiwopsezo cha Nyukliya Kodi Chatha Tsopano?
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Zamkatimu
    Galamukani!—2006
  • Kodi Nkhondo ya Nyukiliya Angaichititse Ndani?
    Galamukani!—2004
  • Kulondola Zoyambitsa za Kuipitsa
    Galamukani!—1988
Onani Zambiri
Galamukani!—2006
g 4/06 tsamba 14-16

Ulendo wa Tsiku Limodzi wa ku Chernobyl

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU UKRAINE

Ngozi ngati yomwe inachitika ku Chernobyl zaka 20 zapitazo, ya kuphulika kwa fakitale ya mphamvu za nyukiliya, inali isanachitikepo. Pa April 26, 1986, chithanki chimodzi mwa mathanki anayi opangira mphamvu za nyukiliya pamalowa, chinasungunuka n’kuphulika, yomwe inali ngozi yoopsa kwambiri. Pambuyo pa tsoka lililonse, kaya lochitika chifukwa cha anthu kapena lachilengedwe, zimatheka kukonzanso bwinobwino malo omwe pachitikira tsokalo n’kuwabwezeretsa mwakale. Koma ngozi iyi inawononga kwambiri malowo ndipo m’povuta kuti akonzedwenso bwinobwino.

KWA zaka zingapo zapitazo, pa May 9 chaka chilichonse, anthu omwe ankakhala m’matawuni akufupi ndi malowa, limodzi ndi anzawo ndiponso achibale awo, akhala akupanga ulendo wapadera wopita ku nyumba zowonongeka zimene ankakhalamo kale. Nthawi zina iwo akhala akupitako kukachita miyambo ya maliro. Akatswiri a sayansi akhala akupitako kukaona mmene mpweya wapoizoni umawonongera zinthu. Komanso, chaposachedwapa makampani a ku Ukraine osonyeza anthu malo, akhala akukonza maulendo a tsiku limodzi okaonetsa anthu malowa.

Mu June 2005, patsamba loyamba la nyuzipepala ya The New York Times panali nkhani yomwe inafotokoza za “maulendo [afupiafupi] okhala ndi woperekeza,” opita ku Pripet omwe “sangaike umoyo wa munthu pangozi.”a Mzinda wa Pripet, womwe uli pamtunda wa makilomita pafupifupi atatu kuchokera pafakitale yopanga mphamvu za nyukiliyayo, unakhazikitsidwa m’ma 1970, ndipo unali ndi anthu pafupifupi 45,000. Koma anthu anasamukamo, ngati momwenso anachitira m’mizinda ina yambiri, pambuyo pa ngozi ya nyukiliyayo. Kuchokera nthawi imeneyo, malo ngati amenewa anakhala oletsedwa chifukwa cha mpweya wa poizoni. Panthawi yomwe chithanki chinaphulikayo, n’kuti Anna ndi Victor Rudnik atakhala ku Pripet pafupifupi chaka chimodzi.b

Tawuni ya Chernobyl (lomwenso ndi dzina la malo amene pali fakitale yopanga mphamvu za nyukiliya), yomwe ndi yaing’ono kwambiri, ili pafupifupi makilomita 15 kuchokera pa fakitaleyo. Patha zaka zingapo tsopano kuchokera pamene anthu amene ankakhala m’tawuniyi anayamba kuloledwa kupitako kamodzi pachaka. Popeza kuti ku Chernobyl ndiye kwawo kwenikweni kwa banja la a Rudnik, iwonso amapitako. Ndiloleni ndilongosole za ulendo wokaonako umene ine ndi mkazi wanga ndi banja la a Rudnik tinapanga zaka zingapo zapitazo.

Tchuthi Chomvetsa Chisoni Kwambiri

Tinanyamuka ku Kiev, likulu la dziko la Ukraine, n’kutenga msewu wa magalimoto awiri wolowera kumpoto. Tinadutsa m’matawuni ang’onoang’ono omwe ali ndi nyumba m’mphepete mwa msewu, zimene zili ndi maluwa okongola m’mabwalo a kumaso kwake, ndipo anthu anali m’minda yawo ya ndiwo zamasamba. Pakati pa matawuniwo panali minda ikuluikulu ya chimanga, tirigu, ndi mpendadzuwa.

Koma titafika penapake tinaona kusintha mwadzidzidzi ngati kuti tawoloka malire. Koma sikuti mu msewu munali chizindikiro chilichonse chosonyeza kusinthaku. M’matawuni omwe tinkadutsa munali bata. Nyumba zomwe zinali zitayamba kusanduka mabwinja zinali ndi mawindo oswedwa, ndiponso zitseko zake zinali zokhoma. Kumaso kwa nyumbazi kunali kutamerera udzu ndipo namonso m’minda munali tchire.

Tinali titalowa m’malo oletsedwa, mwina makilomita 30 kuchokera pafakitale ya mphamvu ya nyukiliya ija. Anna anatiuza kuti: “M’matawuni akuno muli mpweya wambiri wa poizoni. Anthu oposa 150,000 ochokera m’matawuni ndi kumidzi yambiri ya kuno anawasamutsira ku madera osiyanasiyana m’dziko lonse lakale la Soviet Union.”

Titangopitira pang’ono ndi ulendo wathu, tinafika pamalo ena, omwe ali ndi mpanda wautali wa waya wamingaminga womwe unazungulira malo onse oletsedwawo. Pafupi ndi malowa, alonda omwe anali m’nyumba ina ya matabwa, ngati pamalo olipirira kasitomu, ankaona za galimoto zonse zodutsapo. Mlonda wina anaona ziphaso zathu, n’kulemba za galimoto yathu m’buku, kenako n’kutitsekulira geti.

Apa tsopano tinali titalowa m’malo oletsedwa. Msewu wake unadutsa m’katikati mwa mitengo yongophuka kumene masamba. Ndipo m’kati mwa mitengoyo munali zitsamba zothinana kwambiri, zosagwirizana m’pang’ono pomwe ndi zimene ndinali kuyembekezera kuona. Ndinkaganiza kuti ndiona mitengo yowauka ndiponso zitsamba zokhwinyatakhwinyata. Kutsogolo kwathu tinaona chipilala cha njerwa zoyera chili ndi malemba obiriwira osonyeza kuti ndi tawuni ya Chernobyl.

M’malire mwa tawuni ya Chernobyl munali sitolo yogulitsira mankhwala. Nthawi ina amayi a Victor ankagwira ntchito m’sitoloyi. Pawindo la sitoloyo, lomwe ndi lafumbi ndiponso matope, padakali kachikwangwani kosuluka kosonyeza nthawi zotsegulira sitiloyo. Chakufupi ndi paki ya tawuniyi pali nyumba ya zachikhalidwe. Anna anakumbukira kuti iye ndi anthu ena m’tawuniyo ankapita ku nyumbayi kukapuma akamaliza ntchito, n’kumaonerera zionetsero za akatswiri osiyanasiyana. Kufupi ndi nyumba imeneyi, kunali nyumba yoonetseramo mafilimu, yotchedwa Ukraina, komwe ana ankati kunja kukatentha kwambiri ankapitako kukaonerera mafilimu atsopano, m’malo ozizira bwino. Lero, m’chipinda china cha mdima m’nyumbayo, simumvekanso anthu akuseka. Anna ndi Victor anatilondolera ku nyumba yawo, yomwe siili patali kwenikweni kuchokera pakatikati pa tawuniyi. Mitengo yosasadzila inatseka khomo la kumaso kwa nyumbayi, moti tinachita kundondozana, tikuwanda tchire lomwe linamerera panyumbayo, n’kupita ku khomo la kuseri, limene panthawiyi linangokhala chibowo basi.

M’kati mwake munali mowonongeka kwambiri. Pabedi lina lomwe linachita dzimbiri panali matilesi omwe anachita nkhungu. Khoma lamapepala m’nyumbayo linali lomatukamatuka, ndipo mapepala omatukawo ankangooneka ngati madzi amatope omwe anali kuyenderera n’kuuma mwadzidzidzi chifukwa cha kuzizira. Anna anawerama kuti atole chithunzi chinachake chakale chomwe chinali pazinyalala zomwe zinangoti mbwee m’chipindamo. Analankhula mwachisoni kuti: “Ndakhala ndikufunitsitsa kubwerera n’kudzapeza zonse mmene tinazisiyira. Zimandiwawa kuona nyumba yathuyi itasanduka bwinja; katundu wathu atabedwa!”

Tinachoka ku nyumba ya a Rudnik n’kuyenda motsata msewu. Penapake tinapeza gulu la anthu likucheza mosangalala. Tinayenda mwina theka la kilomita n’kufika pothera msewuwo, m’paki ina yomwe ili pakamtunda komwe kali m’mphepete mwa mtsinje wina wabata kwambiri. Kamphepo kayeziyezi kanali kuomba maluwa a mitengo ina yomwe imabala mtedza. Pamalo amenewa, anthu ankhaninkhani anaima pa masitepe ake mu 1986, kudikirira kusamutsidwa pa bwato.

Chaka chathachi, banja la a Rudnik linapita kwa nthawi yoyamba kukaona nyumba yawo yakale ku Pripet. Panthawiyi anali atatha zaka 19 chisamukire mu mzindawo chifukwa cha kuphulika kwa chithanki kuja.

Nthawi Yoganizira Zinthu Mofatsa

Mu April 2006, anthu akhala akuchita miyambo yosiyanasiyana yokumbukira kuti patha zaka 20 chichitikireni ngozi ya nyulikiya ija. Kwa anthu ambiri, miyambo imeneyi imawakumbutsa za kulephera kwa anthu, ngakhale atayesetsa motani, kulongosola zochitika padziko lapansi pano popanda kutsogoloredwa ndi Mulungu.—Yeremiya 10:23.

Mu September wapitayu munatuluka lipoti la akatswiri a sayansi la zomwe anapeza ataonanso mmene ngoziyo inawonongera zinthu. Lipotilo, lomwe bungwe la United Nations ndilo linatulutsa, linanena kuti poyambirira ngoziyo inapha anthu 56 ndipo linati imfa 4,000 zokha ndi zomwe zinganenedwe kuti zinachitika chifukwa cha matenda obwera ndi mpweya wa poizoni. Kale ankati anthu pakati pa 15,000 ndi 30,000 ndiwo angamwalire. Nkhani ya mkonzi m’nyuzipepala ya New York Times ya pa September 8, 2005, inafotokoza za lipoti la United Nations limeneli kuti “mabungwe angapo oona za chilengedwe anatsutsa za mu lipotilo ndipo anati ndi lokondera longofuna kuphimba kuopsa kwenikweni kwa mphamvu za nyukiliya.”

Victor amene pambuyo pa ngoziyo anaphunzira za Mlengi wake, Yehova Mulungu, anati: “Sitikuvutikanso maganizo, chifukwa tikudziwa kuti Ufumu wa Mulungu ukadzabwera, ngozi zoopsa ngati zimenezi sizidzachitikanso. Tikuyembekezera nthawi yomwe midzi yozungulira kumudzi kwathu kufupi ndi Chernobyl idzabwerere mwakale n’kukhala mbali ya paradiso wokongola kwambiri.”

Kuchokera nthawi ya ngozi ya ku Chernobyl, anthu ambiri akhala ndi chikhulupiriro pa lonjezo la m’Baibulo lakuti Paradaiso woyambirira adzabwezeretsedwa padziko lapansi ndipo adzafutukuka kufika padziko lonse. (Genesis 2:8, 9; Chivumbulutso 21:3, 4) Ku Ukraine kokha, anthu oposa 100,000 ayamba kukhulupirira nawo zimenezi m’zaka 20 zapitazi. Tikukupemphani kuti nanunso muganizire za tsogolo labwino lomwe anthu ofuna kuphunzira zolinga za Mulungu akulonjezedwa.

[Mawu a M’munsi]

a Ngakhale kuti akuluakulu ena a boma amati maulendo afupiafupi amenewo n’ngosaopsa, Galamukani! sikulimbikitsa munthu kupanga ulendo uliwonse wokaona malowa.

b Onani Galamukani! ya April 22, 1997, masamba 12 mpakana 15.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 16]

Chipilala cha Anthu Omwe Anathandiza pa Ngozi

Chipilala chachikuluchi anachimanga popereka ulemu kwa anthu amene anagwira ntchito zosiyanasiyana pamalo amene panachitikira ngozi ya ku Chernobyl. Anthuwa anazimitsa moto, anamata chithanki chomwe chinkafuka moto, ndiponso anachotsako mpweya wa poizoni. M’kupita kwa nthawi, chiwerengero cha anthuwa chinafika mpaka masauzande ambirimbiri. Anthu amati chiwerengero cha anthu ofa ndi ngoziyi chingakwane pafupifupi 4,000 ndipo ambiri mwa anthu omwalirawo ndi anthu amene anagwira ntchito imeneyi.

[Zithunzi patsamba 15]

Chizindikiro cha tawuni ya Chernobyl, ndi nyumba yake yoonetseramo mafilimu

[Zithunzi patsamba 15]

Banja la a Rudnik ndi nyumba yawo ku Chernobyl

[Zithunzi patsamba 16]

Pachithanki chomwe chinasungunuka n’kuphulika, makilomita pafupifupi atatu kuchokera ku nyumba ya a Rudnik ku Pripet (m’chithunzi chaching’onochi)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena