Mutu 1
Kodi Pali Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja?
1. Kodi nchifukwa ninji mabanja olimba ali ofunika m’chitaganya cha anthu?
BANJA ndilo chigwirizano chakale kuposa zonse padziko lapansi, ndipo limachita mbali yofunika kwambiri m’chitaganya cha anthu. M’mbiri yonse yakale, mabanja olimba achititsa kukhala ndi zitaganya zolimba za anthu. Banja ndilo kakonzedwe kabwino koposa kolereramo ana kuti akule ndi kukhala achikulire anzeru.
2-5. (a) Longosolani chisungiko chimene mwana amamva kukhala nacho m’banja lachimwemwe. (b) Kodi ndi mavuto otani omwe amamveka m’mabanja ena?
2 Banja lachimwemwe ndilo malo othaŵirako achisungiko ndi achitetezo. Kwa kamphindi, tayerekezerani za banja labwino. Pachakudya chawo chamadzulo, makolo osamalawo akhala pansi ndi ana awo akumakambitsirana zochitika za tsikulo. Anawo akulankhula mokondwa pamene akusimbira atate ndi amayi awo zimene zachitika kusukulu. Nthaŵi yakupumula imeneyi ikutsitsimula onse ndi kuwakonzekeretsa tsiku lotsatira pamene adzakhala kunja.
3 M’banja lachimwemwe, mwana amadziŵa kuti atate ndi amayi ake adzamsamalira akadwala, mwinamwake kulandizana pomyang’anira usiku ali m’kama wodwalira. Amadziŵa kuti akhoza kupita kwa amayi kapena atate wake ndi mavuto apaubwana wake ndi kupeza uphungu ndi chichirikizo. Inde, mwana amamva kukhala wosungika, mosasamala kanthu za mavuto ochuluka amene ali kunjako m’dziko.
4 Pamene ana akula, kaŵirikaŵiri amakwatira ndi kukhala ndi banja lawo. Mwambi wina wa Kummaŵa umati: “Munthu amazindikira kuchuluka kwa mangaŵa ake kwa makolo ake atakhala ndi mwana wakewake.” Pokhala ndi chiyamikiro ndi chikondi chachikulu, ana amene tsopano ali achikulire amayesa kuchititsa mabanja awo kukhala achimwemwe, ndipo amasamaliranso makolo awo amene tsopano akukalamba, amenenso amasangalala kukhala pamodzi ndi adzukulu awo.
5 Mwinamwake tsopano mukulingalira kuti: ‘Inde, ndimakonda banja langa, koma silofanana ndi limene lalongosoledwalo. Ine ndi mnzanga timagwira ntchito zosiyana ndipo sitimaonana kaŵirikaŵiri. Nthaŵi zambiri, timangokambitsirana za mavuto azandalama.’ Kapena kodi mukunena kuti, ‘Ana anga ndi adzukulu anga amakhala kutauni ina, ndipo sindimatha kukawaona’? Inde, kaamba ka zifukwa zina zimene sangachitepo kanthu, moyo wa mabanja ambiri sumakhala wabwino kwenikweni. Chikhalirechobe, ena amakhalabe ndi moyo wa banja wachimwemwe. Motani? Kodi pali chinsinsi cha chimwemwe cha banja? Yankho nlakuti chilipo. Koma tisanakambitsirane zimenezo, tiyenera kuyankha funso lofunika kwambiri.
KODI BANJA NCHIYANI?
6. Kodi ndi mabanja a mtundu wotani amene tidzakambitsirana m’buku lino?
6 Kumaiko a Azungu, mabanja ochuluka amakhala a tate, mayi, ndi ana awo. Agogo angamakhale paokha ngati angakhoze. Ngakhale kuti pamakhala kuonana ndi ena achibale chapatali, sipamakhala mathayo kwenikweni kulinga kwa ameneŵa. Kwakukulukulu, banja limeneli n’limene tidzakambitsirana m’buku lino. Komabe, pazaka zaposachedwapa mitundu inanso ya banja yakhala yofala—banja la kholo limodzi, banja lopeza, ndi banja limene makolo sakukhala pamodzi pazifukwa zina.
7. Kodi banja lapachibale nlotani?
7 M’zitaganya zina, banja lapachibale lakhala lofala. M’banja lotero, ngati kuli kotheka agogo amayang’aniridwa nthaŵi zonse ndi ana awo, ndipo mayanjano oyandikana ndi chisamaliro zimaperekedwa kwa achibale ena. Mwachitsanzo, apabanja angathandize kusamalira, kulera, ndipo ngakhale kupereka kusukulu ana a abale kapena a alongo awo, ngakhalenso ena achibale chapatali. Mapulinsipulo amene tidzakambitsirana m’buku lino akugwiranso ntchito pa mabanja apachibale.
BANJA LILI PAVUTO
8, 9. Kodi ndi maumboni otani m’maiko ena amene amasonyeza kuti banja likusintha?
8 Lerolino banja likusintha—nzachisoni kunena kuti, kusinthako sikowongolera zinthu. Chitsanzo chake chikuoneka ku India, kumene mkazi angamakhale pamodzi ndi banja la mwamuna wake ndi kugwira ntchito panyumbapo moyang’aniridwa ndi apongozi ake. Komabe, masiku ano sikwachilendo kuona akazi achiindiya akukaloŵa ntchito kwina. Ngakhale ndi choncho, iwo amafunikabe kuchita ntchito zawo zapanyumba malinga ndi mwambo. Funso limene lafunsidwa m’maiko ambiri nlakuti, Kodi mkazi wogwira ntchito kunja ayenera kuchita ntchito zapanyumba pamlingo wotani poyerekezera ndi ena apabanjapo?
9 Kumaiko a Kummaŵa, maunansi olimba a banja lapachibale ali mwambo. Komabe, posonkhezeredwa ndi mkhalidwe wa Kumadzulo wa dziŵa zako ndi kusamala kwambiri za mavuto azachuma, banja lamwambo lapachibale likufooka. Chotero, ambiri amaona kusamalira achibale okalamba kukhala mtolo m’malo mwa thayo kapena mwaŵi. Makolo ena okalamba amachitiridwa nkhanza. Ndithudi, nkhanza ndi kunyanyala okalamba kumachitika m’maiko ambiri lerolino.
10, 11. Kodi ndi malipoti otani osonyeza kuti banja likusintha m’maiko a ku Ulaya?
10 Kusudzulana kwakhala kofala kwambiri. Mu Spain chiŵerengero cha zisudzulo chinakwera kufika ku 1 pa maukwati 8 pofika kuchiyambi kwa ma 1990—kukwera kwakukulu kochokera pa 1 pa maukwati 100 zaka 25 zokha zinapitapo. Britain, amene akunenedwa kukhala ndi chiŵerengero chachikulu cha zisudzulo kuposa onse mu Ulaya (4 pa maukwati 10 akuoneka kuti adzatha), waona kukwera kwadzidzidzi kwa chiŵerengero cha mabanja a kholo limodzi.
11 Anthu ambiri m’Germany akuoneka kuti akusiyiratu mkhalidwe wa banja lamwambo. M’ma 1990 munali 35 peresenti ya mabanja achijeremani a kholo limodzi ndi 31 peresenti a anthu aŵiri okha. Afalansa ambiri nawonso samakwatira, ndipo amene amatero kaŵirikaŵiri amasudzulana ndipo amatero mofulumira kuposa kale. Owonjezereka amakonda kungokhala pamodzi popanda ukwati. Mikhalidwe yotere ikuoneka padziko lonse.
12. Kodi ana amavutika motani chifukwa cha kusintha kwa banja lamakono?
12 Bwanji ponena za ana? Ku United States ndi kumaiko ena ochuluka, kumabadwa ana ambiri apathengo, ena amabadwa kwa atsikana aang’ono. Atsikana ambiri ali ndi ana angapo a atate osiyanasiyana. Malipoti ochokera padziko lonse amasimba za mamiliyoni a ana opanda kokhala omayendayenda m’makwalala; ambiri amathaŵa nkhanza kunyumba kapena amakanidwa ndi mabanja osakhozanso kuwasamalira.
13. Kodi ndi mavuto ofala ati amene akusoŵetsa chimwemwe m’mabanja?
13 Inde, banja lili pavuto. Kuwonjezera pa zimene tatchulazo, kupanduka kwa achichepere, kugona ana, kumenyana kwa m’nyumba, uchidakwa, ndi mavuto ena othetsa nzeru akusoŵetsa chimwemwe m’mabanja ambiri. Kwa ana ndi achikulire ambiri, banja silili konse malo othaŵirako.
14. (a) Malinga ndi kunena kwa ena, kodi chochititsa mavuto m’banja nchiyani? (b) Kodi loya wa m’zaka za zana loyamba analilongosola motani dziko lamakono, ndipo kukwaniritsidwa kwa mawu ake kwakhala ndi chiyambukiro chotani pamoyo wa m’banja?
14 Kodi nchifukwa ninji banja lili pavuto? Ena amati chochititsa vutoli ndicho kuyamba kuloŵa ntchito kwa akazi. Ena amati chochititsa ndicho kutayika kwa makhalidwe abwino kwamakono. Ndiponso pamatchulidwanso zochititsa zina. Pafupifupi zaka zikwi ziŵiri zapitazo, loya wodziŵika kwambiri ananeneratu kuti mavuto ambiri adzakantha banja, pamene analemba kuti: “Masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiŵembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu.” (2 Timoteo 3:1-4) Ndani kodi amene angakayikire kuti mawuŵa akukwaniritsidwa lerolino? M’dziko la mikhalidwe yonga imeneyi, kodi nkodabwitsa kuti mabanja ambiri ali pavuto?
CHINSINSI CHA CHIMWEMWE CHA BANJA
15-17. Kodi buku lino lidzasonyeza kuti chinsinsi cha chimwemwe cha banja chingapezeke kuti?
15 Uphungu wa mmene anthu angapezere chimwemwe m’banja umaperekedwa kuchokera kulikonse. Kumaiko a Azungu, mabuku ndi magazini ambiri ophunzitsa mmene munthu angadzithandizire payekha amatulutsidwa mosalekeza. Vuto nlakuti aphungu aumunthu amanena zotsutsana ndi anzawo, ndipo umene ungakhale uphungu wabwino lero maŵa ungaonedwe kukhala wosagwira ntchito.
16 Pamenepo, kodi nkuti kumene tingapezeko chitsogozo cha banja chodalirika? Chabwino, kodi mungatembenukire ku buku lolembedwa pafupifupi zaka 1,900 zapitazo? Kapena kodi mungaganize kuti buku lotero liyenera kukhala lachikale losagwiranso ntchito mpang’ono pomwe? Choonadi nchakuti, chinsinsi chenicheni cha chimwemwe cha banja chimapezeka m’buku limenelo.
17 Buku limenelo ndilo Baibulo. Malinga ndi maumboni onse, ilo linauziridwa ndi Mulungu mwiniyo. M’Baibulo timapeza mawu aŵa: “Lemba lili lonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo.” (2 Timoteo 3:16) M’buku lino tidzakulimbikitsani kuona mmene Baibulo lingakuthandizireni ‘kukonza’ zinthu pamene muchita ndi zipsinjo ndi mavuto a m’banja lerolino.
18. Kodi nchifukwa ninji kuli kwanzeru kuvomereza Baibulo monga maziko a uphungu wa ukwati?
18 Ngati mukuona kukhala kosatheka kuti Baibulo lingathandize banja kukhala lachimwemwe, talingalirani izi: Amene anauzira kulembedwa kwa Baibulo alinso Woyambitsa kakonzedwe ka ukwati. (Genesis 2:18-25) Baibulo limati dzina lake ndi Yehova. (Salmo 83:18) Iye ali Mlengi ndi ‘Atate, amene kuchokera kwa iye [banja lililonse, NW] alitcha dzina.’ (Aefeso 3:14, 15) Yehova waona mmene moyo wa banja wakhalira kuchokera pachiyambi cha anthu. Amadziŵa mavuto amene angabuke ndipo wapereka uphungu wowathetsera. M’mbiri yonse yakale, awo amene moona mtima anagwiritsira ntchito mapulinsipulo a Baibulo m’banja lawo anapeza chimwemwe chachikulu.
19-21. Kodi ndi zochitika zamakono ziti zosonyeza kuti Baibulo likhoza kuthetsa mavuto a muukwati?
19 Mwachitsanzo, mkazi wina wapanyumba ku Indonesia anali wotchova juga womwerekera. Kwa zaka zambiri ananyanyala ana ake atatu ndipo anali kukangana nthaŵi zonse ndi mwamuna wake. Ndiyeno anayamba kuphunzira Baibulo. M’kupita kwa nthaŵi mkaziyo anakhulupirira zimene Baibulo limanena. Pamene anagwiritsira ntchito uphungu wake, anakhala mkazi wabwino. Zoyesayesa zake, zozikidwa pa mapulinsipulo a Baibulo, zinabweretsa chimwemwe pabanja lake lonse.
20 Mkazi wina wapanyumba ku Spain anati: “Tinangokhala chaka chimodzi titakwatirana ndipo tinayamba kukhala ndi mavuto aakulu.” Iye ndi mwamuna wake anali osiyana pazinthu zambiri, ndipo sanali kukambitsirana kwambiri koma pokangana. Ngakhale kuti anali ndi mwana wamng’ono wamkazi, iwo anafuna kukapatukana kukhoti. Komabe zimenezo zisanachitike, analimbikitsidwa kuona m’Baibulo. Anaŵerenga uphungu wake wonena za amuna ndi akazi okwatirana ndi kuyamba kuugwiritsira ntchito. Posapita nthaŵi, anayamba kulankhulana mwaubwino ndipo banja lawo laling’onolo linakhalanso logwirizana mwachimwemwe.
21 Baibulo limathandizanso anthu achikulire. Mwachitsanzo, talingalirani za chochitika cha okwatirana aŵiri achijapani. Mwamuna anali wa mtima wapachala ndipo nthaŵi zina wachiwawa. Choyamba, ana awo aakazi anayamba kuphunzira Baibulo, ngakhale kuti makolo awo anatsutsa zimenezo. Ndiyeno, mwamunayo anagwirizana ndi anawo, koma mkazi anapitiriza kutsutsa. Koma m’kupita kwa zaka anaona kuti mapulinsipulo a Baibulo anapangitsa masinthidwe abwino pabanja lake. Ana ake aakaziwo anamusamalira bwino, ndipo mwamuna wakeyo anakhala wofatsa. Masinthidwe otero anasonkhezera mkaziyo kudzionera yekha zimene zili m’Baibulo, ndipo nayenso zinamuthandiza kupanga masinthidwe abwino. Mkazi wachikulireyo ananena mobwerezabwereza kuti: “Tinakhala okwatirana enieni.”
22, 23. Kodi Baibulo limathandiza motani anthu a mitundu yonse kupeza chimwemwe cha moyo wawo wa banja?
22 Ameneŵa ali pakati pa anthu ambirimbiri omwe aphunzira chinsinsi cha chimwemwe cha banja. Alandira uphungu wa Baibulo ndi kuugwiritsira ntchito. Zoona, iwo akukhala m’dziko limodzimodzi lachiwawa, chisembwere, ndi mavuto azachuma mofanana ndi wina aliyense. Ndiponso, iwo ali opanda ungwiro, koma amapeza chimwemwe poyesa kuchita chifuniro cha Woyambitsa kakonzedwe ka banja. Monga momwe Baibulo limanenera, Yehova Mulungu ndiye ‘Amene akuphunzitsani kupindula, Amene akutsogolerani m’njira yoyenera inu kupitamo.’—Yesaya 48:17.
23 Ngakhale kuti Baibulo linamalizidwa pafupifupi zaka zikwi ziŵiri zapitazo, uphungu wake ulidi wapanthaŵi yake. Ndiponso, unalembedwera anthu onse. Baibulo si buku la Aamereka kapena Azungu. Yehova, “ndi mmodzi analenga mitundu yonse ya anthu,” ndipo iye amadziŵa kapangidwe ka anthu kulikonse. (Machitidwe 17:26) Mapulinsipulo a Baibulo amagwira ntchito kwa aliyense. Ngati muwagwiritsira ntchito, inunso mudzadziŵa chinsinsi cha chimwemwe cha banja.