Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ll gawo 1 tsamba 4-5
  • Kodi Mulungu Amalankhula Nafe Motani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mulungu Amalankhula Nafe Motani?
  • Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha
  • Nkhani Yofanana
  • Chigawo 1
    Mverani Mulungu
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Luso Lomvetsera Ena Mwachikondi
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha
ll gawo 1 tsamba 4-5

CHIGAWO 1

Kodi Mulungu Amalankhula Nafe Motani?

Mulungu amalankhula nafe kudzera m’Baibulo. 2 Timoteyo 3:16

Yehova ali pampando wake wachifumu kumwamba, anauzira anthu kuti alembe Baibulo

Mulungu woona anathandiza anthu kuti alembe maganizo ake m’buku limodzi lopatulika. Buku limeneli ndi Baibulo. M’Baibulo muli zinthu zofunika kwambiri zimene Mulungu amafuna kuti muzidziwe.

Mulungu amadziwa zinthu zimene zingatithandize, ndipo iye ndi amene angatipatse nzeru. Choncho ife tingakhale anzeru tikamamvetsera zimene akunena.​—Miyambo 1:5.

Baibulo m’zilankhulo zambirimbiri; munthu akuwerenga Baibulo m’chilankhulo chake

Mulungu amafuna kuti munthu aliyense padziko lapansi aziwerenga Baibulo. Ndipo masiku ano Baibulo likupezeka m’zinenero zambirimbiri.

Ngati mukufuna kumvera Mulungu, muyenera kuwerenga Baibulo ndi kulimvetsa bwino.

Padziko lonse, anthu akumvetsera zimene Mulungu akunena. Mateyu 28:19

Wa Mboni za Yehova akuwerengera munthu lemba kenako akuyamba kuphunzira naye Baibulo

Anthu a Mboni za Yehova angakuthandizeni kuti mulimvetse bwino Baibulo.

Padziko lonse lapansi, iwo amaphunzitsa choonadi chonena za Mulungu.

Misonkhano ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova

Maphunziro amenewa ndi aulere. Mungathe kuphunziranso za Mulungu ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova imene ikupezeka kwanuko.

  • Mawu a Mulungu ndiwo choonadi.​—Yohane 17:17.

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kudalira Mulungu?—Numeri 23:19.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena