Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • scl tsamba 79-83
  • Makhalidwe Oyenera Akhristu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Makhalidwe Oyenera Akhristu
  • Malemba Othandiza pa Moyo wa Chikhristu
Malemba Othandiza pa Moyo wa Chikhristu
scl tsamba 79-83

Makhalidwe Oyenera Akhristu

N’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene amakhulupirira?

Mt 5:14-16; Yak 1:22-25

Kodi Akhristufe tiyenera kutengera zitsanzo ziti?

Yoh 13:15; 1Pe 2:21

Onaninso 1Ak 11:1; 1Yo 2:6

Kodi pangakhale zotsatirapo zotani Akhristu akamatsatira mfundo za Mulungu pa moyo wawo?

2Ak 6:3, 4; 1Pe 2:12

Onaninso 1Ti 4:12; Tit 2:4-8; 1Pe 3:1, 2; 2Pe 2:2

Kodi malemba otsatirawa angathandize bwanji Akhristu kupewa kuchita zoipa?

Miy 4:23-27; Yak 1:14, 15

Onaninso Mt 5:28; 15:19; Aro 1:26, 27; Aef 2:2, 3

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ge 3:1-6​—Hava analephera kugonjetsa maganizo oipa mpaka anachimwa

    • Yos 7:1, 4, 5, 20-25​—Anthu ambiri anaphedwa chifukwa cha tchimo la Akani

Kodi malemba otsatirawa angathandize bwanji Akhristu kuchita zoyenera?

Aro 12:2; Aef 4:22-24; Afi 4:8; Akl 3:9, 10

Onaninso Miy 1:10-19; 2:10-15; 1Pe 1:14-16

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ge 39:7-12​—Yosefe anathawa mayesero ochokera kwa mkazi wa Potifara

    • Yob 31:1, 9-11​—Yobu anatsimikiza mtima kuti sadzayang’ana mosirira mkazi yemwe si wake

    • Mt 4:1-11​—Yesu anakana mayesero ochokera kwa Satana

Kodi Akhristu Ayenera kupewa maganizo olakwika ati?

Onani “Maganizo Olakwika”

Kodi Akhristu ayenera kupewa makhalidwe oipa ati?

Onani “Makhalidwe Oipa”

Ndi makhalidwe abwino ati amene Akhristu ayenera kukhala nawo?

Khalidwe loyera

2Ak 11:3; 1Ti 4:12; 5:1, 2, 22; 1Pe 3:1, 2

Onaninso Afi 4:8; Tit 2:3-5

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ge 39:4-12​—Yosefe anakhalabe ndi khalidwe loyera ngakhale kuti mkazi wa Potifara ankamunyengerera kuti agone naye

    • Nym 4:12; 8:6​—Msulami anakhalabe wokhulupirika kwa mnyamata amene ankakondana naye ndipo anakana kuchita chiwerewere; iye anali ngati munda umene watsekedwa

Kudalira Yehova

Onani “Kudalira Yehova”

Kuona ena kukhala otiposa

Onani “Kudzichepetsa”

Kukhutira

Onani “Kukhutira”

Kugwirizana ndi ena

Mla 4:9, 10; 1Ak 16:16; Aef 4:15, 16

Onaninso Sl 110:3; Afi 1:27, 28; Ahe 13:17

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 1Mb 25:1-8​—Davide anasonkhanitsa akatswiri oimba nyimbo komanso oimba ndi zida kuti azichita utumiki wopatulika. Kuti zimenezi zitheke, anthuwa ankafunika kumachita zinthu mogwirizana

    • Ne 3:1, 2, 8, 9, 12; 4:6-8, 14-18, 22, 23; 5:16; 6:15​—Yehova anadalitsa anthu ake chifukwa anali ndi mtima wofunitsitsa kugwira ntchito limodzi mogwirizana, moti anatha kumanganso mpanda wa Yerusalemu masiku 52 okha

Kulimba mtima

Onani “Kulimba Mtima”

Kulimbikitsa ena; kukhala wolimbikitsa

Yes 35:3, 4; Aro 1:11, 12; Ahe 10:24, 25

Onaninso Aro 15:2; 1At 5:11

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • 1Sa 23:15-18​—Yonatani analimbikitsa Davide pa nthawi imene Mfumu Sauli inkafuna kumupha

    • Mac 15:22-31​—Bungwe lolamulira la m’nthawi ya atumwi linatumiza kalata kumipingo ndipo mipingo inalimbikitsidwa

Kupirira; kukhala olimba; kusasunthika

Mt 24:13; Lu 21:19; 1Ak 15:58; Aga 6:9; Ahe 10:36

Onaninso Aro 12:12; 1Ti 4:16; Chv 2:2, 3

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ahe 12:1-3​—Mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito chitsanzo cha Yesu polimbikitsa Akhristu pa nkhani yopirira

    • Yak 5:10, 11​—Yakobo anagwiritsa ntchito chitsanzo cha kupirira kwa Yobu komanso mmene Yehova anamudalitsira

Kukhulupirika m’zinthu zonse

Lu 16:10

Onaninso Ge 6:22; Eks 40:16

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Da 1:3-5, 8-20​—Mneneri Danieli ndi anzake atatu sanasunthike pa nkhani yosadya zakudya zomwe zinali zoletsedwa m’Chilamulo cha Mose

    • Lu 21:1-4​—Yesu anayamikira mkazi wamasiye amene anapereka timakobidi tiwiri tating’ono chifukwa anasonyeza chikhulupiriro champhamvu

Kuopa Yehova

Yob 28:28; Sl 33:8; Miy 1:7

Onaninso Sl 111:10

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ne 5:14-19​—Bwanamkubwa Nehemiya ankaopa Yehova ndipo sankapondereza anthu a Mulungu mosiyana ndi mmene ankachitira abwanamkubwa ena

    • Ahe 5:7, 8​—Yesu anatisonyeza chitsanzo chabwino pa nkhani yoopa Yehova

Makhalidwe amene anthu amakhala nawo mothandizidwa ndi mzimu

Onani “Chipatso cha Mzimu wa Mulungu”

Kuwolowa manja

Onani “Kuwolowa Manja”

Kukhala wodzipereka kwa Mulungu

1Ti 6:6; 2Pe 2:9; 3:11

Onaninso 1Ti 5:4; 2Ti 3:12

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Mac 10:1-7​—Ngakhale kuti Koneliyo sanali Myuda, Yehova anamuona kuti anali wodzipereka pa nkhani yopemphera, anali woopa Mulungu komanso wopatsa mosaumira

    • 1Ti 3:16​—Yesu anali chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yodzipereka kwa Mulungu

Kulankhula mokoma mtima, molimbikitsa

Miy 12:18; 16:24; Akl 4:6; Tit 2:6-8

Onaninso Miy 10:11; 25:11; Akl 3:8

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Sl 45:2​—Ulosi wokhudza Mesiya unaneneratu kuti Mfumu imene Yehova adzasankhe izidzalankhula mokoma mtima

    • Lu 4:22​—Anthu anakhudzika ndi mawu okoma mtima amene Yesu ankalankhula

Kuona mtima

Onani “Kuona Mtima”

Kuchereza

Onani “Kuchereza”

Kudzichepetsa; kusadzikweza

Onani “Kudzichepetsa”

Kupanda tsankho

Onani “Kupanda Tsankho”

Kugwira ntchito mwakhama; moyo wonse

Onani “Ntchito”

Mtima woongoka

Onani “Mtima Woongoka”

Kuchita zinthu moganizira ena

1Ak 10:24; Afi 2:4; 1At 5:14, 15

Kukhulupirika

Onani “Kukhulupirika”

Chifundo

Onani “Chifundo”

Kuchita zinthu mosapitirira malire

1Ti 3:2, 11; Tit 2:2

Onaninso Miy 23:1-3; 25:16

Kumvera

Onani “Kumvera”

Dongosolo

Aga 5:25; 1Ti 3:2

Onaninso Afi 3:16

Kulimbikira kupemphera

Sl 141:1, 2; Aro 12:12; Akl 4:2; 1At 5:17; 1Pe 4:7

Onaninso “Pemphero”

Kukonzeka kukhululuka

Onani “Kukhululuka”

Kusonyeza ulemu

Afi 2:3, 4; 1Pe 3:15

Onaninso Aef 5:33; 1Pe 3:1, 2, 7

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Nu 14:1-4, 11​—Aisiraeli sanalemekeze mneneri Mose ndi Mkulu wa Ansembe Aroni ndipo Yehova anaona kuti zimene anachitazi kunali kusalemekeza iyeyo

    • Mt 21:33-41​—Yesu anagwiritsa ntchito fanizo posonyeza zomwe zidzachitikire anthu amene salemekeza aneneri a Yehova komanso Mwana Wake

Uzimu; kuika zofuna za Yehova pamalo oyamba

Mt 6:33; Aro 8:5; 1Ak 2:14-16

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ahe 11:8-10​—Abulahamu analolera kukhala m’matenti m’dziko lachilendo chifukwa ankaona kuti Ufumu wa Mulungu ndi weniweni

    • Ahe 11:24-27​—Zimene mneneri Mose anasankha kuchita pa moyo wake zinkasonyeza kuti ankaona kuti Yehova ndi weniweni

Kugonjera

Aef 5:21; Ahe 13:17

Onaninso Yoh 6:38; Aef 5:22-24; Akl 3:18

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Lu 22:40-43​—Yesu anasonyeza chitsanzo chabwino pa nkhani yogonjera Atate wake ngakhale pa nthawi imene zinali zovuta kwambiri kuchita zimenezi

    • 1Pe 3:1-6​—Mtumwi Petulo anagwiritsa ntchito chitsanzo cha Sara posonyeza zimene akazi a Chikhristu ayenera kuchita pa nkhani yogonjera

Chifundo chachikulu

Onani “Kumvera Ena Chisoni”

Kunena zoona

Onani “Kuona Mtima”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena