15 NAOMI NDI RUTE
Anathandizana pa Nthawi ya Mavuto
NAOMI anakumana ndi mavuto motsatizanatsatizana. Ku Isiraeli kutagwa njala, mwamuna wake anaganiza zosamutsa banja lawo ku Betelehemu, kupita ku Mowabu. Koma nthawi ina, mwamuna wakeyo anamwalira ndipo anamusiya ndi ana aamuna awiri m’dziko lachilendo. Patapita nthawi, ana aja anadzakwatira atsikana a ku Mowabu omwe sankalambira Yehova. Patatha zaka 10, anyamata aja anamwalira asanakhale n’komwe ndi ana. Tsopano Naomi anataya mwamuna wake komanso ana ake aamuna ndipo analibenso chiyembekezo chodzaona zidzukulu.
Naomi anaona kuti palibenso chifukwa chokhalira ku Mowabu, choncho anaganiza zobwerera ku Betelehemu ndipo ulendowu ukanamutengera wiki yathunthu. Azipongozi ake, Rute ndi Olipa, ananyamuka nawo pa ulendowo. Naomi sankafuna kuwatenga ndi kuwasiyanitsa ndi achibale awo. Mwina ankaganiza kuti akapita nawo ku Isiraeli, sadzakhala ndi mwayi wokwatiwanso n’kukhala ndi ana. Choncho iye anauza azipongozi akewa kuti abwerere. Naomi analimba mtima kuti akhoza kuyenda yekha pa ulendowo. Olipa analira n’kubwerera. Ngakhale kuti Rute nayenso analira, koma sanafune kusiyana ndi apongozi ake.
Rute anauza apongozi ake kuti: “Musandichonderere kuti ndikusiyeni, . . . chifukwa kumene inu mupite inenso ndipita komweko ndipo kumene mugone inenso ndigona komweko. Anthu a mtundu wanu adzakhala anthu a mtundu wanga ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga. Kumene inu mudzafere inenso ndidzafera komweko ndipo ndidzaikidwanso komweko.” Mtsikana wokhulupirika komanso wolimba mtimayu anasankha kuti nayenso azitumikira Yehova, Mulungu wa Naomi.
Azimayi awiri omwe anaferedwa, anatonthozedwa atakhala pakati pa anthu a Yehova
Choncho Rute analolera kusiya achibale ake, chikhalidwe chake komanso milungu ya ku Mowabu n’kupita ku Isiraeli. Rute ndi Naomi atafika ku Betelehemu, azimayi ambiri anadabwa kuona Naomi atasintha kwambiri. Iye anadandaula kuti Yehova anamulanda chilichonse n’kumusiya ali wokhumudwa komanso wopanda kanthu. N’kutheka kuti Rute anakhumudwa ndi zomwe apongozi ake analankhula chifukwa anawachitira zambiri powathandiza. Koma Baibulo silifotokoza ngati Rute anadandaula nazo. M’malomwake, iye ankagwira ntchito yokunkha m’minda yapafupi kuti apeze chakudya cha iye ndi apongozi ake.
Munthu wina wolemera dzina lake Boazi, mwana wa Rahabi, anaona kuti Rute ankagwira ntchito mwakhama ndipo iye anafunsa munthu wina kuti adziwe za Rute. Boazi anali mtumiki wokhulupirika wa Yehova. Iye anamva mmene Rute anathandizira apongozi ake ndipo anamuyamikira chifukwa chodalira Yehova Mulungu kuti adzawasamalira. Anaonetsetsanso kuti Rute sakuvutitsidwa ndi antchito ake aamuna.
Madzulo a tsikulo, Naomi atamva zomwe Boazi anachitira Rute, anasangalala kwambiri. Anaganiza kuti mwina Boazi akwatira Rute. Boazi anali wachibale, ndipo Chilamulo cha Mulungu chinkapereka mwayi kwa akazi amasiye achitsikana kuti akhoza kukwatiwa ndi wachibale wa mwamuna wawo amene anamwalira. Zimenezi zinkathandiza kuti akhale ndi mwana wodziwika ndi dzina la mwamuna wawo wakale n’cholinga choti mzere wa banja lake mwamunayo ndiponso cholowa chake zikhalepobe. (Deut. 25:5, 6) Ndipo Naomi anauza Rute zoti achite.
Iye anavomera kuchita zomwe apongozi ake anamuuza ngakhale kuti zinali zachilendo komanso zochititsa mantha. Rute anapita kumalo opunthira mbewu usiku komwe nthawi zambiri amuna ankagona pamulu wa tirigu womwe akolola. Iye anafika mwakachetechete n’kuvundukula chofunda kumapazi a Boazi n’kugona komweko. Boazi atadzidzimuka, modzichepetsa, Rute anamufunsa ngati angathe kumuwombola. N’kutheka kuti Boazi anazindikira kuti Rute ankachita mantha. Boazi anayamikira Rute chifukwa cha kulimba mtima komanso chikondi chake chokhulupirika kwa Yehova ndi apongozi ake. Iye anavomera zomukwatira koma anamuuza kuti atsimikizire kaye ngati zinalidi zotheka.
Tsiku lotsatira, Boazi anapita kwa akuluakulu amumzindawo ndipo anachita zonse mogwirizana ndi Chilamulo n’kukwatira Rute. Patapita nthawi, Rute anakhala ndi mwana wamwamuna dzina lake Obedi. Naomi ankasangalala kwambiri ndi chidzukulu chakechi. Mumzere wa Obedi ndi mmene munadzabadwa Mfumu Davide komanso m’kupita kwa nthawi, Mesiya anadzabadwiranso mumzere womwewo. (Mat. 1:5, 6, 16) Yehova anadalitsa Naomi ndi Rute chifukwa cha kulimba mtima kwawo.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Naomi ndi Rute anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. Kodi n’chifukwa chiyani lamulo loti osauka azikunkha, linali lapadera? (ia 39 ¶23, mawu a m’munsi) A
Chithunzi A
Chithunzi A
2. N’chifukwa chiyani sitinganene kuti Rute anapita kwa Boazi usiku ali ndi zolinga zolakwika? (ia 47 ¶17-18)
3. Boazi anatchula Rute kuti “mwana wanga.” Kodi zimenezi zikutiuza chiyani zokhudza Boazi? (Rute 2:8; w16.11 3)
4. Mosiyana ndi munthu wongodziwika kuti Uje, kodi Boazi anasonyeza bwanji kuti sanali wodzikonda povomera kukwatira Rute? (w23.03 14) B
Chithunzi B
Zomwe Tikuphunzirapo
Kodi tingaphunzire chiyani pa khama ndi mtima woyamikira wa Rute tikamalimbana ndi mavuto azachuma? C
Chithunzi C
Naomi ali wokhumudwa, Rute anamuthandiza. Tingaphunzire chiyani kwa Naomi pokhala odzichepetsa ndi kuvomera kuti ena atithandize? Nanga tingaphunzire chiyani kwa Rute pa nkhani yolimbikitsa anzathu?
Kodi tingatsanzire kulimba mtima kwa Naomi ndi Rute m’njira zinanso ziti?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Naomi ndi Rute akadzaukitsidwa?
Phunzirani Zambiri
Kodi tapeza maphunziro otani m’buku la Rute pa nkhani yosonyeza chikondi chokhulupirika, nanga tingawagwiritse ntchito bwanji pa moyo wathu?
“Pitirizani Kusonyezana Chikondi Chokhulupirika” (w21.11 8-13)
Gwiritsani ntchito zithunzi zofotokoza nkhani za m’Baibulo kuthandiza banja lanu kuyerekezera kuti mukuona mmene zinthu zinalili pa nthawiyo.