17 YAELI
“Mkazi Wodalitsika Kwambiri”
SISERA anathawa asilikali ake m’chigwa cha Yezereeli n’kuwasiya okha kuti afe. N’kutheka sanakhulupirire kuti asilikali ake amphamvu okhala ndi magaleta oopsa okwana 900, angagonjetsedwe ndi asilikali oyenda pansi a Aisiraeli omwenso analibe zida zamphamvu. Sisera ankangoganizira za malo oti abisale. Iye anathawira ku tenti ya Hiberi Mkeni.
Akeni anali pa ubale ndi Aisiraeli. Ubale wawo unayambira m’nthawi ya Mose. Mkazi wa Mose anali Mkeni. Pa nthawiyi, Akeni ankakhala ku Isiraeli. Koma mosiyana ndi Akeni anzake omwe ankagwirizana ndi Aisiraeli, Hiberi ankagwirizana ndi Yabini mfumu ya ku Kanani. N’chifukwa chake Sisera anaona kuti akhoza kutetezeka ngati atathawira ku tenti ya Hiberi. Zikuoneka kuti sanaganizireko kuti Yaeli mkazi wa Hiberi, angakhale kumbali ya Aisiraeli.
Mwamuna wake atachokapo, Yaeli anatsala mutenti. Ataona Sisera akuyandikira tenti yawo, anafunika kuganiza mwamsanga zoti achite. Iye ankadziwa bwino kuti Sisera anali munthu woopsa. N’kutheka kuti sankadziwa kuti Yehova analosera kudzera mwa mneneri wamkazi Debora zokhudza Sisera, kuti adzaphedwa ndi munthu wamkazi osati mwamuna. Komabe zikuoneka kuti Yaeli ankadziwa zomwe Yehova ankayembekezera kuti iye achite. N’chifukwa chiyani tikutero?
Patapita nthawi, mouziridwa Debora anapeka nyimbo yonena za nkhondo ya Baraki yomwe anagonjetsa Sisera. Iye anati: “Mkazi wodalitsika kwambiri ndi Yaeli mkazi wa Hiberi Mkeni. Ndi wodalitsika kwambiri pakati pa akazi onse okhala mʼmatenti.” Choncho Yaeli sanali mkazi woipa komanso wabodza ngati mmene ena amanenera. Koma anali wolimba mtima pomenya nkhondo za Yehova. Mofanana ndi Rahabi, iye anasankha kukhala kumbali ya Yehova. Ankadziwa kuti Sisera ndi mdani wa Yehova ndipo ankafunika kuphedwa. Koma kodi Yaeli akanakwanitsa bwanji kupha Sisera?
Yaeli ankadziwa kuti analibe mphamvu zoti n’kumenyana ndi Sisera. Sisera anali msilikali wodziwa nkhondo ndipo n’zosakayikitsa kuti anali wamphamvu. Yaeli anamuitanira mutenti mwake kuti apume ndipo anamufunditsa bulangete. Sisera atamupempha madzi akumwa, Yaeli anamupatsa mkaka. Zitatero anamuuza kuti aime kutsogolo kwa tentiyo ndipo aliyense akafunsa za iye, amuuze kuti kulibe. Kenako anagona tulo tofa nato.
Mulungu anasankha munthu wamkazi kuti aphe msilikali woopsa kwambiri
Yaeli anaona kuti tsopano unali mwayi wake woti aphe Sisera. Iye anatenga hamala ndi chikhomo cha tenti zomwe ankazigwiritsa ntchito nthawi zonse ndipo mwina zinali zamtengo. Iye anayenda monyang’ama n’kukafika pomwe Sisera anagona ndipo anawerama kuti amuphe. Ngati Yaeli akanachita zinthu mosasamala, akanaphedwa mwankhanza. Komabe iye anachita zinthu mosamala kwambiri. M’kanthawi kochepa, anapha Sisera pomukhomerera ndi chikhomo cha tenti m’mutu.
Kenako Woweruza Baraki anatulukira akusakasaka Sisera ndipo Yaeli anatuluka kukakumana naye. Iye anamuuza kuti: “Bwerani ndikuonetseni munthu amene mukumʼfunafunayo.” Atalowa mutentimo, anaona kuti mawu a mneneri wamkazi Debora, akwaniritsidwa akuti, “Yehova adzapereka Sisera mʼmanja mwa munthu wamkazi.”
Munyimbo yomwe anaimba atapambana pa nkhondo, Baraki ndi Debora anayamikira kwambiri Yaeli. Kenako Baibulo silinenanso chilichonse chokhudza Yaeli. Ngakhale kuti padutsa zaka zoposa 3,200 timaphunzirabe pa chitsanzo chake. Masiku ano atumiki a Mulungu samenya nkhondo ya zida. Koma ali pa nkhondo yauzimu. Kuposa kale lonse, panopo m’pamene tikufunika kukhala olimba mtima kwambiri ngati Yaeli.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Yaeli anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa nkhondo ya Sisera ndi nkhondo ya Aramagedo? (w19.09 8-9 ¶3-6)
2. Hiberi mwamuna wa Yaeli anachita mgwirizano ndi Akanani omwe anali adani a Aisiraeli. Koma kodi panali ubale wotani pakati pa Hiberi ndi Aisiraeli? (it “Hiberi” Na. 2-wcgr)
3. Kodi nkhondo imene Aisiraeli anagonjetsa Sisera ndi Yabini, inalimbitsa bwanji chikhulupiriro cha anthu a Mulungu patadutsa zaka zambiri? (w08 10/15 14-15 ¶12-15)
4. N’chifukwa chiyani n’zochititsa chidwi kuti Debora anayamikira kwambiri Yaeli, nanga tikuphunzirapo chiyani? (w15 8/1 15 ¶3) A
Chithunzi A
Chithunzi A
Zomwe Tikuphunzirapo
Ndi pa nthawi iti yomwe mlongo amene ali pa banja ndi mwamuna yemwe satumikira Yehova, angafunikire kulimba mtima ngati Yaeli?
Yaeli sanali mneneri ngati Debora kapenanso msilikali ngati Baraki. Koma anachita zomwe akanakwanitsa. Kodi tingamutsanzire bwanji ngati tikuona kuti sitingakwanitse kuchita zinthu zinazake? B
Chithunzi B
Kodi mungatsanzire kulimba mtima kwa Yaeli m’njira zinanso ziti?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Yaeli akadzaukitsidwa?
Phunzirani Zambiri
Muvidiyoyi, onani mmene chitsanzo cha Yaeli chalimbikitsira mlongo wina wachitsikana kuti alalikire.
Musamatsanzire Anthu Amantha, Koma Olimba Mtima—Osati Anthu a ku Merozi, Koma Yaeli (1:40)
Yaeli ndi mmodzi wa azimayi omwe tingaphunzire zambiri kuchokera pa zomwe anachita. Werengani nkhani zokhudza azimayi enawo.
“Kodi Tingaphunzire Chiyani kwa Akazi Otchulidwa M’Baibulo?” (ijwbq nkhani 161)