Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wcg mutu 18 tsamba 86-tsamba 89
  • Anali Wolimba Mtima Komanso Ankachita Zinthu Mosamala

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anali Wolimba Mtima Komanso Ankachita Zinthu Mosamala
  • Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zoti Mufufuze
  • Zomwe Tikuphunzirapo
  • Ganizirani Mfundo Yaikulu
  • Phunzirani Zambiri
  • “Lupanga la Yehova ndi la Gideoni”
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Gidiyoni Anagonjetsa Amidiyani
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Gideon ndi Amuna Ake 300
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Zimene Akulu Angaphunzire pa Chitsanzo cha Gidiyoni
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
Onani Zambiri
Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
wcg mutu 18 tsamba 86-tsamba 89

18 GIDIYONI

Anali Wolimba Mtima Komanso Ankachita Zinthu Mosamala

Losindikizidwa
Losindikizidwa

MUNTHU wolimba mtima, amafunikanso kuchita zinthu mosamala. Akamachita zinthu mosamala, sakhala ndi mtima wodzidalira kwambiri kapena kuchita zinthu mwachisawawa. Gidiyoni anali ndi makhalidwe awiri onsewa. Iye anakhalapo pa nthawi imene Aisiraeli anayambiranso kulambira milungu yabodza. Choncho Mulungu anasiya kuwateteza ndipo Amidiyani analowa m’dzikolo n’kuyamba kuwazunza moti sankatha kukolola mbewu zawo. Komabe, Gidiyoni anali wolimba mtima moti ankapuntha tirigu kuti ena apeze chakudya. Koma ankachita zimenezi mosamala moti tiriguyo ankamupunthira muchoponderamo mphesa chomwe chiyenera kuti chinali chooneka ngati mtsuko chomwe ankachigoba kuchokera ku mwala.

Zinthu zinafika poipa, moti pamapeto pake Aisiraeli anapempha Yehova kuti awathandize. Choncho Yehova anatumiza mneneri kukawakumbutsa chifukwa chake anawasiya. Pambuyo pake, Yehova anatumiza mngelo kwa Gidiyoni kukamuuza zoti wasankhidwa kuti akapulumutse anthu ake. Gidiyoni anapempha kuti aone chizindikiro chakuti mngeloyo watumidwadi ndi Yehova. Choncho mngeloyo anachititsa kuti moto uyake pamwala womwe Gidiyoni amafuna kuperekerapo nsembe. Kenako mngelo uja anazimiririka. Usiku umenewo, Yehova anauza Gidiyoni kuti agwetse guwa lansembe la Baala ndi kudula mzati wopatulika kuti amangepo guwa lansembe la Yehova n’kuperekapo nsembe. Gidiyoni anamvera, koma chifukwa choopa bambo ake komanso amuna amumzinda, iye anachita zimenezi usiku kuti asamuone.

Zitachitika zimenezi, Amidiyani ndi Aamaleki pamodzi ndi anthu onse a Kum’mawa, anasonkhanitsa gulu lalikulu la asilikali ndipo anadzaza ngati dzombe m’chigwa cha Yezereeli. Zitatero, mzimu wa Yehova unayamba kuthandiza Gidiyoni ndipo anaitanitsa amuna a mafuko osiyanasiyana a Aisiraeli kuti abwere adzathandizane naye kumenya nkhondo. Apanso, mosamala Gidiyoni anapempha Yehova kuti amuonetse chizindikiro pofuna kumutsimikizira kuti ali naye. Yehova anamulezera mtima ndipo anamuonetsa zodabwitsa ziwiri. Usiku umenewo, Gidiyoni anaika ubweya wa nkhosa pansi ndipo Yehova anachititsa kuti ubweya wokhawo unyowe ndi mame koma nthaka yonse n’kukhala youma. Usiku wa mawa lake, anachititsa kuti ubweya wokha ukhale wouma koma nthaka yonse inyowe ndi mame.

Poyamba Gidiyoni ndi asilikali ake analipo ochepa poyerekeza ndi adani awo, koma Yehova anamuuza kuti achepetsebe asilikaliwo

Zodabwitsa ziwirizi zinalimbitsa mtima Gidiyoni ndipo anasonkhanitsa asilikali ake 32,000 kuti akamenyane ndi asilikali 135,000. Pa nthawi yomwe Gidiyoni ndi asilikali a Aisiraeli anali pa Kasupe wa Harodi, Yehova anamuuza kuti asilikali ake achuluka kwambiri ndipo abweze asilikali onse amantha. Asilikali 10,000 ndi omwe anatsala. Koma Yehova anaona kuti anali adakali ambiri moti anauza Gidiyoni kuti aonetsetse mmene amunawo akumwera madzi. Onse omwe anamwa madziwo atagwada n’kuweramitsa pansi nkhope zawo, anawabweza. Koma ena anali tcheru moti ananjuta n’kumamwa madziwo ndi manja akuyang’ana uku ndi uku. Pamapeto pake, Gidiyoni anatsala ndi asilikali 300 okha. Asilikali amenewa ndi omwe anapita nawo kunkhondo.

Molimba mtima, Gidiyoni anakonzeka kukamenya nkhondo. Yehova anapatsa Gidiyoni chizindikiro chomutsimikizira kuti ali naye. Anamuuza kuti akalowe mozemba mumsasa wa adani awo usiku, ndipo iye anachitadi zomwezo. Atafika, anamva msilikali wina akuuza mnzake zomwe analota, zosonyeza kuti Aisiraeli adzapambana pankhondoyo. Yehova anathandiza Gidiyoni kuti akhale wolimba mtima ndipo iye anabwerera kwa asilikali ake n’kukawapatsa malangizo omenyera nkhondoyo. Usiku, Gidiyoni ndi asilikali ake anapita kumsasa wa adani. Gidiyoni atawapatsa chizindikiro, anagwiritsa ntchito mitsuko yaikulu, miyuni komanso malipenga a nyanga ya nkhosa n’kuchita phokoso lalikulu ndipo panaoneka kuwala. Iwo anafuula kuti, “Nkhondo ya Yehova komanso ya Gidiyoni!” Njira yomwe anagwiritsa ntchitoyi, inachititsa gulu la adaniwo kuona kuti aukiridwa. Yehova anasokoneza adaniwo moti anayamba kumenyana okhaokha. Asilikali pafupifupi 15,000 okha ndi omwe anapulumuka.

Gidiyoni ndi anyamata ake agwira miyuni kudzanja lamanzere ndipo akuimba malipenga omwe awagwira ndi dzanja lawo lamanja. Pafupi ndi mapazi awo pali mapale a mitsuko yosweka.

Gidiyoni anayamba kuwathamangitsa ndipo anawagonjetsa n’kuphanso mtsogoleri wawo. Iye anaperekanso chilango kwa anthu ena omwe anakana kuwathandiza ndi chakudya pomwe ankapita kukamenyana ndi adani a Mulungu. Kenako anthu anaganiza zomuika kuti akhale mfumu. Koma modzichepetsa, iye anakana ndi kuwauza kuti: “Yehova ndi amene azikulamulirani.” Yehova anadalitsa Gidiyoni chifukwa cha kulimba mtima komanso kuchita zinthu mosamala. Nthawi yonse yomwe Gidiyoni anali woweruza, ku Isiraeli sikunachitike nkhondo ndipo iye anakhala ndi moyo kwa zaka zambiri. Mtumwi Paulo anatchula Gidiyoni pa mndandanda wa amuna ndi akazi omwe anasonyeza chikhulupiriro cholimba.—Aheb. 11:32.

Werengani nkhaniyi m’Baibulo:

  • Oweruza 6:1–7:22; 8:​4-23, 28

Funso lokambirana:

Kodi Gidiyoni anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?

Zoti Mufufuze

  1. 1. N’chifukwa chiyani tingati “mkate wa balere wozungulira” womwe msilikali wina analota, ndi chizindikiro chabwino choimira gulu lankhondo la Gidiyoni? (Ower. 7:13; it “Balere” ¶7-wcgr)

  2. 2. N’chifukwa chiyani Amidiyani anasokonezeka komanso kuchita mantha ndi kulira kwa nyanga za nkhosa 300? (it “Nyanga ya Nkhosa” ¶3-wcgr) A

    Nyanga za nkhosa.

    Chithunzi A: Aisiraeli ankagwiritsa ntchito nyanga za nkhosa popereka chizindikiro

  3. 3. Kodi Gidiyoni ndi asilikali ake ankafunika kuchita chiyani kuti agonjetse Amidiyani? (w04 10/15 16 ¶9-10) B

    Mapu osonyeza dera la zigwembe komanso mtunda umene Gidiyoni ndi anyamata ake anayenda pamene ankathamangitsa Amidiyani kuchokera kuchigwa cha Yezereeli kukafika ku Yogebeha.

    Chithunzi B: Gidiyoni anathamangitsa Amidiyani mpaka ku Yogebeha, mtunda wa makilomita pafupifupi 80 (njira yeniyeni yomwe anadutsa sidziwika)

  4. 4. Kodi pali umboni wotani womwe umatsimikizira kuti nkhaniyi inachitikadi? (w05 4/15 32)

Zomwe Tikuphunzirapo

  • Ngakhale kuti Gidiyoni anathandiza anthu a Mulungu kuti apambane nkhondo, anakhalabe wodzichepetsa komanso ankalankhula ndi anthu ena mwamtendere. (Ower. 8:​1-3) Kodi mitu ya mabanja komanso akulu angatsanzire bwanji Gidiyoni ngati munthu wina atakhumudwa ndi zochita zawo?

  • Ndi pa zochitika ziti pomwe tingafunike kuchita zinthu molimba mtima komanso mosamala? C

    Zithunzi: Mtsikana wa Mboni akukakamizidwa kusukulu kuti achite zosemphana ndi zimene amakhulupirira. Zithunzi zina zotsatira zikusonyeza zochitika zimenezi paderapadera. Mtsikana wa Mboni uja akuyenda m’kolido kusukulu ndipo akuona chithunzi cholimbikitsa khalidwe la kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha. Kumbuyo kwake kukubwera atsikana awiri atavala makhoza amitundu ya utawaleza ndipo agwirana manja. Kenako pamene ali m’kalasi, mtsikana wina akumuuza kuti avale khoza la mitundu ya utawaleza. Akukana mwaulemu pamene ophunzira ena akumuyang’ana modabwa.

    Chithunzi C

  • Mungatsanzire bwanji kulimba mtima kwa Gidiyoni?

Ganizirani Mfundo Yaikulu

  • Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?

  • Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?

  • Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Gidiyoni akadzaukitsidwa?

Phunzirani Zambiri

Kodi mungatsanzire bwanji Gidiyoni ngati mutapatsidwa mwayi wochita utumiki winawake?

“Nzeru Ili Ndi Odzichepetsa” (w00 8/1 16-18 ¶11-15-wcgr)

Gwiritsani ntchito zithunzi zofotokoza nkhani ya m’Baibulo pothandiza ana anu kuti azidalira Mulungu.

“Yehova Analimbikitsa Gidiyoni” (ijwis nkhani 13)

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena