41 ZEKARIYA NDI ELIZABETI
“Anali Olungama Pamaso pa Mulungu”
ZEKARIYA anali mmodzi wa ansembe amene ankachokera m’banja la Aroni. Tsiku lina, Zekariya ankafunika kugwira ntchito inayake yofunika kwambiri. Ankafunika akapereke zofukiza paguwa lansembe m’kachisi. Zimenezi zinali zapadera kwambiri chifukwa n’kutheka kuti wansembe ankachita zimenezi kamodzi pa moyo wake wonse. Ndiye pa tsikuli, Zekariya ndi mkazi wake Elizabeti anasangalala kwambiri.
Zekariya ndi Elizabeti anali atakhala m’banja zaka zambiri. Iwo ankasangalala ndi madalitso ambiri koma panali chinthu china chimene ankachifunitsitsa. Ankafuna kukhala ndi ana. M’nthawi yakale kukhala opanda ana inali nkhani yaikulu. Zekariya ndi Elizabeti anali atakula ndipo ‘anali ndi zaka zambiri.’ Baibulo limanena kuti “anali olungama pamaso pa Mulungu.” Choncho iwo anapitiriza kupemphera kwa Mulungu wawo ndipo ankakhulupirira kuti ayankha pemphero lawo ngakhale kuti zinkaoneka zosatheka kuti angakhale ndi mwana.
Tsiku lina Zekariya analowa m’nyumba yopatulika ya Yehova ndipo gulu la anthu linkapemphera panja. Ali yekhayekha m’kachisimo, mngelo wa Yehova anamuonekera ataima pafupi ndi guwa lansembe. Mngeloyo anauza Zekariya kuti Mulungu wamva pemphero lake. Elizabeti adzamuberekera mwana wamwamuna ndipo adzamupatse dzina lakuti Yohane. Akadzakula, adzakhala ndi “mzimu ndi mphamvu ngati za Eliya.” Ndipo adzagwira ntchito yapadera yothandiza anthu kuti abwerere kwa Yehova.
Chifukwa chokayikira, Zekariya anauza mngeloyo kuti amupatse chizindikiro choti zomwe wanenazo zidzachitikadi. Mngeloyo anamuuza kuti: “Ine ndine Gabirieli amene ndimaima pamaso pa Mulungu.” Panalibe chifukwa chokayikira mawu a mngelo wamphamvu wa Yehova. Koma chifukwa choti anakayikira, Gabirieli anamuuza Zekariya kuti asiya kulankhula mpaka tsiku limene zimenezi zidzachitike. Zekariya atatuluka m’nyumba yopatulikayo, ankagwiritsa ntchito manja polankhula ndi anthu kuwafotokozera zomwe zamuchitikira.
Banja lachikulire lomwe linalibe mwana, linalandira uthenga wochokera kumwamba womwe unasinthiratu moyo wawo
Zekariya anapeza njira yomufotokozera Elizabeti kuti akhala woyembekezera. “Patapita masiku angapo,” Elizabeti anakhaladi woyembekezera ndipo anakhala kwayekha miyezi 5. Utafika mwezi wa 6, wachibale wake Mariya anapita kukamuona. Iye anali wochokera ku Nazareti ndipo bambo ake anali Heli. Mariya atangolowa m’nyumba mwa Elizabeti, khanda lomwe linali m’mimba mwa Elizabetiyo linadumpha mosangalala. Pa nthawiyi Elizabeti anadzazidwa ndi mzimu woyera, iye anazindikira kuti Mariya anali woyembekezera ndipo mwanayo adzakhala Mesiya. Choncho anatchula Mariya kuti “mayi wa Mbuye wanga.” M’malo momuchitira nsanje, Elizabeti analimbikitsa Mariya pomuuza kuti Yehova adzamuthandiza.
Elizabeti atakhala ndi mwana, achibale ake komanso anthu okhala nawo pafupi ankafuna kuti iye am’patse mwanayo dzina la bambo ake. Koma Elizabetiyo ankadziwa zimene Gabirieli anauza Zekariya kuti: “Udzamupatse dzina lakuti Yohane.” Choncho anakana kuchita zimene anthuwo ankafuna. Iye anawayankha kuti: “Limenelo ayi! Dzina lake akhala Yohane.” Komabe achibalewo sanamukhulupirire choncho anapita kukamufunsa Zekariya. Popeza kuti sakanakwanitsa kulankhula, anapempha poti alembepo ndipo analemba kuti: “Dzina lake ndi Yohane.” Nthawi yomweyo anayamba kulankhula.
Zekariya anadzazidwa ndi mzimu woyera ndipo anayamba kulosera. Iye anauziridwa kupereka uthenga wa chiyembekezo komanso wa chipulumutso. Analosera kuti mwana wake Yohane, ‘adzatsogola pamaso pa Yehova kuti akakonze njira zake.’ Ndipo ndi zomwe zinachitikadi. Yohane M’batizi anatsogola Mesiya asanaonekere ndipo anakonzekeretsa anthu kudzamvetsera uthenga wa Yesu wonena za Ufumu wa Mulungu.
Yesu anaphunzitsa anthu njira yatsopano ya mmene angamachitire zinthu ndi anthu amene salambira Yehova komanso amene amatsutsa anthu a Mulungu. M’mbuyomu, atumiki ambiri a Mulungu ankasonyeza kulimba mtima pomenya nkhondo zolimbana ndi adani a Mulungu. Masiku ano, Yehova samafuna kuti atumiki ake azimenya nkhondo. Komabe iwo amafunika kulimba mtima. Anthu amene amatsanzira Mesiya, amafunika kugwiritsa ntchito mphatso yawo yakulankhula ngati mmene Zekariya ndi Elizabeti anachitira. Iwo amachita zimenezi polemekeza Yehova Mulungu ndiponso polalikira uthenga wabwino wonena za Yesu Khristu.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Zekariya ndi Elizabeti anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. Ngakhale kuti Zekariya ndi Elizabeti anali opanda ungwiro, n’chifukwa chiyani Baibulo limanena kuti “ankayenda mokhulupirika”? (Luka 1:6; it “Mokhulupirika” ¶2-wcgr)
2. Kodi Baibulo limanena chiyani zokhudza Gabirieli? (it “Gabirieli” ¶2-3-wcgr) A
Chithunzi A
Chithunzi A
3. Gabirieli anauza Zekariya kuti adzamupatse mwana wake dzina lakuti Yohane. Kodi dzinali limatanthauza chiyani? (it “Yohane” ¶1-wcgr)
4. Kodi pamene Zekariya anasiya kulankhula anasiyanso kumva? (w08 3/15 30 ¶6)
Zomwe Tikuphunzirapo
Aphunzitsi a Chiyuda a m’nthawi ya Zekariya ankalola kuti mwamuna akhoza kusiya mkazi wake ngati sanamuberekere ana. Kodi amuna akuphunzira chiyani kwa Zekariya pa nkhani yokhudza kukhalabe okhulupirika kwa akazi awo? B
Chithunzi B
Elizabeti anali wokhulupirika ndipo anatsatira malangizo a mwamuna wake m’malo mochita zimene anthu okhala nawo pafupi ndi achibale ake ankafuna. (Luka 1:58-61) Kodi akazi okwatiwa akuphunzira chiyani pamenepa?
Kodi tingatsanzire bwanji kulimba mtima kwa Zekariya ndi Elizabeti?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Ngati Zekariya ndi Elizabeti angadzaukitsidwire padziko lapansi, kodi ndingakonde kudzawafunsa chiyani?a
Phunzirani Zambiri
Onani Zekariya akuyambiranso kulankhula ndipo akugwiritsa ntchito mphatsoyi potamanda Mulungu.
Kodi zimene Mariya anachita pokaona Elizabeti zikutiphunzitsa chiyani za mmene Yehova angatipatsire mphamvu?
a Ngati Zekariya ndi Elizabeti anamwalira nthawi ya Pentekosite wa mu 33 C.E. isanakwane, ndiye kuti adzaukitsidwira padziko lapansi.