48 SITEFANO
“Munthu wa Chikhulupiriro Cholimba Ndiponso Wodzaza Ndi Mzimu Woyera”
SITEFANO sanali munthu wangwiro. Komabe atakumana ndi zoopsa, Baibulo limanena kuti: ‘Nkhope yake inkaoneka ngati ya mngelo.’ Iye ankaoneka wodekha komanso wosatekeseka ngakhale kuti anali atatsala pang’ono kuti alankhule pamaso pa Khoti Lalikulu la Ayuda. Panali patangodutsa miyezi yochepa kuchokera pamene khoti lomweli linapereka chigamulo choti Yesu aphedwe. Koma kodi zinatheka bwanji kuti munthu yemwe anakumana ndi zoopsa chonchi azionekabe wodekha? Zimenezi zinatheka chifukwa choti anali wolimba mtima.
Baibulo limanena kuti Sitefano anali munthu wa “chikhulupiriro cholimba ndiponso wodzaza ndi mzimu woyera.” Atumwi anamupatsa udindo woti aziyang’anira ntchito yopereka zofunika kwa anthu mumpingo. Tsiku lina Ayuda ena anayamba kumutsutsa kwambiri. Koma iye analankhula molimba mtima moti iwo analephera kupeza umboni woti anali wolakwa. Zimenezi zinachititsa kuti anthuwo akwiye kwambiri ndipo anapita naye ku Khoti Lalikulu la Ayuda. Kumeneko, khotilo linkayenera kugamula ngati ankafunika kuphedwa kapena ayi.
N’kutheka kuti Sitefano anakumbukira zimene Yesu analonjeza otsatira ake omwe adzakumane ndi mavuto ngati amenewa. Anati: “Musafulumire kuda nkhawa kuti mukanena chiyani. Zimene mukapatsidwe mu ola lomwelo, mukanene zomwezo chifukwa wolankhula si inu, koma mzimu woyera.” (Maliko 13:11) N’zosakayikitsa kuti lonjezo limeneli linamuthandiza Sitefano kukhala wolimba mtima. Ndipo mothandizidwa ndi mzimu wa Yehova, pamene anaima pamaso pa Khoti Lalikulu la Ayuda ankaoneka wosatekeseka komanso ngati mngelo.
Oweruza a khotilo ankakhalapo 71 ndipo anali anthu otchuka komanso atsogoleri achipembedzo cha Chiyuda. Anthuwa ankakhala m’mizere itatu ya mipando yomwe inkaikidwa mozungulira ndipo pankakhala alembi awiri omwe ankalemba zomwe zikunenedwazo. Sitefano ankaimbidwa mlandu woti ananyoza Chilamulo cha Mose komanso kachisi. Munthu amene wapalamula milandu imeneyi ankaphedwa. Kayafa, yemwe anali mkulu wa ansembe, anauza Sitefano kuti ayankhepo.
Sitefano anayambadi kulankhula. Anafotokoza mbiri ya mmene Yehova ankachitira zinthu ndi anthu ake kuyambira pa Abulahamu. Anafotokozanso za Yosefe, yemwe anazunzidwa ndi azichimwene ake omwenso anali makolo a mafuko Aisiraeli. Sitefano anafotokoza mwaulemu zokhudza Mose, ananena kuti mtundu wa Aisiraeli unakana kumvera Moseyo. Mouziridwa ndi Mulungu, Sitefano anatchulanso zinthu zina zokhudza Mose zomwe sizinalembedwe m’Malemba a Chiheberi.
Mawu amene Sitefano analankhula anasonyeza kuti iye ankalemekeza kwambiri Chilamulo, chihema komanso kachisi, malo amene Yehova anakhazikitsa kuti anthu azilambirirako movomerezeka. Koma zimene Sitefano ananena zinasonyezanso kuti anthu a Mulungu sankamvera anthu amene Mulunguyo ankawatumizira.
Sitefano ankafunika kufotokoza zimene ankakhulupirira kwa anthu omwe ankadana ndi Akhristu komanso omwe anali atasankha kale kuti amuphe
Sitefano anadziwa kuti anthu ouma mitimawa samuchitira chifundo. Mpake kuti mzimu wa Mulungu unamuchititsa kuti amalize mawu ake ndi uthenga wachiweruzo. Anawauza kuti ndi “anthu okanika” omwe ‘nthawi zonse ankatsutsana ndi mzimu woyera’ ngati mmene makolo awo ankachitira. Choipa kwambiri n’chakuti, anapha mneneri amene Mose ananeneratu kuti adzabwera, yemwe ndi wamkulu kuposa Moseyo. Sitefano ananena kuti anthu amenewa ‘anapereka ndiponso kupha’ Yesu yemwe ndi Mesiya.
Oweruza a Khoti Lalikulu la Ayuda sanasangalale ndi zimenezi moti “anayamba kumukukutira mano.” Koma Yehova anamulimbikitsa pomuonetsa masomphenya. Sitefano anati: “Taonani! Ndikuona kumwamba kutatseguka, ndipo Mwana wa munthu waima kudzanja lamanja la Mulungu.” Atangonena zimenezi anthuwo anakwiya kwambiri ndipo anamuukira, chifukwa mawu amenewa sanali achilendo kwa iwo. Miyezi yochepa m’mbuyomo pamene Yesu Khristu ankaimbidwa mlandu, ananeneratu kuti: “Mudzaona Mwana wa munthu atakhala kudzanja lamanja lamphamvu.” (Mat. 26:64) Choncho Sitefano anasonyeza kuti mawu amenewa anakwaniritsidwa. Apa n’kuti Yesu ali kumwamba ndi Yehova.
Anthuwo anathamangira pamene panali Sitefano, kumugwira n’kumutulutsira kunja kwa mzindawo kukamuponya miyala. Pamene ankamuponya miyala Sitefano, yemwe n’kutheka kuti ankaonabe Yesu m’masomphenya, anapempha Mbuye wakeyo kuti alandire mzimu wake. Kenako analankhula mawu ake omaliza ndipo anapempha Yehova kuti: “Musawaimbe mlandu wa tchimo ili.” Ndiyeno anafa ali wokhulupirika ndipo anali Mkhristu woyamba kuphedwa chifukwa cha zimene ankakhulupirira. Koma mnyamata wina amene analipo, yemwenso anavomereza kuti Sitefano aphedwe, sanaiwale mawu omaliza a munthu wokhulupirikayu. Tidzakambirana zambiri za mnyamatayu m’Mutu 50, 51 ndi 53.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Sitefano anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. N’chifukwa chiyani atumwi anasankha Sitefano ndi amuna ena ‘amene anali ndi mzimu komanso nzeru’ kuti aziyang’anira ntchito yogawa chakudya? (Mac. 6:3-5; bt 41-42 ¶17-18) A
Chithunzi A
2. Kodi ndi mfundo zochititsa chidwi ziti zokhudza Mose zimene zimapezeka m’mawu amene Sitefano analankhula? (bt 48 ¶13, mawu a m’munsi)
3. Kodi zinatheka bwanji kuti Sitefano akhalebe wodekha pamene ankazunzidwa? (w18.10 32)
4. Kodi lemba la Machitidwe 7:59 limasonyeza kuti Sitefano anapemphera kwa Yesu? (w05 1/1 31)
Zomwe Tikuphunzirapo
Sitefano anali munthu wa “chikhulupiriro cholimba ndiponso wodzaza ndi mzimu woyera.” Komanso “anali ndi mphamvu ndipo ankachita kuonekeratu kuti Mulungu ali naye.” Koma anavomera kuti azigwira nawo ntchito yogawa chakudya. (Mac. 6:2, 5, 8) Kodi abale omwe ali ndi luso kapenanso amene ali ndi maudindo akuluakulu angatsanzire bwanji Sitefano? B
Chithunzi B
Sitefano anapempherera anthu amene ankamuzunza. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda anthu amene amatitsutsa ndiponso kutizunza masiku ano? (Mat. 5:44-48)
Kodi mungatsanzire kulimba mtima kwa Sitefano m’njira ziti?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi mukumva bwanji mukaganizira zoti Sitefano anasankhidwa kukalamulira ndi Khristu kumwamba?
Phunzirani Zambiri
Phunzirani kwa Sitefano mmene mungafotokozere anthu ena zimene mumakhulupirira mwaulemu koma molimba mtima.
“Sitefano Anali ndi Mphamvu Ndipo Ankachita Kuonekeratu Kuti Mulungu Ali Naye” (bt 47-50 ¶9-19)
Anthu a Mulungu akamazunzidwa, kodi angatani kuti achite zinthu molimba mtima ngati Sitefano?