Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wcg mutu 52 tsamba 232-tsamba 235
  • “Amandithandiza”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Amandithandiza”
  • Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zoti Mufufuze
  • Zomwe Tikuphunzirapo
  • Ganizirani Mfundo Yaikulu
  • Phunzirani Zambiri
  • Maliko ‘Anali Wofunika Potumikira’
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Maliko Sanafooke
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Achinyamata, Muzitsanzira Maliko ndi Timoteyo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • “Mwana Wotonthoza”
    Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
Onani Zambiri
Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
wcg mutu 52 tsamba 232-tsamba 235

52 MALIKO

“Amandithandiza”

Losindikizidwa
Losindikizidwa

YOHANE MALIKO anasonyeza kulimba mtima ngakhale pamene anali wachinyamata. Pa nthawiyo Yesu Khristu anali atangomangidwa n’kutengedwa ndi anthu onyamula zida. Atumwi onse anali atathawa. Ndiyeno Baibulo limanena za “mnyamata wina” amene analimba mtima n’kumatsatirabe Yesu ndipo anthu atamuona ankafuna kumugwira. Koma iye anangowasiyira chovala chake n’kuthawa ali maliseche kapena kuti atangovala chovala chamkati. Buku la Maliko lokha ndi limene limanena za nkhaniyi, choncho ambiri amaganiza kuti mnyamatayo anali Maliko yemweyo.

Maliko ankakhala ku Yerusalemu. Iye ayenera kuti ankakhala limodzi ndi mayi ake ndipo zikuoneka kuti mayi akewo anali olemera. Yesu atamwalira, mpingo unkasonkhana kunyumba kwawo. Mtumwi Petulo atamasulidwa ndi mngelo kundende, anapita kunyumba imeneyi usiku. N’zosakayikitsa kuti Maliko ankadziwana ndi atumwi komanso ophunzira ena a Yesu. Iye ayenera kuti anaphunzira kulimba mtima kuchokera kwa anthu amenewa.

Cha m’ma 46 C.E., Baranaba, yemwe anali msuweni wa Maliko anapita ku Yerusalemu ndi mtumwi Paulo ndipo anachita chidwi kwambiri ndi mnyamatayu. Pamene anthuwa ankabwerera ku Antiokeya, Maliko anapita nawo. Patatha pafupifupi chaka chimodzi, Paulo ndi Baranaba anapempha Maliko kuti ayende nawo pa ulendo waumishonale. Iye analimba mtima n’kuvomera kuti apite n’cholinga choti azikatumikira amishonalewa.

Pa nthawiyo, kuyenda ulendo kunali kovuta komanso koopsa. Paja Paulo anadzalemba kuti pa maulendo ake anakumana ndi zoopsa ‘mʼmitsinje, kuchokera kwa achifwamba, mumzinda, mʼchipululu komanso panyanja.’ (2 Akor. 11:26) Popeza Maliko anali mtumiki wa anthu awiri omwe ankalemekezedwa kwambiri mumpingo, iye anali wokonzeka kuchita chilichonse chimene anamupempha. Kodi ntchito imeneyi inali yovuta? Baibulo silinena chilichonse. Limangonena kuti Maliko anawasiya anthu awiriwa ku Pamfuliya ndipo anabwerera kwawo ku Yerusalemu. Zimene anachitazi ziyenera kuti zinakhumudwitsa anthuwa, koma makamaka Paulo.

Pambuyo poyenda ulendo wautaliwu, Paulo ndi Baranaba anaganiza zopitanso ku ulendo wina. Baranaba ankafuna kupereka mwayi winanso kwa Maliko kuti ayende naye. Koma Paulo sanagwirizane nazo. N’kutheka kuti ankaona kuti Maliko ndi wosadalirika. Paulo ndi Baranaba anasemphana maganizo moti Baibulo limati “anakangana koopsa.” Baranaba anatenga Maliko n’kupita naye ku Kupuro kumene anakapitiriza kulalikira. Ndipo Paulo anapeza munthu wina n’kupitiriza naye ulendo wake.

Zimenezi ziyenera kuti zinakhumudwitsa Maliko. Tikutero chifukwa chakuti iye anakhumudwitsa Paulo amene ankamulemekeza kwambiri komanso anachititsa kuti anthu amene ankagwirizana asiyane. Kodi Maliko ankangokhalira kudziimba mlandu, kukwiya kapena kusunga zifukwa? Ayi ndithu.

Utumiki wa Maliko unaima kwa kanthawi koma iye sanangokhalabe wokhumudwa

Maliko ankachita zomwe angathe pothandiza Akhristu anzake. Cha mu 60 mpaka 61 C.E., Paulo anali pa ukaidi wosachoka pakhomo ku Roma. Iye analemba kalata ndipo m’kalatayo anatchulamo Maliko yemwe anali naye limodzi. Ponena za Maliko, iye anati: “Amandilimbikitsa kwambiri.” Ndiyeno cha m’ma 62 ndi 64 C.E., Maliko anatchulidwanso m’kalata imene Petulo analemba. Zikuoneka kuti Maliko anayenda ulendo wautali wopita ku Babulo kukakhala ndi mtumwi wachikulireyu. Petulo anatchula Maliko kuti “mwana wanga.” Maliko ayenera kuti ankamulimbikitsa kwambiri Petulo. Petuloyo ayenera kuti anamufotokozera Maliko zinthu zambiri zomwe zinachitika pamene ankayenda ndi Yesu Khristu. Zikuoneka kuti Maliko analemba Uthenga Wabwino wodziwika ndi dzina lake ali ku Roma ndipo umasonyeza kuti analembamo zinthu zimene Petuloyo anaona ndi maso.

Maliko akucheza ndi Paulo yemwe wakhala pafupi ndi tebulo komanso wamangidwa limodzi ndi msilikali. Maliko wagwira Paulo paphewa ndipo akumupatsa zakumwa. Abale ena awiri akulemba komanso kuona m’mipukutu.

Mtumwi Paulo anatchula Maliko komaliza m’kalata yake yopita kwa Timoteyo. Pa nthawiyi, Paulo analinso kundende ndipo anapempha Timoteyo kuti apite kukamuona limodzi ndi Maliko. N’chifukwa chiyani anapempha kuti Maliko apite nawo? Paulo anati: “Chifukwa amandithandiza pa utumiki wanga.” N’zosachita kufunsa kuti anthu awiriwa ankafunitsitsa kupita kwa Paulo komanso kukamulimbikitsa pa masiku omaliza a moyo wake. Ngakhale kuti Maliko anakumana ndi zinthu zambiri zokhumudwitsa, iye analimba mtima n’kumapitiriza kutumikira Mulungu. Izi zinachititsa kuti azithandiza abale ake komanso kuti Yehova Mulungu azimukonda kwambiri.

Werengani nkhaniyi m’Baibulo:

  • Maliko 14:​50-52

  • Machitidwe 13:​2-5, 13; 15:​36-40

  • Akolose 4:​10, 11

  • 2 Timoteyo 4:11

  • 1 Petulo 5:13

Funso lokambirana:

Kodi Maliko anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?

Zoti Mufufuze

  1. 1. N’chiyani chikusonyeza kuti Maliko ankachokera m’banja lolemera? (w10 3/15 6 ¶6–7 ¶1)

  2. 2. Kodi n’kutheka kuti Maliko ankagwira ntchito ziti potumikira Baranaba ndi Paulo? (Mac. 13:5; w10 3/15 7 ¶5)

  3. 3. Kodi Maliko anayenda malo ati? (w10 3/15 8 ¶6-8) A

    Maliko akuyenda m’chipululu kupita kumzinda umene ukuoneka chapatali. Mapu akusonyeza mizinda ina imene iye anapitako monga: 1. Roma. 2. Efeso. 3. Kolose. 4. Pega. 5. Kupuro. 6. Antiokeya (wa ku Siriya). 7. Yerusalemu. 8. Babulo.

    Chithunzi A: Mizinda ina imene Maliko ayenera kuti anapitako

  4. 4. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti mu Uthenga Wabwino wa Maliko muli zinthu zimene Petulo anaona ndi maso. (w08 2/1 26 ¶1)

Zomwe Tikuphunzirapo

  • Maliko satchulidwa kuti mtumwi kapena mneneri. Komabe ankatumikira ena modzichepetsa. Kodi ifenso tingatumikire bwanji anthu ena masiku ano?

  • Pa nthawi ina Maliko anataya mwayi wotumikira ndi Paulo, koma iye anakhalabe wokhulupirika. Kodi tingaphunzire chiyani kwa Maliko ngati nafenso utumiki wathu watha? B

    Zithunzi: Utumiki umene m’bale wina amaukonda mumpingo watha koma iye akutumikirabe anthu ena mokhulupirika. Zithunzi za zimenezi zabwerezedwa. M’bale ndi mkazi wake ndi okhumudwa pamene akumvetsera chilengezo ku Nyumba ya Ufumu. Pamisonkhano ina, m’bale uja akutsegula chitseko mosangalala kuti mlongo wachikulire ndi mlongo wina alowe. Pa nthawi ina, m’baleyu akupereka khadi la jw.org kwa munthu wogwira ntchito mushopu ina ndipo akumusonyeza zinthu zina pafoni yake. Mkazi wake waima chapafupi ndipo akumwetulira.

    Chithunzi B

  • Kodi tingatsanzire kulimba mtima kwa Maliko m’njira ziti?

Ganizirani Mfundo Yaikulu

  • Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?

  • Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?

  • N’chifukwa chiyani mumayamikira mukaganizira kuti Maliko anasankhidwa kuti akalamulire ndi Khristu kumwamba?

Phunzirani Zambiri

Kodi Uthenga Wabwino wa Maliko ndi wapadera m’njira ziti?

Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Maliko (3:18)

Gwiritsani ntchito chitsanzo cha Maliko pophunzitsa ana anu ubwino wopitirizabe kutumikira Yehova ngakhale titakumana ndi mavuto.

“Maliko Sanafooke” (w08 2/1 24-26)

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena