Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wcg mutu 3 tsamba 24-tsamba 27
  • Anakana Kumangoganizira Zam’mbuyo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anakana Kumangoganizira Zam’mbuyo
  • Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zoti Mufufuze
  • Zomwe Tikuphunzirapo
  • Ganizirani Mfundo Yaikulu
  • Phunzirani Zambiri
  • “Ndiwe Mkazi Wokongola”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
  • Yehova Anamutchula Kuti “Mfumukazi”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
  • Anakhala Ndi Mwana Atakalamba
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Abrahamu ndi Sara Mungatsanzire Chikhulupiriro Chawo!
    Nsanja ya Olonda—2004
Onani Zambiri
Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
wcg mutu 3 tsamba 24-tsamba 27

3 SARA

Anakana Kumangoganizira Zam’mbuyo

Losindikizidwa
Losindikizidwa

SARA anakwatiwa ndi Abulahamu yemwe ankamukonda kwambiri. Iwo ankakhala ku Uri m’dziko la Sinara. Uri unali mzinda waukulu womwe unali mumpanda wautali komanso m’mbali mwa mtsinje waukulu wa Firate. Anthu amumzindawu ankalambira mafano koma Abulahamu sankachita nawo zimenezi. Iye ankalambira Yehova, Mulungu woona. Saranso ankakhulupirira Mulungu woona. Tsiku lina, Sara anakumana ndi mayesero omwe anayesa chikhulupiriro komanso kulimba mtima kwake.

Abulahamu anamuuza kuti walandira uthenga wochokera kwa Yehova ndipo n’kutheka kuti Sara anasangalala atamva zimenezi. Komabe zomwe anamuuza zinali zovuta. Ankafunika kusiya nyumba ndi achibale awo n’kupita kudziko lakutali, kuyenda pa ngamila komanso kumakhala m’matenti. Tsopano sakanakhalanso m’nyumba yaikulu ya madzi am’mipopi, kukhala moyo wapamwamba ndi kupita kumsika. Panali mavuto ambiri, komabe Sara anavomera kusamuka. Iye anakhulupirira Yehova ndipo anapakira katundu wake, kutsanzikana ndi achibale komanso anzake n’kunyamuka limodzi ndi Abulahamu kupita kudera lachilendo.

M’malo mokakamiza Abulahamu kuti abwerere ku Uri, Sara anamuthandiza kupita kulikonse kumene Yehova anawauza

Sara anasonyeza kulimba mtima m’njira inanso. Mtumwi Paulo analemba za iye ndi mwamuna wake kuti: “Koma akanakhala kuti ankangoganizira za kumene anachokera, akanapeza chifukwa chowapangitsa kuti abwerere.” (Aheb. 11:15) Zikanatheka kuti Sara azingoganizira za ku Uri, koma analimba mtima kuti asamangoganizira zam’mbuyo.

Sara ndi Abulahamu akusamuka ku Uri. Akwera pa ngamila ndipo ali limodzi ndi anthu ambiri am’banja lawo.

Atangofika ku Kanani, Sara anaona kuti kunalibe mtsinje waukulu ngati wa Firate womwe amalonda ankagwiritsa ntchito pobweretsa katundu kuchokera kumadera osiyanasiyana. Choncho ku Kanani kutagwa njala, sakanachitira mwina koma kusamuka. Koma Sara sanapezerepo mwayi wokakamiza mwamuna wake kuti abwererenso ku Uri. M’malomwake analolera kupita ku Iguputo ndi mwamuna wake.

Chifukwa chakuti Sara anali wokongola kwambiri, Abulahamu ankaopa kuti munthu wina akhoza kupha iyeyo n’kutenga mkaziyo. Choncho Sara ananena kuti anali mchimwene wake. Koma Farao wa ku Iguputo atamva za kukongola kwake, pulaniyi siinathandize. Iye analamula antchito ake kuti akamutenge n’kubwera naye kunyumba yachifumu. Moyo wakunyumba yachifumu unali wabwino kwambiri kusiyana ndi moyo woyendayenda wokhala m’matenti. Koma kodi Sara anaganiza zongomusiya Abulahamu kuti akwatirane ndi Farao kuti azikhala moyo wapamwamba? Ayi. Iye anasonyeza kulimba mtima ndipo anakhalabe wokhulupirika kwa mwamuna wake komanso Yehova anamupulumutsa kwa mfumuyo. Posakhalitsa, anabwereranso kwa mwamuna wake.a

Yehova anali atalonjeza kuti kudzera mwa Abulahamu, adzatulutsa mtundu waukulu. Komabe, zinali zovuta kukhulupirira zimenezi chifukwa Sara anali asanaberekepo. Koma patatha zaka zambiri adakali ku Kanani komweko, Yehova anadalitsa Sara. Ngakhale kuti anali ndi zaka 90, Yehova anamudalitsa pomupatsa mwana wamwamuna. Yehova analamula kuti mwanayo amupatse dzina lakuti Isaki, lomwe limatanthauza “Kuseka.” Abulahamu ndi Sara atamva kuti adzakhala ndi mwana, anasangalala kwambiri ndipo anaseka. Sara naye ankayembekezera kuti anthu adzasangalala naye limodzi akadzamva kuti Yehova wamuchitira zodabwitsa.

Sara anakhala ndi moyo wautali ndipo anakwanitsa kulera mwana wake kufika pokhala mwamuna wodalirika. Izi zinatheka chifukwa Sara anali mayi wachikondi ndipo ankateteza mwanayo molimba mtima. Kufikira pamene anamwalira, Sara anakana kumangoganizira moyo wabwino womwe anausiya m’mbuyo. M’malomwake, ankaganizira za madalitso am’tsogolo. Ngakhale kuti sanaone kukwaniritsidwa kwa malonjezowo, sitikukayikira kuti adzawaona posachedwapa.

Werengani nkhaniyi m’Baibulo:

  • Genesis 12:​1-20; 15:18; 16:​1, 2; 17:​3-8, 15-19; 18:​9-15; 20:​1-17; 21:​1-13

  • Machitidwe 7:​1-7

Funso lokambirana:

Kodi Sara anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?

Zoti Mufufuze

  1. 1. Kodi zinali zolakwika kuti Sara akwatirane ndi Abulahamu popeza bambo awo anali amodzi? (wp17.3 12 ¶5, mawu a m’munsi)

  2. 2. Fotokozani moyo womwe Sara anasiya ku Uri. (wp17.3 13 ¶4–14 ¶3) A

    Chidutswa cha mkanda wam’khosi wopangidwa ndi miyala yamtengo wapatali.

    Photograph taken by courtesy of the British Museum

    Chithunzi A: Chidutswa cha mkanda wam’khosi chomwe anachifukula pomwe panali mzinda wakale wa Uri

  3. 3. N’chiyani chikusonyeza kuti Abulahamu anachita zinthu mwanzeru pamene anabisa zoti Sara ndi mkazi wake? (wp17.3 14 ¶6–15 ¶1)

  4. 4. Ngakhale kuti Sara ankagonjera Abulahamu, kodi zikutanthauza kuti sankamasuka kufotokoza maganizo ake? Fotokozani. (g 1/08 29 ¶4-5) B

    Sara akulankhula ndi Abulahamu mosabisa mawu koma Abulahamu akuoneka wokhumudwa.

    Chithunzi B

Zomwe Tikuphunzirapo

  • Ganizirani zokhudza Sara ndi mkazi wa Loti.

    • Kodi ankafanana pa zinthu ziti? (Gen. 12:1; 13:​5-7; 19:​12, 15)

    • Kodi ankasiyana pa zinthu ziti? (Gen. 19:​17, 26; Luka 17:​28-32)

    • Kodi tingaphunzire chiyani pa zomwe anasankha komanso zotsatirapo zake?

  • Sara anali wokongola kwambiri komanso mwamuna wake anali wolemera. Kodi anatisiyira chitsanzo chotani pa nkhani ya mmene tiyenera kuonera maonekedwe athu komanso zinthu zomwe tingakhale nazo? (Miy. 31:30; 1 Tim. 6:​17-19)

  • Kodi mungatsanzire bwanji Sara pa nkhani yokhala wolimba mtima? C

    Zithunzi: 1. Banja lachinyamata likusamuka m’nyumba yapamwamba ya m’tauni ndipo likupakira katundu wawo mosangalala. 2. Banja lija lili kudera lakumudzi ndipo likulalikira mlimi wina mosangalala.

    Chithunzi C

Ganizirani Mfundo Yaikulu

  • Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?

  • Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?

  • Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Sara akadzaukitsidwa?

Phunzirani Zambiri

Kodi akazi okwatiwa okha ndi amene angaphunzire pa chitsanzo cha Sara, kapena amuna okwatira angaphunzireponso kanthu?

Zimene Tingaphunzire kwa Sara (6:27)

Ganizirani zimene Abulahamu ndi Sara ankachita kuti aliyense aziona kuti amalemekezedwa.

“Musazimitse ‘Lawi la Ya’” (w23.05 24-25 ¶15-17)

a Patapita nthawi, Sara anakumananso ndi zangati zomwezi pamene Mfumu Abimeleki inamutenga. Pa nthawiyi, Sara anamveranso malangizo a mwamuna wake ndipo Yehova anamuteteza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena