Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w26 January tsamba 20-25
  • Kodi “Inuyo” Mungasonyeze Bwanji Kuti Mumayamikira Dipo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi “Inuyo” Mungasonyeze Bwanji Kuti Mumayamikira Dipo?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • OPHUNZIRA BAIBULO
  • AKHRISTU OBATIZIDWA
  • NKHOSA ZIMENE ZINASOCHERA
  • KODI DIPO LIZIKULIMBIKITSANI KUCHITA CHIYANI?
  • Madalitso Amene Timapeza Chifukwa cha Chikondi cha Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Kodi Dipo Limatiphunzitsa Chiyani?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • N’chifukwa Chiyani Timafunikira Dipo?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
  • Kodi Mwakonzeka Kudzapezekapo pa Tsiku Lofunika Kwambiri pa Chaka?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2026
w26 January tsamba 20-25

MARCH 23-29, 2026

NYIMBO NA. 18 Tikuthokoza Chifukwa cha Dipo

Kodi Inuyo Mungasonyeze Bwanji Kuti Mumayamikira Dipo?

“Chikondi chimene Khristu ali nacho chimatikakamiza.”—2 AKOR. 5:14.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Munkhaniyi tiona zimene tonsefe tingachite posonyeza kuti timayamikira dipo.

1-2. Kodi nsembe ya dipo ya Yesu iyenera kutilimbikitsa kuchita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani? (2 Akorinto 5:​14, 15) (Onaninso chithunzi.)

NGATI munthu wina atakupulumutsani nyumba itakugwerani, kodi mungamamve bwanji mukaganizira za munthuyo? Ngakhale zitakhala kuti wapulumutsanso anthu ena, n’zosachita kufunsa kuti inuyo panokha mungafune kumuyamikira posonyeza kuti zimene wakuchitiranizo simukuzitenga mopepuka.

2 Monga mmene nkhani yapita ija inafotokozera, sitingathe kudzipulumutsa tokha ku uchimo umene tinatengera kwa makolo athu. Komabe, nsembe ya dipo ya Yesu ikhoza kutipulumutsa potithandiza kuti (1) tizikhululukidwa machimo, (2) tiziyembekezera kudzakhala angwiro komanso (3) tikhalenso pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Zotsatira zake, tingakhale ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo mpaka kalekale m’dziko latsopano. Dipo limasonyeza kuti Yesu amakonda kwambiri anthu, ndipotu anayamba kuwakonda asanabwere padzikoli. (Miy. 8:​30, 31) Mtumwi Paulo analemba kuti “chikondi chimene Khristu ali nacho chimatikakamiza.” (Werengani 2 Akorinto 5:​14, 15.) Zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kusonyeza kuti timayamikira chikondi chimene Yesu anatisonyeza ndipo sitiona mopepuka nsembe ya dipo.

Munthu amene tinamuona munkhaniyi yapita ija, wafukulidwa ndi munthu wogwira ntchito yopulumutsa anthu.

Kaya munthu wina watipulumutsa nyumba itatigwera, kapena tapulumutsidwa ku uchimo ndi imfa, timafunika kuyamikira amene watipulumutsayo (Onani ndime 1 ndi 2)


3. N’chifukwa chiyani zimene mungachite posonyeza kuyamikira nsembe ya dipo zingasiyane ndi zimene ena angachite?

3 Kodi inuyo mungasonyeze bwanji kuti mumayamikira dipo? Zimene mungachite zingasiyane ndi zimene munthu wina angachite. Kuti timvetse chifukwa chake, tiyerekeze kuti anthu atatu amene akuchokera m’mizinda yosiyana akupita kumalo amodzi. Anthuwa sangadutse njira zofanana. Mofanana ndi zimenezi, “njira” imene inuyo mungagwiritse ntchito posonyeza kuti mumayamikira dipo, imatengera mmene ubwenzi wanu ndi Yehova ulili. Choncho munkhaniyi tikambirana zokhudza magulu atatu a anthu: (1) ophunzira Baibulo, (2) Akhristu obatizidwa ndiponso (3) nkhosa zimene zinasochera.

OPHUNZIRA BAIBULO

4. Kodi Yehova amamva bwanji akaona anthu amene akuphunzira Baibulo?

4 Ngati mukuphunzira Baibulo, taganizirani mfundo iyi: Zimene munachita polola kuti mumvetsere uthenga wabwino ndi umboni wakuti ndinu mmodzi mwa anthu amene Yehova akuwakoka kuti akhale anzake. (Yoh. 6:44; Mac. 13:48) Paja “Yehova ndi amene amayesa mitima.” Zimenezi zikutanthauza kuti amaona khama limene mumasonyeza pophunzira zokhudza iye, amasangalala kukuonani mukupita patsogolo komanso kusintha makhalidwe anu kuti azigwirizana ndi mfundo zake. (Miy. 17:3; 27:11) Dipo ndi limene limachititsa kuti mukhale pa ubwenzi ndi Yehova. (Aroma 5:​10, 11) Mwayi umenewu musamautenge mopepuka.

5. Kodi ophunzira Baibulo angatsatire bwanji malangizo a pa Afilipi 3:16?

5 Ngati mukuphunzira Baibulo, kodi mungasonyeze bwanji kuti mumayamikira dipo? Njira imodzi ndi kutsatira malangizo amene mtumwi Paulo anapereka kwa Afilipi akuti: “Mulimonse mmene tapitira patsogolo, tiyeni tipitirize kupita patsogolo pochita zomwe tikuchitazo.” (Afil. 3:16) Pomasulira vesili, Baibulo lina limati: “Tiyeni tipitirize kuyenda m’njira imene tikuyenda panopa.” Mogwirizana ndi malangizowa, musalole kuti chilichonse chikulepheretseni kupitiriza kuyenda pamsewu wopita ku moyo wosatha.—Mat. 7:14; Luka 9:62.

6. Kodi ophunzira Baibulo angatani ngati akuvutika kumvetsa mfundo zina kapenanso kusintha zinthu pa moyo wawo? (Deuteronomo 30:​11-14) (Onaninso chithunzi.)

6 Kodi mungatani ngati mukuvutika kuvomereza mfundo inayake ya m’Baibulo imene mwangoiphunzira kumene? Muzifufuza mokwanira komanso kupempha Yehova kuti akuthandizeni kumvetsa mfundoyo. (Sal. 86:11) Ngati simukuimvetsabe, musadandaule, mudzaimvetsa m’tsogolo. Koma panopa pitirizani kuphunzira Baibulo. Nanga bwanji ngati zikukuvutani kusiya khalidwe linalake limene Baibulo limaletsa? Muzikumbukira kuti Yehova satipempha kuchita zinthu zimene sitingakwanitse. N’zotheka ndithu kumatsatira mfundo zake. (Werengani Deuteronomo 30:​11-14.) Yehova akulonjeza kuti azikuthandizani. (Yes. 41:​10, 13; 1 Akor. 10:13) Choncho musafooke. M’malo moganizira kwambiri zimene mukulephera kuchita, muziganizira komanso kuyamikira zimene Yehova akukupatsani, kuphatikizapo dipo. Pamene chikondi chanu pa Yehova chikukula, mudzaona kuti ‘malamulo ake si ovuta kuwatsatira.’—1 Yoh. 5:3.a

Munthu akuwerenga phunziro 40 m’buku lakuti “Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale.” Patebulo pake pali paketi ya fodya komanso kambale kamene muli ndudu zimene wasuta kale.

Yehova satipempha kuchita zinthu zomwe sitingakwanitse. Iye amatithandiza kuti tizitsatira mfundo zake (Onani ndime 6)


7. Kodi achinyamata amene akuleredwa m’banja la Mboni azikumbukira chiyani?

7 Achinyamata amene muli m’banja la Mboni, nanunso muli m’gulu la ophunzira Baibulo. Ndipotu makolo anu amaona kuti ndinu ophunzira Baibulo awo ofunika kwambiri. Baibulo limanena kuti: “Yandikirani Mulungu ndipo iyenso adzakuyandikirani.” (Yak. 4:8; 1 Mbiri 28:9) Mukayamba inuyo kuchita zonse zomwe mungathe kuti mukhale mnzake wa Yehova, nayenso amachita zonse zomwe angathe kuti akhale mnzanu. Yehova samangokuonani ngati munthu winawake amene ali m’gulu la anthu basi. Iye amakoka munthu aliyense payekha, kuphatikizapo amene akuleredwa m’banja la Mboni. Kodi mukudziwa zimene zachititsa kuti zikhale zotheka kuti inuyo panokha mukhale pa ubwenzi ndi Yehova? Ndi dipo, ndipotu musamalitenge mopepuka. (Aroma 5:​1, 2) Ndiye musanachite Chikumbutso cha chaka chino, bwanji muganizire mozama mmene imfa ya Yesu imakukhudzirani inuyo panokha? Kenako muganizirenso zimene mukufuna kumachita pa moyo wanu komanso zolinga zimene mukufuna kuzikwaniritsa, posonyeza kuti mumayamikira dipo limene Yehova anapereka kudzera mwa Mwana wake.b

AKHRISTU OBATIZIDWA

8. Kodi Akhristu obatizidwa anasonyeza bwanji kuti amakhulupirira dipo?

8 Ngati ndinu Mkhristu wobatizidwa, munasonyeza kale kuti mumakhulupirira dipo m’njira zambiri. Mwachitsanzo, munachita zonse zomwe mungathe kuti mukhale pa ubwenzi ndi Yehova komanso muzitsatira mfundo zake. Munamvera lamulo la Yesu loti muzithandiza anthu kuti akhale ophunzira ake powauza zimene mumakhulupirira. Munadzipereka kwa Yehova ndipo munabatizidwa. Mwinanso n’kutheka kuti ena ankakutsutsani chifukwa chosankha kutumikira Yehova. (2 Tim. 3:12) Koma munapitirizabe kutumikira Yehova mokhulupirika ndipo zimenezi zimasonyeza kuti mumamukonda komanso mumayamikira dipo limene iye anapereka kudzera mwa Mwana wake.—Aheb. 12:​2, 3.

9. Kodi Akhristu obatizidwa ayenera kusamala ndi chiyani?

9 Monga Akhristu obatizidwa, pali chinthu china chimene timafunika kusamala nacho. N’kupita kwa nthawi, tikhoza kuyamba kuona dipo mopepuka. Kodi zimenezi zingachitike bwanji? Taganizirani zomwe zinachitikira Akhristu a ku Efeso. Yesu ataukitsidwa, anawayamikira chifukwa cha kupirira kwawo. Komabe anawauza kuti: “Ndakupeza ndi mlandu wakuti wasiya kusonyeza chikondi ngati mmene unkachitira poyamba.” (Chiv. 2:​3, 4) Zimene Yesu ananenazi zikusonyeza kuti Mkhristu akhoza kumachita zinthu zokhudza kulambira mwachizolowezi. Munthu wotereyu akhoza kumapemphera, kupita kumisonkhano komanso kulalikira, koma akungozichita mwamwambo chabe osati chifukwa chokonda Yehova. Ndiye kodi mungatani ngati mukuona kuti panopa simukukonda kwambiri Yehova ngati mmene munkachitira poyamba?

10. Kodi mungatani kuti ‘muziganizira mozama’ komanso ‘muzidzipereka’ pa zinthu zokhudza kulambira? (1 Timoteyo 4:​13, 15)

10 Mtumwi Paulo anauza Timoteyo kuti ‘aziganizira mozama’ komanso ‘azidzipereka’ pa zinthu zokhudza kulambira. (Werengani 1 Timoteyo 4:​13, 15.) Mogwirizana ndi malangizo amenewa, inunso mungaganizire zomwe mungachite kuti muzichita khama pa zinthu zokhudza kulambira n’cholinga choti mupitirize ‘kuyaka ndi mzimu.’ (Aroma 12:11) Mwachitsanzo, mungakonze zoti muzikonzekera misonkhano mokwanira kuti muzikamvetsera mwatcheru. Mungakonzenso zoti mukamaphunzira Baibulo panokha, muzikhala pamalo opanda phokoso kuti muzikwanitsa kuganizira mozama komanso kupindula ndi zimene mukuphunzirazo. Kuti moto uziyakabe pamafunika kusonkhezera nkhuni. Mofanana ndi zimenezi, inunso mungafunike kumachita zinthu zimene takambiranazi, kuti mupitirizebe kuyamikira zonse zimene Yehova wakupatsani, kuphatikizapo dipo. Milungu ingapo Chikumbutso chisanachitike, mungakonze zoti muzidzaganizira zinthu zabwino zimene mumasangalala nazo chifukwa choti ndinu wa Mboni za Yehova. Zimenezi zidzakuthandizani kuti muziyamikira kwambiri dipo, lomwe limachititsa kuti zikhale zotheka kukhala pa ubwenzi ndi Yehova.

11-12. Ngati nthawi zina mumadzimva kuti mwasiya kuchita khama ngati mmene munkachitira poyamba, kodi zikutanthauza kuti Yehova wasiya kukupatsani mzimu woyera? Fotokozani. (Onaninso chithunzi.)

11 Ngati nthawi zina mumadzimva kuti mwasiya kuchita khama pa zinthu zokhudza kulambira ngati mmene mumafunira, musamafooke kapena kuganiza kuti Yehova wasiya kukupatsani mzimu wake. Muzikumbukira zimene mtumwi Paulo analembera Akhristu a ku Korinto zokhudza utumiki wake. Iye anati: “Ngakhale nditachita mokakamizika, ndinebe woyangʼanira mogwirizana ndi udindo umene ndinapatsidwa.” (1 Akor. 9:17) Kodi ankatanthauza chiyani pamenepa?

12 Nthawi zina Paulo ankadzimva kuti sakufuna kulalikira. Komabe anali wotsimikiza kupitirizabe kulalikira posatengera mmene akumvera pa nthawiyo. Nanunso mukhoza kukhala otsimikiza kuchita zimenezi. Muziyesetsa kuchita zinthu zoyenera ngakhale pamene simukufuna kuchita zinthuzo. Muzipempha Yehova kuti akupatseni “mtima wofuna kuchita zinthu zimene iye amakonda komanso mphamvu zochitira zinthuzo.” (Afil. 2:13) Muzipitirizabe kuchita zinthu zokhudza kulambira. Musamakayikire kuti n’kupita kwa nthawi, zimene mukuchitazo zikuthandizani kuti muyambirenso kukonda Yehova komanso kuchita khama pomutumikira ngati mmene munkachitira poyamba.

Mlongo akuoneka wokhumudwa, akuyendetsa mwana wake pa kanjinga ka ana ndipo ali mu utumiki ndi mlongo wina amene wamugwira paphewa.

Muzipitirizabe kuchita zinthu zokhudza kulambira ngakhale kuti nthawi zina simungafune kuchita zimenezo (Onani ndime 11 ndi 12)


13. Kodi tingatani kuti tipitirize ‘kudziyesa kuti tione ngati tidakali ndi chikhulupiriro’?

13 Nthawi ndi nthawi tingachite bwino kumadzifufuza mogwirizana ndi malangizo amene ali pa 2 Akorinto 13:​5, akuti: “Pitirizani kudziyesa kuti muone ngati mukadali ndi chikhulupiriro. Pitirizani kudziyesa kuti mudziwe kuti ndinu munthu wotani.” Nthawi zonse tizidzifunsa mafunso ngati awa: ‘Kodi ndimaika zinthu zokhudza Ufumu pamalo oyamba?’ (Mat. 6:33) ‘Kodi zosangalatsa zimene ndimakonda, zimasonyeza kuti ndimadana ndi zoipa?’ (Sal. 97:10) ‘Kodi ndimalimbikitsa mtendere ndi mgwirizano pakati pa Akhristu anzanga?’ (Aef. 4:​2, 3) Chikumbutso chimatipatsa mwayi woganizira kwambiri za dipo limene Yehova anatipatsa komanso mwayi wodzifufuza n’kumaonetsetsa kuti tikuchita zinthu mogwirizana ndi Khristu, m’malo mokhala moyo wongodzisangalatsa tokha.c

NKHOSA ZIMENE ZINASOCHERA

14. N’chiyani chimachititsa abale ndi alongo ena kusiya kusonkhana?

14 Akhristu ena anasiya kusonkhana ndi mpingo pambuyo poti akhala akutumikira Yehova mokhulupirika kwa miyezi kapenanso zaka zambiri. Zili choncho chifukwa analemedwa ndi “nkhawa za moyo.” (Luka 21:34) Ena anakhumudwa chifukwa cha zolankhula kapena zochita za Mkhristu mnzawo. (Yak. 3:2) Pamene enanso anachita tchimo lalikulu koma amachita manyazi kupempha thandizo. Kaya munafooka pa zifukwa ziti, kodi mungatani kuti mubwererenso m’banja la Yehova? Nanga mphatso ya chikondi ya dipo, ingakulimbikitseni kuchita chiyani?

15. Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti amakonda nkhosa zomwe zinasochera? (Ezekieli 34:​11, 12, 16)

15 Taganizirani mmene Yehova amamvera akaona nkhosa zomwe zinasochera. Iye samazikwiyira kapena kuziiwala. M’malomwake amazifufuza, amazidyetsa komanso kuzithandiza kuti zibwerere kwa iye. (Werengani Ezekieli 34:​11, 12, 16.) Kodi mukuganiza kuti ndi zomwenso Yehova akuchita ndi inuyo? Inde. Ndipotu zomwe mukuchita pophunzira nawo nkhaniyi ndi umboni wakuti mukufunabe kumachita zomusangalatsa. Popeza kuti poyamba Yehova anaona mtima wanu wabwino ndipo anakukokerani m’gulu lake, kodi sangakhalenso kuti panopa akukukokani kuti mubwererenso kwa iye?

16. N’chiyani chingathandize nkhosa zosochera kubwereranso kwa Yehova? (Onaninso chithunzi.)

16 Kabuku kakuti Bwererani kwa Yehova kali ndi mawu olimbikitsa awa: “Dziwani kuti Yehova adzakulandirani bwino mukabwerera kwa iye. Adzakuthandizani kuti musiye kuda nkhawa, kukhumudwa ndiponso kudziimba mlandu. Zikatero, mudzakhala ndi mtendere mumtima n’kumatumikira Yehova limodzi ndi anzanu.” Muzikumbukiranso kuti akulu ndi ofunitsitsa kukuthandizani. Iwo akhoza kukhala “ngati malo obisalirapo mphepo, [komanso] malo obisalirapo mvula yamkuntho.” (Yes. 32:2) Posonyeza kuyamikira dipo, mungadzifunse kuti, ‘Kodi ndingatani panopa kuti “ndikambirane” ndi Yehova?’ (Yes. 1:18; 1 Pet. 2:25) Mwachitsanzo, kodi mungakonze zoti mukapezeke nawo pamisonkhano ku Nyumba ya Ufumu? Kodi mungakonzenso zoti mukakumane ndi akulu n’kuwapempha kuti akuthandizeni, zomwe zingaphatikizepo kuyambiranso kuphunzira Baibulo kwa kanthawi? N’zosakayikitsa kuti Yehova adzadalitsa khama limene mukuchita posonyeza kuti mumayamikira dipo la Mwana wake.

Bambo wachikulire wanyamula Baibulo m’manja mwake, ndipo waima chapafupi ndi Nyumba ya Ufumu. Iye akuona abale ndi alongo akulandirana mwansangala pamene akufika.

Muzidzifunsa kuti, ‘Kodi ndikuyenera kuchita chiyani panopa kuti “ndikambirane” ndi Yehova?’ (Onani ndime 16)


KODI DIPO LIZIKULIMBIKITSANI KUCHITA CHIYANI?

17-18. Kodi tingatani kuti tigwiritse ntchito nthawi yathu mwanzeru tisanachite Chikumbutso chaka chino?

17 Yesu ananena kuti dipo linaperekedwa “kuti aliyense womukhulupirira asawonongedwe koma akhale ndi moyo wosatha.” (Yoh. 3:16) Dipo ndi njira imene Yehova akugwiritsa ntchito pofuna kutipulumutsa ku uchimo ndi imfa. Aliyense wa ife aziona kuti dipo ndi mphatso ya mtengo wapatali. (Aroma 3:​23, 24; 2 Akor. 6:1) Mwambo wa Chikumbutso ukamayandikira, tiziganizira chikondi chimene Yehova ndi Yesu anatisonyeza ndipo chikondichi chizitichititsa kuyamikira zimene anatichitirazi.

18 Kodi dipo lizikulimbikitsani kuchita chiyani? Zimene mungachite zingasiyane ndi zimene wina angachite. Musamakayikire kuti Yehova adzadalitsa khama lanu komanso la abale ndi alongo ambiri, amene ‘sakhala moyo wongodzisangalatsa okha, koma amakhala moyo wosangalatsa amene anawafera.’—2 Akor. 5:15.

KODI MAGULU A ANTHU OTSATIRAWA ANGASONYEZE BWANJI KUTI AMAYAMIKIRA DIPO?

  • Ophunzira Baibulo

  • Akhristu obatizidwa

  • Nkhosa zimene zinasochera

NYIMBO NA. 14 Tamandani Mfumu Yatsopano Yolamulira Dziko Lapansi

a Pofuna kukuthandizani kuti muzigwiritsa ntchito zimene mukuphunzira m’Baibulo, muzitsatira zimene zili m’kabokosi kakuti “Zoti Muchite,” kamene kamapezeka kumapeto kwa phunziro lililonse m’buku la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale.

b Kuti mudziwe zolinga zauzimu zimene mungakhale nazo, werengani nkhani yakuti “Achinyamata, ‘Pitirizani Kukonza Chipulumutso Chanu’” yomwe ili mu Nsanja ya Olonda ya December 2017.

c Kuti mudziwe zimene mungachite kuti mupitirize kuyamikira zimene Yehova amakuchitirani, werengani nkhani yakuti “Kodi N’chiyani Chimakusonkhezerani Kutumikira Mulungu?” mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 1995.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena