Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yb16 tsamba 168-tsamba 169 ndime 2
  • “Yehova Anatichitira Zinthu Zoposa Zimene Tinkayembekezera”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Yehova Anatichitira Zinthu Zoposa Zimene Tinkayembekezera”
  • Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2016
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Nyumba ya Ufumu Yanu Mumaiona Bwanji?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Malo Olambirira Yehova
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
  • Tizilemekeza Malo Athu Olambirira Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Ntchito Yomanga Nyumba za Ufumu Ikuyenda Bwino
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
Onani Zambiri
Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2016
yb16 tsamba 168-tsamba 169 ndime 2

INDONESIA

Yehova Anatichitira Zinthu Zoposa Zimene Tinkayembekezera

Angeragō Hia

  • CHAKA CHOBADWA 1957

  • CHAKA CHOBATIZIDWA 1997

  • MBIRI YAKE Anabwerera kumudzi wakwawo womwe uli pachilumba cha Nias ndipo anathandiza kuti Nyumba ya Ufumu imangidwe m’mudziwo.

Angeragō Hia

MPINGO wathu uli m’dera la Tugala Oyo ndipo muli ofalitsa ochepa. M’chaka cha 2013, abale ndi alongo a mumpingo wathu anasangalala atamva chilengezo choti atimangira Nyumba ya Ufumu. Nawonso akuluakulu a m’derali anasangalala moti anatipatsa chilolezo chomanga nyumbayo. Komanso anthu 60 okhala m’derali anasaina chikalata chovomereza kuti timange Nyumba ya Ufumuyi. Munthu wina anati: “Ngati mukufuna anthu 200 oti asaine chikalatachi ndikhoza kukupezerani msangamsanga.”

Abale awiri odziwa bwino ntchito yomanga Nyumba za Ufumu ndi amene ankayang’anira ntchitoyi ndipo inamalizidwa mu November 2014. Sitinkayembekezera kuti mpingo wathu ungakhale ndi malo abwino ngati amenewa ochitira misonkhano. Ndithudi, Yehova anatichitira zinthu zoposa zimene tinkayembekezera.

Angeragō Hia ali pamodzi ndi anthu ena amene anadzipereka kumanga nawo Nyumba ya Ufumu ku Tugala Oyo, pachilumba cha Nias
    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena