Zamkati
January 15, 2015
© 2015 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
YOPHUNZILA
MARCH 2-8, 2015
Yamikani Yehova Ndipo Mudzadalitsidwa
TSAMBA 8 • NYIMBO: 2, 75
MARCH 9-15, 2015
Cifukwa Cake Timacita Mgonelo wa Ambuye
TSAMBA 13 • NYIMBO: 8, 109
MARCH 16-22, 2015
Khalani ndi Banja Lolimba ndi Lacimwemwe
TSAMBA 18 • NYIMBO: 36, 51
MARCH 23-29, 2015
Lolani Yehova Kulimbitsa ndi Kuteteza Cikwati Canu
TSAMBA 23 • NYIMBO: 87, 50
MARCH 30, 2015–APRIL 5, 2015
Kodi N’zotheka Kukhala m’Cikondi Ceniceni?
TSAMBA 28 • NYIMBO: 72, 63
NKHANI ZOPHUNZILA
▪ Yamikani Yehova Ndipo Mudzadalitsidwa
Tikamasinkhasinkha ndi kuyamikila zinthu zabwino zimene Yehova waticitila, tidzakhala ndi mzimu woyamikila. Kukhala ndi mtima woyamikila kudzatithandiza kugonjetsa mzimu wosafuna kuyamikila ndipo tidzapilila mayeselo. Lemba lathu la caka ca 2015 lidzatikumbutsa za mfundo imeneyi kwa caka conse.
▪ Cifukwa Cake Timacita Mgonelo wa Ambuye
Nkhani imeneyi itionetsa bwino cifukwa cake tiyenela kucita mwambo wokumbukila imfa ya Yesu. Idzafotokoza cimene mkate ndi vinyo zimene timagwilitsila nchito pa Cikumbutso zimaimila. Idzafotokozanso mmene munthu amadziŵila kuti ayenela kudya zizindikilo zimenezo. Nkhaniyi idzatithandiza kuona zimene aliyense wa ife ayenela kucita pokonzekela Mgonelo wa Ambuye.
▪ Khalani ndi Banja Lolimba ndi Lacimwemwe
▪ Lolani Yehova Kulimbitsa ndi Kuteteza Cikwati Canu
Amene ali pa banja akulimbana ndi mavuto ndi mayeselo ambili. Koma ndi thandizo la Yehova, n’zotheka kukhala ndi cikwati colimba ndi cacimwemwe. Nkhani yoyamba idzafotokoza njila zisanu zimene zingathandize cikwati kukhala colimba ndi cokhalitsa, ndiponso cimene cingathandize okwatilanawo kuti asalekane. Nkhani yaciŵili idzafokoza zinthu zimene okwatilana ayenela kucita kuti cikwati cao cikhale colimba mwakuuzimu.
▪ Kodi N’zotheka Kukhala m’Cikondi Ceniceni?
Kodi cikondi ceniceni cimene cimakhala pakati pa mwamuna ndi mkazi n’cotani? Kodi n’zotheka kukhala m’cikondi ceniceni? Kodi cikondi cimeneco cingasonyezedwe bwanji? Dziŵani zimene Nyimbo ya Solomo imatiphunzitsa ponena za cikondi ceniceni.
NKHANI ZINA M’MAGAZINI INO
PA CIKUTO: Akulalikila atagwila Baibulo m’manja, mumzinda wokongola wocedwa Grindelwald, ndipo mapili amene akuonekela ca kumbuyo amacedwa Bernese Alps
SWITZERLAND
KULI ANTHU
7,876,000
OFALITSA
18,646
OPEZEKA PA CIKUMBUTSO (2013)
31,980