CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | YESAYA 47-51
Kumvela Yehova Kumabweletsa Madalitso
48:17
Mwacikondi Yehova amationetsa ‘njila imene tiyenela kuyendamo’ kuti tikondwele na umoyo. Tikamumvela zinthu zimatiyendela bwino.
“Mtendele . . . udzakhala ngati mtsinje”
48:18
Yehova akulonjeza bata na mtendele woculuka woyendelela monga mtsinje.
“Cilungamo . . . cidzakhala ngati mafunde a m’nyanja”
Zocita zathu zacilungamo zingakhale zosaŵelengeka monga mafunde a m’nyanja